< Книга пророка Иеремии 17 >

1 Грех Иудин написан есть писалом железным на ногти адамантове, начертан на скрижали сердца их и на розех олтарей их.
“Tchimo la Yuda lazokotedwa ndi cholembera cha chitsulo, lalembedwa ndi msonga ya mwala wadayimondi. Uchimowo walembedwa pa mitima yawo ndiponso pa nyanga za maguwa awo.
2 Егда воспомянут сынове их олтари своя и дубравы своя при древе лиственне и на холмех высоких,
Ngakhale ana awo amakumbukira maguwa awo ndi zoyimiritsa ngati zifanizo za mulungu wawo Asera, pa tsinde la mitengo ya masamba ambiri, pa mapiri aatali mʼdzikomo.
3 о, нагорный (жителю)! Крепость твою и сокровища твоя в расхищение дам, и высокая твоя, грех ради твоих, яже во всех пределех твоих,
Chuma chanu ndiponso katundu wanu yense ndidzazipereka kwa ofunkha kuti zikhale dipo lawo chifukwa cha machimo ochitika mʼdziko lonse.
4 и останешися един от наследия твоего, еже дах тебе: и служити тя сотворю врагом твоим в земли, еяже не веси: яко огнь разжегл еси в ярости Моей, даже во век горети будет. Сия глаголет Господь:
Mudzataya dziko limene ndinakupatsani kuti likhale cholowa chanu. Ndidzakusandutsani akapolo otumikira adani anu mʼdziko limene inu simukulidziwa, chifukwa mwabutsa mkwiyo wanga ngati moto, ndipo udzayaka mpaka muyaya.”
5 проклят человек, иже надеется на человека и утвердит плоть мышцы своея на нем, и от Господа отступит сердце его:
Yehova akuti, “Ndi wotembereredwa munthu amene amadalira munthu mnzake, amene amatsamira pa munthu mnzake kuti amuthandize pamene mtima wake wafulatira Yehova.
6 и будет яко дивия мирика в пустыни и не узрит, егда приидут благая, и обитати будет в сухоте и в пустыни, в земли сланей и необитаемей.
Munthuyo adzakhala ngati chitsamba mʼchipululu; iye sadzapeza zabwino. Adzakhala mʼchipululu mopanda madzi, mʼdziko lamchere limene munthu sangathe kukhalamo.
7 И благословен человек, иже надеется на Господа, и будет Господь упование его:
“Koma ndi wodala munthu amene amadalira Yehova, amene amatsamira pa Iye.
8 и будет яко древо насажденное при водах, и во влаге пустит корение свое: не убоится, егда приидет зной, и будет на нем стеблие зелено, и во время бездождия не устрашится и не престанет творити плода.
Adzakhala ngati mtengo wodzalidwa mʼmphepete mwa madzi umene umatambalitsa mizu yake mʼmbali mwa mtsinje. Mtengowo suopa pamene kukutentha; masamba ake amakhala obiriwira nthawi zonse. Suchita mantha pa chaka cha chilala ndipo sulephera kubereka chipatso.”
9 Глубоко сердце (человеку) паче всех, и человек есть, и кто познает его?
Mtima wa munthu ndi wonyenga kupambana zinthu zonse ndipo kuyipa kwake nʼkosachizika. Ndani angathe kuwumvetsa?
10 Аз Господь испытуяй сердца и искушаяй утробы, еже воздати комуждо по пути его и по плодом изобретений его.
“Ine Yehova ndimafufuza mtima ndi kuyesa maganizo, ndimachitira munthu aliyense molingana ndi makhalidwe ake ndiponso moyenera ntchito zake.”
11 Возгласи ряб, собра, ихже не роди, творяй богатство свое не с судом: в преполовении дний своих оставит е и на последок свой будет безумен.
Munthu amene amapeza chuma mwachinyengo ali ngati nkhwali imene imafungatira mazira amene sinayikire. Pamene ali pakatikati pa moyo wake, chumacho chidzamuthera, ndipo potsiriza adzasanduka chitsiru.
12 Престол славы возвышен от начала, место святыни нашея.
Nyumba yathu yopemphereramo ili ngati mpando waufumu waulemerero wokhazikitsidwa pa phiri lalitali chiyambire.
13 Чаяние Израилево, Господи! Вси оставляющии Тя да постыдятся, отступающии (от Тебе) на земли да напишутся, яко оставиша источник живых вод, Господа.
Inu Yehova, chiyembekezo cha Israeli, onse amene amakusiyani adzachita manyazi. Iwo amene amakufulatirani mayina awo adzafafanizika ngati olembedwa pa fumbi chifukwa anakana Yehova, kasupe wa madzi amoyo.
14 Изцели мя, Господи, и изцелею: спаси мя, и спасен буду, яко хвала моя Ты еси.
Inu Yehova, chiritseni, ndipo ndidzachira; pulumutseni ndipo ndidzapulumuka, chifukwa ndinu amene ndimakutamandani.
15 Се, тии глаголют ко мне: где есть слово Господне? Да приидет.
Anthu akumandinena kuti, “Mawu a Yehova ali kuti? Zichitiketu lero kuti tizione!”
16 Аз же не утрудихся, Тебе (пастырю) последуяй, и дне человеча не пожелах: Ты веси исходящая от устен моих, пред лицем Твоим суть:
Ine sindinakuwumirizeni kuti muwalange. Mukudziwa kuti ine sindilakalaka tsiku la tsoka. Zonse zimene ndinayankhula Inu mukuzidziwa.
17 не буди ми во отчуждение, упование мое Ты в день лют.
Musandichititse mantha; ndinu pothawira panga pa tsiku la mavuto.
18 Да постыдятся гонящии мя, аз же да не постыждуся: да устрашатся тии, аз же да не устрашуся: наведи на них день озлобления, сугубым сокрушением сотри их.
Ondizunza anga achite manyazi, koma musandichititse manyazi; iwo achite mantha kwambiri, koma ine mundichotsere manthawo. Tsiku la mavuto liwafikire; ndipo muwawononge kotheratu.
19 Сия глаголет Господь ко мне: иди и стани во вратех сынов людий твоих, имиже входят царие Иудины и исходят, и во всех вратех Иерусалимских и речеши к ним:
Yehova anandiwuza kuti, “Pita ukayime pa chipata chodzerapo anthu, chimene mafumu a ku Yuda amalowerapo ndi kutulukirapo. Ukayimenso pa zipata zina zonse za Yerusalemu.
20 слышите слово Господне, царие Иудины и вся Иудеа и весь Иерусалим, входящии во врата сия.
Ukawawuze kuti, ‘Imvani mawu a Yehova, inu mafumu onse a ku Yuda ndi anthu onse a ku Yuda ndi inu nonse okhala mu Yerusalemu amene mumatulukira pa zipata izi.’
21 Сия глаголет Господь: сохраните душы вашя и не носите бремен в день суббот, и не исходите враты Иерусалима,
Yehova akuti: samalani kuti pa tsiku la Sabata musanyamule katundu kapena kulowa naye pa zipata za Yerusalemu.
22 и не износите бремен из домов ваших в день субботный, и всякаго дела не творите: освятите день субботный, якоже заповедах отцем вашым:
Musalowetse katundu mʼnyumba zanu kapena kugwira ntchito pa tsiku la Sabata, koma mulipatule tsiku la Sabatalo, monga ndinalamulira makolo anu.
23 и не услышаша, ни приклониша уха своего, но ожесточиша выи своя паче отец своих, да не услышат мя и да не приимут наказания.
Komatu iwo sanandimvere kapena kulabadira. Ndi mitima yawo yowumayo sanamvere kapena kulandira malangizo anga.
24 И будет, аще послушаете Мене, глаголет Господь, еже не вносити бремен во врата града сего в день субботный, и святити день субботный, не творити в онь всякаго дела,
Yehova akuti, ‘Muzimvera Ine ndi kuleka kulowetsa kapena kutulutsa katundu pa zipata za mzinda pa tsiku la Sabata. Muzisunga tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika posachita ntchito iliyonse pa tsikuli.
25 и внидут во врата града сего царие и началницы, седящии на престоле Давидове и восходящии на колесницах и конех своих, тии и началницы их, мужие Иудины и обитателие Иерусалима: и обитати будут во граде сем во веки:
Mukatero ndiye mafumu anu amene akukhala pa mpando wa Davide adzatulukira pa zipata za mzindawu pamodzi ndi nduna zawo. Iwo pamodzi ndi nduna zawo azidzalowa atakwera magaleta ndi akavalo, akuperekezedwa ndi anthu a ku Yuda ndi amene amakhala mu Yerusalemu, ndipo mu mzinda muno mudzakhala anthu mpaka muyaya.
26 и приидут от градов Иудиных и от окрестных Иерусалима, и от земли Вениамини и от польных, и от горних и от юга, носяще всесожжения и жертву, и фимиам и манау и ливан, носяще хвалу в дом Господень.
Anthu adzabwera kuchokera ku mizinda ya Yuda ndi ku midzi yozungulira Yerusalemu, kuchokera ku dziko la Benjamini ndi ku mapiri a kumadzulo, kuchokera ku dziko la mapiri ndi ku Negevi. Adzabwera ndi nsembe zopsereza, nsembe zaufa ndi za chakudya, nsembe za lubani ndi zopereka zachiyamiko ku nyumba ya Yehova.
27 И будет, аще не послушаете Мене еже святити день субботный и не носити бремен, ниже входити вратами Иерусалима в день субботный, то зажгу огнь во вратех его, и пожрет домы Иерусалимли и не угаснет.
Koma ngati simundimvera; mukapanda kusunga tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika ndi kumanyamula katundu nʼkumalowa naye pa zipata za Yerusalemu pa tsikuli, Ine ndidzabutsa moto pa zipata za Yerusalemu. Moto umenewo udzanyeketsa nyumba zaufumu za ku Yerusalemu ndipo moto wake sudzazima.’”

< Книга пророка Иеремии 17 >