< От Иоанна 18 >

1 Сказав сие, Иисус вышел с учениками Своими за поток Кедрон, где был сад, в который вошел Сам и ученики Его.
Yesu atamaliza kupemphera, Iye anachoka ndi ophunzira ake ndi kuwoloka chigwa cha Kidroni. Kumbali inayo kunali munda wa Olivi, ndipo Iye ndi ophunzira ake analowamo.
2 Знал же это место и Иуда, предатель Его, потому что Иисус часто собирался там с учениками Своими.
Tsopano Yudasi, amene anamupereka amadziwa malowo chifukwa Yesu ankakumana ndi ophunzira ake kumeneko.
3 Итак Иуда, взяв отряд воинов и служителей от первосвященников и фарисеев, приходит туда с фонарями, и светильниками, и оружием.
Choncho Yudasi anabwera ku munda, akutsogolera gulu la asilikali ndi akuluakulu ena ochokera kwa akulu a ansembe ndi Afarisi. Iwo anali atanyamula miyuni, nyale ndi zida.
4 Иисус же, зная все, что с Ним будет, вышел и сказал им: кого ищете?
Yesu, podziwa zonse zimene zimati zichitike kwa Iye, anatuluka ndi kuwafunsa kuti, “Kodi mukufuna ndani?”
5 Ему отвечали: Иисуса Назорея. Иисус говорит им: это Я. Стоял же с ними и Иуда, предатель Его.
Iwo anayankha kuti, “Yesu wa ku Nazareti.” Yesu anati, “Ndine.” (Ndipo Yudasi womuperekayo anali atayima nawo pamenepo).
6 И когда сказал им: это Я, они отступили назад и пали на землю.
Pamene Yesu anati, “Ndine,” iwo anabwerera mʼmbuyo ndi kugwa pansi.
7 Опять спросил их: кого ищете? Они сказали: Иисуса Назорея.
Iye anawafunsanso kuti, “Kodi mukumufuna ndani?” Ndipo iwo anati, “Yesu wa ku Nazareti.”
8 Иисус отвечал: Я сказал вам, что это Я; итак, если Меня ищете, оставьте их, пусть идут,
Yesu anayankha kuti, “Ine ndakuwuzani kuti Ndine. Ngati inu mukufuna Ine, asiyeni anthu awa apite.”
9 да сбудется слово, реченное Им: из тех, которых Ты Мне дал, Я не погубил никого.
Izi zinachitika kuti mawu amene Iye anayankhula akwaniritsidwe: “Ine sindinataye ndi mmodzi yemwe mwa iwo amene mwandipatsa.”
10 Симон же Петр, имея меч, извлек его, и ударил первосвященнического раба, и отсек ему правое ухо. Имя рабу было Малх.
Kenaka Simoni amene anali ndi lupanga analitulutsa ndi kutema nalo wantchito wa wamkulu wa ansembe, nadula khutu lake la kudzanja lamanja. (Dzina la wantchitoyo ndi Makusi).
11 Но Иисус сказал Петру: вложи меч в ножны; неужели Мне не пить чаши, которую дал Мне Отец?,
Yesu analamula Petro kuti, “Bwezera lupanga mʼchimake! Kodi Ine ndisamwere chikho chimene Atate andipatsa?”
12 Тогда воины, и тысяченачальник, и служители Иудейские взяли Иисуса и связали Его,
Kenaka gulu la asilikali ndi olamulira wawo ndi akuluakulu a Ayuda anamugwira Yesu. Iwo anamumanga.
13 и отвели Его сперва к Анне, ибо он был тесть Каиафе, который был на тот год первосвященником.
Poyamba anapita naye kwa Anasi amene anali mkamwini wa Kayafa, mkulu wa ansembe chaka chimenecho.
14 Это был Каиафа, который подал совет Иудеям, что лучше одному человеку умереть за народ.
Kayafa anali amene analangiza Ayuda kuti kukanakhala kwabwino ngati munthu mmodzi akanafera anthu.
15 За Иисусом следовали Симон Петр и другой ученик; ученик же сей был знаком первосвященнику и вошел с Иисусом во двор первосвященнический.
Simoni Petro ndi ophunzira wina ankamutsatira Yesu chifukwa ophunzira uyu amadziwika kwa mkulu wa ansembe. Iye analowa ndi Yesu mʼbwalo la mkulu wa ansembe
16 А Петр стоял вне за дверями. Потом другой ученик, который был знаком первосвященнику, вышел, и сказал придвернице, и ввел Петра.
koma Petro anadikira kunja pa khomo. Ophunzira winayo amene amadziwika kwa mkulu wa ansembe, anatuluka ndi kuyankhula ndi mtsikana amene anali mlonda wa pa khomo ndi kumulowetsa Petro.
17 Тут раба придверница говорит Петру: и ты не из учеников ли Этого Человека? Он сказал: нет.
Mtsikanayo anafunsa Petro kuti, “Kodi iwe sindiwe mmodzi wa ophunzira a Munthu uyu?” Iye anayankha kuti, “Ayi, sindine.”
18 Между тем рабы и служители, разведя огонь, потому что было холодно, стояли и грелись. Петр также стоял с ними и грелся.
Popeza kunkazizira, anyamata antchito ndi akuluakulu ena anasonkha moto wamakala namawotha atayimirira mozungulira. Petro nayenso anayimirira pamodzi ndi iwo namawotha nawo motowo.
19 Первосвященник же спросил Иисуса об учениках Его и об учении Его.
Pa nthawi imeneyi, mkulu wa ansembe anamufunsa Yesu za ophunzira ake ndi chiphunzitso chake.
20 Иисус отвечал ему: Я говорил явно миру; Я всегда учил в синагоге и в храме, где всегда Иудеи сходятся, и тайно не говорил ничего.
Yesu anayankha kuti, “Ine ndinayankhula poyera ku dziko lapansi. Nthawi zonse ndimaphunzitsa mʼsunagoge kapena mʼNyumba ya Mulungu kumene Ayuda onse amasonkhana pamodzi. Ine sindimanena kanthu mseri.
21 Что спрашиваешь Меня? спроси слышавших, что Я говорил им; вот, они знают, что Я говорил.
Nʼchifukwa chiyani mukundifunsa Ine? Afunseni amene amamva. Zoonadi akudziwa zimene Ine ndinanena.”
22 Когда Он сказал это, один из служителей, стоявший близко, ударил Иисуса по щеке, сказав: так отвечаешь Ты первосвященнику?
Yesu atanena izi, mmodzi wa akuluakulu amene anali pafupi anamumenya kumaso. Iye anafunsa kuti, “Mayankhidwe awa ndi woti ndi kuyankha mkulu wa ansembe?”
23 Иисус отвечал ему: если Я сказал худо, покажи, что худо; а если хорошо, что ты бьешь Меня?
Yesu anayankha kuti, “Ngati Ine ndanena kanthu kolakwika, chitirani umboni chimene ndalakwa. Koma ngati ndanena zoona, nʼchifukwa chiyani mwandimenya?”
24 Анна послал Его связанного к первосвященнику Каиафе.
Kenaka Anasi anamutumiza Iye, ali womangidwabe, kwa Kayafa, mkulu wa ansembe.
25 Симон же Петр стоял и грелся. Тут сказали ему: не из учеников ли Его и ты? Он отрекся и сказал: нет.
Pamene Simoni Petro anali chiyimirire kuwotha moto, anafunsidwa kuti, “Kodi iwe si mmodzi wa ophunzira ake?” Iye anayankha kuti, “Ayi, sindine.”
26 Один из рабов первосвященнических, родственник тому, которому Петр отсек ухо, говорит: не я ли видел тебя с Ним в саду?
Mmodzi wa antchito a mkulu wa ansembe, mʼbale wa munthu amene anadulidwa khutu ndi Petro anamutsutsa iye kuti, “Kodi sindinakuone iwe pamodzi ndi Iye mʼmunda muja?”
27 Петр опять отрекся; и тотчас запел петух.
Petro anakananso, ndipo pa nthawi yomweyo tambala analira.
28 От Каиафы повели Иисуса в преторию. Было утро; и они не вошли в преторию, чтобы не оскверниться, но чтобы можно было есть пасху.
Kenaka Ayuda anamutenga Yesu kuchoka kwa Kayafa ndi kupita ku nyumba yaufumu ya bwanamkubwa wa Chiroma. Tsopano kunali mmamawa, ndipo polewa kudetsedwa monga mwa mwambo Ayuda sanalowe mʼnyumba yaufumuyo; iwo anafuna kuti adye Paska.
29 Пилат вышел к ним и сказал: в чем вы обвиняете Человека Сего?
Choncho Pilato anatuluka napita kwa iwo ndipo anati, “Kodi ndi milandu yanji imene mukumuzenga munthu uyu?”
30 Они сказали ему в ответ: если бы Он не был злодей, мы не предали бы Его тебе.
Iwo anayankha kuti, “Ngati Iye akanakhala kuti si wolakwa, ife sitikanamupereka kwa inu.”
31 Пилат сказал им: возьмите Его вы и по закону вашему судите Его. Иудеи сказали ему: нам не позволено предавать смерти никого,
Pilato anati, “Mutengeni inu eni ake ndi kumuweruza Iye monga mwa malamulo anu.” Ayuda anatsutsa nati, “Koma tilibe ulamuliro wakupha aliyense.”
32 да сбудется слово Иисусово, которое сказал Он, давая разуметь, какою смертью Он умрет.
Izi zinachitika kuti mawu a Yesu amene anayankhula kusonyeza mtundu wa imfa imene Iye anati adzafe nayo akwaniritsidwe.
33 Тогда Пилат опять вошел в преторию, и призвал Иисуса, и сказал Ему: Ты Царь Иудейский?
Kenaka Pilato anapita mʼkati mwa nyumba yaufumu nayitanitsa Yesu, ndipo anamufunsa kuti, “Kodi iwe ndi mfumu ya Ayuda?”
34 Иисус отвечал ему: от себя ли ты говоришь это или другие сказали тебе о Мне?
Yesu anafunsa kuti, “Kodi amenewo ndi maganizo anu wokha? Kapena kuti ena anakuwuzani za Ine?”
35 Пилат отвечал: разве я Иудей? Твой народ и первосвященники предали Тебя мне; что Ты сделал?
Pilato anayankha kuti, “Kodi iwe ukuganiza kuti ine ndine Myuda? Ndi anthu ako ndi akulu a ansembe ako amene akupereka iwe kwa ine. Kodi walakwanji?”
36 Иисус отвечал: Царство Мое не от мира сего; если бы от мира сего было Царство Мое, то служители Мои подвизались бы за Меня, чтобы Я не был предан Иудеям; но ныне Царство Мое не отсюда.
Yesu anati, “Ufumu wanga si wa dziko lapansi lino. Ukanakhala wa pansi pano, antchito anga akanachita nkhondo kulepheretsa Ayuda kundigwira. Koma tsopano ufumu wanga ndi wochokera kumalo ena.”
37 Пилат сказал Ему: итак, Ты Царь? Иисус отвечал: ты говоришь, что Я Царь. Я на то родился и на то пришел в мир, чтобы свидетельствовать о истине; всякий, кто от истины, слушает гласа Моего.
Pilato anati, “Kani ndiwe mfumu!” Yesu anayankha kuti, “Inu mwalondola ponena kuti, Ine ndine mfumu. Kunena zoona, Ine ndinabadwa chifukwa cha chimenechi, ndipo nʼchifukwa chake ndinabwera mʼdziko lapansi, kudzachitira umboni choonadi. Aliyense amene ali mbali yachoonadi amamvera mawu anga.”
38 Пилат сказал Ему: что есть истина? И, сказав это, опять вышел к Иудеям и сказал им: я никакой вины не нахожу в Нем.
Pilato anafunsa kuti, “Kodi choonadi nʼchiyani?” Ndi mawu awa iye anapitanso kwa Ayuda ndipo anati, “Ine sindikupeza mlandu mwa Iye.
39 Есть же у вас обычай, чтобы я одного отпускал вам на Пасху; хотите ли, отпущу вам Царя Иудейского?
Koma ndi mwambo wanu kuti pa nthawi ya Paska, ine ndikumasulireni wamʼndende mmodzi. Kodi mufuna ndikumasulireni ‘Mfumu ya Ayuda?’”
40 Тогда опять закричали все, говоря: не Его, но Варавву. Варавва же был разбойник.
Iwo anafuwula nati, “Ameneyu ayi! Mutipatse ife Baraba!” Barabayo anali wachifwamba.

< От Иоанна 18 >