< Откровение ап. Иоанна Богослова 3 >

1 И Ангелу Сардийския церкве напиши: тако глаголет Имеяй седмь духов Божиих и седмь звезд: вем твоя дела, яко имя имаши яко жив, а мертв еси.
“Lembera mngelo wampingo wa ku Sarde kuti: Awa ndi mawu ochokera kwa amene amasunga mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu ndi nyenyezi zisanu ndi ziwiri. Iye akuti: Ndimadziwa ntchito zako; umadziwika kuti ndiwe wamoyo koma ndiwe wakufa.
2 Буди бдя и утверждая прочая, имже умрети: не обретох бо дел твоих скончаных пред Богом (твоим).
Dzuka! Limbitsa zimene zatsalira zomwe zatsala pangʼono kufa, pakuti ndaona kuti ntchito zako nʼzosakwanira pamaso pa Mulungu.
3 Поминай убо, како приял еси и слышал еси, и соблюдай и покайся. Аще убо не бдиши, прииду на тя яко тать, и не имаши почути, в кий час прииду на тя.
Choncho, kumbukira zimene unalandira ndi kumva; uzisunge ndipo ulape. Koma ngati sudzuka, ndidzabwera ngati mbala ndipo sudzadziwa nthawi imene ndidzabwere kwanu.
4 Но имаши мало имен и в Сардии, иже не оскверниша риз своих, и ходити имут со Мною в белых, яко достойни суть.
Komabe uli ndi anthu angapo mu Sarde amene sanadetse zovala zawo. Amenewa adzayenda ndi Ine atavala zoyera popeza ndi oyenera kutero.
5 Побеждаяй, той облечется в ризы белыя, и не имам отмыти имене его от книг животных, и исповем имя его пред Отцем Моим и пред Ангелы Его.
Amene adzapambane adzavala zoyera ngati ena aja. Sindidzafafaniza dzina lake mʼbuku lamoyo, koma ndidzamuchitira umboni pamaso pa Atate anga ndi angelo ake.
6 Имеяй ухо да слышит, что Дух глаголет церквам.
Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo.”
7 И Ангелу Филаделфийския церкве напиши: тако глаголет Святый Истинный, имеяй ключь Давидов, отверзаяй, и никтоже затворит, затворяяй, и никтоже отверзет:
“Lembera mngelo wampingo wa ku Filadefiya kuti: Awa ndi mawu ochokera kwa amene ndi woyera ndi woonadi, amene ali ndi kiyi ya Davide. Iye akatsekula palibe amene angatseke; ndipo akatseka palibe amene angatsekule.
8 вем твоя дела: се, дах пред тобою двери отверсты, и никтоже может затворити их: яко малу имаши силу, и соблюл еси Мое слово, и не отверглся еси имене Моего.
Iye akuti, ‘Ine ndimadziwa ntchito zako. Taona, ndakutsekulira pa khomo ndipo palibe wina amene angatseke. Ndikudziwa kuti uli ndi mphamvu zochepa komabe wasunga mawu anga ndipo sunandikane.
9 Се, даю от сонмища сатанина глаголющыяся быти Иудеи, и не суть, но лгут: се, сотворю их, да приидут и поклонятся пред ногама твоима, и уразумеют, яко Аз возлюбих тя.
Amene ndi mpingo wa Satana, amene amadzitcha kuti ndi Ayuda pamene sali choncho, koma ndi onama, ndidzawabweretsa kwa inu ndi kuwagwetsa pansi pa mapazi anu kuti adzazindikire kuti ndimakukondani.
10 Яко соблюл еси слово терпения Моего, и Аз тя соблюду от годины искушения, хотящия приити на всю вселенную искусити живущыя на земли.
Popeza mwasunga mawu anga woti mupirire ndipo mwawugwira mtima, Inenso ndidzakupulumutsani nthawi ya mayesero imene idzabwera pa dziko lonse lapansi kuyesa onse okhala pa dziko lapansi.
11 Се, гряду скоро: держи, еже имаши, да никтоже приимет венца твоего.
Ine ndikubwera msanga. Gwiritsitsa chimene uli nacho kuti wina angakulande chipewa chako chaufumu.
12 Побеждающаго сотворю столпа в церкви Бога Моего, и боле не имать изыти ктому: и напишу на нем имя Бога Моего и имя града Бога Моего, новаго Иерусалима, сходящаго с небес от Бога Моего, и имя Мое новое.
Iye amene adzapambane ndidzamusandutsa mzati wa mʼNyumba ya Mulungu wanga. Sadzatulukamonso. Pa iye ndidzalemba dzina la Mulungu wanga ndi dzina la mzinda wa Mulungu wanga, Yerusalemu watsopano, umene ukubwera pansi kuchokera kumwamba kwa Mulungu wanga; ndipo pa iye ndidzalembanso dzina langa latsopano.
13 Имеяй ухо да слышит, что Дух глаголет церквам.
Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo.’”
14 И Ангелу Лаодикийския церкве напиши: тако глаголет Аминь, свидетель верный и истинный, начаток создания Божия:
“Lembera mngelo wampingo wa ku Laodikaya kuti: Awa ndi mawu ochokera kwa Ameni, mboni yokhulupirika ndi yoona, gwero la zolengedwa zonse za Mulungu.
15 вем твоя дела, яко ни студен еси ни тепл: не да студен бы был ни тепл.
Ine ndimadziwa ntchito zako, kuti sindiwe wozizira kapena wotentha. Ndikanakonda ukanakhala wozizira kapena wotentha!
16 Тако, яко обуморен еси, и ни тепл ни студен, изблевати тя от уст Моих имам.
Tsono popeza ndiwe wofunda chabe, sindiwe wotentha kapena wozizira, ndatsala pangʼono kuti ndikulavule mʼkamwa mwanga.
17 Зане глаголеши, яко богат есмь и обогатихся и ничтоже требую: и не веси, яко ты еси окаянен и беден, и нищь и слеп и наг.
Iwe umati: ‘Ndine wolemera, ndine wachuma ndipo sindisowa kanthu.’ Koma sudziwa kuti ndiwe wovutika, womvetsa chisoni, waumphawi, wosaona ndi wamaliseche.
18 Совещаю тебе купити от Мене злато разжжено огнем, да обогатишися, и одеяние бело, да облечешися, и да не явится срамота наготы твоея: и коллурием помажи очи твои, да видиши.
Ndikukulangiza kuti ugule kwa Ine golide woyengedwa ndi moto kuti ukhale wolemera. Ugule zovala zoyera kuti uvale ndi kuphimba umaliseche wako wochititsa manyaziwo. Ndiponso ugule kwa Ine mankhwala a mʼmaso kuti uwone.
19 Аз, ихже аще люблю, обличаю и наказую. Ревнуй убо и покайся.
Amene ndimawakonda ndimawadzudzula ndi kuwalanga. Choncho chita changu ndipo lapa.
20 Се, стою при дверех и толку: аще кто услышит глас Мой и отверзет двери, вниду к нему и вечеряю с ним, и той со Мною.
Taonani ndayima pa khomo ndikugogoda. Ngati wina amva mawu anga natsekula chitseko, Ine ndidzalowamo ndi kudya naye, Ine ndi iyeyo.
21 Побеждающему дам сести со Мною на престоле Моем, якоже и Аз победих и седох со Отцем Моим на престоле Его.
Amene adzapambana, ndidzamupatsa ufulu wokhala nane pamodzi pa mpando wanga waufumu monga mmene Ine ndinapambana ndi kukhala pansi ndi Atate anga pa mpando wawo waufumu.
22 Имеяй ухо да слышит, что Дух глаголет церквам.
Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo.”

< Откровение ап. Иоанна Богослова 3 >