< От Иоанна 7 >

1 После сего Иисус ходил по Галилее, ибо по Иудее не хотел ходить, потому что Иудеи искали убить Его.
Zitatha izi Yesu anayendayenda mu Galileya, ndi cholinga chakuti asafike ku Yudeya chifukwa Ayuda kumeneko amadikira kuti amuphe.
2 Приближался праздник Иудейский поставление кущей.
Koma phwando la Ayuda lamisasa litayandikira,
3 Тогда братья Его сказали Ему: выйди отсюда и пойди в Иудею, чтобы и ученики Твои видели дела, которые Ты делаешь.
abale a Yesu anati kwa Iye, “Inu muyenera kuchoka kuno ndi kupita ku Yudeya, kuti ophunzira anu akaone zodabwitsa zomwe mumachita.
4 Ибо никто не делает чего-либо втайне и ищет сам быть известным. Если Ты творишь такие дела, то яви Себя миру.
Palibe wina aliyense amene amafuna kukhala wodziwika amachita zinthu mseri. Popeza Inu mukuchita zinthu izi, mudzionetsere nokha ku dziko la pansi.”
5 Ибо и братья Его не веровали в Него.
Pakuti ngakhale abale ake omwe sanamukhulupirire.
6 На это Иисус сказал им: Мое время еще не настало, а для вас всегда время.
Choncho Yesu anawawuza iwo kuti, “Nthawi yanga yoyenera sinafike; kwa inu nthawi ina iliyonse ndi yoyenera.
7 Вас мир не может ненавидеть, а Меня ненавидит, потому что Я свидетельствую о нем, что дела его злы.
Dziko lapansi silingakudeni inu, koma limandida Ine chifukwa Ine ndimachitira umboni kuti zomwe limachita ndi zoyipa.
8 Вы пойдите на праздник сей; а Я еще не пойду на сей праздник, потому что Мое время еще не исполнилось.
Inu pitani kuphwando. Ine sindipita tsopano kuphwando ili chifukwa kwa Ine nthawi yoyenera sinafike.”
9 Сие сказав им, остался в Галилее.
Atanena izi, Iye anakhalabe mu Galileya.
10 Но когда пришли братья Его, тогда и Он пришел на праздник не явно, а как бы тайно.
Komabe, abale ake atanyamuka kupita kuphwando, Iye anapitanso, osati moonekera, koma mseri.
11 Иудеи же искали Его на празднике и говорили: где Он?
Tsopano kuphwandoko Ayuda anakamufunafuna ndi kumafunsana kuti, “Kodi munthu ameneyu ali kuti?”
12 И много толков было о Нем в народе: одни говорили, что Он добр; а другие говорили: нет, но обольщает народ.
Pakuti pa chigulu cha anthu panali kunongʼona ponseponse za Iye. Ena ankanena kuti, “Iye ndi munthu wabwino.” Ena ankayankha kuti, “Ayi, Iye amanamiza anthu.”
13 Впрочем, никто не говорил о Нем явно, боясь Иудеев.
Koma panalibe amene ankanena kalikonse poyera za Iye chifukwa choopa Ayuda.
14 Но в половине уже праздника вошел Иисус в храм и учил.
Phwando lili pakatikati, Yesu anapita ku bwalo la Nyumba ya Mulungu ndi kuyamba kuphunzitsa.
15 И дивились Иудеи, говоря: как Он знает Писания, не учившись?
Ayuda anadabwa ndipo anafunsa kuti, “Kodi munthu uyu nzeru izi anazitenga kuti popanda kuphunzira?”
16 Иисус, отвечая им, сказал: Мое учение - не Мое, но Пославшего Меня;
Yesu anayankha kuti, “Chiphunzitso changa si cha Ine ndekha. Chimachokera kwa Iye amene anandituma.
17 кто хочет творить волю Его, тот узнает о сем учении, от Бога ли оно, или Я Сам от Себя говорю.
Ngati munthu asankha kuchita chifuniro cha Mulungu, adzazindikira ngati chiphunzitso changa nʼchochokera kwa Mulungu kapena ngati ndi mwa Ine ndekha.
18 Говорящий сам от себя ищет славы себе; а Кто ищет славы Пославшему Его, Тот истинен, и нет неправды в Нем.
Iye amene amayankhula za Iye mwini amatero kuti adzipezere ulemu, koma amene amagwira ntchito kuti amene anamutuma alandire ulemu, ameneyo ndiye munthu woona; mu mtima mwake mulibe chinyengo chilichonse.
19 Не дал ли вам Моисей закона? и никто из вас не поступает по закону. За что ищете убить Меня?
Kodi Mose sanakupatseni lamulo? Komatu palibe ndi mmodzi yemwe mwa inu amene akusunga lamulo. Nʼchifukwa chiyani mukufuna kundipha Ine?”
20 Народ сказал в ответ: не бес ли в Тебе? кто ищет убить Тебя?
Gulu la anthu linayankha kuti, “Iwe ndiye wagwidwa ndi ziwanda. Ndani akufuna kukupha?”
21 Иисус, продолжая речь, сказал им: одно дело сделал Я, и все вы дивитесь.
Yesu anawawuza kuti, “Ine ndinachita chodabwitsa chimodzi ndipo inu mwadabwa.
22 Моисей дал вам обрезание хотя оно не от Моисея, но от отцов, и в субботу вы обрезываете человека.
Koma, chifukwa chakuti Mose anakulamulani kuti muzichita mdulidwe (ngakhale kuti sunachokere kwa Mose, koma kwa makolo anu), inuyo mumachita mdulidwe mwana tsiku la Sabata.
23 Если в субботу принимает человек обрезание, чтобы не был нарушен закон Моисеев, - на Меня ли негодуете за то, что Я всего человека исцелил в субботу?
Tsopano ngati mwana angachite mdulidwe pa Sabata kuti lamulo la Mose lisaswedwe, nʼchifukwa chiyani mukundipsera mtima chifukwa chochiritsa munthu pa Sabata?
24 Не судите по наружности, но судите судом праведным.
Musamaweruze potengera maonekedwe chabe, koma weruzani molungama.”
25 Тут некоторые из Иерусалимлян говорили: не Тот ли это, Которого ищут убить?
Pa nthawi imeneyi anthu ena a ku Yerusalemu anayamba kufunsana kuti, “Kodi uyu si munthu uja akufuna kumuphayu?
26 Вот, Он говорит явно, и ничего не говорят Ему: не удостоверились ли начальники, что Он подлинно Христос?
Uyu ali apa, kuyankhula poyera, ndipo iwo sakunena kanthu kwa Iye. Kodi olamulira atsimikizadi kuti Iye ndi Khristu?
27 Но мы знаем Его, откуда Он; Христос же когда придет, никто не будет знать, откуда Он.
Koma ife tikudziwa kumene achokera munthuyu; pamene Khristu adzabwere, palibe amene adzadziwa kumene akuchokera.”
28 Тогда Иисус возгласил в храме, уча и говоря: и знаете Меня, и знаете, откуда Я; и Я пришел не Сам от Себя, но истинен Пославший Меня, Которого вы не знаете.
Kenaka Yesu, akuphunzitsabe mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu anafuwula kuti, “Zoona, mukundidziwa Ine, ndipo mukudziwa kumene ndikuchokera. Ine sindili pano mwa Ine ndekha, koma Iye amene anandituma Ine ndi woona. Inu simukumudziwa,
29 Я знаю Его, потому что Я от Него, и Он послал Меня.
koma Ine ndikumudziwa chifukwa ndichokera kwa Iyeyo ndipo ndiye amene anandituma Ine.”
30 И искали схватить Его, но никто не наложил на Него руки, потому что еще не пришел час Его.
Chifukwa cha izi iwo anayesa kumugwira Iye, koma palibe aliyense amene anayika dzanja lake pa Iye, chifukwa nthawi yake inali isanafike.
31 Многие же из народа уверовали в Него и говорили: когда придет Христос, неужели сотворит больше знамений, нежели сколько Сей сотворил?
Komabe, ambiri a mʼchigulucho anamukhulupirira Iye. Iwo anati, “Kodi pamene Khristu abwera, adzachita zizindikiro zodabwitsa zambiri kuposa munthu uyu?”
32 Услышали фарисеи такие толки о Нем в народе, и послали фарисеи и первосвященники служителей - схватить Его.
Afarisi anamva chigulucho chikunongʼona zinthu zotere za Iye. Kenaka akulu a ansembe ndi Afarisi anatumiza asilikali a mʼNyumba ya Mulungu kuti akamumange Iye.
33 Иисус же сказал им: еще недолго быть Мне с вами, и пойду к Пославшему Меня;
Yesu anati, “Ine ndili ndi inu kwa kanthawi kochepa chabe, ndipo kenaka ndizipita kwa Iye amene anandituma Ine.
34 будете искать Меня, и не найдете; и где буду Я, туда вы не можете придти.
Inu mudzandifunafuna koma simudzandipeza; ndipo kumene Ine ndili inu simungathe kubwera.”
35 При сем Иудеи говорили между собою: куда Он хочет идти, так что мы не найдем Его? Не хочет ли Он идти в Еллинское рассеяние и учить Еллинов?
Ayuda anati kwa wina ndi mnzake, “Kodi munthu uyu akuganizira zoti apite kuti kumene ife sitingathe kumupeza Iye? Kodi Iye adzapita kumene anthu amakhala mobalalikana pakati pa Agriki, ndi kuphunzitsa Agriki?
36 Что значат сии слова, которые Он сказал: будете искать Меня, и не найдете; и где буду Я, туда вы не можете придти?
Kodi Iye amatanthauza chiyani pamene anati, ‘Inu mudzandifunafuna koma simudzandipeza,’ ndi ‘Kumene Ine ndili, inu simungathe kubwera?’”
37 В последний же великий день праздника стоял Иисус и возгласил, говоря: кто жаждет, иди ко Мне и пей.
Pa tsiku lomaliza ndi lalikulu kwambiri laphwando, Yesu anayimirira nafuwula nati, “Ngati munthu ali ndi ludzu, abwere kwa Ine kuti adzamwe.
38 Кто верует в Меня, у того, как сказано в Писании, из чрева потекут реки воды живой.
Malemba kuti ‘Aliyense amene akhulupirira Ine, mitsinje yamadzi amoyo idzatuluka kuchokera mʼkati mwake.’”
39 Сие сказал Он о Духе, Которого имели принять верующие в Него: ибо еще не было на них Духа Святаго, потому что Иисус еще не был прославлен.
Ponena izi Iye amatanthauza Mzimu Woyera, amene adzalandire amene amakhulupirira Iye. Pa nthawiyi nʼkuti Mzimu Woyera asanaperekedwe, pakuti Yesu anali asanalemekezedwe.
40 Многие из народа, услышав сии слова, говорили: Он точно пророк.
Pakumva mawu ake, ena a anthuwo anati, “Zoonadi munthu uyu ndi mneneri.”
41 Другие говорили: это Христос. А иные говорили: разве из Галилеи Христос придет?
Ena anati, “Iye ndiye Khristu.” Komanso ena anafunsa kuti, “Kodi Khristu angachokere bwanji ku Galileya?
42 Не сказано ли в Писании, что Христос придет от семени Давидова и из Вифлеема, из того места, откуда был Давид?
Kodi Malemba samanena kuti Khristu adzachokera mʼbanja la Davide, ndi ku Betelehemu mu mzinda umene Davide anakhalamo?”
43 Итак произошла о Нем распря в народе.
Kotero anthu anagawikana chifukwa cha Yesu.
44 Некоторые из них хотели схватить Его; но никто не наложил на Него рук.
Ena anafuna kumugwira Iye, koma palibe amene anayika dzanja pa Iye.
45 Итак служители возвратились к первосвященникам и фарисеям, и сии сказали им: для чего вы не привели Его?
Pomaliza asilikali a mʼNyumba ya Mulungu anabwerera kwa akulu a ansembe ndi Afarisi amene anawafunsa iwo kuti, “Kodi ndi chifukwa chiyani simunamugwire Iye?”
46 Служители отвечали: никогда человек не говорил так, как Этот Человек.
Asilikali aja anati, “Palibe wina amene anayankhula ngati Munthu ameneyo nʼkale lonse.”
47 Фарисеи сказали им: неужели и вы прельстились?
Afarisi anawadzudzula nati, “Kodi mukutanthauza kuti Iye anakunamizani inunso?”
48 Уверовал ли в Него кто из начальников или из фарисеев?
“Kodi alipo ena a olamulira kapena a Afarisi, anamukhulupirira Iye?
49 Но этот народ невежда в законе, проклят он.
Ayi! Koma gulu limene silidziwa malamulo ndi lotembereredwa.”
50 Никодим, приходивший к Нему ночью, будучи один из них, говорит им:
Nekodimo, amene anapita kwa Yesu poyamba paja ndipo anali mmodzi wa iwo, anafunsa kuti,
51 судит ли закон наш человека, если прежде не выслушают его и не узнают, что он делает?
“Kodi lamulo lathu limatsutsa munthu popanda kumva mbali yake kuti tipeze chimene wachita?”
52 На это сказали ему: и ты не из Галилеи ли? рассмотри и увидишь, что из Галилеи не приходит пророк.
Iwo anayankha kuti, “Kodi ndiwenso wochokera ku Galileya? Tayangʼananso, ndipo udzapeza kuti mneneri sachokera ku Galileya.”
53 И разошлись все по домам.
Kenaka onse anachoka, napita kwawo.

< От Иоанна 7 >