< Откровение 4 >

1 После сего я взглянул, и вот дверь отверста на небе и прежний голос, который я слышал как бы звук трубы, говоривший со мною, сказал: взойди сюда, и покажу тебе, чему надлежит быть после сего.
Kenaka, nditayangʼana patsogolo panga ndinaona khomo lotsekuka la kumwamba. Ndipo liwu lija ndinalimva poyamba lokhala ngati lipenga linati, “Bwera kuno, ndipo ndidzakuonetsa zimene zichitike zikatha izi.”
2 И тотчас я был в духе; и вот престол стоял на небе, и на престоле был Сидящий;
Nthawi yomweyo ndinatengedwa ndi Mzimu Woyera, ndipo patsogolo panga ndinaona mpando waufumu wina atakhalapo.
3 и Сей Сидящий видом был подобен камню яспису и сардису; и радуга вокруг престола, видом подобная смарагду.
Ndipo amene anakhalapoyo anali wa maonekedwe ngati miyala ya jasipa ndi sardiyo. Utawaleza wooneka ngati simaragido unazinga mpando waufumuwo.
4 И вокруг престола двадцать четыре престола; а на престолах видел я сидевших двадцать четыре старца, которые облечены были в белые одежды и имели на головах своих золотые венцы.
Kuzungulira mpando waufumuwu panalinso mipando ina yaufumu yokwana 24 ndipo panakhala akuluakulu 24 atavala zoyera ndipo anavala zipewa zaufumu zagolide pamutu.
5 И от престола исходили молнии и громы и гласы, и семь светильников огненных горели перед престолом, которые суть семь духов Божиих;
Kumpando waufumuwo kunkatuluka mphenzi, phokoso ndi mabingu. Patsogolo pake pa mpando waufumuwo panali nyale zisanu ndi ziwiri zoyaka. Iyi ndiyo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu.
6 и перед престолом море стеклянное, подобное кристаллу; и посреди престола и вокруг престола четыре животных, исполненных очей спереди и сзади.
Patsogolo pa mpando waufumu pomwepo panalinso ngati nyanja yagalasi yonyezimira ngati mwala wa krustalo. Pakatinʼpakati, kuzungulira mpando waufumuwo panali zamoyo zinayi zokhala ndi maso ponseponse, kutsogolo ndi kumbuyo komwe.
7 И первое животное было подобно льву, и второе животное подобно тельцу, и третье животное имело лице, как человек, и четвертое животное подобно орлу летящему.
Chamoyo choyamba chinali ngati mkango, chachiwiri chinali ngati mwana wangʼombe, chachitatu chinali ndi nkhope ngati munthu, chachinayi chinali ngati chiwombankhanga chowuluka.
8 И каждое из четырех животных имело по шести крыл вокруг, а внутри они исполнены очей; и ни днем, ни ночью не имеют покоя, взывая: свят, свят, свят Господь Бог Вседержитель, Который был, есть и грядет.
Chamoyo chilichonse chinali ndi mapiko asanu ndi limodzi, ndipo chinali ndi maso ponseponse ndi mʼkati mwa mapiko momwe. Usana ndi usiku zimanena mosalekeza kuti,
9 И когда животные воздают славу и честь и благодарение Сидящему на престоле, Живущему во веки веков, (aiōn g165)
Nthawi zonse zamoyozo zimapereka ulemerero, ulemu ndi mayamiko kwa uja wokhala pa mpando waufumu, amene ali ndi moyo wamuyaya. (aiōn g165)
10 тогда двадцать четыре старца падают пред Сидящим на престоле, и поклоняются Живущему во веки веков, и полагают венцы свои перед престолом, говоря: (aiōn g165)
Izi zikamachitika akuluakulu 24 aja amadzigwetsa pansi pamaso pa wokhala pa mpando waufumuyo, namupembedza wokhala ndi moyo wamuyayayo. Iwo amaponya pansi zipewa zawo zaufumu patsogolo pa mpando waufumu nati: (aiōn g165)
11 достоин Ты, Господи, приять славу и честь и силу: ибо Ты сотворил все, и все по Твоей воле существует и сотворено.
“Ndinu woyeneradi kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu, Ambuye ndi Mulungu wathu, pakuti munalenga zinthu zonse, ndipo mwakufuna kwanu zinalengedwa monga zilili.”

< Откровение 4 >