< От Матфея 22 >

1 Иисус, продолжая говорить им притчами, сказал:
Yesu anayankhula nawonso mʼmafanizo, nati,
2 Царство Небесное подобно человеку царю, который сделал брачный пир для сына своего
“Ufumu wakumwamba uli ngati mfumu imene inakonzera phwando mwana wake wamwamuna.
3 и послал рабов своих звать званых на брачный пир; и не хотели придти.
Anatumiza antchito ake kwa amene anayitanidwa kuphwando koma anakana kubwera.
4 Опять послал других рабов, сказав: скажите званым: вот, я приготовил обед мой, тельцы мои и что откормлено, заколото, и все готово; приходите на брачный пир.
“Kenaka anatumiza antchito ena nati, ‘Awuzeni oyitanidwa kuti phwando lakonzedwa: ndapha ngʼombe yayimuna ndi nyama zina zonenepa ndipo zonse zakonzedwa. Bwerani ku phwando laukwati.’
5 Но они, пренебрегши то, пошли, кто на поле свое, а кто на торговлю свою;
“Koma iwo sanalabadire ndipo anachoka; wina anapita ku munda wake ndi wina ku malonda ake.
6 прочие же, схватив рабов его, оскорбили и убили их.
Ndipo otsalawo anagwira antchito ake, nawazunza ndi kuwapha.
7 Услышав о сем, царь разгневался, и, послав войска свои, истребил убийц оных и сжег город их.
Mfumu inakwiya. Inatumiza asilikali ake ndipo anawononga opha anzawowo ndi kutentha mzinda wawo.
8 Тогда говорит он рабам своим: брачный пир готов, а званые не были достойны;
“Pamenepo anati kwa antchito ake, ‘Phwando laukwati lakonzedwa, koma amene ndinawayitana sanali oyenera.
9 итак пойдите на распутия и всех, кого найдете, зовите на брачный пир.
Pitani ku mphambano za misewu ndipo kayitaneni aliyense amene mukamupeze kuti abwere ku phwando.’
10 И рабы те, выйдя на дороги, собрали всех, кого только нашли, и злых и добрых; и брачный пир наполнился возлежащими.
Pamenepo antchitowo anapita ku misewu nakasonkhanitsa anthu onse amene anakawapeza, abwino ndi oyipa omwe, ndipo nyumba ya madyerero inadzaza ndi oyitanidwa.
11 Царь, войдя посмотреть возлежащих, увидел там человека, одетого не в брачную одежду,
“Koma pamene mfumu inabwera kudzaona oyitanidwawo, inaona munthu amene sanavale zovala zaukwati.
12 и говорит ему: друг! как ты вошел сюда не в брачной одежде? Он же молчал.
Inamufunsa kuti, ‘Bwenzi walowa bwanji muno wopanda zovala zaukwati?’ Munthuyo anakhala chete.
13 Тогда сказал царь слугам: связав ему руки и ноги, возьмите его и бросьте во тьму внешнюю; там будет плач и скрежет зубов;
“Pamenepo mfumuyo inawuza otumikira kuti, ‘Mʼmangeni manja ndi miyendo, ndipo muponyeni kunja, ku mdima kumene kudzakhale kulira ndi kukuta mano.’
14 ибо много званых, а мало избранных.
“Popeza oyitanidwa ndi ambiri koma osankhidwa ndi ochepa.”
15 Тогда фарисеи пошли и совещались, как бы уловить Его в словах.
Kenaka Afarisi anatuluka nakakonza njira zomupezera zifukwa Yesu mʼmawu ake.
16 И посылают к Нему учеников своих с иродианами, говоря: Учитель! мы знаем, что Ты справедлив, и истинно пути Божию учишь, и не заботишься об угождении кому-либо, ибо не смотришь ни на какое лице;
Anatumiza ophunzira awo kwa Iye pamodzi ndi Aherodia. Anati, “Aphunzitsi, tidziwa kuti ndinu wangwiro ndi kuti mumaphunzitsa mawu a Mulungu monga mwa choonadi. Simutekeseka ndi anthu, popeza simusamala kuti kodi ndi ndani?
17 итак скажи нам: как Тебе кажется? позволительно ли давать подать кесарю или нет?
Tiwuzeni tsono maganizo anu ndi otani, kodi nʼkololedwa kupereka msonkho kwa Kaisara kapena ayi?”
18 Но Иисус, видя лукавство их, сказал: что искушаете Меня, лицемеры?
Koma Yesu podziwa maganizo awo oyipa anati, “Inu achiphamaso, bwanji mufuna kundipezera chifukwa?
19 покажите Мне монету, которою платится подать. Они принесли Ему динарий.
Onetseni ndalama imene mumapereka msonkho.” Iwo anabweretsa dinari,
20 И говорит им: чье это изображение и надпись?
ndipo anawafunsa kuti, “Kodi chithunzi ichi ndi malemba awa ndi za ndani?”
21 Говорят Ему: кесаревы. Тогда говорит им: итак отдавайте кесарево кесарю, а Божие Богу.
Iwo anayankha kuti, “Ndi za Kaisara.” Pamenepo anawawuza kuti, “Perekani kwa Kaisara zake za Kaisara, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.”
22 Услышав это, они удивились и, оставив Его, ушли.
Atamva izi, anadabwa, ndipo anamusiya Iye, nachoka.
23 В тот день приступили к Нему саддукеи, которые говорят, что нет воскресения, и спросили Его:
Tsiku lomwelo Asaduki amene amati kulibe za kuukanso, anabwera kwa Iye ndi funso.
24 Учитель! Моисей сказал: если кто умрет, не имея детей, то брат его пусть возьмет за себя жену его и восстановит семя брату своему;
Iwo anati, “Aphunzitsi, Mose anatiwuza kuti munthu akamwalira wosasiya ana, mʼbale wake akuyenera kukwatira mkazi wamasiyeyo kuti amuberekere ana mʼbale wakeyo.
25 было у нас семь братьев; первый, женившись, умер и, не имея детей, оставил жену свою брату своему;
Tsopano panali abale asanu ndi awiri pakati pathu. Woyambayo anakwatira ndipo anamwalira, ndipo popeza analibe ana, mʼbale wake analowa chokolo.
26 подобно и второй, и третий, даже до седьмого;
Izi zinachitikiranso mʼbale wa chiwiri ndi wachitatu mpaka wachisanu ndi chiwiri.
27 после же всех умерла и жена;
Pa mapeto pake mkaziyo anamwaliranso.
28 итак, в воскресении которого из семи будет она женою? ибо все имели ее.
Tsopano, kodi akadzaukitsidwa adzakhala mkazi wa ndani mwa asanu ndi awiriwa popeza aliyense anamukwatirapo?”
29 Иисус сказал им в ответ: заблуждаетесь, не зная Писаний, ни силы Божией,
Yesu anayankha kuti, “Inu mukulakwitsa chifukwa simukudziwa malemba kapena mphamvu ya Mulungu.
30 ибо в воскресении не женятся, не выходят замуж, но пребывают, как Ангелы Божии на небесах.
Anthu akadzaukitsidwa, sadzakwatira kapena kukwatiwa; adzakhala ngati angelo kumwamba.
31 А о воскресении мертвых не читали ли вы реченного вам Богом:
Koma za kuukitsidwa kwa akufa, kodi simunawerenge zimene Mulungu ananena kwa inu kuti,
32 Я Бог Авраама, и Бог Исаака, и Бог Иакова? Бог не есть Бог мертвых, но живых.
‘Ine ndine Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake ndi Mulungu wa Yakobo?’ Iyeyo si Mulungu wa akufa koma wa amoyo.”
33 И, слыша, народ дивился учению Его.
Magulu a anthu atamva zimenezi, anazizwa ndi chiphunzitso chake.
34 А фарисеи, услышав, что Он привел саддукеев в молчание, собрались вместе.
Pakumva kuti Yesu anawakhalitsa chete Asaduki, Afarisi anasonkhana pamodzi.
35 И один из них, законник, искушая Его, спросил, говоря:
Mmodzi wa iwo, katswiri wa malamulo anamuyesa Iye ndi funso ndipo anati,
36 Учитель! какая наибольшая заповедь в законе?
“Aphunzitsi, kodi lamulo lalikulu koposa mu malamulo ndi liti?”
37 Иисус сказал ему: возлюби Господа Бога твоего всем сердцем твоим и всею душею твоею и всем разумением твоим:
Yesu anayankha kuti, “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse ndi moyo wako wonse ndi nzeru zako zonse.
38 сия есть первая и наибольшая заповедь;
Ili ndi lamulo loyamba ndi loposa onse.
39 вторая же, подобная ей: возлюби ближнего твоего, как самого себя;
Ndipo lachiwiri ndi lofanana nalo: ‘Konda mnansi wako monga iwe mwini.’
40 на сих двух заповедях утверждается весь закон и пророки.
Malamulo onse ndi aneneri zakhazikika pa malamulo awiriwa.”
41 Когда же собрались фарисеи, Иисус спросил их:
Afarisi atasonkhana pamodzi, Yesu anawafunsa kuti,
42 что вы думаете о Христе? чей Он Сын? Говорят Ему: Давидов.
“Kodi mukuganiza bwanji za Khristu? Ndi Mwana wa ndani?” Iwo anayankha kuti, “Mwana wa Davide.”
43 Говорит им: как же Давид, по вдохновению, называет Его Господом, когда говорит:
Iye anawawuza kuti, “Nanga zikutheka bwanji kuti Davide poyankhula mwa Mzimu Woyera amatchula Iye ‘Ambuye?’ Pakuti akuti,
44 сказал Господь Господу моему: седи одесную Меня, доколе положу врагов Твоих в подножие ног Твоих?
“Ambuye anati kwa Ambuye wanga: ‘Khala pa dzanja langa lamanja mpaka ndiyike adani ako pansi pa mapazi ako.’
45 Итак, если Давид называет Его Господом, как же Он сын ему?
Ngati tsono Davide amamutchula ‘Ambuye,’ zingatheke bwanji kukhala mwana wake?”
46 И никто не мог отвечать Ему ни слова; и с того дня никто уже не смел спрашивать Его.
Panalibe wina anatha kuyankha, ndipo kuchokera pamenepo, panalibe wina anayerekeza kumufunsa funso.

< От Матфея 22 >