< От Марка 11 >

1 Когда приблизились к Иерусалиму, к Виффагии и Вифании, к горе Елеонской, Иисус посылает двух из учеников Своих
Atayandikira ku Yerusalemu, anafika ku Betifage ndi Betaniya ku phiri la Olivi. Yesu anatuma awiri a ophunzira ake
2 и говорит им: пойдите в селение, которое прямо перед вами; входя в него, тотчас найдете привязанного молодого осла, на которого никто из людей не садился; отвязав его, приведите.
nati kwa iwo, “Pitani ku mudzi uli patsogolo panu, ndipo mukamakalowa, mukapeza mwana wabulu atamangiriridwa pamenepo, amene wina aliyense sanakwerepo. Kamumasuleni ndi kubwera naye kuno.
3 И если кто скажет вам: что вы это делаете? - отвечайте, что он надобен Господу; и тотчас пошлет его сюда.
Ngati wina aliyense akakufunsani kuti, ‘Mukuchita zimenezi chifukwa chiyani?’ Kamuwuzeni kuti, ‘Ambuye akumufuna ndipo akamutumiza kuno msanga.’”
4 Они пошли, и нашли молодого осла, привязанного у ворот на улице, и отвязали его.
Anapita ndipo anakapeza mwana wabulu ali kunja mu msewu waukulu atamumangirira pa chipata. Pamene anamumasula,
5 И некоторые из стоявших там говорили им: что делаете? зачем отвязываете осленка?
anthu ena amene anayima pomwepo anafunsa kuti, “Mukuchita chiyani, kumasula mwana wabuluyo?”
6 Они отвечали им, как повелел Иисус; и те отпустили их.
Iwo anayankha monga mmene Yesu anawawuzira, ndipo anthu aja anawalola kuti apite.
7 И привели осленка к Иисусу, и возложили на него одежды свои; Иисус сел на него.
Atafika naye mwana wabulu kwa Yesu, nayika mikanjo yawo pa buluyo, Iye anakwerapo.
8 Многие же постилали одежды свои по дороге; а другие резали ветви с дерев и постилали по дороге.
Anthu ambiri anayala mikanjo yawo pa msewu, pamene ena anayala nthambi zomwe anadula mʼminda.
9 И предшествовавшие и сопровождавшие восклицали: осанна! благословен Грядущий во имя Господне!
Amene anatsogola ndi iwo amene ankatsatira ankafuwula kuti, “Hosana! “Odala Iye amene akudza mʼdzina la Ambuye!”
10 благословенно грядущее во имя Господа царство отца нашего Давида! осанна в вышних!
“Odala ndi ufumu umene ukubwera wa abambo athu Davide!” “Hosana Mmwambamwamba!”
11 И вошел Иисус в Иерусалим и в храм; и, осмотрев все, как время уже было позднее, вышел в Вифанию с двенадцатью.
Yesu analowa mu Yerusalemu napita ku Nyumba ya Mulungu. Anayangʼana zonse, koma popeza kuti nthawi inali itapita, anatuluka kupita ku Betaniya pamodzi ndi khumi ndi awiriwo.
12 На другой день, когда они вышли из Вифании, Он взалкал;
Mmawa mwake pamene amachoka ku Betaniya, Yesu anamva njala.
13 и, увидев издалека смоковницу, покрытую листьями, пошел, не найдет ли чего на ней; но, придя к ней, ничего не нашел, кроме листьев, ибо еще не время было собирания смокв.
Ataonera patali mtengo wamkuyu uli ndi masamba, anapita kuti akaone ngati unali ndi chipatso chilichonse. Atafika, sanapezemo kanthu koma masamba, chifukwa sinali nthawi ya nkhuyu.
14 И сказал ей Иисус: отныне да не вкушает никто от тебя плода вовек! И слышали то ученики Его. (aiōn g165)
Ndipo Iye anati kwa mtengo, “Palibe amene adzadyenso chipatso kuchokera kwa iwe.” Ndipo ophunzira ake anamva Iye akunena izi. (aiōn g165)
15 Пришли в Иерусалим. Иисус, войдя в храм, начал выгонять продающих и покупающих в храме; и столы меновщиков и скамьи продающих голубей опрокинул;
Atafika ku Yerusalemu, Yesu analowa mʼbwalo lakunja la Nyumba ya Mulungu ndipo anayamba kupirikitsa anthu amene amagula ndi kugulitsa mʼmenemo. Anagubuduza matebulo a osintha ndalama ndi mipando ya ogulitsa nkhunda,
16 и не позволял, чтобы кто пронес через храм какую-либо вещь.
ndipo Iye sanalole aliyense kugulitsa malonda mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu.
17 И учил их, говоря: не написано ли: дом Мой домом молитвы наречется для всех народов? а вы сделали его вертепом разбойников.
Ndipo pamene ankawaphunzitsa, Iye anati, “Kodi sikunalembedwe kuti, ‘Nyumba yanga idzatchedwa Nyumba ya mapemphero kwa anthu a mitundu yonse?’ Koma inu mwayisandutsa ‘phanga la achifwamba.’”
18 Услышали это книжники и первосвященники, и искали, как бы погубить Его, ибо боялись Его, потому что весь народ удивлялся учению Его.
Akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo anamva izi ndipo anayamba kufuna njira yoti amuphere Iye, pakuti amamuopa, chifukwa gulu lonse la anthu linazizwa ndi chiphunzitso chake.
19 Когда же стало поздно, Он вышел вон из города.
Pofika madzulo, iwo anatuluka mu mzindamo.
20 Поутру, проходя мимо, увидели, что смоковница засохла до корня.
Mmamawa, pamene ankayenda, anaona mtengo wamkuyu uja utafota kuyambira ku mizu.
21 И, вспомнив, Петр говорит Ему: Равви! посмотри, смоковница, которую Ты проклял, засохла.
Petro anakumbukira nati kwa Yesu, “Aphunzitsi, taonani! Mtengo wamkuyu munawutemberera uja wafota!”
22 Иисус, отвечая, говорит им:
Yesu anayankha kuti, “Khalani ndi chikhulupiriro mwa Mulungu.
23 имейте веру Божию, ибо истинно говорю вам, если кто скажет горе сей: поднимись и ввергнись в море, и не усомнится в сердце своем, но поверит, что сбудется по словам его, - будет ему, что ни скажет.
Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti ngati wina aliyense angalamule phiri ili kuti, ‘Pita, kadziponye mʼnyanja,’ ndipo wosakayika mu mtima mwake koma kukhulupirira kuti chimene akunena chidzachitika, chidzachitikadi kwa iyeyo.
24 Потому говорю вам: все, чего ни будете просить в молитве, верьте, что получите, - и будет вам.
Nʼchifukwa chake ndikukuwuzani kuti chilichonse chimene mupempha mʼpemphero, khulupirirani kuti mwalandira, ndipo chidzakhala chanu.
25 И когда стоите на молитве, прощайте, если что имеете на кого, дабы и Отец ваш Небесный простил вам согрешения ваши.
Pamene muyimirira kupemphera, ngati muli ndi chifukwa ndi wina, mukhululukireni, kuti Atate anu akumwamba akukhululukireni machimo anu.”
26 Если же не прощаете, то и Отец ваш Небесный не простит вам согрешений ваших.
(Koma ngati simukhululukirana, ngakhale Atate anu akumwamba sadzakhululukira machimo anu).
27 Пришли опять в Иерусалим. И когда Он ходил в храме, подошли к Нему первосвященники и книжники, и старейшины
Iwo anafikanso ku Yerusalemu, ndipo pamene Yesu amayenda mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu, akulu a ansembe, aphunzitsi amalamulo ndi akuluakulu anabwera kwa Iye.
28 и говорили Ему: какою властью Ты это делаешь? и кто Тебе дал власть делать это?
Iwo anafunsa kuti, “Mukuchita izi ndi ulamuliro wanji? Ndipo anakupatsani ulamuliro umenewu ndi ndani?”
29 Иисус сказал им в ответ: спрошу и Я вас об одном, отвечайте Мне; тогда и Я скажу вам, какою властью это делаю.
Yesu anayankha kuti, “Ndikufunsani funso limodzi. Mundiyankhe, ndipo ndikuwuzani ndi ulamuliro wanji umene ndikuchitira izi.
30 Крещение Иоанново с небес было, или от человеков? отвечайте Мне.
Ubatizo wa Yohane, unali wochokera kumwamba, kapena kwa anthu? Ndiwuzeni.”
31 Они рассуждали между собою: если скажем: с небес, - то Он скажет: почему же вы не поверили ему?
Iwo anakambirana pakati pawo ndipo anati, “Tikati, ‘Wochokera kumwamba,’ atifunsa kuti, ‘Nanga nʼchifukwa chiyani simunamukhulupirire?’
32 а сказать: от человеков - боялись народа, потому что все полагали, что Иоанн точно был пророк.
Koma ife tikati, ‘Wochokera kwa anthu.’” (Amaopa anthu, pakuti aliyense amakhulupirira kuti Yohane analidi mneneri).
33 И сказали в ответ Иисусу: не знаем. Тогда Иисус сказал им в ответ: и Я не скажу вам, какою властью это делаю.
Ndipo anamuyankha Yesu kuti, “Sitikudziwa.” Yesu anati, “Nanenso sindikuwuzani kuti ndi ulamuliro wanji ndichitira zimenezi.”

< От Марка 11 >