< К Ефесянам 4 >

1 Итак я, узник в Господе, умоляю вас поступать достойно звания, в которое вы призваны,
Ine monga wamʼndende chifukwa chotumikira Ambuye, ndikukulimbikitsani kuti mukhale moyo woyenera mayitanidwe amene munalandira.
2 со всяким смиренномудрием, и кротостью, и долготерпением, снисходя друг ко другу любовью,
Mukhale odzichepetsa kwathunthu ndi ofatsa; mukhale oleza mtima, ololerana wina ndi mnzake mwachikondi.
3 стараясь сохранять единство духа в союзе мира.
Muyesetse kusunga umodzi wa Mzimu; umodzi umene umatimangirira pamodzi mu mtendere.
4 Одно тело и один дух, как вы и призваны к одной надежде вашего звания;
Pali thupi limodzi ndiponso Mzimu mmodzi, monganso pali chiyembekezo chimodzi chimene anakuyitanirani.
5 один Господь, одна вера, одно крещение,
Pali Ambuye mmodzi, chikhulupiriro chimodzi, ubatizo umodzi;
6 один Бог и Отец всех, Который над всеми, и через всех, и во всех нас.
Mulungu mmodzi ndi Atate a onse, ndipo ali mwa onse.
7 Каждому же из нас дана благодать по мере дара Христова.
Koma aliyense wa ife wapatsidwa chisomo molingana ndi muyeso wa mphatso ya Khristu.
8 Посему и сказано: восшед на высоту, пленил плен и дал дары человекам.
Nʼchifukwa chake akunena kuti, “Iye atakwera kumwamba, anatenga chigulu cha a mʼndende ndipo anapereka mphatso kwa anthu.”
9 А “восшел” что означает, как не то, что Он и нисходил прежде в преисподние места земли?
Kodi mawu akuti, “Iye anakwera” akutanthauza chiyani, ngati Iyeyo sanatsikire kunsi kwa dziko lapansi?
10 Нисшедший, Он же есть и восшедший превыше всех небес, дабы наполнить все.
Iye amene anatsika ndi yemweyo anakwera koposa mʼmayiko a kumwamba onse, ndi cholinga choti zinthu zonse zikhale zodzaza ndi Iye.
11 И Он поставил одних Апостолми, других пророками, иных Евангелистами, иных пастырями и учителями,
Iye ndiye amene anapereka mphatso kwa ena kuti akhale atumwi ndi ena aneneri, ena alaliki, ndi ena abusa ndi aphunzitsi.
12 к совершению святых, на дело служения, для созидания Тела Христова,
Ntchito yawo ndi kukonza oyera mtima kuti agwire ntchito ya utumiki kuti thupi la Khristu lilimbikitsidwe.
13 доколе все придем в единство веры и познания Сына Божия, в мужа совершенного, в меру полного возраста Христова;
Izi zidzatifikitsa tonse ku umodzi wachikhulupiriro, kumudziwa Mwana wa Mulungu, kukhwima msinkhu ndi kufika pa muyeso wangwiro weniweni wopezeka mwa Khristu.
14 дабы мы не были более младенцами, колеблющимися и увлекающимися всяким ветром учения, по лукавству человеков, по хитрому искусству обольщения,
Motero sitidzakhalanso makanda, ogwedezekagwedezeka ndi mafunde, otengekatengeka ndi mphepo iliyonse ya chiphunzitso ndi kuchenjera kwa anthu achinyengo amene amasocheretsa anthu ndi kuchenjera kwawo.
15 но истинною любовью все возращали в Того, Который есть Глава Христос,
Mʼmalo mwake, poyankhula choonadi mwachikondi, tidzakula mu zinthu zonse ndi kukhala thupi la Khristu, amene ndi Mutu, omwe ndi mpingo.
16 из Которого все тело, составляемое и совокупляемое посредством всяких взаимно скрепляющих связей, при действии в свою меру каждого члена, получает приращение для созидания самого себя в любви.
Mwa Iye thupi lonse lalumikizidwa ndi kugwirana pamodzi ndi mitsempha yothandizira. Likukula ndi kudzilimbitsa lokha mwachikondi, pomwe chiwalo chilichonse chikugwira ntchito yake.
17 Посему я говорю и заклинаю Господом, чтобы вы более не поступали, как поступают прочие народы, по суетности ума своего,
Tsono ine ndikukuwuzani izi, ndipo ndikunenetsa mwa Ambuye, kuti musayendenso monga amachitira anthu a mitundu ina potsata maganizo awo opanda pake.
18 будучи помрачены в разуме, отчуждены от жизни Божией, по причине их невежества и ожесточения сердца их.
Maganizo awo ndi odetsedwa, ndi osiyanitsidwa ndi moyo wa Mulungu chifukwa cha umbuli umene uli mwa iwo chifukwa cha kuwuma mtima kwawo.
19 Они, дойдя до бесчувствия, предались распутству так, что делают всякую нечистоту с ненасытимостью.
Popeza sazindikiranso kanthu kalikonse, adzipereka okha kuti akhumbe zonyansa, kuti achite mtundu uliwonse wa zoyipa ndi zilakolako zosatha.
20 Но вы не так познали Христа;
Koma inu simunadziwe Khristu mʼnjira yotere.
21 потому что вы слышали о Нем и в Нем научились, - так как истина во Иисусе, -
Zoonadi munamva za Iye ndipo munaphunzitsidwa mwa Iye molingana ndi choonadi chimene chili mwa Yesu.
22 отложить прежний образ жизни ветхого человека, истлевающего в обольстительных похотях,
Inu munaphunzitsidwa molingana ndi moyo wanu wakale, kuchotsa umunthu wakale, umene ukupitirira kuwonongeka ndi zilakolako zachinyengo;
23 а обновиться духом ума вашего
kuti mukonzedwe mwatsopano mʼmitima mwanu;
24 и облечься в нового человека, созданного по Богу, в праведности и святости истины.
ndi kuti muvale umunthu watsopano, wolengedwa kuti ufanane ndi Mulungu mu chilungamo chenicheni ndi chiyero.
25 Посему, отвергнув ложь, говорите истину каждый ближнему своему, потому что мы члены друг другу.
Chifukwa chake, aliyense wa inu aleke kunama ndipo ayankhule zoona kwa mʼbale wake, pakuti ife tonse ndife ziwalo za thupi limodzi.
26 Гневаясь, не согрешайте: солнце да не зайдет во гневе вашем;
Kwiyani koma musachimwe. Dzuwa lisalowe mukanali chikwiyire.
27 и не давайте места диаволу.
Musamupatse mpata Satana.
28 Кто крал, вперед не кради, а лучше трудись, делая своими руками полезное, чтобы было из чего уделять нуждающемуся.
Iye amene wakhala akuba asabenso, koma agwire ntchito ndi kuchita kenakake kaphindu ndi manja ake, kuti akhale ndi kenakake kogawana ndi amene akusowa.
29 Никакое гнилое слово да не исходит из уст ваших, а только доброе для назидания в вере, дабы оно доставляло благодать слушающим.
Mʼkamwa mwanu musatuluke mawu aliwonse onyansa, koma okhawo amene ndi othandiza kulimbikitsa ena molingana ndi zosowa zawo, kuti athandize amene akawamve.
30 И не оскорбляйте Святаго Духа Божия, Которым вы запечатлены в день искупления.
Ndipo musamvetse chisoni Mzimu Woyera wa Mulungu amene mwasindikizidwa naye chizindikiro cha tsiku la kuwomboledwa.
31 Всякое раздражение и ярость, и гнев, и крик, и злоречие со всякою злобою да будут удалены от вас;
Chotsani kuzondana, ukali ndi kupsa mtima, chiwawa ndi kuyankhula zachipongwe, pamodzi ndi choyipa chilichonse.
32 но будьте друг ко другу добры, сострадательны, прощайте друг друга, как и Бог во Христе простил вас.
Mukomerane mtima ndi kuchitirana chifundo wina ndi mnzake. Khululukiranani wina ndi mnzake, monga momwe Mulungu anakukhululukirani mwa Khristu.

< К Ефесянам 4 >