< От Матфея 4 >

1 Тогда Иисус возведен был Духом в пустыню, для искушения от диавола,
Pambuyo pake Yesu anatsogozedwa ndi Mzimu Woyera kupita ku chipululu kukayesedwa ndi mdierekezi.
2 и, постившись сорок дней и сорок ночей, напоследок взалкал.
Ndipo atasala kudya masiku makumi anayi usana ndi usiku, anamva njala.
3 И приступил к Нему искуситель и сказал: если Ты Сын Божий, скажи, чтобы камни сии сделались хлебами.
Woyesayo anadza kwa Iye nati, “Ngati ndinu mwana wa Mulungu, sandutsani miyala iyi kuti ikhale buledi.”
4 Он же сказал ему в ответ: написано: не хлебом одним будет жить человек, но всяким словом, исходящим из уст Божиих.
Yesu anayankha kuti, “Zalembedwa, ‘Munthu sadzakhala ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu aliwonse ochokera mʼkamwa mwa Mulungu.’”
5 Потом берет Его диавол в святой город, и поставляет Его на крыле храма,
Pamenepo mdierekezi anapita naye ku mzinda woyera namuyimiritsa pamwamba penipeni pa Nyumba ya Mulungu.
6 и говорит Ему: если Ты Сын Божий, бросься вниз, ибо написано: Ангелам Своим заповедает о Тебе, и на руках понесут Тебя, да не преткнешься о камень ногою Твоею.
Ndipo anati, “Ngati ndinu Mwana wa Mulungu, dziponyeni nokha pansi. Pakuti kwalembedwa: “‘Adzalamulira angelo ake za iwe, ndipo adzakunyamula ndi manja awo kuti phazi lako lisagunde pa mwala.’”
7 Иисус сказал ему: написано также: не искушай Господа Бога твоего.
Yesu anamuyankha kuti, “Kwalembedwanso: ‘Musamuyese Yehova Mulungu wanu.’”
8 Опять берет Его диавол на весьма высокую гору и показывает Ему все царства мира и славу их,
Kenaka mdierekezi anamutengera Yesu ku phiri lalitali kwambiri namuonetsa maufumu onse a dziko lapansi ndi ulemerero wawo.
9 и говорит Ему: все это дам Тебе, если, пав, поклонишься мне.
Ndipo anati kwa Iye, “Zonsezi ndidzakupatsani ngati mutandiweramira ndi kundipembedza ine.”
10 Тогда Иисус говорит ему: отойди от Меня, сатана, ибо написано: Господу Богу твоему поклоняйся и Ему одному служи.
Yesu anati kwa iye, “Choka Satana! Zalembedwa, ‘Pembedza Yehova Mulungu wako ndi kumutumikira Iye yekha.’”
11 Тогда оставляет Его диавол, и се, Ангелы приступили и служили Ему.
Pamenepo mdierekezi anamusiya ndipo angelo anamutumikira Iye.
12 Услышав же Иисус, что Иоанн отдан под стражу, удалился в Галилею
Yesu atamva kuti Yohane anamutsekera mʼndende, anabwerera ku Galileya.
13 и, оставив Назарет, пришел и поселился в Капернауме приморском, в пределах Завулоновых и Неффалимовых,
Ndipo atachoka ku Nazareti anapita ku Kaperenawo ndi kukhala mʼmbali mwa nyanja, mʼdera la Zebuloni ndi Nafutali;
14 да сбудется реченное через пророка Исаию, который говорит:
pokwaniritsa zimene zinanenedwa kudzera mwa mneneri Yesaya kuti,
15 земля Завулонова и земля Неффалимова, на пути приморском, за Иорданом, Галилея языческая,
“Dziko la Zebuloni ndi dziko la Nafutali, njira ya ku nyanja, kutsidya lija la Yorodani, Galileya wa anthu a mitundu ina,
16 народ, сидящий во тьме, увидел свет великий, и сидящим в стране и тени смертной воссиял свет.
anthu okhala mu mdima awona kuwala kwakukulu; ndi kwa iwo okhala mʼdziko la mthunzi wa imfa kuwunika kwawafikira.”
17 С того времени Иисус начал проповедывать и говорить: покайтесь, ибо приблизилось Царство Небесное.
Kuyambira nthawi imeneyo, Yesu anayamba kulalikira nati, “Tembenukani mtima ufumu wakumwamba wayandikira.”
18 Проходя же близ моря Галилейского, Он увидел двух братьев: Симона, называемого Петром, и Андрея, брата его, закидывающих сети в море, ибо они были рыболовы,
Pamene Yesu ankayenda mʼmbali mwa nyanja ya Galileya, anaona abale awiri, Simoni wotchedwa Petro ndi mʼbale wake Andreya akuponya khoka mʼnyanja popeza anali asodzi.
19 и говорит им: идите за Мною, и Я сделаю вас ловцами человеков.
Yesu anati, “Bwerani, tsateni Ine ndipo ndidzakusandutsani asodzi a anthu.”
20 И они тотчас, оставив сети, последовали за Ним.
Nthawi yomweyo anasiya makoka awo namutsata Iye.
21 Оттуда, идя далее, увидел Он других двух братьев, Иакова Зеведеева и Иоанна, брата его, в лодке с Зеведеем, отцом их, починивающих сети свои, и призвал их.
Atapita patsogolo, anaona abale ena awiri, Yakobo ndi mʼbale wake Yohane ana a Zebedayo. Iwowa anali mʼbwato ndi abambo awo, Zebedayo, akukonza makoka awo ndipo Yesu anawayitana.
22 И они тотчас, оставив лодку и отца своего, последовали за Ним.
Nthawi yomweyo anasiya bwato ndi abambo awo namutsata Iye.
23 И ходил Иисус по всей Галилее, уча в синагогах их, и проповедуя Евангелие Царствия, и исцеляя всякую болезнь и всякую немощь в людях.
Yesu anayendayenda mu Galileya kuphunzitsa mʼmasunagoge awo, nalalikira Uthenga Wabwino wa ufumu ndi kuchiritsa matenda onse pakati pa anthu.
24 И прошел о Нем слух по всей Сирии; и приводили к Нему всех немощных, одержимых различными болезнями и припадками, и бесноватых, и лунатиков, и расслабленных, и Он исцелял их.
Mbiri yake yonse inawanda ku Siriya konse ndipo anthu anabweretsa kwa Iye onse amene anali odwala nthenda zosiyanasiyana, womva maululu aakulu, ogwidwa ndi ziwanda, odwala matenda akugwa ndi olumala ndipo Iye anawachiritsa.
25 И следовало за Ним множество народа из Галилеи и Десятиградия, и Иерусалима, и Иудеи, и из-за Иордана.
Magulu ambiri a anthu anachokera ku Galileya, Dekapoli, Yerusalemu, Yudeya ndi ku madera a kutsidya la mtsinje wa Yorodani namutsata Iye.

< От Матфея 4 >