< От Луки 11 >

1 Случилось, что когда Он в одном месте молился, и перестал, один из учеников Его сказал Ему: Господи! научи нас молиться, как и Иоанн научил учеников своих.
Tsiku lina Yesu amapemphera pamalo ena. Atamaliza, mmodzi wa ophunzira ake anati kwa Iye, “Ambuye tiphunzitseni kupemphera, monga momwe Yohane anaphunzitsira ophunzira ake.”
2 Он сказал им: когда молитесь, говорите: Отче наш, сущий на небесах! да святится имя Твое; да приидет Царствие Твое; да будет воля Твоя и на земле, как на небе;
Yesu anawawuza kuti, “Pamene mukupemphera muzinena kuti: “‘Atate, dzina lanu lilemekezedwe, ufumu wanu ubwere.
3 хлеб наш насущный подавай нам на каждый день;
Mutipatse chakudya chathu chalero,
4 и прости нам грехи наши, ибо и мы прощаем всякому должнику нашему; и не введи нас в искушение, но избавь нас от лукавого.
mutikhululukire machimo athu, monga ifenso timakhululukira aliyense amene watilakwira. Ndipo musalole kuti tigwe mʼmayesero.’”
5 И сказал им: положим, что кто-нибудь из вас, имея друга, придет к нему в полночь и скажет ему: друг! дай мне взаймы три хлеба,
Kenaka anawawuza kuti, “Tiyerekeze: Mmodzi mwa inu atakhala ndi bwenzi lake, ndipo iye nʼkupita ku nyumba yake pakati pa usiku, nakanena kuti, ‘Mnzanga, bwereke malofu atatu abuledi,
6 ибо друг мой с дороги зашел ко мне, и мне нечего предложить ему;
chifukwa ndalandira bwenzi langa amene ali pa ulendo ndipo ine ndilibe choti ndimupatse.’
7 а тот изнутри скажет ему в ответ: не беспокой меня, двери уже заперты, и дети мои со мною на постели; не могу встать и дать тебе.
“Ndipo yerekezani kuti amene ali mʼnyumbamo ndi kuyankha kuti, ‘Usandivutitse ine, ndatseka kale chitseko, ndipo ine ndi ana anga tagona. Ine sindingadzukenso kuti ndidzakupatse.’
8 Если, говорю вам, он не встанет и не даст ему по дружбе с ним, то по неотступности его, встав, даст ему, сколько просит.
Ine ndikukuwuzani kuti adzadzuka ndi kumupatsa bulediyo, osati chifukwa ndi bwenzi lake, koma chifukwa cha liwuma la munthu wopemphayo, ndipo kudzamupatsa zonse zimene akuzifuna.
9 И Я скажу вам: просите, и дано будет вам; ищите, и найдете; стучите, и отворят вам,
“Choncho Ine ndikunena kwa inu kuti: Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza. Gogodani ndipo adzakutsekulirani.
10 ибо всякий просящий получает, и ищущий находит, и стучащему отворят.
Pakuti aliyense amene amapempha amalandira. Munthu amene amafunafuna amapeza. Iye amene amagogoda amamutsekulira.
11 Какой из вас отец, когда сын попросит у него хлеба, подаст ему камень? или, когда попросит рыбы, подаст ему змею вместо рыбы?
“Ndani mwa inu abambo, kodi mwana wanu atapempha nsomba, mʼmalo mwake mungamupatse njoka?
12 Или, если попросит яйца, подаст ему скорпиона?
Kapena atapempha dzira, kodi mungamupatse chinkhanira?
13 Итак, если вы, будучи злы, умеете даяния благие давать детям вашим, тем более Отец Небесный даст Духа Святаго просящим у Него.
Tsono ngati inu, anthu oyipa, mumadziwa kupereka mphatso zabwino kwa ana anu, koposa kotani Atate anu akumwamba, angalephere bwanji kupereka Mzimu Woyera kwa amene awapempha!”
14 Однажды изгнал Он беса, который был нем; и когда бес вышел, немой стал говорить; и народ удивился.
Yesu amatulutsa chiwanda chimene chinali chosayankhula. Chiwandacho chitatuluka, munthu wosayankhulayo anayankhula, ndipo gulu la anthu linadabwa.
15 Некоторые же из них говорили: Он изгоняет бесов силою веельзевула, князя бесовского.
Koma ena mwa iwo anati, “Iye akutulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebabu mfumu ya ziwanda.”
16 А другие, искушая, требовали от Него знамения с неба.
Ena anamuyesa pomufunsa chizindikiro chochokera kumwamba.
17 Но Он, зная помышления их, сказал им: всякое царство, разделившееся само в себе, опустеет, и дом, разделившийся сам в себе, падет;
Yesu anadziwa maganizo awo ndipo anawawuza kuti, “Ufumu uliwonse wogawikana udzawonongeka, ndipo nyumba yogawikana idzapasuka.
18 если же и сатана разделится сам в себе, то как устоит царство его? а вы говорите, что Я силою веельзевула изгоняю бесов;
Ngati Satana adziwukira yekha, ufumu wake ungalimbe bwanji? Ine ndikunena izi chifukwa inu mukuti Ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebabu.
19 и если Я силою веельзевула изгоняю бесов, то сыновья ваши чьею силою изгоняют их? Посему они будут вам судьями.
Tsopano ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebabu, nanga ophunzira anu amazitulutsa ndi mphamvu ya ndani? Choncho, iwowo ndiye adzakhala oweruza anu.
20 Если же Я перстом Божиим изгоняю бесов, то, конечно, достигло до вас Царствие Божие.
Koma ngati ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Mulungu, ndiye kuti ufumu wa Mulungu wafika pakati panu.
21 Когда сильный с оружием охраняет свой дом, тогда в безопасности его имение;
“Munthu wamphamvu, amene ali ndi zida, akamalondera nyumba yake, katundu wake amatetezedwa.
22 когда же сильнейший его нападет на него и победит его, тогда возьмет все оружие его, на которое он надеялся, и разделит похищенное у него.
Koma pakabwera wina wamphamvu zoposa namugonjetsa, amalanda zida zimene munthuyo amazidalirazo ndi kugawa katundu wake.
23 Кто не со Мною, тот против Меня; и кто не собирает со Мною, тот расточает.
“Munthu amene sali mbali yanga ndi wotsutsana nane. Ndipo wosandithandiza kusonkhanitsa, ameneyo ndi womwaza.
24 Когда нечистый дух выйдет из человека, то ходит по безводным местам, ища покоя, и, не находя, говорит: возвращусь в дом мой, откуда вышел;
“Mzimu woyipa ukatuluka mwa munthu, umakayendayenda ku malo owuma, kufunafuna malo opumulirako ndipo suwapeza. Kenaka umati, ‘Ndibwerera ku nyumba kwanga kumene ndachokera.’
25 и, придя, находит его выметенным и убранным;
Ukafika umapeza mʼnyumba mosesedwa bwino ndi mokonza.
26 тогда идет и берет с собою семь других духов, злейших себя, и, войдя, живут там, - и бывает для человека того последнее хуже первого.
Pamenepo umakatenga mizimu ina isanu ndi iwiri yoyipa kwambiri kuposa iwowo ndipo imakalowa ndi kukhala mʼmenemo. Ndipo makhalidwe otsiriza a munthuyo amakhala oyipa kuposa oyamba aja.”
27 Когда же Он говорил это, одна женщина, возвысив голос из народа, сказала Ему: блаженно чрево, носившее Тебя, и сосцы, Тебя питавшие!
Pamene Yesu ankanena zonsezi, mayi wina mʼgulu la anthuwo anafuwula nati, “Ndi wodala amayi amene anakubalani ndi kukulerani!”
28 А Он сказал: блаженны слышащие слово Божие и соблюдающие его.
Koma Yesu anayankha kuti, “Odala ndi amene amamva mawu a Mulungu ndi kuwasunga.”
29 Когда же народ стал сходиться во множестве, Он начал говорить: род сей лукав, он ищет знамения, и знамение не дастся ему, кроме знамения Ионы пророка;
Pamene gulu la anthu limachuluka, Yesu anati, “Uno ndi mʼbado oyipa. Umafuna kuona chizindikiro chodabwitsa. Koma sadzachiona kupatula chizindikiro chija cha Yona.
30 ибо как Иона был знамением для Ниневитян, так будет и Сын Человеческий для рода сего.
Monga Yona uja anali chizindikiro kwa anthu ku Ninive, momwemonso Mwana wa Munthu adzakhala chizindikiro kwa anthu a mʼbado uno.
31 Царица южная восстанет на суд с людьми рода сего и осудит их, ибо она приходила от пределов земли послушать мудрости Соломоновой; и вот, здесь больше Соломона.
Mfumu yayikazi yakummwera idzayimirira tsiku lachiweruzo pamodzi ndi anthu a mʼbado uno ndipo idzawatsutsa, chifukwa iyo inachokera kumapeto a dziko lapansi kudzamva nzeru za Solomoni. Ndipo tsopano pano pali wina woposa Solomoni.
32 Ниневитяне восстанут на суд с родом сим и осудят его, ибо они покаялись от проповеди Иониной, и вот, здесь больше Ионы.
Anthu a ku Ninive adzayimirira tsiku lachiweruzo pamodzi ndi mʼbado uno ndipo adzawutsutsa, pakuti anatembenuka mtima ndi ulaliki wa Yona. Ndipo tsopano pano pali wina woposa Yona.
33 Никто, зажегши свечу, не ставит ее в сокровенном месте, ни под сосудом, но на подсвечнике, чтобы входящие видели свет.
“Palibe amene amayatsa nyale ndi kuyiika pa malo poti sionekera, kapena pansi pa mtsuko. Mʼmalo mwake amayika pa choyikapo chake, kuti iwo amene akulowamo aone kuwunika.
34 Светильник тела есть око; итак, если око твое будет чисто, то и все тело твое будет светло; а если оно будет худо, то и тело твое будет темно.
Diso lanu ndi nyale ya thupi lanu. Pamene maso anu ali bwino, thupi lanu lonse limadzaza ndi kuwunika. Koma ngati ali oyipa, thupi lanunso ndi lodzaza ndi mdima.
35 Итак, смотри: свет, который в тебе, не есть ли тьма?
Onetsetsani tsono, kuti kuwunika kuli mwa inu si mdima.
36 Если же тело твое все светло и не имеет ни одной темной части, то будет светло все так, как бы светильник освещал тебя сиянием.
Choncho, ngati thupi lanu lonse ndi lodzaza ndi kuwunika, ndiye kuti palibe dera lina lili mdima, lonselo lidzakhala kuwunika, monga momwe kuwunika kwa nyale kumakuwalirani.”
37 Когда Он говорил это, один фарисей просил Его к себе обедать. Он пришел и возлег.
Yesu atamaliza kuyankhula, Mfarisi wina anamuyitana kuti akadye naye. Tsono Yesu analowa mʼnyumba ndi kukhala podyera.
38 Фарисей же удивился, увидев, что Он не умыл рук перед обедом.
Mfarisiyo anadabwa atazindikira kuti Yesu anayamba kudya wosatsata mwambo wawo wakasambidwe ka mʼmanja.
39 Но Господь сказал ему: ныне вы, фарисеи, внешность чаши и блюда очищаете, а внутренность ваша исполнена хищения и лукавства.
Kenaka Ambuye anamuwuza kuti, “Inu Afarisi mumatsuka kunja kwa chikho ndi mbale, koma mʼkati mwanu ndi modzaza ndi kudzikonda ndi zoyipa.
40 Неразумные! не Тот же ли, Кто сотворил внешнее, сотворил и внутреннее?
Anthu opusa inu! Kodi amene anapanga zamʼkati sanapangenso zakunja?
41 Подавайте лучше милостыню из того, что у вас есть, тогда все будет у вас чисто.
Koma popereka kwa osauka, perekani chimene chili mʼkati ndipo chilichonse chidzakhala choyera.
42 Но горе вам, фарисеям, что даете десятину с мяты, руты и всяких овощей, и нерадите о суде и любви Божией: сие надлежало делать, и того не оставлять.
“Tsoka kwa inu Afarisi, chifukwa mumapereka kwa Mulungu chakhumi cha timbewu tonunkhira, ndi timbewu tokometsera chakudya ndi mbewu zina zonse za mʼmunda, koma mumakana chilungamo ndi chikondi cha Mulungu. Mumayenera kuchita zomalizirazi osalekanso kuchita zoyambazi.
43 Горе вам, фарисеям, что любите председания в синагогах и приветствия в народных собраниях.
“Tsoka kwa inu Afarisi, chifukwa mumakonda mipando yofunika kwambiri mʼmasunagoge ndi malonje mʼmalo a pa msika.
44 Горе вам, книжники и фарисеи, лицемеры, что вы - как гробы скрытые, над которыми люди ходят и не знают того.
“Tsoka kwa inu Afarisi, chifukwa muli ngati manda osawaka, amene anthu amangoyendapo, osawadziwa.”
45 На это некто из законников сказал Ему: Учитель! Говоря это, Ты и нас обижаешь.
Mmodzi mwa akatswiri a Malamulo anamuyankha Iye nati, “Aphunzitsi, pamene mukunena zinthu izi, mukutinyoza ifenso?”
46 Но Он сказал: и вам, законникам, горе, что налагаете на людей бремена неудобоносимые, а сами и одним перстом своим не дотрагиваетесь до них.
Yesu anayankha kuti, “Tsoka kwa inunso akatswiri a Malamulo chifukwa mumawalemetsa anthu ndi mtolo umene iwo sangathe kunyamula, ndipo inu eni ake simutenga chala chanu kuti muwathandize.
47 Горе вам, что строите гробницы пророкам, которых избили отцы ваши:
“Tsoka kwa inu, chifukwa mumawaka manda a aneneri, komatu ndi makolo anu amene anawapha.
48 сим вы свидетельствуете о делах отцов ваших и соглашаетесь с ними, ибо они избили пророков, а вы строите им гробницы.
Tsono potero mumachitira umboni za zimene makolo anu anachita. Anapha aneneri, ndipo inu mumawaka manda awo.
49 Потому и премудрость Божия сказала: пошлю к ним пророков и Апостолов, и из них одних убьют, а других изгонят,
Chifukwa cha ichi, Mulungu mu nzeru zake anati, ‘Ine ndidzawatumizira aneneri ndi atumwi, ena mwa iwo adzawapha ndipo ena adzawazunza.’
50 да взыщется от рода сего кровь всех пророков, пролитая от создания мира,
Choncho mʼbado uwu udzasenza magazi a aneneri onse amene anakhetsedwa kuyambira pachiyambi cha dziko,
51 от крови Авеля до крови Захарии, убитого между жертвенником и храмом. Ей, говорю вам, взыщется от рода сего.
kuyambira magazi a Abele kufikira magazi a Zakariya amene anaphedwa pakati pa guwa lansembe ndi malo opatulika. Inde, Ine ndikuwuzani inu, mʼbado uno udzasenza zonsezi.
52 Горе вам, законникам, что вы взяли ключ разумения: сами не вошли, и входящим воспрепятствовали.
“Tsoka kwa inu akatswiri a Malamulo, chifukwa mwachotsa kiyi wachidziwitso inu eni akenu musanalowemo, ndipo mwatsekerezanso iwo amene amalowa.”
53 Когда Он говорил им это, книжники и фарисеи начали сильно приступать к Нему, вынуждая у Него ответы на многое,
Pamene Yesu anachokamo, Afarisi ndi aphunzitsi a Malamulo anayamba kumamutsutsa koopsa ndi kumupanikiza ndi mafunso,
54 подыскиваясь под Него и стараясь уловить что-нибудь из уст Его, чтобы обвинить Его.
pofuna kumukola muchina chilichonse chimene Iye angayankhule.

< От Луки 11 >