< К Римлянам 3 >

1 Итак, какое преимущество быть Иудеем или какая польза от обрезания?
Nanga kodi pali ubwino wotani pokhala Myuda, kapena muli ubwino wanjinso mu mdulidwe?
2 Великое преимущество во всех отношениях, а наипаче в том, что им вверено слово Божие.
Ubwino wake ndi wambiri mʼnjira zonse! Choyambirira iwo anapatsidwa Mawu a Mulungu kuti awasunge.
3 Ибо что же? Если некоторые и неверны были, неверность их уничтожит ли верность Божию?
Nanga zili bwanji ngati ena analibe chikhulupiriro? Kodi kupanda chikhulupiriro kwawo kukanalepheretsa kukhulupirika kwa Mulungu?
4 Никак. Бог верен, а всякий человек лжив, как написано: Ты праведен в словах Твоих и победишь в суде Твоем.
Ayi. Mʼnjira iliyonse ayi! Mulungu akhale woona, ndi munthu aliyense akhale wonama. Monga kwalembedwa kuti, “Kotero kuti inu mwapezeka kuti ndinu wolungama pamene muyankhula ndi kupambana pamene muweruza.”
5 Если же наша неправда открывает правду Божию, то что скажем? Не будет ли Бог несправедлив, когда изъявляет гнев? Говорю по человеческому рассуждению.
Koma ngati kuyipa mtima kwathu kuonetsa poyera kuti Mulungu ndi wolungama, ife tinganene chiyani? Kodi tinganene kuti Mulungu ndi wosalungama pamene aonetsa mkwiyo wake pa ife? (Ine ndikuyankhula monga mmene anthu ena amayankhulira).
6 Никак. Ибо иначе как Богу судить мир?
Ayi. Mʼnjira iliyonse ayi! Ngati zikanakhala zotero, kodi Mulungu akanaweruza bwanji dziko lapansi?
7 Ибо, если верность Божия возвышается моею неверностью к славе Божией, за что еще меня же судить, как грешника?
Wina atanena kuti, “Ngati kunama kwanga kukuonetsa koposa kuti Mulungu ndi woona, ndi kuwonjezera pa ulemerero wake, nanga nʼchifukwa chiyani ndikuweruzidwa kuti ndine wochimwa?”
8 И не делать ли нам зло, чтобы вышло добро, как некоторые злословят нас и говорят, будто мы так учим? Праведен суд на таковых.
Nʼchifukwa chiyani osanena kuti, monga ena amanena mosasamala kuti, “Tiyeni tichite zoyipa kuti zabwino zionekere?” Anthu onena zoterewa kulangidwa kwawo ndi koyenera.
9 Итак, что же? Имеем ли мы преимущество? Нисколько. Ибо мы уже доказали, что, как Иудеи, так и Еллины, все под грехом,
Kodi timalize bwanji? Kodi Ayuda ndife oposa anthu ena? Ayi. Mʼnjira iliyonse ayi! Ife tinanena kale kuti Ayuda ndi a mitundu ina omwe ndi ochimwa.
10 как написано: нет праведного ни одного;
Monga kwalembedwa kuti, “Palibe munthu wolungama, inde palibe ndi mmodzi yemwe.
11 нет разумеющего; никто не ищет Бога;
Palibe ndi mmodzi yemwe amene amazindikira, palibe amene amafunafuna Mulungu.
12 все совратились с пути, до одного негодны; нет делающего добро, нет ни одного.
Onse apatukira kumbali, onse pamodzi asanduka opandapake. Palibe ndi mmodzi yemwe amene amachita zabwino, palibe ngakhale mmodzi.”
13 Гортань их - открытый гроб; языком своим обманывают; яд аспидов на губах их.
“Kummero kwawo kuli ngati manda apululu; ndi lilime lawo amayankhula zachinyengo.” “Ululu wa mamba uli pa milomo yawo.”
14 Уста их полны злословия и горечи.
“Mʼkamwa mwawo ndi modzaza ndi zotemberera ndi mawu owawa.”
15 Ноги их быстры на пролитие крови;
“Mapazi awo afulumira kukakhetsa magazi.
16 разрушение и пагуба на путях их;
Kusakaza ndi chisoni kumaonekera mʼnjira zawo,
17 они не знают пути мира.
ndipo njira ya mtendere sayidziwa.”
18 Нет страха Божия перед глазами их.
“Saopa Mulungu ndi pangʼono pomwe.”
19 Но мы знаем, что закон, если что говорит, говорит к состоящим под законом, так что заграждаются всякие уста, и весь мир становится виновен пред Богом,
Tsopano tikudziwa kuti chilichonse Malamulo amanena, amanena kwa amene amalamulidwa ndi Malamulowo, ndi cholinga chakuti aliyense asowe chonena, ndipo dziko lonse lidzayimbidwa mlandu ndi Mulungu.
20 потому что делами закона не оправдается пред Ним никакая плоть; ибо законом познается грех.
Chifukwa chake palibe mmodzi amene adzayesedwa wolungama pamaso pake chifukwa chosunga Malamulo, kuti ife timazindikira tchimo kupyolera mu Malamulo.
21 Но ныне, независимо от закона, явилась правда Божия, о которой свидетельствуют закон и пророки,
Koma tsopano chilungamo chochokera kwa Mulungu, osati chochokera ku Malamulo, chaonetsedwa. Ichi ndi chimene Malamulo ndi Aneneri amachitira umboni.
22 правда Божия через веру в Иисуса Христа во всех и на всех верующих, ибо нет различия,
Timakhala olungama pamaso pa Mulungu pamene takhulupirira Yesu Khristu. Mulungu amachitira zimenezi anthu onse amene akhulupirira Khristu. Palibe kusiyana pakati pa Myuda ndi a mitundu ina,
23 потому что все согрешили и лишены славы Божией,
pakuti onse anachimwa naperewera pa ulemerero wa Mulungu
24 получая оправдание даром, по благодати Его, искуплением во Христе Иисусе,
ndipo onse alungamitsidwa mwaulere mwa chisomo chake chifukwa cha Khristu Yesu amene anawawombola.
25 Которого Бог предложил в жертву умилостивления в Крови Его через веру, для показания правды Его в прощении грехов, соделанных прежде,
Mulungu anamupereka Iyeyu kuti pokhetsa magazi ake, akhale nsembe yokhululukira machimo. Mulungu anachita zimenezi kufuna kuonetsa chilungamo chake. Chifukwa cha kuleza mtima kwake, sanalange anthu chifukwa cha machimo amene anachita kale.
26 во время долготерпения Божия, к показанию правды Его в настоящее время, да явится Он праведным и оправдывающим верующего в Иисуса.
Iye anachita izi kuti aonetse chilungamo chake lero lino. Anthu azindikire kuti Iye ndi wolungama ndipo amalungamitsa aliyense amene akhulupirira Yesu.
27 Где же то, чем бы хвалиться? Уничтожено. Каким законом? Законом дел? Нет, но законом веры.
Nanga tsono pamenepa munthu anganyadenso? Kunyadatu kwachotsedwa. Chifukwa cha Malamulo? Kodi Malamulo samafuna ntchito za munthu? Ayi, koma mwachikhulupiriro.
28 Ибо мы признаем, что человек оправдывается верою, независимо от дел закона.
Ife tikunenabe kuti munthu amalungamitsidwa mwachikhulupiriro osati mwakusunga Malamulo.
29 Неужели Бог есть Бог Иудеев только, а не и язычников? Конечно, и язычников,
Kodi Mulungu ndi Mulungu wa Ayuda okha? Kodi si Mulungu wa a mitundu inanso? Inde wa a mitundu inanso,
30 потому что один Бог, Который оправдает обрезанных по вере и необрезанных через веру.
popeza ndi Mulungu mmodzi yemweyo amene adzalungamitsa mwachikhulupiriro ochita mdulidwe ndi osachita mdulidwe kudzera mʼchikhulupiriro chomwecho.
31 Итак, мы уничтожаем закон верою? Никак; но закон утверждаем.
Kodi tsono ife, tikutaya Malamulo pamene tikunena kuti pafunika chikhulupiriro? Ayi. Mʼnjira iliyonse ayi! Komatu ife tikukwaniritsadi Malamulo.

< К Римлянам 3 >