< К Евреям 7 >

1 Ибо Мелхиседек, царь Салима, священник Бога Всевышнего, тот, который встретил Авраама и благословил его, возвращающегося после поражения царей,
Melikizedeki ameneyu anali mfumu ya ku Salemu, ndiponso wansembe wa Mulungu Wammwambamwamba. Anakumana ndi Abrahamu pamene ankabwerera kuchokera ku nkhondo atagonjetsa mafumu aja, Melikizedeki anakumana naye namudalitsa.
2 Которому и десятину отделил Авраам от всего, - во первых по знаменованию имени царь правды, а потом и царь Салима, то есть, царь мира,
Ndipo Abrahamu anamupatsa chakhumi cha zonse anafunkha. Choyamba dzina la Melikizedeki likutanthauza, “Mfumu ya chilungamo,” kenakanso, “Mfumu ya Salemu,” kutanthauza, “Mfumu ya mtendere.”
3 Без отца, без матери, без родословия, не имеющий ни начала дней, ни конца жизни, уподобляясь Сыну Божию, пребывает священником навсегда.
Alibe abambo kapena mayi, alibe chiyambi kapena chitsiriziro cha moyo wake. Iye ali ngati Mwana wa Mulungu ndipo akupitirira kukhala wansembe wamuyaya.
4 Видите, как велик тот, которому и патриарх Авраам дал десятину из лучших добыч своих.
Mukuona tsono kuti munthuyo anali wamkulu ndithu, pakuti Abrahamu kholo lathu anamupatsa chakhumi cha zimene anafunkha.
5 Получающие священство из сынов Левиных имеют заповедь - брать по закону десятину с народа, то есть, со своих братьев, хотя и сии произошли от чресл Авраамовых.
Tsono lamulo likuti, ana a Levi amene amakhala ansembe azilandira chakhumi kuchokera kwa Aisraeli, abale awo ngakhale kuti abale awowo ndi ochokera kwa Abrahamu.
6 Но сей, не происходящий от рода их, получил десятину от Авраама и благословил имевшего обетования.
Melikizedeki sanali wochokera kwa Levi, komabe analandira chakhumi kuchokera kwa Abrahamu nadalitsa Abrahamuyo amene analandira malonjezo a Mulungu.
7 Без всякого же прекословия меньший благословляется большим.
Mosakayika konse, munthu amene amadalitsa ndi wamkulu kuposa amene akudalitsidwayo.
8 И здесь десятины берут человеки смертные, а там имеющий о себе свидетельство, что он живет.
Ansembe amene amalandira chakhumi amafa, choncho Melikizedeki ndi wamkulu kuwaposa iwo chifukwa Malemba amamuchitira umboni kuti ndi wamoyo.
9 И, так сказать, сам Левий, принимающий десятины, в лице Авраама дал десятину:
Wina angathe kunena kuti Levi, amene amalandira chakhumi, anapereka chakhumicho kudzera mwa Abrahamu,
10 Ибо он был еще в чреслах отца, когда Мелхиседек встретил его.
chifukwa pamene Melikizedeki anakumana ndi Abrahamu nʼkuti Levi ali mʼthupi la kholo lake.
11 Итак, если бы совершенство достигалось посредством левитского священства, - и с ним сопряжен закон народа, - то какая бы еще нужда была восставать иному священнику по чину Мелхиседека, а не по чину Аарона именоваться?
Kukanatheka kukhala wangwiro mwa unsembe wa Levi, pakuti Malamulo anapatsidwa kwa anthu mwa unsembe wa Levi, nʼchifukwa chiyani panafunikanso wansembe wina kuti abwere, wofanana ndi Melikizedeki, osati Aaroni?
12 Потому что с переменой священства необходимо быть перемене закона.
Pakuti pamene unsembe usintha, malamulonso amayenera kusintha.
13 Ибо Тот, о Котором говорится сие, принадлежал к иному колену, из которого никто не приступал к жертвеннику;
Ambuye athu Yesu, amene mawuwa akunena za Iye, anali wa fuko lina, ndipo palibe aliyense wochokera fuko lakelo amene anatumikira pa guwa lansembe.
14 Ибо известно, что Господь наш воссиял из колена Иудина, о котором Моисей ничего не сказал относительно священства.
Pakuti nʼzodziwika bwino kuti Ambuye athu anachokera fuko la Yuda. Kunena za fuko limeneli, Mose sananenepo kanthu za ansembe.
15 И это еще яснее видно из того, что по подобию Мелхиседека восстает священник иной,
Ndipo zimene tanenazi zimamveka bwino ngati tiona kuti pafika wansembe wina wofanana ndi Melikizedeki.
16 Который таков не по закону заповеди плотской, но по силе жизни непрестающей.
Yesu sanakhale wansembe chifukwa cha malamulo monga mwa mabadwidwe ake koma mwamphamvu ya moyo wosatha.
17 Ибо засвидетельствовано: “Ты священник вовек по чину Мелхиседека”. (aiōn g165)
Pakuti Mulungu anamuchitira umboni kuti, “Iwe ndi wansembe wamuyaya, monga mwa dongosolo la unsembe wa Melikizedeki.” (aiōn g165)
18 Отменение же прежде бывшей заповеди бывает по причине ее немощи и бесполезности,
Choncho lamulo loyamba lachotsedwa chifukwa linali lofowoka ndi lopanda phindu.
19 Ибо закон ничего не довел до совершенства; но вводится лучшая надежда, посредством которой мы приближаемся к Богу.
Tsono Malamulo sangathe kusandutsa chilichonse kukhala changwiro, koma mʼmalo mwake mwalowa chiyembekezo chabwino, chimenechi timayandikira nacho kwa Mulungu.
20 И как сие не без клятвы, -
Izi sizinachitiketu wopanda lumbiro. Ena ankakhala ansembe popanda lumbiro.
21 Ибо те были священниками без клятвы, а Сей с клятвою, потому что о Нем сказано: “клялся Господь и не раскается: Ты священник вовек по чину Мелхиседека”, - (aiōn g165)
Koma Yesu ankakhala wansembe ndi lumbiro pamene Mulungu anati, “Ambuye analumbira ndipo sangasinthe maganizo ake, ‘Iwe ndi wansembe wamuyaya.’” (aiōn g165)
22 То лучшего завета поручителем соделался Иисус.
Chifukwa cha lumbiroli, Yesu wakhala Nkhoswe ya Pangano lopambana.
23 Притом тех священников было много, потому что смерть не допускала пребывать одному;
Tsono ansembe akale aja analipo ambiri, popeza imfa imawalepheretsa kupitiriza ntchitoyi.
24 А Сей, как пребывающий вечно, имеет и священство непреходящее, (aiōn g165)
Koma Yesu popeza ndi wamuyaya, unsembe wake ndi wosatha. (aiōn g165)
25 Посему и может всегда спасать приходящих чрез Него к Богу, будучи всегда жив, чтобы ходатайствовать за них.
Chifukwa chake Iye amapulumutsa kwathunthu amene amabwera kwa Mulungu kudzera mwa Iyeyo. Iye ali ndi moyo nthawi zonse kuti adziwapempherera iwo.
26 Таков и должен быть у нас первосвященник: святый, непричастный злу, непорочный, отделенный от грешников и превознесенный выше небес,
Uyu ndi Mkulu wa ansembe amene tikumufuna chifukwa ndi woyera, wopanda choyipa kapena chodetsa chilichonse, wosiyana ndi anthu ochimwa, ndiponso wokwezedwa kuposa zonse zakumwambaku.
27 Который не имеет нужды ежедневно, как те первосвященники, приносить жертвы сперва за свои грехи, потом за грехи народа; ибо Он совершил это однажды, принесши в жертву Себя Самого.
Kusiyana ndi akulu a ansembe ena aja, Yesu sanafunike kupereka nsembe tsiku ndi tsiku poyamba chifukwa cha machimo ake, ndipo kenaka chifukwa cha machimo a anthu ena. Iye anadzipereka nsembe chifukwa cha machimo awo kamodzi kokha pamene anadzipereka yekha.
28 Ибо закон поставляет первосвященниками человеков, имеющих немощи; а слово клятвенное, после закона, поставило Сына, навеки совершенного. (aiōn g165)
Pakuti lamulo limasankha anthu amene ndi ofowoka kukhala akulu a ansembe; koma lumbiro, lomwe linabwera pambuyo pa lamulo, linasankha Mwana, amene anapangidwa kukhala wangwiro kwamuyaya. (aiōn g165)

< К Евреям 7 >