< От Марка 1 >

1 Начало Евангелия Иисуса Христа, Сына Божия,
Chiyambi cha Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu,
2 как написано у пророков: вот, Я посылаю Ангела Моего пред лицем Твоим, который приготовит путь Твой пред Тобою.
monga zalembedwera mʼbuku la mneneri Yesaya: “Ine ndidzatuma mthenga wanga patsogolo panu, amene adzakonza njira yanu,”
3 Глас вопиющего в пустыне: приготовьте путь Господу, прямыми сделайте стези Ему.
“Mawu a wofuwula mʼchipululu, ‘Konzani njira ya Ambuye, wongolani njira zake.’”
4 Явился Иоанн, крестя в пустыне и проповедуя крещение покаяния для прощения грехов.
Ndipo Yohane anabwera mʼmadera a mʼchipululu nabatiza, ndi kulalikira za ubatizo wa kutembenuka mtima ndi wa chikhululukiro cha machimo.
5 И выходили к нему вся страна Иудейская и Иерусалимляне, и крестились от него все в реке Иордане, исповедуя грехи свои.
Madera onse a ku Yudeya ndi anthu onse a ku Yerusalemu anatuluka napita kwa iye. Akavomereza machimo awo, amawabatiza mu mtsinje wa Yorodani.
6 Иоанн же носил одежду из верблюжьего волоса и пояс кожаный на чреслах своих, и ел акриды и дикий мед.
Yohane amavala zovala zopangidwa ndi ubweya wangamira, ndi lamba wachikopa mʼchiwuno mwake, ndipo amadya dzombe ndi uchi wamthengo.
7 И проповедывал, говоря: идет за мною Сильнейший меня, у Которого я недостоин, наклонившись, развязать ремень обуви Его;
Ndipo uthenga wake unali uwu: “Pambuyo panga pakubwera wina wondiposa ine mphamvu. Ine si woyenera kuwerama ndi kumasula zingwe za nsapato zake.
8 я крестил вас водою, а Он будет крестить вас Духом Святым.
Ine ndikubatizani ndi madzi, koma Iye adzakubatizani ndi Mzimu Woyera.”
9 И было в те дни, пришел Иисус из Назарета Галилейского и крестился от Иоанна в Иордане.
Pa nthawi imeneyo Yesu anabwera kuchokera ku Nazareti wa ku Galileya ndipo anabatizidwa ndi Yohane mu mtsinje wa Yorodani.
10 И когда выходил из воды, тотчас увидел Иоанн разверзающиеся небеса и Духа, как голубя, сходящего на Него
Pamene Yesu ankatuluka mʼmadzi, anaona kumwamba kukutsekuka ndipo Mzimu Woyera akutsikira pa Iye ngati nkhunda.
11 И глас был с небес: Ты Сын Мой возлюбленный, в Котором Мое благоволение.
Ndipo Mawu anamveka kuchokera kumwamba: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa; ndipo ndikondwera nawe.”
12 Немедленно после того Дух ведет Его в пустыню.
Nthawi yomweyo Mzimu Woyera anamutumiza Iye ku chipululu,
13 И был Он там в пустыне сорок дней, искушаемый сатаною, и был со зверями; и Ангелы служили Ему.
ndipo anali mʼchipululumo masiku makumi anayi, akuyesedwa ndi Satana. Anali pakati pa nyama zakuthengo; ndipo angelo anamutumikira.
14 После же того, как предан был Иоанн, пришел Иисус в Галилею, проповедуя Евангелие Царствия Божия
Yohane atamutsekera mʼndende, Yesu anapita ku Galileya nalalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu nati,
15 и говоря, что исполнилось время и приблизилось Царствие Божие: покайтесь и веруйте в Евангелие.
“Nthawi yafika, ufumu wa Mulungu wayandikira. Tembenukani mtima ndi kukhulupirira Uthenga Wabwino!”
16 Проходя же близ моря Галилейского, увидел Симона и Андрея, брата его, закидывающих сети в море, ибо они были рыболовы.
Pamene Yesu ankayenda mʼmbali mwa nyanja ya Galileya, anaona Simoni ndi mʼbale wake Andreya akuponya khoka mʼnyanja, popeza anali asodzi.
17 И сказал им Иисус: идите за Мною, и Я сделаю, что вы будете ловцами человеков.
Yesu anati, “Bwerani, tsateni Ine, ndipo ndidzakusandutsani asodzi a anthu.”
18 И они тотчас, оставив свои сети, последовали за Ним.
Nthawi yomweyo anasiya makoka awo namutsata Iye.
19 И, пройдя оттуда немного, Он увидел Иакова Зеведеева и Иоанна, брата его, также в лодке починивающих сети;
Atapita patsogolo pangʼono, anaona Yakobo ndi mʼbale wake Yohane ana a Zebedayo, ali mʼbwato akukonza makoka awo.
20 и тотчас призвал их. И они, оставив отца своего Зеведея в лодке с работниками, последовали за Ним.
Mosataya nthawi anawayitana, ndipo anasiya abambo awo Zebedayo ndi anyamata aganyu ali mʼbwatomo, namutsata Iye.
21 И приходят в Капернаум; и вскоре в субботу вошел Он в синагогу и учил.
Iwo anapita ku Kaperenawo, ndipo tsiku la Sabata litafika, Yesu analowa mʼsunagoge nayamba kuphunzitsa.
22 И дивились Его учению, ибо Он учил их, как власть имеющий, а не как книжники.
Anthu anadabwa ndi chiphunzitso chake, chifukwa anawaphunzitsa ngati munthu amene anali ndi ulamuliro, osati ngati aphunzitsi amalamulo.
23 В синагоге их был человек, одержимый духом нечистым, и вскричал:
Pomwepo munthu wina mʼsunagogemo amene anali wogwidwa ndi mzimu woyipa anafuwula kuti,
24 оставь! что Тебе до нас, Иисус Назарянин? Ты пришел погубить нас! знаю Тебя, кто Ты, Святый Божий.
“Mukufuna chiyani kwa ife, Yesu wa ku Nazareti? Kodi mwabwera kudzatiwononga? Ndikudziwa kuti ndinu ndani, ndinu Woyerayo wa Mulungu!”
25 Но Иисус запретил ему, говоря: замолчи и выйди из него.
Yesu anadzudzula chiwandacho mwamphamvu nati, “Khala chete! Tuluka mwa iye!”
26 Тогда дух нечистый, сотрясши его и вскричав громким голосом, вышел из него.
Mzimu woyipawo unamugwedeza mwamphamvu ndipo unatuluka mwa iye ukufuwula.
27 И все ужаснулись, так что друг друга спрашивали: что это? что это за новое учение, что Он и духам нечистым повелевает со властью, и они повинуются Ему?
Anthu anadabwa kwambiri kotero kuti anafunsana wina ndi mnzake kuti, “Ichi nʼchiyani? Chiphunzitso chatsopano ndi ulamuliro! Iye akulamula, ngakhale mizimu yoyipa ikumumvera.”
28 И скоро разошлась о Нем молва по всей окрестности в Галилее.
Mbiri yake inafalikira kudera lonse la Galileya mofulumira.
29 Выйдя вскоре из синагоги, пришли в дом Симона и Андрея, с Иаковом и Иоанном.
Atangochoka mu sunagoge, Yesu pamodzi ndi Yakobo ndi Yohane anakalowa mʼnyumba ya Simoni ndi Andreya.
30 Теща же Симонова лежала в горячке; и тотчас говорят Ему о ней.
Mpongozi wa Simoni anali chigonere akudwala malungo, ndipo anamuwuza Yesu za iye.
31 Подойдя, Он поднял ее, взяв ее за руку; и горячка тотчас оставила ее, и она стала служить им.
Ndipo Yesu anapita kwa iye, namugwira dzanja namuthandiza kudzuka. Malungo anachoka ndipo anayamba kuwatumikira.
32 При наступлении же вечера, когда заходило солнце, приносили к Нему всех больных и бесноватых.
Madzulo omwewo dzuwa litalowa anthu anabweretsa kwa Yesu anthu onse odwala ndi ogwidwa ndi ziwanda.
33 И весь город собрался к дверям.
Anthu onse a mʼmudzimo anasonkhana pa khomo,
34 И Он исцелил многих, страдавших различными болезнями; изгнал многих бесов, и не позволял бесам говорить, что они знают, что Он Христос.
Yesu anachiritsa ambiri amene anali ndi matenda osiyanasiyana, komanso anatulutsa ziwanda zambiri, ndipo sanalole kuti ziwandazo ziyankhule chifukwa zinkamudziwa Iye.
35 А утром, встав весьма рано, вышел и удалился в пустынное место, и там молился.
Mmamawa, kukanali kamdima, Yesu anadzuka, nachoka pa nyumbapo kupita kumalo kwa yekha, kumene anakapemphera.
36 Симон и бывшие с ним пошли за Ним
Simoni ndi anzake anapita kokamufunafuna Iye,
37 и, найдя Его, говорят Ему: все ищут Тебя.
ndipo atamupeza, anamuwuza kuti, “Aliyense akukufunani!”
38 Он говорит им: пойдем в ближние селения и города, чтобы Мне и там проповедывать, ибо Я для того пришел.
Yesu anayakha kuti, “Tiyeni tipite kwina ku midzi ya pafupi kuti ndikalalikirenso kumeneko. Ichi ndi chifukwa chimene ndinabwerera.”
39 И Он проповедывал в синагогах их по всей Галилее и изгонял бесов.
Potero anayendayenda mu Galileya, kulalikira mʼmasunagoge awo ndi kutulutsa ziwanda.
40 Приходит к Нему прокаженный и, умоляя Его и падая пред Ним на колени, говорит Ему: если хочешь, можешь меня очистить.
Munthu wakhate anabwera kwa Iye, nagwada, namupempha kuti, “Ngati mukufuna, mukhoza kundiyeretsa.”
41 Иисус, умилосердившись над ним, простер руку, коснулся его и сказал ему: хочу, очистись.
Yesu pomva naye chifundo, anatambasula dzanja lake namukhudza munthuyo nati, “Ndikufuna, yeretsedwa!”
42 После сего слова проказа тотчас сошла с него, и он стал чист.
Nthawi yomweyo khate linachoka ndipo anachiritsidwa.
43 И, посмотрев на него строго, тотчас отослал его
Nthawi yomweyo Yesu anamuwuza kuti apite koma anamuchenjeza kuti,
44 и сказал ему: смотри, никому ничего не говори, но пойди, покажись священнику и принеси за очищение твое, что повелел Моисей, во свидетельство им.
“Wonetsetsa kuti usawuze aliyense za zimenezi. Koma pita, kadzionetse wekha kwa wansembe ndi kukapereka nsembe zimene Mose analamulira zotsimikizira kuyeretsedwa kwanu, ngati umboni kwa iwo.”
45 А он, выйдя, начал провозглашать и рассказывать о происшедшем, так что Иисус не мог уже явно войти в город, но находился вне, в местах пустынных. И приходили к Нему отовсюду.
Mʼmalo mwake anapita nayamba kuyankhula momasuka, nafalitsa mbiriyo. Zotsatira zake, Yesu sanathe kulowa mʼmudzi moonekera, koma anakhala kunja kumalo kopanda anthu. Komabe anthu amabwera kwa Iye kuchokera kulikonse.

< От Марка 1 >