< Иисус Навин 4 >

1 Когда весь народ перешел чрез Иордан, Господь сказал Иисусу:
Anthu onse atatha kuwoloka Yorodani, Yehova anati kwa Yoswa,
2 возьмите себе из народа двенадцать человек, по одному человеку из колена,
“Sankha amuna khumi ndi awiri, mmodzi pa fuko lililonse.
3 и дайте им повеление и скажите: возьмите себе отсюда, из средины Иордана, где стояли ноги священников неподвижно, двенадцать камней, и перенесите их с собою, и положите их на ночлеге, где будете ночевать в эту ночь.
Tsono uwalamule kuti, ‘Tengani miyala khumi ndi iwiri pakati penipeni pa mtsinje wa Yorodani, pamalo pamene ansembe anayimirirapo. Miyalayo muwoloke nayo ndi kudzayitula pamalo pamene mukagone usiku uno.’”
4 Иисус призвал двенадцать человек, которых назначил из сынов Израилевых, по одному человеку из колена,
Choncho Yoswa anayitana amuna khumi ndi awiri amene anawasankha aja kuchokera pakati pa Aisraeli, mmodzi pa fuko lililonse,
5 и сказал им Иисус: пойдите пред ковчегом Господа Бога вашего в средину Иордана и возьмите оттуда и положите на плечо свое каждый по одному камню, по числу колен сынов Израилевых,
ndipo anawawuza kuti, “Lowani pakati pa mtsinje wa Yorodani, patsogolo pa Bokosi la Yehova Mulungu wanu. Ndipo aliyense wa inu atenge mwala pa phewa lake, monga mwa chiwerengero cha mafuko a Aisraeli,
6 чтобы они были у вас лежащим всегда знамением; когда спросят вас в последующее время сыны ваши и скажут: “к чему у вас эти камни?”,
kuti ikhale chizindikiro kwa inu. Mʼtsogolo muno ana anu akamadzakufunsani kuti, ‘Kodi miyala iyi ikutanthauza chiyani?’
7 вы скажете им: “в память того, что вода Иордана разделилась пред ковчегом завета Господа всей земли; когда он переходил чрез Иордан, тогда вода Иордана разделилась”; таким образом камни сии будут у вас для сынов Израилевых памятником навек.
Muzidzawawuza kuti, ‘Madzi a Yorodani analeka kuyenda pamene Bokosi la Chipangano la Yehova linkawoloka mtsinjewo. Miyala iyi idzakhala chikumbutso kwa anthu a Israeli kwa muyaya.’”
8 И сделали сыны Израилевы так, как приказал Иисус: взяли двенадцать камней из Иордана, как говорил Господь Иисусу, по числу колен сынов Израилевых, и перенесли их с собою на ночлег, и положили их там.
Aisraeli anachitadi monga Yoswa anawalamulira. Iwo ananyamula miyala khumi ndi iwiri kuchokera pakati pa Yorodani, fuko lililonse la Israeli mwala wake, monga Yehova analamulira Yoswa. Miyalayo anapita nayo ku misasa yawo nakayikhazika kumeneko.
9 И другие двенадцать камней поставил Иисус среди Иордана на месте, где стояли ноги священников, несших ковчег завета Господня. Они там и до сего дня.
Yoswa anayimika miyala khumi ndi iwiri imene inali pakati pa Yorodani pamalo pamene ansembe onyamula Bokosi la Chipangano anayimapo. Ndipo miyalayo ili pamalo pomwepo mpaka lero lino.
10 Священники, несшие ковчег завета Господня, стояли среди Иордана, доколе не окончено было Иисусом все, что Господь повелел Иисусу сказать народу так, как завещал Моисей Иисусу; а народ между тем поспешно переходил.
Ansembe onyamula Bokosi lija anayimirirabe pakati pa Yorodani mpaka zonse zimene Yehova analamulira Yoswa kuti awuze anthu zinatha. Zimenezi zinali monga momwe Mose anamufotokozera Yoswa. Tsono anthu anawoloka mtsinjewo mofulumira.
11 Когда весь народ перешел Иордан, тогда перешел и ковчег завета Господня, и священники пред народом;
Anthu atatha kuwoloka, ansembe anatsogolera anthuwo atanyamula Bokosi la Yehova.
12 и сыны Рувима и сыны Гада и половина колена Манассиина перешли вооруженные впереди сынов Израилевых, как говорил им Моисей.
Anthu a fuko la Rubeni, Gadi ndi theka la fuko la Manase anawoloka patsogolo pa Aisraeli ali ndi zida, monga momwe Mose anawalamulira.
13 Около сорока тысяч вооруженных на брань перешло пред Господом на равнины Иерихонские, чтобы сразиться.
Asilikali pafupifupi 40,000 anawoloka napita kukayima mʼchigwa cha Yeriko kukonzekera nkhondo.
14 В тот день прославил Господь Иисуса пред очами всего Израиля и стали бояться его, как боялись Моисея, во все дни жизни его.
Zimene Yehova anachita tsiku limeneli zinapatsa anthu mtima wolemekeza Yoswa. Ndipo anamulemekeza masiku onse a moyo wake, monga momwe analemekezera Mose.
15 И сказал Господь Иисусу, говоря:
Kenaka Yehova anati kwa Yoswa,
16 прикажи священникам, несущим ковчег откровения, выйти из Иордана.
“Lamula ansembe onyamula Bokosi la Chipanganowo kuti atuluke mu Yorodani.”
17 Иисус приказал священникам и сказал: выйдите из Иордана.
Choncho Yoswa anawalamuladi ansembe aja kuti atuluke mu Yorodani muja.
18 И когда священники, несшие ковчег завета Господня, вышли из Иордана, то, лишь только стопы ног их ступили на сушу, вода Иордана устремилась по своему месту и пошла, как вчера и третьего дня, выше всех берегов своих.
Ansembe onyamula Bokosi la Chipangano la Yehova aja atangotuluka mu mtsinje muja nʼkuponda powuma, madzi a mu Yorodani anayambanso kuyenda ngati poyamba mpaka kumasefukira.
19 И вышел народ из Иордана в десятый день первого месяца и поставил стан в Галгале, на восточной стороне Иерихона.
Aisraeli anawoloka Yorodani tsiku lakhumi la mwezi woyamba ndipo anakamanga misasa yawo ku Giligala mbali ya kummawa kwa Yeriko.
20 И двенадцать камней, которые взяли они из Иордана, Иисус поставил в Галгале
Ku Giligala, Yoswa anayimikako miyala khumi ndi iwiri imene anayitenga mu Yorodani ija.
21 и сказал сынам Израилевым: когда спросят в последующее время сыны ваши отцов своих: “что значат эти камни?”,
Ndipo iye anati kwa Aisraeli, “Mʼtsogolo muno pamene adzukulu anu adzafunsa makolo awo kuti, ‘Kodi miyala iyi ikutanthauza chiyani?’
22 скажите сынам вашим: “Израиль перешел чрез Иордан сей по суше”,
Muzidzawawuza kuti, ‘Aisraeli anawoloka Yorodani pansi pali powuma.’
23 ибо Господь Бог ваш иссушил воды Иордана для вас, доколе вы не перешли его, так же, как Господь, Бог ваш, сделал с Чермным морем, которое иссушил Господь, Бог ваш, перед нами, доколе мы не перешли его,
Pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye anawumitsa Yorodani pamaso panu mpaka inu mutawoloka. Yehova Mulungu wanu anaphwetsa madzi a Yorodani monga mmene anachitira ndi Nyanja Yofiira mpaka ife tinawoloka powuma.
24 дабы все народы земли познали, что рука Господня сильна, и дабы вы боялись Господа, Бога вашего, во все дни.
Iye anachita zimenezi kuti anthu onse pa dziko lapansi adziwe kuti dzanja la Yehova ndi lamphamvu, ndi kuti inu muziopa Yehova Mulungu wanu masiku onse.”

< Иисус Навин 4 >