< К Галатам 6 >

1 Братия! если и впадет человек в какое согрешение, вы, духовные, исправляйте такового в духе кротости, наблюдая каждый за собою, чтобы не быть искушенным.
Abale, ngati munthu agwa mʼtchimo lililonse, inu amene Mzimu amakutsogolerani, mumuthandize munthuyo ndi mtima wofatsa kuti akonzekenso. Koma mukhale maso kuti inu nomwe mungayesedwe.
2 Носите бремена друг друга, и таким образом исполните закон Христов.
Thandizanani kusenza zolemetsa zanu, ndipo mʼnjira imeneyi mudzakwanitsa lamulo la Khristu.
3 Ибо кто почитает себя чем-нибудь, будучи ничто, тот обольщает сам себя.
Ngati wina adziyesa kanthu pamene iyeyo sali kanthu konse, akudzinamiza yekha.
4 Каждый да испытывает свое дело, и тогда будет иметь похвалу только в себе, а не в другом,
Munthu aliyense aziyesa yekha ntchito zake mmene zilili. Ngati zili bwino, adzatha kunyadira chifukwa cha ntchito zake zokhazo, iyeyo asadzifanizire ndi munthu wina wake,
5 ибо каждый понесет свое бремя.
pakuti aliyense ayenera kusenza katundu wake.
6 Наставляемый словом, делись всяким добром с наставляющим.
Koma munthu amene akuphunzira mawu, agawireko mphunzitsi wake zinthu zonse zabwino zimene iye ali nazo.
7 Не обманывайтесь: Бог поругаем не бывает. Что посеет человек, то и пожнет:
Musanamizidwe: nʼkosatheka kupusitsa Mulungu. Munthu amakolola zimene wafesa.
8 сеющий в плоть свою от плоти пожнет тление, а сеющий в дух от духа пожнет жизнь вечную. (aiōnios g166)
Pakuti amene amafesa zokondweretsa thupi lake la uchimo, kuchokera ku khalidwe limenelo adzakolola chiwonongeko; amene amafesa zokondweretsa Mzimu, kuchokera kwa Mzimu adzakolola moyo wosatha. (aiōnios g166)
9 Делая добро, да не унываем, ибо в свое время пожнем, если не ослабеем.
Tisatope nʼkuchita zabwino, pakuti pa nthawi yoyenera tidzakolola ngati sititopa.
10 Итак, доколе есть время, будем делать добро всем, а наипаче своим по вере.
Nʼchifukwa chake ngati tapeza mpata, tiyenera kuchitira zabwino anthu onse, makamaka amene ndi a banja la okhulupirira.
11 Видите, как много написал я вам своею рукою.
Onani zilembo zazikulu zimene ine ndikulemba ndi dzanja langa.
12 Желающие хвалиться по плоти принуждают вас обрезываться только для того, чтобы не быть гонимыми за крест Христов,
Onse amene akufuna kuoneka abwino pamaso pa anthu akukukakamizani kuti muchite mdulidwe. Akuchita izi ndi cholinga chimodzi chokha, chakuti apewe kuzunzidwa chifukwa cha mtanda wa Khristu.
13 ибо и сами обрезывающиеся не соблюдают закона, но хотят, чтобы вы обрезывались, дабы похвалиться в вашей плоти.
Pakuti ngakhale iwowa amene anachita mdulidwe satsata Malamulo, komabe akufuna kuti muchite mdulidwe kuti anyadire mdulidwe wanuwo.
14 А я не желаю хвалиться, разве только крестом Господа нашего Иисуса Христа, которым для меня мир распят, и я для мира.
Ine sindingathe kunyadira kanthu kena koma mtanda wa Ambuye athu Yesu Khristu, kudzera mwa mtandawo dziko lapansi linapachikidwa kwa ine ndi ine ku dziko lapansi.
15 Ибо во Христе Иисусе ничего не значит ни обрезание, ни необрезание, а новая тварь.
Pakuti kaya mdulidwe kapena kusachita mdulidwe, sizitanthauza kanthu; chofunika ndi kulengedwa mwatsopano.
16 Тем, которые поступают по сему правилу, мир им и милость, и Израилю Божию.
Mtendere ndi chifundo zikhale kwa onse amene amatsata chiphunzitso ichi, ndi pa Israeli wa Mulungu.
17 Впрочем, никто не отягощай меня, ибо я ношу язвы Господа Иисуса на теле моем.
Pomaliza wina asandivutitse, pakuti mʼthupi mwanga muli zizindikiro za Yesu.
18 Благодать Господа нашего Иисуса Христа со духом вашим, братия. Аминь.
Chisomo cha Ambuye athu Yesu Khristu zikhale ndi mzimu wanu abale. Ameni.

< К Галатам 6 >