< Деяния 28 >

1 Спасшись же, бывшие с Павлом узнали, что остров называется Мелит.
Titapulumuka choncho, tinamva kuti chilumbacho chimatchedwa Melita.
2 Иноплеменники оказали нам немалое человеколюбие, ибо они, по причине бывшего дождя и холода, разложили огонь и приняли всех нас.
Anthu a pa chilumbacho anatichitira zokoma zimene sizichitika kawirikawiri. Iwo anakoleza moto natilandira tonse chifukwa kumagwa mvula ndipo kumazizira.
3 Когда же Павел набрал множество хвороста и клал на огонь, тогда ехидна, выйдя от жара, повисла на руке его.
Paulo anatola mtolo wankhuni, pamene amayika pa moto, munatulukamo njoka chifukwa cha kutentha, ndipo inamuluma pa dzanja.
4 Иноплеменники, когда увидели висящую на руке его змею, говорили друг другу: верно этот человек - убийца, когда его, спасшегося от моря, суд Божий не оставляет жить.
Anthu a pa chilumbacho ataona njokayo ili lende pa dzanja lake, iwo anawuzana kuti, “Munthu uyu akuyenera kukhala munthu wopha anthu; pakuti ngakhale wapulumuka pa nyanja, chilungamo sichinamulore kuti akhale ndi moyo.”
5 Но он, стряхнув змею в огонь, не потерпел никакого вреда.
Koma Paulo anayikutumulira pa moto njokayo, ndipo sanamve kupweteka.
6 Они ожидали было, что у него будет воспаление или он внезапно упадет мертвым; но, ожидая долго и видя, что не случилось с ним никакой беды, переменили мысли и говорили, что он Бог.
Anthu anayembekezera kuti thupi lake litupa kapena agwa ndi kufa mwadzidzidzi, koma anadikira nthawi yayitali. Ataona kuti palibe kanthu kachilendo kanamuchitikira anasintha maganizo awo nanena kuti iye ndi mulungu.
7 Около того места были поместья начальника острова, именем Публия; он принял нас и три дня дружелюбно угощал.
Pafupi ndi malowa panali munda wa Popliyo, mkulu wa boma la pa chilumbacho. Iye anatilandira natisamala bwino masiku atatu.
8 Отец Публия лежал, страдая горячкою и болью в животе; Павел вошел к нему, помолился и, возложив на него руки свои, исцелил его.
Abambo ake anali gone, chifukwa amadwala malungo ndi kamwazi. Paulo analowa mʼchipinda chake kukawaona, ndipo atapemphera, anasanjika manja ake pa iwo nawachiritsa.
9 После сего события и прочие на острове, имевшие болезни, приходили, и были исцеляемы,
Zitachitika zimenezi, anthu onse odwala a pa chilumbacho anabwera ndipo anachiritsidwa.
10 и оказывали нам много почести, и при отъезде снабдили нужным.
Anthuwo anatilemekeza ife mʼnjira zambiri ndipo pamene tinakonzeka kuti tiyambe ulendo, anatipatsa zonse zomwe tinazisowa.
11 Через три месяца мы отплыли на Александрийском корабле, называемом Диоскуры, зимовавшем на том острове,
Patapita miyezi itatu, tinanyamuka pa sitima ina imene inakhala pa chilumbacho chifukwa cha kuzizira. Inali sitima ya ku Alekisandriya imene inali ndi chizindikiro cha milungu ya mapasa yotchedwa Kastro ndi Polikisi.
12 и, приплыв в Сиракузы, пробыли там три дня.
Tinakafika ku Surakusa ndipo kumeneko tinakhalako masiku atatu.
13 Оттуда отплыв, прибыли в Ригию; и как через день подул южный ветер, прибыли на второй день в Путеол,
Kuchokera kumeneko tinayenda ndi kukafika ku Regio. Mmawa mwake mphepo yochokera kummwera inawomba, ndipo tsiku linalo tinakafika ku Potiyolo.
14 где нашли братьев, и были упрошены пробыть у них семь дней, а потом пошли в Рим.
Kumeneko tinapezako abale amene anatiyitana kuti tikhale nawo sabata limodzi. Ndipo kenaka tinapita ku Roma.
15 Тамошние братья, услышав о нас, вышли нам навстречу до Аппиевой площади и трех гостиниц. Увидев их, Павел возблагодарил Бога и ободрился.
Abale kumeneko atamva kuti tikubwera, anabwera kudzakumana nafe mpaka ku bwalo la Apiyo ndiponso ku nyumba za alendo zitatu. Atawaona anthu amenewa Paulo anayamika Mulungu ndipo analimbikitsidwa.
16 Когда же пришли мы в Рим, то сотник передал узников военачальнику, а Павлу позволено жить особо с воином, стерегущим его.
Titafika ku Roma, Paulo analoledwa kukhala pa yekha ndi msilikali womulondera.
17 Через три дня Павел созвал знатнейших из Иудеев и, когда они сошлись, говорил им: мужи братия! не сделав ничего против народа или отеческих обычаев, я в узах из Иерусалима предан в руки Римлян.
Patapita masiku atatu, Paulo anasonkhanitsa pamodzi atsogoleri a Ayuda. Atasonkhana, Paulo anawawuza kuti, “Abale anga, ngakhale kuti ine sindinachite kanthu kalikonse kulakwira mtundu wathu kapena miyambo ya makolo athu, koma anandigwira mu Yerusalemu ndi kundipereka mʼmanja mwa Aroma.
18 Они, судив меня, хотели освободить, потому что нет во мне никакой вины, достойной смерти;
Iwo anandifufuza ndipo anafuna kundimasula chifukwa sanandipeze wopalamula mlandu woyenera kuphedwa.
19 но так как Иудеи противоречили, то я принужден был потребовать суда у кесаря, впрочем, не с тем, чтобы обвинить в чем-либо мой народ.
Koma Ayuda atakana, ine ndinakakamizidwa kupempha kuti ndikaonekere pamaso pa Kaisara, sikuti ndinali ndi kanthu konenezera mtundu wanga.
20 По этой причине я и призвал вас, чтобы увидеться и поговорить с вами, ибо за надежду Израилеву обложен я этими узами.
Pa chifukwa ichi ndapempha kuti ndionane nanu ndi kuyankhula nanu. Pakuti nʼchifukwa cha chiyembekezo cha Israeli ndamangidwa unyolo uwu.”
21 Они же сказали ему: мы ни писем не получали о тебе из Иудеи, ни из приходящих братьев никто не известил о тебе и не сказал чего-либо худого.
Iwo anayankha kuti, “Ife sitinalandire kalata iliyonse yochokera ku Yudeya yonena za iwe, ndipo palibe mmodzi wa abale amene anachokera kumeneko anafotokoza kapena kunena kalikonse koyipa ka iwe.
22 Впрочем, желательно нам слышать от тебя, как ты мыслишь; ибо известно нам, что об этом учении везде спорят.
Koma ife tikufuna kumva maganizo ako ndi otani, pakuti tikudziwa kuti ponseponse anthu akuyankhula zotsutsana ndi mpatuko umenewu.”
23 И, назначив ему день, очень многие пришли к нему в гостиницу; и он от утра до вечера излагал им учение о Царствии Божием, приводя свидетельства и удостоверяя их о Иисусе из закона Моисеева и пророков.
Iwo anakonza tsiku lina loti akumane ndi Paulo, ndipo anabwera anthu ambiri ku nyumba kumene amakhala. Kuyambira mmawa mpaka madzulo, Paulo anawafotokozera ndi kuwawuza za ufumu wa Mulungu ndipo anayesa kuwakopa kuti akhulupirire Yesu kuchokera mʼMalamulo a Mose ndiponso mʼmabuku a Aneneri.
24 Одни убеждались словами его, а другие не верили.
Ena anakopeka ndi zimene Paulo ananena, koma enanso sanakhulupirire.
25 Будучи же не согласны между собою, они уходили, когда Павел сказал следующие слова: хорошо Дух Святый сказал отцам нашим через пророка Исаию:
Ndipo anayamba kuchoka popeza sanagwirizane pakati pawo Paulo atanena mawu awa omaliza akuti, “Mzimu Woyera anayankhula zoona za makolo anu pamene Iye ananena kudzera mwa Mneneri Yesaya kuti,
26 “пойди к народу сему и скажи: слухом услышите, и не уразумеете, и очами смотреть будете, и не увидите.
“Pita kwa anthu awa ndi kuwawuza kuti, ‘Kumva mudzamva, koma osamvetsetsa; kupenya mudzapenya, koma osaona kanthu.’
27 Ибо огрубело сердце людей сих, и ушами с трудом слышат, и очи свои сомкнули, да не узрят очами, и не услышат ушами, и не уразумеют сердцем, и не обратятся, чтобы Я исцелил их”.
Pakuti mtima wa anthu ndi wokanika; mʼmakutu mwawo ndi mogontha, ndipo atsinzina kuti asaone kanthu. Mwina angapenye ndi maso awo, angamve ndi makutu awo, angamvetse ndi nzeru zawo ndi kutembenuka, Ineyo nʼkuwachiritsa.
28 Итак да будет вам известно, что спасение Божие послано язычникам: они и услышат.
“Chifukwa chake ine ndikufuna mudziwe kuti chipulumutso cha Mulungu chatumizidwa kwa anthu a mitundu ina, ndipo iwo adzamvera.”
29 Когда он сказал это, Иудеи ушли, много споря между собою.
Paulo atanena mawu amenewa, Ayuda aja anachoka akutsutsana kwambiri.
30 И жил Павел целых два года на своем иждивении и принимал всех приходивших к нему,
Paulo anakhala kumeneko zaka ziwiri zathunthu mʼnyumba yobwereka yomwe amalipira ndipo ankalandira aliyense amene amabwera kudzamuona.
31 проповедуя Царствие Божие и уча о Господе Иисусе Христе со всяким дерзновением невозбранно.
Molimba mtima ndi popanda womuletsa, Paulo analalikira za ufumu wa Mulungu ndi kuphunzitsa za Ambuye Yesu Khristu.

< Деяния 28 >