< От Иоанна 20 >

1 В первый же день недели Мария Магдалина приходит ко гробу рано, когда было еще темно, и видит, что камень отвален от гроба.
Mmamawa tsiku loyamba la sabata, kukanali kamdimabe, Mariya wa ku Magadala anapita ku manda ndipo anaona kuti mwala unali utachotsedwa pa khomo la manda.
2 Итак, бежит и приходит к Симону Петру и к другому ученику, которого любил Иисус, и говорит им: унесли Господа из гроба, и не знаем, где положили Его.
Choncho anabwerera akuthamanga kwa Simoni Petro ndi wophunzira winayo, amene Yesu anamukonda, ndipo anati, “Iwo amuchotsa Ambuye mʼmanda, ndipo ife sitikudziwa kumene iwo amuyika Iye!”
3 Тотчас вышел Петр и другой ученик, и пошли ко гробу.
Choncho Petro ndi wophunzira winayo ananyamuka kupita ku manda.
4 Они побежали оба вместе; но другой ученик бежал скорее Петра и пришел ко гробу первый.
Onse awiri anathamanga pamodzi koma wophunzira winayo anamupitirira Petro, nafika ku manda moyambirira.
5 И, наклонившись, увидел лежащие пелены; но не вошел во гроб.
Ndipo mmene anawerama nasuzumira mʼkati mwa manda anaona nsalu zili potero koma sanalowemo.
6 Вслед за ним приходит Симон Петр, и входит во гроб, и видит одни пелены лежащие
Kenaka Simoni Petro, amene anali pambuyo pake, anafika ndi kulowa mʼmanda. Iye anaona nsaluzo zili pamenepo,
7 и плат, который был на главе Его, не с пеленами лежащий, но особо свитый на другом месте.
pamodzinso ndi nsalu imene anakulungira nayo mutu wa Yesu. Nsaluyi inali yopindidwa pa yokha yosiyanitsidwa ndi inayo.
8 Тогда вошел и другой ученик, прежде пришедший ко гробу, и увидел, и уверовал.
Pomaliza wophunzira winayo, amene anafika ku manda moyambirira, analowanso mʼkati, iye anaona ndi kukhulupirira.
9 Ибо они еще не знали из Писания, что Ему надлежало воскреснуть из мертвых.
(Iwo sanazindikire kuchokera mʼmalemba kuti Yesu anayanera kuuka kuchokera kwa akufa).
10 Итак ученики опять возвратились к себе.
Kenaka ophunzira anabwerera ku nyumba zawo,
11 А Мария стояла у гроба и плакала. И, когда плакала, наклонилась во гроб
koma Mariya anayima kunja kwa manda akulira. Pamene akulira, anawerama ndi kusuzumira mʼmanda
12 и видит двух Ангелов, в белом одеянии сидящих, одного у главы и другого у ног, где лежало тело Иисуса.
ndipo anaona angelo awiri atavala zoyera, atakhala pamene panali mtembo wa Yesu, mmodzi kumutu ndi wina kumapazi.
13 И они говорят ей: жена! что ты плачешь? Говорит им: унесли Господа моего, и не знаю, где положили Его.
Iwo anamufunsa iye kuti, “Amayi, nʼchifukwa chiyani mukulira?” Iye anati, “Amuchotsa Mbuye wanga, ndipo ine sindikudziwa kumene iwo amuyika.”
14 Сказав сие, обратилась назад и увидела Иисуса стоящего; но не узнала, что это Иисус.
Atanena izi, iye anatembenuka ndipo anaona Yesu atayima potero koma iye sanazindikire kuti anali Yesu.
15 Иисус же говорит ей: жена! что ты плачешь, кого ищешь? Она, думая, что это садовник, говорит Ему: господин! если ты вынес Его, скажи мне, где ты положил Его, и я возьму Его.
Iye anati, “Amayi, mukulira chifukwa chiyani? Ndani amene mukumufunafuna?” Poganiza kuti anali mwini munda, iye anati, “Bwana, ngati inu mwamuchotsa, ndiwuzeni kumene mwamuyika, ndipo ine ndikamutenga.”
16 Иисус говорит ей: Мария! Она обратившись говорит Ему: Раввуни!- что значит: Учитель!
Yesu anati kwa iye, “Mariya.” Anatembenukira kwa Iye nafuwula mu Chiaramaiki kuti, “Raboni!” (kutanthauza Mphunzitsi).
17 Иисус говорит ей: не прикасайся ко Мне, ибо Я еще не восшел к Отцу Моему; а иди к братьям Моим и скажи им: восхожу к Отцу Моему и Отцу вашему и к Богу Моему и к Богу вашему.
Yesu anati, “Usandigwire Ine, pakuti sindinapite kwa Atate. Mʼmalo mwake pita kwa abale anga ndikukawawuza kuti, ndikupita kwa Atate ndi kwa Atate anunso, kwa Mulungu wanga ndi Mulungu wanunso.”
18 Мария Магдалина идет и возвещает ученикам, что видела Господа и что Он это сказал ей.
Mariya wa ku Magadala anapita kwa ophunzira ndi uthenga wakuti, “Ndamuona Ambuye!” Iye anawawuza iwo kuti Yesu ananena zinthu izi kwa iye.
19 В тот же первый день недели вечером, когда двери дома, где собирались ученики Его были заперты из опасения от Иудеев, пришел Иисус, стал посреди, и говорит им: мир вам!
Madzulo a tsiku limenelo limene linali loyamba la Sabata ophunzira ake ali pamodzi, atatseka ndi kukhoma zitseko chifukwa choopa Ayuda, Yesu anabwera ndi kuyima pakati pawo nati, “Mtendere ukhale nanu!”
20 Сказав это, Он показал им руки (и ноги) и ребра Свои. Ученики обрадовались, увидевши Господа.
Iye atatha kunena izi, anawaonetsa manja ake ndi mʼnthiti mwake. Ophunzira anasangalala kwambiri pamene anaona Ambuye.
21 Иисус же сказал им вторично: мир вам! как послал Меня Отец, так и Я посылаю вас.
Yesu anatinso, “Mtendere ukhale nanu! Monga Atate anandituma Ine, Inenso ndikukutumani.”
22 Сказав это, дунул, и говорит им: примите Духа Святого;
Ndi mawu amenewo Iye anawapumira ndipo anati, “Landirani Mzimu Woyera.
23 кому простите грехи, тому простятся; на ком оставите, останутся.
Ngati mukhululukira aliyense machimo ake, iwo akhululukidwa; ngati simuwakhululukira, iwo sanakhululukidwe.”
24 Фома же, один из двенадцати, называемый Близнец, не был с ними, когда приходил Иисус.
Koma Tomasi (otchedwa Didimo), mmodzi wa khumi ndi awiriwo, sanali ndi ophunzira pamene Yesu anabwera.
25 Другие ученики сказали ему: мы видели Господа. Но он сказал им: если не увижу на руках Его ран от гвоздей, и не вложу перста моего в раны от гвоздей, и не вложу руки моей в ребра Его, не поверю.
Ophunzira enawo atamuwuza Tomasi kuti iwo anaona Ambuye, iye ananenetsa kuti, “Pokhapokha nditaona zizindikiro za misomali mʼmanja ake ndi kuyikamo chala changa mʼmene munali misomali ndi kukhudza dzanja langa mʼnthiti mwake, ine sindidzakhulupirira.”
26 После восьми дней опять были в доме ученики Его и Фома с ними. Пришел Иисус, когда двери были заперты, стал посреди и сказал: мир вам!
Patapita sabata, ophunzira ake analinso mʼnyumbamo ndipo Tomasi anali nawo. Ngakhale makomo anali otsekedwa, Yesu anabwera nayima pakati pawo, ndipo anati, “Mtendere ukhale nanu!”
27 Потом говорит Фоме: подай перст свой сюда и посмотри руки Мои; подай руку твою и вложи в ребра Мои; и не будь неверующим, но верующим.
Kenaka anati kwa Tomasi, “Ika chala chako apa; ona manja anga. Tambasula dzanja lako ndi kukhudza mʼnthiti mwanga. Leka kukayika, khulupirira.”
28 Фома сказал Ему в ответ: Господь мой и Бог мой!
Tomasi anati kwa Iye, “Ambuye wanga ndi Mulungu wanga!”
29 Иисус говорит ему: ты поверил, потому что увидел; блаженны не видевшие и уверовавшие.
Kenaka Yesu anamuwuza kuti, “Kodi wakhulupirira chifukwa wandiona Ine? Ndi odala amene amakhulupirira ngakhale asanaone.”
30 Много сотворил Иисус пред учениками Своими и других чудес, о которых не написано в книге этой;
Yesu anachita zodabwitsa zambiri pamaso pa ophunzira ake zimene sizinalembedwe mʼbuku lino.
31 Это же написано, дабы вы уверовали, что Иисус есть Христос, Сын Божий, и, веруя, имели жизнь во имя Его.
Koma izi zalembedwa kuti mukhulupirire kuti Yesu ndi Khristu, Mwana wa Mulungu, ndi kuti mukakhulupirira mukhale nawo moyo mʼdzina lake.

< От Иоанна 20 >