< От Матфея 24 >

1 И выйдя, Иисус шел от храма; и приступили ученики Его, чтобы показать Ему здания храма.
Yesu anatuluka mʼNyumba ya Mulungu ndipo akuchoka ophunzira ake anadza kwa Iye ndi kumuonetsa mamangidwe a Nyumbayo.
2 Иисус же сказал им: видите ли все это? Истинно говорю вам: не останется здесь камня на камне; все будет разрушено.
Iye anawafunsa kuti, “Kodi mukuona zinthu zonsezi? Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti palibe mwala pano umene udzasiyidwe pa unzake; uliwonse udzagwetsedwa pansi.”
3 Когда же сидел Он на горе Елеонской, то приступили к Нему ученики наедине и спросили: скажи нам, когда это будет? и какой признак Твоего пришествия и кончины века? (aiōn g165)
Pamene Yesu anakhala pansi pa phiri la Olivi, ophunzira ake anabwera kwa Iye mwamseri nati, “Tiwuzeni, kodi izi zidzachitika liti, ndipo chizindikiro cha kubwera kwanu ndi zizindikiro za kutha kwa dziko zidzakhala chiyani?” (aiōn g165)
4 Иисус сказал им в ответ: берегитесь, чтобы кто не прельстил вас,
Yesu anayankha kuti, “Onetsetsani kuti wina asakunyengeni.
5 ибо многие придут под именем Моим, и будут говорить: “Я Христос”, и многих прельстят.
Pakuti ambiri adzabwera mʼdzina langa nadzati, ‘Ndine Khristu,’ ndipo adzanyenga ambiri.
6 Также услышите о войнах и о военных слухах. Смотрите, не ужасайтесь, ибо надлежит всему тому быть, но это еще не конец:
Mudzamva za nkhondo ndi mbiri za nkhondo, koma onetsetsani kuti musadzidzimuke nazo. Zotere ziyenera kuchitika, koma chimaliziro sichinafike.
7 ибо восстанет народ на народ и царство на царство; и будут глады, моры и землетрясения по местам;
Mtundu ndi mtundu udzawukirana, ndipo ufumu ndi ufumu udzawukirana. Kudzakhala njala ndi zivomerezi mʼmalo osiyanasiyana.
8 все же это начало болезней.
Zonsezi ndi chiyambi chabe cha zowawa.
9 Тогда будут предавать вас на мучения и убивать вас; и вы будете ненавидимы всеми народами за имя Мое;
“Pamenepo adzakuperekani kuti mukazunzidwe ndi kuphedwa, ndipo mitundu yonse idzakudani chifukwa cha Ine.
10 и тогда соблазнятся многие, и друг друга будут предавать, и возненавидят друг друга
Pa nthawi imeneyo ambiri adzasiya chikhulupiriro ndipo adzadana ndi kuperekana wina ndi mnzake,
11 и многие лжепророки восстанут и прельстят многих;
ndipo aneneri onama ambiri adzaoneka ndi kunyenga anthu ambiri.
12 и, по причине умножения беззакония, во многих охладеет любовь;
Chifukwa cha kuchuluka kwa zoyipa, chikondi cha ambiri chidzazirala,
13 претерпевший же до конца спасется.
koma wopirira kufikira chimaliziro adzapulumuka.
14 И проповедано будет сие Евангелие Царствия по всей вселенной, во свидетельство всем народам; и тогда придет конец.
Ndipo uthenga wa ufumu udzalalikidwa ku dziko lonse lapansi ngati umboni kwa mitundu yonse, ndipo pomwepo chimaliziro chidzafika.”
15 Итак, когда увидите мерзость запустения, реченную через пророка Даниила, стоящую на святом месте, - читающий да разумеет, -
“Tsono mukadzaona chinthu chonyansa chosakaza chitayima pamalo oyera chimene anayankhula mneneri Danieli, owerengayo azindikire.
16 тогда находящиеся в Иудее да бегут в горы;
Pamenepo amene ali ku Yudeya athawire ku mapiri.
17 и кто на кровле, тот да не сходит взять что-нибудь из дома своего;
Yemwe ali pa denga la nyumba yake asatsike kukatulutsa chinthu chilichonse mʼnyumba.
18 и кто на поле, тот да не обращается назад взять одежды свои.
Yemwe ali ku munda asapite kukatenga mkanjo wake.
19 Горе же беременным и питающим сосцами в те дни!
Kudzakhala koopsa kwambiri masiku amenewo kwa amayi oyembekezera ndi kwa oyamwitsa!
20 Молитесь, чтобы не случилось бегство ваше зимою или в субботу,
Pempherani kuti kuthawa kwanu kusadzachitike nthawi yozizira kapena pa Sabata.
21 ибо тогда будет великая скорбь, какой не было от начала мира доныне и не будет.
Popeza kudzakhala masautso aakulu, omwe safanana ndi ena ali onse chiyambireni cha dziko lapansi mpaka lero lino ndipo sadzafanananso ndi ena.
22 И если бы не сократились те дни, то не спаслась бы никакая плоть; но ради избранных сократятся те дни.
Ngati masiku amenewo sakanafupikitsidwa, palibe mmodzi akanapulumuka, koma chifukwa cha osankhidwawo masiku amenewo adzafupikitsidwa.
23 Тогда, если кто скажет вам: вот, здесь Христос или там, - не верьте.
Pa nthawi imeneyo ngati wina adzati kwa inu, ‘Onani, Khristu ali pano!’ Kapena, ‘Uyo ali ukoyo!’ Musakhulupirire.
24 Ибо восстанут лжехристы и лжепророки и дадут великие знамения и чудеса, чтобы прельстить, если возможно, и избранных.
Chifukwa akhristu onama ndi aneneri onama adzaoneka ndipo adzachita zizindikiro zazikulu ndi zodabwitsa kuti akanyenge ngakhale osankhidwawo ngati kukanakhala kotheka kutero.
25 Вот, Я наперед сказал вам.
Onani, ndakuwuzani izi nthawi isanafike.
26 Итак, если скажут вам: “вот, Он в пустыне”, - не выходите; “вот, Он в потаенных комнатах”, - не верьте;
“Ndiye ngati wina akuwuzani inu kuti, ‘Uyo ali ku chipululu,’ inu musapiteko; kapena akati, ‘Uyu ali kuno mʼchipinda chamʼkati,’ musakhulupirire.
27 ибо, как молния исходит от востока и видна бывает даже до запада, так будет пришествие Сына Человеческого;
Monga momwe mphenzi ingʼanima kuchokera kummawa kupita kumadzulo, momwemonso kudzakhala kubwera kwa Mwana wa Munthu.
28 ибо, где будет труп, там соберутся орлы.
Kulikonse kuli chinthu cha kufa, makwangwala adzasonkhanako.
29 И вдруг, после скорби дней тех, солнце померкнет, и луна не даст света своего, и звезды спадут с неба, и силы небесные поколеблются;
“Akadzangotha mavuto a masiku amenewo, “‘dzuwa lidzadetsedwa, ndipo mwezi sudzawala; nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba, ndipo mphamvu za mmwamba zidzagwedezeka.’
30 тогда явится знамение Сына Человеческого на небе; и тогда восплачутся все племена земные и увидят Сына Человеческого, грядущего на облаках небесных с силою и славою великою;
“Pa nthawi imeneyo chizindikiro cha Mwana wa Munthu chidzaoneka mlengalenga, ndipo mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzalira. Idzaona Mwana wa Munthu akubwera ndi mitambo, mphamvu ndi ulemerero waukulu.
31 и пошлет Ангелов Своих с трубою громогласною, и соберут избранных Его от четырех ветров, от края небес до края их.
Ndipo adzatuma angelo ake, ndi kulira kwa lipenga kwakukulu, nadzasonkhanitsa osankhidwa ake kuchokera ku mphepo zinayi, ndi kuchokera kumathero a thambo kufika mbali ina.
32 От смоковницы возьмите подобие: когда ветви ее становятся уже мягки и пускают листья, то знаете, что близко лето;
“Tsopano kuchokera ku mtengo wamkuyu phunzirani ichi: Pamene uyamba kuphukira, masamba ake akatuluka, mumadziwa kuti dzinja layandikira.
33 так, когда вы увидите все сие, знайте, что близко, при дверях.
Momwemonso, pamene mudzaona zinthu zonsezi mudzadziwe kuti ali pafupi pa khomo penipeni.
34 Истинно говорю вам: не прейдет род сей, как все сие будет;
Zoonadi, ndikuwuzani kuti mʼbado uwu sudzatha mpaka zinthu zonse zitachitika.
35 небо и земля прейдут, но слова Мои не прейдут.
Kumwamba ndi dziko lapansi zidzatha, koma mawu anga sadzatha.”
36 О дне же том и часе никто не знает, ни Ангелы небесные, а только Отец Мой один;
“Palibe amene adziwa za tsikulo kapena nthawi, angakhale angelo akumwamba, angakhale Mwana, koma Atate okha.
37 но, как было во дни Ноя, так будет и в пришествие Сына Человеческого:
Monga momwe zinalili nthawi ya Nowa, momwemonso zidzatero pobwera kwa Mwana wa Munthu.
38 ибо, как во дни перед потопом ели, пили, женились и выходили замуж, до того дня, как вошел Ной в ковчег,
Pakuti masiku amenewo chisanafike chigumula, anthu amadya ndi kumwa, kukwatira ndi kukwatiwa, mpaka tsiku limene Nowa analowa mʼchombo;
39 и не думали, пока не пришел потоп и не истребил всех, - так будет и пришествие Сына Человеческого;
ndipo sanadziwe za chimene chikanachitika mpaka pamene chigumula chinafika ndi kuwamiza onse. Umu ndi mmene zidzakhalira pobwera kwa Mwana wa Munthu.
40 тогда будут двое на поле: один берется, а другой оставляется;
Amuna awiri adzakhala mʼmunda; wina adzatengedwa ndi wina adzatsala.
41 две мелющие в жерновах: одна берется, а другая оставляется.
Amayi awiri adzakhala akusinja pa mtondo; wina adzatengedwa ndi wina adzatsala.
42 Итак бодрствуйте, потому что не знаете, в который час Господь ваш приидет.
“Chifukwa chake yangʼanirani, popeza simudziwa tsiku lanji limene Ambuye anu adzabwera.
43 Но это вы знаете, что если бы ведал хозяин дома, в какую стражу придет вор, то бодрствовал бы и не дал бы подкопать дома своего.
Koma zindikirani ichi: Ngati mwini nyumba akanadziwa nthawi yanji ya usiku imene mbala imabwera, sakanagona ndipo sakanalola kuti nyumba yake ithyoledwe.
44 Потому и вы будьте готовы, ибо в который час не думаете, приидет Сын Человеческий.
Inunso tsono muyenera kukhala okonzeka, chifukwa Mwana wa Munthu adzabwera pa nthawi imene inu simukumuyembekezera.
45 Кто же верный и благоразумный раб, которого господин его поставил над слугами своими, чтобы давать им пищу во время?
“Kodi wantchito wokhulupirika ndi wanzeru amene ambuye ake anamuyika kukhala woyangʼanira antchito a mʼnyumba kuti awapatse chakudya chawo pa nthawi yake ndani?
46 Блажен тот раб, которого господин его, придя, найдет поступающим так;
Chidzakhala chabwino kwa wantchitoyo ngati mbuye wake pofika adzamupeza akuchita zimenezi.
47 истинно говорю вам, что над всем имением своим поставит его.
Zoonadi, ndikuwuzani kuti adzamuyika kukhala woyangʼanira katundu wake yense.
48 Если же раб тот, будучи зол, скажет в сердце своем: не скоро придет господин мой,
Koma tiyerekeze kuti wantchitoyo ndi woyipa, nati kwa iye yekha, ‘Mbuye wanga akuchedwa kubwera,’
49 и начнет бить товарищей своих и есть и пить с пьяницами, -
nayamba kumenya antchito anzake, nadya ndi kumwa ndi zidakwa.
50 то придет господин раба того в день, в который он не ожидает, и в час, в который не думает,
Mbuye wa wantchitoyo adzabwera pa tsiku limene iye samamuyembekezera ndi pa nthawi imene iye sakuyidziwa.
51 и рассечет его, и подвергнет его одной участи с лицемерами; там будет плач и скрежет зубов.
Adzamulanga koopsa ndipo adzamuyika kokhala anthu achiphamaso, kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.”

< От Матфея 24 >