< Откровение 7 >

1 И после сего видел я четырех Ангелов, стоящих на четырех углах земли, держащих четыре ветра земли, чтобы не дул ветер ни на землю, ни на море, ни на какое дерево.
Zitatha izi ndinaona angelo anayi atayima pa mbali zinayi za dziko lapansi, atagwira mphepo zinayi za dziko lapansi kuletsa kuti mphepo iliyonse isawombe pa dziko kapena pa nyanja kapena pa mtengo uliwonse.
2 И видел я иного Ангела, восходящего от востока солнца и имеющего печать Бога живаго. И воскликнул он громким голосом к четырем Ангелам, которым дано вредить земле и морю, говоря:
Kenaka ndinaona mngelo wina akuchokera kummawa, ali ndi chidindo cha Mulungu wamoyo. Iye anafuwulira angelo anayi aja amene anapatsidwa mphamvu yowononga dziko ndi nyanja kuti,
3 не делайте вреда ни земле, ни морю, ни деревам, доколе не положим печати на челах рабов Бога нашего.
“Musawononge dziko, nyanja ndi mitengo kufikira titalemba chizindikiro pa mphumi za atumiki a Mulungu wathu.”
4 И я слышал число запечатленных: запечатленных было сто сорок четыре тысячи из всех колен сынов Израилевых.
Choncho ndinamva chiwerengero cha amene ankayenera kulembedwa chizindikiro aja. Analipo okwanira 144,000 kuchokera ku mafuko onse a Israeli.
5 Из колена Иудина запечатлено двенадцать тысяч; из колена Рувимова запечатлено двенадцать тысяч; из колена Гадова запечатлено двенадцать тысяч;
Ochokera fuko la Yuda analipo 12,000 amene analembedwa chizindikiro. Ochokera fuko la Rubeni analipo 12,000; ochokera fuko la Gadi analipo 12,000;
6 из колена Асирова запечатлено двенадцать тысяч; из колена Неффалимова запечатлено двенадцать тысяч; из колена Манассиина запечатлено двенадцать тысяч;
ochokera fuko la Aseri analipo 12,000; ochokera fuko la Nafutali analipo 12,000; ochokera fuko la Manase analipo 12,000;
7 из колена Симеонова запечатлено двенадцать тысяч; из колена Левиина запечатлено двенадцать тысяч; из колена Иссахарова запечатлено двенадцать тысяч;
ochokera fuko la Simeoni analipo 12,000; ochokera fuko la Levi analipo 12,000; ochokera fuko la Isakara analipo 12,000;
8 из колена Завулонова запечатлено двенадцать тысяч; из колена Иосифова запечатлено двенадцать тысяч; из колена Вениаминова запечатлено двенадцать тысяч.
ochokera fuko la Zebuloni analipo 12,000; ochokera fuko la Yosefe analipo 12,000; ochokera fuko la Benjamini analipo 12,000.
9 После сего взглянул я, и вот, великое множество людей, которого никто не мог перечесть, из всех племен и колен, и народов и языков, стояло пред престолы и пред Агнцем в белых одеждах и с пальмовыми ветвями в руках своих.
Zitatha izi ndinayangʼana patsogolo panga ndipo ndinaona gulu lalikulu la anthu loti munthu sangathe kuliwerenga lochokera dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu wa anthu uliwonse ndi chiyankhulo chilichonse, atayima patsogolo pa mpando waufumu, pamaso pa Mwana Wankhosa. Iwo anali atavala mikanjo yoyera ndi kunyamula nthambi za kanjedza mʼmanja mwawo.
10 И восклицали громким голосом, говоря: спасение Богу нашему, сидящему на престоле, и Агнцу!
Ndipo ankafuwula mokweza kuti: “Chipulumutso chimachokera kwa Mulungu wathu, wokhala pa mpando waufumu ndi kwa Mwana Wankhosa.”
11 И все Ангелы стояли вокруг престола и старцев и четырех животных, и пали перед престолом на лица свои, и поклонились Богу,
“Angelo onse anayimirira kuzungulira mpando waufumu uja, kuzunguliranso akuluakulu aja ndi zamoyo zinayi zija. Angelo aja anadzigwetsa pansi chafufumimba patsogolo pa mpando waufumu napembedza Mulungu.
12 говоря: аминь! благословение и слава, и премудрость и благодарение, и честь и сила и крепость Богу нашему во веки веков! Аминь. (aiōn g165)
Iwo anati, “Ameni! Matamando ndi ulemerero, nzeru, mayamiko, ulemu, ulamuliro ndi mphamvu zikhale kwa Mulungu wathu kunthawi zanthawi, Ameni!” (aiōn g165)
13 И, начав речь, один из старцев спросил меня: сии облеченные в белые одежды кто и откуда пришли?
Pamenepo mmodzi wa akuluakulu aja anandifunsa kuti, “Kodi avala mikanjo yoyerawa ndani ndipo akuchokera kuti?”
14 Я сказал ему: ты знаешь, господин. И он сказал мне: это те, которые пришли от великой скорби; они омыли одежды свои и убелили одежды свои Кровию Агнца.
Ine ndinayankha kuti, “Mbuye wanga mukudziwa ndinu.” Tsono iye anandiwuza kuti, “Amenewa ndi amene anatuluka mʼmazunzo aakulu aja. Anachapa mikanjo yawo naziyeretsa mʼmagazi a Mwana Wankhosa.
15 За это они пребывают ныне перед престолом Бога и служат Ему день и ночь в храме Его, и Сидящий на престоле будет обитать в них.
Nʼchifukwa chake, “iwowa ali patsogolo pa mpando waufumu wa Mulungu ndipo akutumikira usana ndi usiku mʼNyumba ya Mulungu; ndipo Iye wokhala pa mpando waufumu adzawaphimba ndi tenti yake.
16 Они не будут уже ни алкать, ни жаждать, и не будет палить их солнце и никакой зной,
‘Iwowa sadzamvanso njala, sadzamvanso ludzu, dzuwa kapena kutentha kulikonse sikudzawawotcha.’
17 ибо Агнец, Который среди престола, будет пасти их и водить их на живые источники вод; и отрет Бог всякую слезу с очей их.
Pakuti Mwana Wankhosa amene ali pakati pa mpando waufumu adzakhala mʼbusa wawo. ‘Iye adzawatsogolera ku akasupe a madzi amoyo.’ ‘Ndipo Mulungu adzawapukuta misozi yonse mʼmaso mwawo.’”

< Откровение 7 >