< Откровение 10 >

1 И видел я другого Ангела сильного, сходящего с неба, облеченного облаком; над головою его была радуга, и лице его, как солнце, и ноги его, как столпы огненные,
Kenaka ndinaona mngelo wina wamphamvu akutsika kuchokera kumwamba. Anavala mtambo ndipo anali ndi utawaleza pamutu pake. Nkhope yake inali ngati dzuwa, ndipo miyendo yake inali ngati mizati yamoto.
2 в руке у него была книжка раскрытая. И поставил он правую ногу свою на море, а левую на землю,
Mʼdzanja lake munali kabuku kakangʼono kotsekulidwa. Phazi lake lamanja linaponda mʼnyanja ndipo phazi lake lamanzere linaponda pa mtunda.
3 и воскликнул громким голосом, как рыкает лев; и когда он воскликнул, тогда семь громов проговорили голосами своими.
Mngeloyo anafuwula kwambiri ngati kubangula kwa mkango. Atangofuwula, kunamveka kugunda kwa mabingu asanu ndi awiri.
4 И когда семь громов проговорили голосами своими, я хотел было писать; но услышал голос с неба, говорящий мне: скрой, что говорили семь громов, и не пиши сего.
Mabingu asanu ndi awiriwo atangogunda, ine ndinkati ndizilemba; koma ndinamva mawu kuchokera kumwamba kuti, “Zisunge mu mtima zimene mabingu asanu ndi awiriwo anena ndipo usazilembe.”
5 И Ангел, которого я видел стоящим на море и на земле, поднял руку свою к небу
Kenaka mngelo amene ndinamuona ataponda mʼnyanja ndi ku mtunda uja, anakweza dzanja lake lamanja kumwamba.
6 и клялся Живущим во веки веков, Который сотворил небо и все, что на нем, землю и все, что на ней, и море и все, что в нем, что времени уже не будет; (aiōn g165)
Mngeloyo analumbira mʼdzina la Iye wokhala ndi moyo mpaka muyaya, amene analenga kumwamba ndi zonse zili kumeneko, dziko lapansi ndi zonse zili mʼmenemo, nyanja ndi zonse zili mʼmenemo, nati, “Pasakhalenso zochedwa tsopano! (aiōn g165)
7 но в те дни, когда возгласит седьмой Ангел, когда он вострубит, совершится тайна Божия, как Он благовествовал рабам Своим пророкам.
Koma patsala pangʼono kuti mngelo wachisanu ndi chiwiri uja awombe lipenga lake, chinsinsi cha Mulungu chidzachitika monga momwe analengezera kwa atumiki ake, aneneri.”
8 И голос, который я слышал с неба, опять стал говорить со мною, и сказал: пойди, возьми раскрытую книжку из руки Ангела, стоящего на море и на земле.
Pamenepo mawu amene ndinamva kuchokera kumwamba aja, anandiyankhulanso, anati, “Pita katenge buku lotsekulidwalo mʼdzanja la mngelo amene waponda pa nyanja ndi pa mtundayo.”
9 И я пошел к Ангелу и сказал ему: дай мне книжку. Он сказал мне: возьми и съешь ее; она будет горька во чреве твоем, но в устах твоих будет сладка, как мед.
Choncho ndinapita kwa mngeloyo ndipo ndinamupempha kuti andipatse kabukuko. Iye anati, “Tenga, idya. Mʼmimba mwako kaziwawa koma mʼkamwa mwako kazizuna ngati uchi.”
10 И взял я книжку из руки Ангела, и съел ее; и она в устах моих была сладка, как мед; когда же съел ее, то горько стало во чреве моем.
Ndinatenga kabukuko mʼdzanja la mngeloyo ndipo ndinadyadi. Mʼkamwa mwanga kankazuna ngati uchi, koma nditakameza, mʼmimbamu munkawawa.
11 И сказал он мне: тебе надлежит опять пророчествовать о народах и племенах, и языках, и царях многих.
Ndipo anandiwuza kuti, “Iwe uyenera kulalikiranso za mitundu yambiri ya anthu, za mayiko, ziyankhulo ndi za mafumu.”

< Откровение 10 >