< 1 Солуњанима 3 >

1 Зато не могући више трпети наумисмо сами остати у Атини,
Nʼchifukwa chake pamene sitinathenso kupirira, tinaganiza kuti kunali bwino kuti atisiye tokha ku Atene.
2 И посласмо Тимотија, брата свог и слугу Божијег, и помагача свог у јеванђељу Христовом, да вас утврди и утеши у вери вашој;
Tinatuma Timoteyo, mʼbale wathu ndi mnzathu wogwira naye ntchito ya Mulungu yofalitsa Uthenga Wabwino wa Khristu, kuti adzakulimbitseni mitima ndi kukukhazikitsani mʼchikhulupiriro chanu,
3 Да се нико не смете у овим невољама; јер сами знате да смо на то одређени.
ndi cholinga chakuti wina asasunthike ndi mavutowa. Inu mukudziwa bwino lomwe kuti ndife oyenera kukumana ndi zimenezi.
4 Јер кад бејасмо код вас казасмо вам напред да ћемо падати у невоље, које и би, и знате.
Kunena zoona, pamene tinali nanu, tinkakuwuzani kuti tidzayenera kuzunzidwa. Ndipo monga mukudziwa bwino, zimenezi zinachitikadi.
5 Тога ради и ја не могући више трпети послах да познам веру вашу, да вас како не искуша кушач, и да узалуд не буде труд наш.
Nʼchifukwa chake, pamene sindikanathanso kupirira, ndinatuma Timoteyo kuti adzaone mmene chikhulupiriro chanu chilili. Ndinkaopa kuti mwina wonyengayo, wakunyengani mʼnjira ina yake ndi kuti ntchito zathu zasanduka zosapindula.
6 А сад кад дође Тимотије к нама од вас и јави нам вашу веру и љубав, и да имате добар спомен о нама свагда, желећи нас видети, као и ми вас,
Koma tsopano Timoteyo wabwera kuchokera kwanuko ndipo watibweretsera nkhani yabwino ya chikhulupiriro chanu ndi chikondi chanu. Iye watiwuzanso kuti masiku onse mumatikumbukira mokondwa, ndipo kuti mumafunitsitsa kutionanso, monga momwe ifenso timalakalakira kukuonani inuyo.
7 Зато се утешисмо, браћо, вама у свакој жалости и невољи својој вашом вером;
Motero abale, mʼmasautso ndi mʼmazunzo athu onse, chikhulupiriro chanu chatilimbikitsa.
8 Јер смо ми сад живи кад ви стојите у Господу.
Ife tsopano tili moyodi, pakuti mukuyima molimbika mwa Ambuye.
9 Јер какву хвалу можемо дати Богу за вас, за сваку радост којом се радујемо вас ради пред Богом својим?
Tingathe bwanji kuyamika Mulungu mokwanira poona chimwemwe chonse chimene tili nacho pamaso pa Mulungu wathu chifukwa cha inu?
10 Дан и ноћ молимо се Богу преизобилно да видимо лице ваше, и да испунимо недостатак вере ваше.
Usana ndi usiku timapemphera ndi mtima wonse kuti tionanenso nanu, ndi kukwaniritsa zimene zikusowa pa chikhulupiriro chanu.
11 А сам Бог и Отац наш и Господ наш Исус Христос да управи пут наш к вама.
Tikupempha kuti Mulungu ndi Atate athu mwini, ndi Ambuye athu Yesu, atikonzere njira yabwino kuti tidzafike kwanuko.
12 А вас Господ да умножи, и да имате изобилну љубав један к другом и к свима, као и ми к вама.
Ambuye achulukitse chikondi chanu ndi kuti chisefukire kwa wina ndi mnzake ndiponso kwa wina aliyense, monga momwe chikondi chathu chichitira kwa inu.
13 Да би се утврдила срца ваша без кривице у светињи пред Богом и Оцем нашим, за долазак Господа нашег Исуса Христа са свима светима Његовим. Амин.
Iye alimbikitse mitima yanu kuti mukhale opanda cholakwa ndi oyera mtima pamaso pa Mulungu ndi Atate athu pamene Ambuye athu Yesu akubwera ndi oyera ake onse.

< 1 Солуњанима 3 >