< От Матфея 1 >

1 Родословие Иисуса Христа, Сына Давидова, Сына Авраамова.
Buku lofotokoza za mʼbado wa Yesu Khristu mwana wa Davide, mwana wa Abrahamu:
2 Авраам родил Исаака; Исаак родил Иакова; Иаков родил Иуду и братьев его;
Abrahamu anabereka Isake, Isake anabereka Yakobo, Yakobo anabereka Yuda ndi abale ake.
3 Иуда родил Фареса и Зару от Фамари; Фарес родил Есрома; Есром родил Арама;
Yuda anabereka Perezi ndi Zara, amene amayi awo anali Tamara. Perezi anabereka Hezironi, Hezironi anabereka Aramu.
4 Арам родил Аминадава; Аминадав родил Наассона; Наассон родил Салмона;
Aramu anabereka Aminadabu, Aminadabu anabereka Naasoni, Naasoni anabereka Salimoni.
5 Салмон родил Вооза от Рахавы; Вооз родил Овида от Руфи; Овид родил Иессея;
Salimoni anabereka Bowazi amene amayi ake anali Rahabe, Bowazi anabereka Obedi amene amayi ake anali Rute, Obedi anabereka Yese.
6 Иессей родил Давида царя; Давид царь родил Соломона от бывшей за Уриею;
Yese anabereka Mfumu Davide. Ndipo Davide anabereka Solomoni, amene amayi ake anali mkazi wa Uriya.
7 Соломон родил Ровоама; Ровоам родил Авию; Авия родил Асу;
Solomoni anabereka Rehabiamu, Rehabiamu anabereka Abiya, Abiya anabereka Asa,
8 Аса родил Иосафата; Иосафат родил Иорама; Иорам родил Озию;
Asa anabereka Yehosafati, Yehosafati anabereka Yoramu, Yoramu anabereka Uziya.
9 Озия родил Иоафама; Иоафам родил Ахаза; Ахаз родил Езекию;
Uziya anabereka Yotamu, Yotamu anabereka Ahazi, Ahazi anabereka Hezekiya.
10 Езекия родил Манассию; Манассия родил Амона; Амон родил Иосию;
Hezekiya anabereka Manase, Manase anabereka Amoni, Amoni anabereka Yosiya.
11 Иосия родил Иоакима; Иоаким родил Иехонию и братьев его, перед переселением в Вавилон.
Yosiya anali atabala Yekoniya ndi abale ake pamene Ayuda anatengedwa ukapolo kupita ku Babuloni.
12 По переселении же в Вавилон Иехония родил Салафииля; Салафииль родил Зоровавеля;
Ali ku ukapolo ku Babuloni, Yekoniya anabereka Salatieli, Salatieli anabereka Zerubabeli.
13 Зоровавель родил Авиуда; Авиуд родил Елиакима; Елиаким родил Азора;
Zerubabeli anabereka Abiudi, Abiudi anabereka Eliakimu, Eliakimu anabereka Azoro.
14 Азор родил Садока; Садок родил Ахима; Ахим родил Елиуда;
Azoro anabereka Zadoki, Zadoki anabereka Akimu, Akimu anabereka Eliudi.
15 Елиуд родил Елеазара; Елеазар родил Матфана; Матфан родил Иакова;
Eliudi anabereka Eliezara, Eliezara anabereka Matani, Matani anabereka Yakobo.
16 Иаков родил Иосифа, мужа Марии, от Которой родился Иисус, называемый Христос.
Yakobo anabereka Yosefe, mwamuna wa Mariya. Mariyayu ndiye anabereka Yesu wotchedwa Khristu.
17 Итак всех родов от Авраама до Давида четырнадцать родов; и от Давида до переселения в Вавилон четырнадцать родов; и от переселения в Вавилон до Христа четырнадцать родов.
Kuyambira pa Abrahamu mpaka pa Davide, pali mibado khumi ndi inayi. Ndipo kuyambira pa Davide mpaka pamene Ayuda anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babuloni, pali mibado khumi ndi inayi. Ndiponso kuyambira nthawi ya ukapolo ku Babuloni mpaka pamene Khristu anabadwa, palinso mibado khumi ndi inayi.
18 Рождество Иисуса Христа было так: по обручении Матери Его Марии с Иосифом, прежде нежели сочетались они, оказалось, что Она имеет во чреве от Духа Святаго.
Kubadwa kwa Yesu Khristu kunali motere: Amayi ake, Mariya, anapalidwa ubwenzi ndi Yosefe, koma asanagone malo amodzi, anapezeka ali woyembekezera mwana mwa mphamvu ya Mzimu Woyera.
19 Иосиф же муж Ее, будучи праведен и не желая огласить Ее, хотел тайно отпустить Ее.
Popeza Yosefe mwamuna wake anali munthu wolungama, sanafune kumuchititsa manyazi pomuleka poyera. Choncho anaganiza zomuleka mosaonetsera.
20 Но когда он помыслил это, - се, Ангел Господень явился ему во сне и сказал: Иосиф, сын Давидов! не бойся принять Марию, жену твою, ибо родившееся в Ней есть от Духа Святаго;
Koma akuganiza zimenezi, taonani, mngelo wa Ambuye anamuonekera mʼmaloto nati, “Yosefe mwana wa Davide, usaope kumutenga Mariya kukhala mkazi wako, chifukwa mwana akuyembekezerayo ndi wochokera kwa Mzimu Woyera.
21 родит же Сына, и наречешь Ему имя Иисус, ибо Он спасет людей Своих от грехов их.
Ndipo adzabala mwana wamwamuna, udzamutcha dzina lake Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ake ku machimo awo.”
22 А все сие произошло, да сбудется реченное Господом через пророка, который говорит:
Zonsezi zinachitika kukwaniritsa zimene Ambuye ananena mwa mneneri kuti,
23 се, Дева во чреве приимет и родит Сына, и нарекут имя Ему Еммануил, что значит: с нами Бог.
“Onani namwali adzakhala woyembekezera ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo mwanayo adzamutcha Imanueli,” kutanthauza kuti, “Mulungu ali nafe.”
24 Встав от сна, Иосиф поступил, как повелел ему Ангел Господень, и принял жену свою,
Yosefe atadzuka, anachita zomwe mngelo wa Ambuye uja anamulamulira. Iye anamutenga Mariya kukhala mkazi wake.
25 и не знал Ее. Как наконец Она родила Сына Своего первенца, и он нарек Ему имя Иисус.
Koma sanagone malo amodzi mpaka mwanayo atabadwa ndipo anamutcha dzina lake Yesu.

< От Матфея 1 >