< К Евреям 11 >

1 Вера же есть осуществление ожидаемого и уверенность в невидимом.
Tsopano chikhulupiriro ndi kusakayika konse pa zinthu zimene tikuziyembekeza, ndi kutsimikiza kuti zinthu zimene sitiziona zilipo ndithu.
2 В ней свидетельствованы древние.
Ndi chikhulupiriro chimenechi makolo athu akale anayamikidwa.
3 Верою познаем, что веки сотворены словом Божиим, так что из невидимого произошло видимое. (aiōn g165)
Ndi chikhulupiriro timazindikira kuti dziko lapansi ndi la mmwamba zinapangidwa ndi Mawu a Mulungu, ndikuti zinthu zoonekazi zinachokera ku zinthu zosaoneka. (aiōn g165)
4 Верою Авель принес Богу жертву лучшую, нежели Каин; ею получил свидетельство, что он праведен, как засвидетельствовал Бог о дарах его; ею он и по смерти говорит еще.
Ndi chikhulupiriro Abele anapereka kwa Mulungu nsembe yoposa imene Kaini anapereka. Ndi chikhulupiriro anatchedwa munthu wolungama Mulungu atayamikira zopereka zake. Ngakhale iye anafa, akuyankhulabe chifukwa cha chikhulupiriro chakecho.
5 Верою Енох переселен был так, что не видел смерти; и не стало его, потому что Бог переселил его. Ибо прежде переселения своего получил он свидетельство, что угодил Богу.
Ndi chikhulupiriro Enoki anatengedwa wamoyo, motero iye sanalawe imfa; sanapezeke chifukwa Mulungu anamutenga. Pakuti asanatengedwe anayamikiridwa kuti ankakondweretsa Mulungu.
6 А без веры угодить Богу невозможно; ибо надобно, чтобы приходящий к Богу веровал, что он есть, и ищущим его воздает.
Ndipo popanda chikhulupiriro nʼkosatheka kukondweretsa Mulungu, chifukwa aliyense amene amabwera kwa Iye ayenera kukhulupirira kuti Mulungu alipodi ndi kuti Iye amapereka mphotho kwa amene akumufunitsitsa.
7 Верою Ной, получив откровение о том что еще не было видно, благоговея приготовил ковчег для спасения дома своего; ею осудил он (весь) мир, и сделался наследником праведности по вере.
Ndi chikhulupiriro, Nowa atachenjezedwa za zinthu zimene zinali zisanaoneke, anachita mantha napanga chombo kuti apulumutsire banja lake. Ndi chikhulupiriro chake anatsutsa dziko lapansi ndipo analandira chilungamo chimene chimabwera ndi chikhulupiriro.
8 Верою Авраам повиновался призванию идти в страну, которую имел получить в наследие, и пошел, не зная куда идет.
Ndi chikhulupiriro Abrahamu atayitanidwa kuti apite ku dziko limene anamulonjeza kuti lidzakhala lake, anamvera ndi kupita, ngakhale sanadziwe kumene ankapita.
9 Верою обитал он на земле обетованной, как на чужой, и жил в шатрах с Исааком и Иаковым, сонаследниками того же обетования;
Ndi chikhulupiriro chomwecho anakhala ngati mlendo mʼdziko lija limene Mulungu anamulonjeza. Anakhala mʼmatenti monganso anachitira Isake ndi Yakobo, amene nawonso analonjezedwanso.
10 Ибо он ожидал города, имеющего основание, которого художник и строитель - Бог.
Pakuti amadikira mudzi wokhala ndi maziko, umene mmisiri ndi womanga wake ndi Mulungu.
11 Верою и сама Сарра (будучи неплодна) получила сила к принятию семени и не по времени возраста родила; ибо знала, что верен Обещавший.
Ndi chikhulupiriro Sara analandira mphamvu zokhala ndi pakati ngakhale kuti zaka zake zobala mwana zinali zitapita kale, popeza anamutenga amene analonjeza kukhala wokhulupirika.
12 И потому от одного, и притом омертвелого, родилось так много, как много звезд на небе и как бесчислен песок на берегу морском.
Nʼchifukwa chake mwa munthu mmodzi, amene anali ngati wakufa, munatuluka mibado yochuluka ngati nyenyezi ndi yosawerengeka ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja.
13 Все сии умерли в вере, не получивши обетований, а только издали видели оные и радовались и говорили о себе, что они странники и пришельцы на земле;
Onsewa anakhalabe mwachikhulupiriro mpaka anafa. Iwo sanalandire zimene Mulungu anawalonjeza; iwo anangozionera chapatali ndi kuzilandira. Ndipo iwo anavomereza kuti analidi alendo ndi osakhazikika pa dziko lapansi.
14 Ибо те, которые так говорят, показывают что они ищут отечества.
Anthu amene amanena zinthu zotere amaonekeratu kuti akufuna dziko lawo lenileni.
15 И если бы они в мыслях имели то отечество, из которого вышли, то имели бы время возвратиться;
Akanakhala kuti akuganizira za dziko limene analisiya akanapeza mpata obwerera kwawo.
16 Но они стремились к лучшему, то есть, к небесному; посему и Бог не стыдится их, называя Себя их Богом: ибо Он уготовил им город.
Mʼmalo mwake, iwo amafunitsitsa dziko labwino, ndilo lakumwamba. Nʼchifukwa chake Mulungu sachita manyazi kutchedwa Mulungu wawo, pakuti Iye anawalonjeza mudzi.
17 Верою Авраам, будучи искушаем, принес в жертву Исаака, и, имея обетование, принес единородного,
Ndi chikhulupiriro Abrahamu, Mulungu atamuyesa, anapereka Isake ngati nsembe. Ngakhale anali munthu woti Mulungu anamulonjeza, anakhala wokonzeka kupereka nsembe mwana wake mmodzi yekhayo.
18 О котором было сказано: “в Исааке наречется тебе семя”;
Za mwana ameneyu Mulungu anamuwuza iye kuti, “Zidzukulu zako zidzachokera mwa Isake.”
19 Ибо он думал, что Бог силен и из мертвых воскресить, почему и получил его в предзнаменование.
Abrahamu amazindikira kuti Mulungu angathe kuukitsa akufa, ndipo tingathe kunena mofanizira kuti iye analandiranso Isake ngati wouka kwa akufa.
20 Верою в будущее Исаак благословил Иакова и Исава.
Ndi chikhulupiriro Isake anadalitsa Yakobo ndi Esau pa zatsogolo lawo.
21 Верою Иаков, умирая, благословил каждого сына Иосифова и поклонился на верх жезла своего.
Ndi chikhulupiriro, pamene Yakobo ankamwalira anadalitsa ana awiri a Yosefe, ndipo anapembedza Mulungu atatsamira ndodo yake.
22 Верою Иосиф, при кончине напоминал об исходе сынов Израилевых и завещал о костях своих.
Ndi chikhulupiriro Yosefe ali pafupi kumwalira anayankhula za kutuluka kwa Aisraeli mu Igupto ndipo anawawuza zoti adzachite ndi mafupa ake.
23 Верою Моисей по рождении три месяца скрываем был родителями своими; ибо видели они, что дитя прекрасно, и не устрашились царского повеления.
Ndi chikhulupiriro Mose atabadwa makolo ake anamubisa miyezi itatu, chifukwa iwo anaona kuti mwanayo anali wokongola ndipo sanaope konse lamulo la mfumu.
24 Верою Моисей, пришед в возраст, отказался называться сыном дочери фараоновой,
Ndi chikhulupiriro Mose atakula, anakana kutchedwa mwana wa mwana wamkazi wa Farao.
25 И лучше захотел страдать с народом Божиим, нежели иметь временное греховное наслаждение,
Iye anasankha kuzunzika nawo limodzi anthu a Mulungu kuposa kusangalala ndi zokondweretsa za uchimo kwa nthawi yochepa.
26 И поношение Христово почел большим для себя богатством, нежели Египетские сокровища; ибо он взирал на воздаяние.
Anaona kuti kuzunzika chifukwa cha Khristu kunali kwa mtengowapatali kuposa chuma cha ku Igupto, chifukwa amaona mphotho ya mʼtsogolo.
27 Верою оставил он Египет, не убоявшись гнева царского; ибо он, как бы видя Невидимого, был тверд.
Ndi chikhulupiriro anachoka ku Igupto wosaopa ukali wa mfumu. Iye anapirira chifukwa anamuona Mulungu amene ndi wosaonekayo.
28 Верою совершил он пасху и пролитие крови, дабы истребитель первенцев не коснулся их.
Ndi chikhulupiriro anachita Paska ndi kuwaza magazi, kuti mngelo wowononga ana oyamba kubadwa asaphe ana oyamba kubadwa a Aisraeli.
29 Верою перешли они Чермное море, как по суше, на что покусившись Египтяне потонули.
Ndi chikhulupiriro Aisraeli anawoloka Nyanja Yofiira ngati pa mtunda powuma, koma Aigupto atayesa kutero anamizidwa.
30 Верою пали стены Иерихонские по семидневном обхождении.
Ndi chikhulupiriro mpanda wa Yeriko unagwa, Aisraeli atawuzungulira kasanu ndi kawiri.
31 Верою Раав блудница, с миром принявши соглядатаев (и проводивши их другим путем), не погибла с неверными.
Ndi chikhulupiriro Rahabe, mkazi wadama sanaphedwe pamodzi ndi osamvera aja chifukwa analandira bwino ozonda aja ku nyumba kwake.
32 И что еще скажу? Не достанет мне времени. чтобы повествовать о Гедеоне, о Вараке, о Самсоне и Иеффае, о Давиде, Самуиле и (других) пророках,
Kodi ndinenenso chiyani? Nthawi yandichepera yoti ndinene za Gideoni, Baraki, Samsoni, Yefita, Davide, Samueli ndi aneneri,
33 Которые верою побеждали царства, творили правду, получали обетования, заграждали уста львов,
amene ndi chikhulupiriro anagonjetsa mafumu, anakhazikitsa chilungamo ndi kulandira zimene zinalonjezedwa. Anatseka pakamwa pa mikango,
34 Угашали силу огня, избегали острия меча, укреплялись от немощи, были крепки на войне, прогоняли полки чужих;
anazimitsa moto waukali, ndipo anapulumuka osaphedwa ndi lupanga. Anali ofowoka koma analandira mphamvu; anasanduka amphamvu pa nkhondo, nathamangitsa magulu a ankhondo a adani awo.
35 Жены получали умерших своих воскресшими; иные же замучены были, не принявши освобождения, дабы получить лучшее воскресение;
Amayi ena analandira anthu awo amene anafa, ataukitsidwanso. Enanso anazunzidwa ndipo anakana kumasulidwa, kuti adzaukenso ndi moyo wabwino.
36 Другие испытали поругания и побои, а также узы и темницу.
Ena anawaseka ndi kuwakwapula, pamenenso ena anamangidwa ndi kupita ku ndende.
37 Были побиваемы камнями, перепиливаемы, подвергаемы пытке, умирали от меча, скитались в милотях и козьих кожах, терпя недостатки, скорби, озлобления;
Anagendedwa miyala; anachekedwa pakati; ena anaphedwa ndi lupanga. Iwo anayendayenda atavala zikopa zankhosa ndi zikopa zambuzi, umphawi okhaokha, ozunzidwa ndi kuvutitsidwa.
38 Те, которых весь мир не был достоин, скитались по пустыням и горам, по пещерам и ущельям земли.
Dziko lapansi silinawayenere. Anayendayenda mʼzipululu ndi mapiri, ndiponso mʼmapanga ndi mʼmaenje.
39 И все сии, свидетельствованные в вере, не получили обещанного,
Onsewa anayamikidwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo, komabe palibe wa iwo amene analandira zimene analonjezedwa.
40 Потому что Бог предусмотрел о нас нечто лучшее, дабы они не без нас достигли совершенства.
Mulungu anatikonzera ife kanthu koposa, kuti iwo asayesedwe angwiro popanda ife.

< К Евреям 11 >