< От Матфея 25 >

1 Тогда подобно будет Царство Небесное десяти девам, которые, взяв светильники свои, вышли навстречу жениху.
“Nthawi imeneyo ufumu wakumwamba udzafanizidwa ndi anamwali khumi amene anatenga nyale zawo napita kukakumana ndi mkwati.
2 Из них пять было мудрых и пять неразумных.
Asanu anali opusa ndipo asanu ena anali ochenjera.
3 Неразумные, взяв светильники свои, не взяли с собою масла.
Opusawo anatenga nyale zawo koma sanatenge mafuta;
4 Мудрые же, вместе со светильниками своими, взяли масла в сосудах своих.
koma ochenjerawo anatenga mafuta awo mʼmabotolo pamodzi ndi nyale zawo.
5 И как жених замедлил, то задремали все и уснули.
Mkwati anachedwa ndipo onse anayamba kusinza nagona.
6 Но в полночь раздался крик: вот, жених идет, выходите навстречу ему.
“Pakati pa usiku kunamveka kufuwula kuti, ‘Onani Mkwati! Tulukani kuti mukakumane naye!’
7 Тогда встали все девы те и поправили светильники свои.
“Pamenepo anamwali onse anadzuka nayatsa nyale zawo.
8 Неразумные же сказали мудрым: дайте нам вашего масла, потому что светильники наши гаснут.
Opusawo anati kwa ochenjerawo, ‘Tipatseniko mafuta anu; nyale zathu zikuzima.’
9 А мудрые отвечали: чтобы не случилось недостатка и у нас и у вас, пойдите лучше к продающим и купите себе.
“Ochenjerawo anayankha, nati, ‘Ayi sangakwanire inu ndi ife. Pitani kwa ogulitsa mafuta ndi kukadzigulira nokha.’
10 Когда же пошли они покупать, пришел жених, и готовые вошли с ним на брачный пир, и двери затворились;
“Koma pamene ankapita kukagula mafutawo, mkwati anafika. Anamwali amene anali okonzeka aja analowa naye pamodzi mʼnyumba ya phwando la ukwati. Ndipo khomo linatsekedwa.
11 после приходят и прочие девы, и говорят: Господи! Господи! отвори нам.
“Pambuyo pake enawo anabwera nati, ‘Ambuye! Ambuye! Titsekulireni!’
12 Он же сказал им в ответ: истинно говорю вам: не знаю вас.
“Koma iye anayankha kuti, ‘Zoonadi, ine ndikuwuzani kuti sindikukudziwani.’
13 Итак, бодрствуйте, потому что не знаете ни дня, ни часа, в который приидет Сын Человеческий.
“Choncho khalani odikira, popeza simudziwa tsiku kapena nthawi.”
14 Ибо Он поступит, как человек, который, отправляясь в чужую страну, призвал рабов своих и поручил им имение свое:
“Komanso udzafanizidwa ndi munthu amene ankapita pa ulendo, ndipo anayitana antchito ake nawasiyira chuma chake.
15 и одному дал он пять талантов, другому два, иному один, каждому по его силе; и тотчас отправился.
Wina anamupatsa ndalama 5,000, kwa wina 2,000 ndi kwa wina 1,000. Aliyense monga mwa nzeru zake. Pamenepo anapita pa ulendo wake.
16 Получивший пять талантов пошел, употребил их в дело и приобрел другие пять талантов;
Munthu amene analandira ndalama 5,000 uja, anapita nthawi yomweyo nachita nazo malonda napindula 5,000 zina.
17 точно так же и получивший два таланта приобрел другие два;
Chimodzimodzinso amene analandira 2,000 uja anapindula 2,000 zina.
18 получивший же один талант пошел и закопал его в землю и скрыл серебро господина своего.
Koma munthu amene analandira 1,000 uja, anapita nakumba dzenje nabisapo ndalama ya mbuye wake.
19 По долгом времени приходит господин рабов тех и требует у них отчета.
“Patapita nthawi yayitali, mbuye wa antchitowo anabwera nawayitana kuti afotokoze chimene anachita ndi ndalama zija.
20 И, подойдя, получивший пять талантов принес другие пять талантов и говорит: господин! пять талантов ты дал мне; вот, другие пять талантов я приобрел на них.
Munthu amene analandira ndalama 5,000 uja anabweretsa 5,000 zina nati, ‘Ambuye munandisungitsa 5,000, taonani ndapindula 5,000 zinanso.’
21 Господин его сказал ему: хорошо, добрый и верный раб! в малом ты был верен, над многим тебя поставлю; войди в радость господина твоего.
“Ambuye ake anayankha nati, ‘Wachita bwino, wantchito wabwino ndi wokhulupirika iwe! Wakhala wokhulupirika pa zinthu zochepa; ndidzakuyika iwe kukhala woyangʼanira zinthu zambiri. Bwera, udzakondwere pamodzi ndi mbuye wako!’
22 Подошел также и получивший два таланта и сказал: господин! два таланта ты дал мне; вот, другие два таланта я приобрел на них.
“Munthu amene anali ndi ndalama 2,000 uja anabweranso nati, ‘Ambuye munandisungitsa 2,000, onani, ndapindula 2,000 zinanso.’
23 Господин его сказал ему: хорошо, добрый и верный раб! в малом ты был верен, над многим тебя поставлю; войди в радость господина твоего.
“Mbuye wake anayankha nati, ‘Wachita bwino, wantchito wabwino ndi wokhulupirika! Wakhala wokhulupirika pa zinthu zochepa; ndidzakuyika kukhala woyangʼanira zinthu zambiri. Bwera, udzakondwere pamodzi ndi mbuye wako!’
24 Подошел и получивший один талант и сказал: господин! я знал тебя, что ты человек жестокий, жнешь, где не сеял, и собираешь, где не рассыпал,
“Kenaka munthu amene analandira ndalama 1,000 uja anabwera nati, ‘Ambuye ndinadziwa kuti ndinu munthu wowuma mtima, amene mumakolola pamene simunadzale ndi kututa kumene simunafese.
25 и, убоявшись, пошел и скрыл талант твой в земле; вот тебе твое.
Choncho ndinachita mantha ndipo ndinapita ndi kukabisa ndalama yanuyo pa dzenje. Onani, si iyi ndalama yanu ija.’
26 Господин же его сказал ему в ответ: лукавый раб и ленивый! ты знал, что я жну, где не сеял, и собираю, где не рассыпал;
“Mbuye wake anayankha nati, ‘Iwe wantchito woyipa ndi waulesi! Iwe umadziwa kuti ndimakolola pamene sindinadzale, ndi kututa kumene sindinafese.
27 посему надлежало тебе отдать серебро мое торгующим, и я, придя, получил бы мое с прибылью;
Bwanji sunayike ndalama yanga kwa osunga ndalama kuti ine pobwera ndidzalandire ndalama yangayo pamodzi ndi chiwongoladzanja?
28 итак, возьмите у него талант и дайте имеющему десять талантов,
“‘Mulandeni ndalamayo, ndipo patsani iye amene ali ndi ndalama 10,000.
29 ибо всякому имеющему дастся и приумножится, а у неимеющего отнимется и то, что имеет;
Pakuti aliyense amene ali nazo adzapatsidwa zambiri, ndipo adzakhala nazo zochuluka. Aliyense amene alibe adzalandidwa ngakhale chimene ali nacho.
30 а негодного раба выбросьте во тьму внешнюю: там будет плач и скрежет зубов. Сказав сие, возгласил: кто имеет уши слышать, да слышит!
Ndipo muponyeni wantchito wopanda phinduyu kunja, ku mdima kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.’”
31 Когда же приидет Сын Человеческий во славе Своей и все святые Ангелы с Ним, тогда сядет на престоле славы Своей
“Pamene Mwana wa Munthu adzabwera mu ulemerero wake, pamodzi ndi angelo ake onse, adzakhala pa mpando waufumu mu ulemerero wakumwamba.
32 и соберутся пред Ним все народы; и отделит одних от других, как пастырь отделяет овец от козлов;
Mitundu yonse ya anthu idzasonkhanitsidwa pamaso pake, ndipo adzawalekanitsa iwo wina ndi mnzake monga mʼbusa amalekanitsa nkhosa ndi mbuzi.
33 и поставит овец по правую Свою сторону, а козлов - по левую.
Adzayika nkhosa ku dzanja lake lamanja ndi mbuzi ku lamanzere.
34 Тогда скажет Царь тем, которые по правую сторону Его: приидите, благословенные Отца Моего, наследуйте Царство, уготованное вам от создания мира:
“Pamenepo mfumu idzati kwa a ku dzanja lamanja, ‘Bwerani inu odalitsika ndi Atate anga; landirani ufumu umene unakonzedwa chifukwa cha inu kuyambira pachiyambi cha dziko.
35 ибо алкал Я, и вы дали Мне есть; жаждал, и вы напоили Меня; был странником, и вы приняли Меня;
Pakuti ndinali ndi njala ndipo munandipatsa chakudya, ndinali ndi ludzu ndipo munandipatsa madzi akumwa, ndinali mlendo ndipo munandilandira,
36 был наг, и вы одели Меня; был болен, и вы посетили Меня; в темнице был, и вы пришли ко Мне.
ndinali wausiwa ndipo munandiveka, ndinali wodwala ndipo munandisamalira, ndinali ku ndende ndipo inu munandiyendera.’
37 Тогда праведники скажут Ему в ответ: Господи! когда мы видели Тебя алчущим и накормили? или жаждущим и напоили?
“Ndipo olungamawo adzamuyankha kuti, ‘Ambuye ndi liti tinakuonani muli ndi njala ndipo tinakudyetsani, kapena ludzu ndipo tinakupatsani madzi akumwa?
38 когда мы видели Тебя странником и приняли? или нагим и одели?
Ndi liti tinakuonani muli mlendo ndipo tinakulandirani, kapena wa usiwa ndipo tinakuvekani?
39 когда мы видели Тебя больным или в темнице и пришли к Тебе?
Ndi liti tinakuonani mutadwala kapena ku ndende ndipo tinakuyenderani?’
40 И Царь скажет им в ответ: истинно говорю вам: так как вы сделали это одному из сих братьев Моих меньших, то сделали Мне.
“Mfumu idzayankha kuti, ‘Zoonadi, ndikuwuzani kuti chilichonse chimene munachitira mmodzi wa abale anga onyozekawa munandichitira Ine.’
41 Тогда скажет и тем, которые по левую сторону: идите от Меня, проклятые, в огонь вечный, уготованный диаволу и ангелам его: (aiōnios g166)
“Pamenepo adzanena kwa akumanzere kwake kuti, ‘Chokani kwa Ine, inu otembereredwa, pitani ku moto wosatha wokonzedwera mdierekezi ndi angelo ake. (aiōnios g166)
42 ибо алкал Я, и вы не дали Мне есть; жаждал, и вы не напоили Меня;
Pakuti ndinali ndi njala ndipo simunandipatse chakudya, ndinali ndi ludzu ndipo simunandipatse madzi akumwa,
43 был странником, и не приняли Меня; был наг, и не одели Меня; болен и в темнице, и не посетили Меня.
ndinali mlendo koma inu simunandilandire, ndinali wa usiwa koma simunandiveke, ndinali wodwala komanso ku ndende simunandisamalire.’
44 Тогда и они скажут Ему в ответ: Господи! когда мы видели Тебя алчущим, или жаждущим, или странником, или нагим, или больным, или в темнице и не послужили Тебе?
“Iwo adzayankha kuti, ‘Ambuye ndi liti tinakuonani muli ndi njala kapena ludzu kapena mlendo kapena wausiwa kapena wodwala kapena mʼndende, ndipo kuti sitinakuthandizeni?’
45 Тогда скажет им в ответ: истинно говорю вам: так как вы не сделали этого одному из сих меньших, то не сделали Мне.
“Iye adzayankha kuti, ‘Zoonadi, ndikuwuzani kuti chilichonse chimene simunachitire mmodzi wa abale anga onyozekawa simunandichitire Ine.’
46 И пойдут сии в муку вечную, а праведники в жизнь вечную. (aiōnios g166)
“Amenewa adzapita ku chilango chosatha pamene olungama ku moyo wosatha.” (aiōnios g166)

< От Матфея 25 >