< Откровение 22 +

1 И показал мне чистую реку воды жизни, светлую, как кристалл, исходящую от престола Бога и Агнца.
Ndipo mngeloyo anandionetsa mtsinje wamadzi amoyo, oyera ngati mwala wa krustalo ukutuluka ku mpando waufumu wa Mulungu ndi wa Mwana Wankhosa,
2 Среди улицы его, и по ту и по другую сторону реки, древо жизни, двенадцать раз приносящее плоды, дающее на каждый месяц плод свой; и листья дерева - для исцеления народов.
Ukuyenda pakati pa msewu waukulu wa mu mzindawo. Mbali iliyonse ya mtsinjewo kunali mtengo wamoyo, utabala zipatso khumi ndi ziwiri. Kubereka zipatso mwezi uliwonse. Ndipo masamba a mtengowo ndi mankhwala wochiritsa anthu a mitundu ina.
3 И ничего уже не будет проклятого; но престол Бога и Агнца будет в нем, и рабы Его будут служить Ему.
Sipadzakhalanso temberero lililonse. Mpando waufumu wa Mulungu ndi wa Mwana Wankhosa udzakhala mu mzindawo, ndipo atumiki ake adzamutumikira.
4 И узрят лице Его, и имя Его будет на челах их.
Iwo adzaona nkhope yake ndipo dzina lake lidzalembedwa pa mphumi zawo.
5 И ночи не будет там, и не будут иметь нужды ни в светильнике, ни в свете солнечном, ибо Господь Бог освещает их; и будут царствовать во веки веков. (aiōn g165)
Sipadzakhalanso usiku. Sadzafuna kuwala kwa nyale kapena kwa dzuwa pakuti Ambuye Mulungu adzakhala kuwala kwawo. Ndipo adzalamulira kwamuyaya. (aiōn g165)
6 И сказал мне: сии слова верны и истинны; и Господь Бог святых пророков послал Ангела Своего показать рабам Своим то, чему надлежит быть вскоре.
Mngeloyo anandiwuza kuti, “Mawu awa ndi okhulupirika ndi owona. Ambuye Mulungu wa mizimu ya aneneri anatumiza mngelo wake kudzaonetsa atumiki ake zinthu zimene ziyenera kuchitika posachedwapa.”
7 Се, гряду скоро: блажен соблюдающий слова пророчества книги сей.
“Taonani, ndikubwera posachedwa! Wodala ndi amene asunga mawu oneneratu za kutsogolo a mʼbuku ili.”
8 Я, Иоанн, видел и слышал сие. Когда же услышал и увидел, пал к ногам Ангела, показывающего мне сие, чтобы поклониться ему;
Ine Yohane, ndine amene ndinamva ndi kuona zinthu izi. Ndipo pamene ndinamva ndi kuona izi ndinagwa pansi kuti ndipembedze mngelo amene amandionetsa zimenezi.
9 но он сказал мне: смотри, не делай сего; ибо я сослужитель тебе и братьям твоим пророкам и соблюдающим слова книги сей; Богу поклонись.
Koma mngeloyo anandiwuza kuti, “Usatero ayi! Ine ndine wotumikira monga iwe pamodzi ndi abale ako aneneri ndi onse amene amasunga mawu a mʼbuku pembedzani Mulungu.”
10 И сказал мне: не запечатывай слов пророчества книги сей; ибо время близко.
Kenaka anandiwuza kuti, “Usabise mawu onena zamʼtsogolo a mʼbuku ili chifukwa nthawi yayandikira.
11 Неправедный пусть еще делает неправду; нечистый пусть еще сквернится; праведный да творит правду еще, и святый да освящается еще.
Wochita zoyipa apitirire kuchita zoyipazo; wochita zonyansa apitirire kuchita zonyansazo; wochita zabwino apitirire kuchita zabwinozo; ndipo woyera mtima apitirire kukhala woyera mtima.”
12 Се, гряду скоро, и возмездие Мое со Мною, чтобы воздать каждому по делам его.
“Taonani, ndikubwera posachedwa! Ndikubwera ndi mphotho zanga kuti ndidzapereke kwa aliyense malinga ndi zimene anachita.
13 Я есмь Алфа и Омега, начало и конец, Первый и Последний.
Ine ndine Alefa ndi Omega, Woyamba ndi Wotsiriza, Chiyambi ndi Chimaliziro ndine.
14 Блаженны те, которые соблюдают заповеди Его, чтобы иметь им право на древо жизни и войти в город воротами.
“Odala amene achapa mikanjo yawo, kuti akhale ndi ufulu wopita ku mtengo wamoyo ndi kuti akalowe mʼzipata za mu mzindawo.
15 А вне - псы и чародеи, и любодеи, и убийцы, и идолослужители, и всякий любящий и делающий неправду.
Kunja kuli agalu, amatsenga, achiwerewere, akupha anthu, opembedza mafano ndi aliyense amene amakonda bodza ndi kulichita.
16 Я, Иисус, послал Ангела Моего засвидетельствовать вам сие в церквах. Я есмь корень и потомок Давида, звезда светлая и утренняя.
“Ine Yesu, ndatuma mngelo wanga kuti achitire umboni uwu ku mipingo. Ine ndine Muzu ndi Chipatso cha Davide ndipo ndine Nthanda Yonyezimira.”
17 И Дух и невеста говорят: прииди! И слышавший да скажет: прииди! Жаждущий пусть приходит, и желающий пусть берет воду жизни даром.
Mzimu Woyera ndi mkwatibwi akuti, “Bwerani!” Ndipo amene akumva anena kuti Bwerani! Iye amene ali ndi ludzu abwere, ndipo aliyense amene afuna alandire mphatso yaulere ya madzi amoyo.
18 И я также свидетельствую всякому слышащему слова пророчества книги сей: если кто приложит что к ним, на того наложит Бог язвы, о которых написано в книге сей;
Ndikuchenjeza aliyense amene akumva mawu onena zamʼtsogolo a mʼbukuli kuti, “Ngati wina awonjezerapo kalikonse, Mulungu adzamuwonjezera miliri imene yalembedwa mʼbuku ili.
19 и если кто отнимет что от слов книги пророчества сего, у того отнимет Бог участие в книге жизни и в святом граде и в том, что написано в книге сей.
Ndipo wina akachotsapo mawu onena zamʼtsogolo a mʼbuku ili, Mulungu adzachotsa gawo lake pa mtengo wamoyo ndi la mu mzinda woyera zimene zanenedwa mʼbuku ili.”
20 Свидетельствующий сие говорит: ей, гряду скоро! Аминь. Ей, гряди, Господи Иисусе!
Iye amene akuchitira umboni pa zinthu izi akuti, “Inde, Ine ndikubwera posachedwa.” Ameni. Bwerani Ambuye Yesu.
21 Благодать Господа нашего Иисуса Христа со всеми вами. Аминь
Chisomo cha Ambuye Yesu chikhale ndi anthu onse. Ameni.

< Откровение 22 +