< От Иоанна 10 >

1 Истинно, истинно говорю вам: кто не дверью входит во двор овчий, но перелазит инде, тот вор и разбойник;
“Zoonadi, Ine ndikukuwuzani inu Afarisi, kuti munthu amene salowera pa khomo mʼkhola la nkhosa, koma amalowera pena pake ndi wakuba ndi wachifwamba.
2 а входящий дверью есть пастырь овцам.
Munthu amene amalowera pa khomo ndi mʼbusa wankhosazo.
3 Ему придверник отворяет, и овцы слушаются голоса его, и он зовет своих овец по имени и выводит их.
Mlonda amamutsekulira khomo, ndipo nkhosa zimamvera mawu ake. Iye amaziyitana mayina nkhosa zakezo, nazitulutsa.
4 И когда выведет своих овец, идет перед ними; а овцы за ним идут, потому что знают голос его.
Akazitulutsa nkhosa zake zonse, iye amazitsogolera, ndipo nkhosa zakezo zimamutsata chifukwa zimadziwa mawu ake.
5 За чужим же не идут, но бегут от него, потому что не знают чужого голоса.
Koma nkhosazo sizidzatsatira mlendo. Izo zidzamuthawa chifukwa sizizindikira mawu a mlendo.”
6 Сию притчу сказал им Иисус; но они не поняли, что такое Он говорил им.
Yesu ananena mawu ophiphiritsawa, koma Afarisi sanazindikire zimene ankawawuza.
7 Итак, опять Иисус сказал им: истинно, истинно говорю вам, что Я дверь овцам.
Choncho Yesu anatinso, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti Ine ndine khomo la nkhosa.
8 Все, сколько их ни приходило предо Мною, суть воры и разбойники; но овцы не послушали их.
Onse amene anadza ndisanabwere Ine ndi akuba ndi achifwamba, ndipo nkhosa sizinawamvere.
9 Я есмь дверь: кто войдет Мною, тот спасется, и войдет, и выйдет, и пажить найдет.
Ine ndine khomo, aliyense amene alowa kudzera mwa Ine adzapulumuka. Iye adzalowa ndi kutuluka ndi kupeza msipu.
10 Вор приходит только для того, чтобы украсть, убить и погубить. Я пришел для того, чтобы имели жизнь, и имели с избытком.
Mbala sibwera chabe koma kuti idzabe, kupha ndi kuwononga. Ine ndabwera kuti iwo akhale ndi moyo, ndi kukhala nawo wochuluka.
11 Я есмь пастырь добрый: пастырь добрый полагает жизнь свою за овец.
“Ine ndine Mʼbusa wabwino. Mʼbusa wabwino amataya moyo wake chifukwa cha nkhosa zake.
12 А наемник, не пастырь, которому овцы не свои, видит приходящего волка, и оставляет овец, и бежит; и волк расхищает овец и разгоняет их.
Wantchito ndi mʼbusa amene nkhosazo si zake. Choncho, pamene aona mmbulu ukubwera, iye amazisiya nkhosazo ndi kuthawa. Ndipo mmbulu umagwira nkhosazo ndikuzibalalitsa.
13 А наемник бежит, потому что наемник, и нерадит об овцах.
Munthuyo amathawa chifukwa ndi wantchito ndipo sasamalira chilichonse cha nkhosazo.
14 Я есмь пастырь добрый; и знаю Моих, и Мои знают Меня.
“Ine ndine mʼbusa wabwino. Ine ndimazidziwa nkhosa zanga ndipo nkhosa zangazo zimandidziwa,
15 Как Отец знает Меня, так и Я знаю Отца; и жизнь Мою полагаю за овец.
monga momwe Atate amandidziwa Ine, ndiponso Ine kudziwira Atatewo. Ndimapereka moyo wanga chifukwa cha nkhosa.
16 Есть у Меня и другие овцы, которые не сего двора, и тех надлежит Мне привести: и они услышат голос Мой, и будет одно стадо и один Пастырь.
Ine ndili ndi nkhosa zina zimene sizili za gulu ili. Ine ndiyenera kuzibweretsanso. Izonso zidzamvera mawu anga, ndipo zidzakhala gulu limodzi ndi mʼbusa mmodzi.
17 Потому любит Меня Отец, что Я отдаю жизнь Мою, чтобы опять принять ее.
Nʼchifukwa chake Atate anga amandikonda, popeza Ine ndikupereka moyo wanga kuti ndiwutengenso.
18 Никто не отнимает ее у Меня, но Я Сам отдаю ее. Имею власть отдать ее и власть имею опять принять ее. Сию заповедь получил Я от Отца Моего.
Palibe amene angawuchotse mwa Ine, koma ndikuwupereka mwakufuna kwanga. Ine ndili ndi ulamuliro wa kuwupereka ndi ulamuliro wakuwutenganso. Lamulo ili ndinalandira kwa Atate anga.”
19 От этих слов опять произошла между Иудеями распря.
Pa mawu awa Ayuda anagawikananso.
20 Многие из них говорили: Он одержим бесом и безумствует; что слушаете Его?
Ambiri a iwo anati, “Iye ndi wogwidwa ndi ziwanda ndi wamisala. Chifukwa chiyani mukumvera Iye?”
21 Другие говорили: это слова не бесноватого; может ли бес отверзать очи слепым?
Koma ena anati, “Awa si mawu a munthu wogwidwa ndi ziwanda. Kodi ziwanda zingathe bwanji kutsekula maso a wosaona?”
22 Настал же тогда в Иерусалиме праздник обновления, и была зима.
Ku Yerusalemu kunali chikondwerero chokumbukira kupatulidwa kwa Nyumba ya Mulungu. Inali nthawi yozizira,
23 И ходил Иисус в храме, в притворе Соломоновом.
ndipo Yesu ankayenda mʼbwalo la Nyumbayo ku malo a Solomoni.
24 Тут Иудеи обступили Его и говорили Ему: долго ли Тебе держать нас в недоумении? если Ты Христос, скажи нам прямо.
Ayuda anamuzungulira Iye akunena kuti, “Kodi iwe udzazunguza malingaliro athu mpaka liti? Ngati iwe ndi Khristu, tiwuze momveka.”
25 Иисус отвечал им: Я сказал вам, и не верите; дела, которые творю Я во имя Отца Моего, они свидетельствуют о Мне.
Yesu anayankha kuti, “Ine ndimakuwuzani, koma inu simukhulupirira. Ntchito zimene ndikuchita mʼdzina la Atate anga zikundichitira umboni,
26 Но вы не верите, ибо вы не из овец Моих, как Я сказал вам.
koma inu simukhulupirira chifukwa simuli a gulu lankhosa zanga.
27 Овцы Мои слушаются голоса Моего, и Я знаю их; и они идут за Мною.
Nkhosa zanga zimamva mawu anga, Ine ndimazidziwa, ndipo zimanditsata Ine.
28 И Я даю им жизнь вечную, и не погибнут вовек; и никто не похитит их из руки Моей. (aiōn g165, aiōnios g166)
Ine ndimazipatsa moyo wosatha ndipo sizidzawonongeka. Palibe amene adzazikwatula mʼdzanja langa. (aiōn g165, aiōnios g166)
29 Отец Мой, Который дал Мне их, больше всех; и никто не может похитить их из руки Отца Моего.
Atate anga, amene anandipatsa Ine, ndi akulu kuposa onse. Palibe amene angazikwatule mʼdzanja la Atate anga.
30 Я и Отец - одно.
Ine ndi Atate ndife amodzi.”
31 Тут опять Иудеи схватили каменья, чтобы побить Его.
Ayuda anatolanso miyala kuti amugende Iye,
32 Иисус отвечал им: много добрых дел показал Я вам от Отца Моего; за которое из них хотите побить Меня камнями?
koma Yesu anawawuza kuti, “Ine ndakuonetsani zinthu zambiri zabwino zodabwitsa kuchokera kwa Atate. Nʼchifukwa chiti mwa izi chimene mukundigendera?”
33 Иудеи сказали Ему в ответ: не за доброе дело хотим побить Тебя камнями, но за богохульство и за то, что Ты, будучи человек, делаешь Себя Богом.
Ayuda anayankha kuti, “Ife sitikukugenda chifukwa cha izi, koma popeza ukunyoza Mulungu, chifukwa iwe, munthu wamba, ukuti ndiwe Mulungu.”
34 Иисус отвечал им: не написано ли в законе вашем: Я сказал: вы боги?
Yesu anawayankha kuti, “Kodi sizinalembedwa mʼmalamulo anu kuti, ‘Ine ndanena kuti ndinu milungu?’
35 Если Он назвал богами тех, к которым было слово Божие, и не может нарушиться Писание, -
Ngati anawatcha milungu anthu amene analandira mawu a Mulungu, pajatu Malemba sangasweke,
36 Тому ли, Которого Отец освятил и послал в мир, вы говорите: богохульствуешь, потому что Я сказал: Я Сын Божий?
nanga bwanji uyu amene Atate anamuyika padera monga wake weniweni ndi kumutuma ku dziko lapansi? Nanga ndi chifukwa chiyani mukundinena Ine kuti ndikuchita chipongwe? Kodi nʼchifukwa choti ndanena kuti, ‘Ine ndine Mwana wa Mulungu?’
37 Если Я не творю дел Отца Моего, не верьте Мне;
Musandikhulupirire Ine ngati sindichita ntchito za Atate anga.
38 а если творю, то, когда не верите Мне, верьте делам Моим, чтобы узнать и поверить, что Отец во Мне и Я в Нем.
Koma ngati Ine ndikuchita zimenezi, ngakhale kuti simundikhulupirira, khulupirirani ntchito zodabwitsazo, ndipo mudziwe ndi kuzindikira kuti Atate ali mwa Ine, ndiponso Ine ndili mwa Atate.”
39 Тогда опять искали схватить Его; но Он уклонился от рук их
Iwo anafuna kumugwiranso koma anawapulumuka mʼmanja mwawo.
40 и пошел опять за Иордан, на то место, где прежде крестил Иоанн, и остался там.
Kenaka Yesu anabwereranso kutsidya la mtsinje wa Yorodani kumalo kumene Yohane ankabatiza mʼmasiku akale. Iye anakhala kumeneko
41 Многие пришли к Нему и говорили, что Иоанн не сотворил никакого чуда, но все, что сказал Иоанн о Нем, было истинно.
ndipo anthu ambiri anabwera kwa Iye. Iwo anati, “Ngakhale kuti Yohane sanachite chizindikiro chodabwitsa, zonse zimene Yohane ananena za munthu uyu zinali zoona.”
42 И многие там уверовали в Него.
Ndipo pamalo amenewo ambiri anakhulupirira Yesu.

< От Иоанна 10 >