< Деяния 2 >

1 При наступлении дня Пятидесятницы все они были единодушно вместе.
Litafika tsiku la chikondwerero cha Pentekosite, onse anali pamodzi.
2 И внезапно сделался шум с неба, как бы от несущегося сильного ветра, и наполнил весь дом, где они находились.
Mwadzidzidzi kunamveka mkokomo kuchokera kumwamba ngati wa mphepo yamphamvu, ndipo inadzaza nyumba yonse imene amakhala.
3 И явились им разделяющиеся языки, как бы огненные, и почили по одному на каждом из них.
Iwo anaona zinthu zokhala ngati malilime amoto ogawikana ndipo anakhala pa aliyense wa iwo.
4 И исполнились все Духа Святаго, и начали говорить на иных языках, как Дух давал им провещевать.
Ndipo onse anadzazidwa ndi Mzimu Woyera, nayamba kuyankhula mu ziyankhulo zina, monga Mzimu Woyerayo anawayankhulitsa.
5 В Иерусалиме же находились Иудеи, люди набожные, из всякого народа под небом.
Ayuda woopa Mulungu ochokera ku mayiko onse a dziko lapansi ankakhala mu Yerusalemu nthawi imeneyi.
6 Когда сделался этот шум, собрался народ и пришел в смятение, ибо каждый слышал их говорящих его наречием.
Utamveka mkokomo uja, gulu la anthu linasonkhana. Anthuwo anadabwa chifukwa aliyense anawamva atumwiwo akuyankhula ziyankhulo zosiyanasiyana.
7 И все изумлялись и дивились, говоря между собою: сии говорящие не все ли Галилеяне?
Mothedwa nzeru anafunsana kuti, “Kodi anthu onse amene akuyankhulawa si Agalileya?
8 Как же мы слышим каждый собственное наречие, в котором родились.
Nanga bwanji aliyense wa ife akuwamva iwo mu chinenero cha kwawo?
9 Парфяне, и Мидяне, и Еламиты, и жители Месопотамии, Иудеи и Каппадокии, Понта и Асии,
Apanti, Amedi ndi Aelami; okhala ku Mesopotamiya, ku Yudeya ndi ku Kapadokiya, ku Ponto ndi ku Asiya,
10 Фригии и Памфилии, Египта и частей Ливии, прилежащих к Киринее, и пришедшие из Рима, Иудеи и прозелиты,
ku Frugiya ndi Pamfiliya, ku Igupto ndi ku madera a ku Libiya kufupi ndi ku Kurene; alendo ochokera ku Roma,
11 критяне и аравитяне, слышим их нашими языками говорящих о великих делах Божиих?
Ayuda ndi otsatira chipembedzo cha Chiyuda onse pamodzi; Akrete ndi Aarabu, ife tonse tikuwamva akuyankhula za ntchito zodabwitsa za Mulungu mu ziyankhulo zathu.”
12 И изумлялись все и, недоумевая, говорили друг другу: что это значит?
Modabwa ndi mothedwa nzeru anafunsana wina ndi mnzake kuti, “Zimenezi zikutanthauzanji?”
13 А иные, насмехаясь, говорили: они напились сладкого вина.
Koma ena anawaseka nati, “Aledzera vinyo watsopano.”
14 Петр же, став с одиннадцатью, возвысил голос свой и возгласил им: мужи Иудейские и все живущие в Иерусалиме! сие да будет вам известно, и внимайте словам моим:
Koma Petro anayimirira pamodzi ndi atumwi khumi ndi mmodziwo ndipo anakweza mawu ake nayankhula kwa gulu la anthu nati: “Ayuda anzanga, ndi nonse amene muli mu Yerusalemu, mvetsetsani izi ndipo tcherani khutu ku zimene ndikunena.
15 они не пьяны, как вы думаете, ибо теперь третий час дня;
Kunena zoona, anthu awa sanaledzere ayi, monga momwe mukuganizira, pakuti ino ndi 9 koloko mmawa!
16 но это есть предреченное пророком Иоилем:
Koma izi ndi zimene ananena Mneneri Yoweli kuti:
17 И будет в последние дни, говорит Бог, излию от Духа Моего на всякую плоть, и будут пророчествовать сыны ваши и дочери ваши; и юноши ваши будут видеть видения, и старцы ваши сновидениями вразумляемы будут.
“‘Mulungu akuti, mʼmasiku otsiriza ndidzakhuthulira Mzimu wanga pa anthu onse. Ana anu aamuna ndi aakazi adzanenera, anyamata anu adzaona masomphenya, nkhalamba zanu zidzalota maloto.
18 И на рабов Моих и на рабынь Моих в те дни излию от Духа Моего, и будут пророчествовать.
Ngakhalenso pa antchito anga aamuna ndi aakazi, ndidzakhuthulira Mzimu wanga masiku amenewo, ndipo iwo adzanenera.
19 И покажу чудеса на небе вверху и знамения на земле внизу, кровь, и огонь, и курение дыма.
Ndipo ndidzaonetsa zodabwitsa mlengalenga ndi zizindikiro pa dziko lapansi pano, ndizo magazi, moto ndi utsi watolotolo.
20 Солнце превратится во тьму, и луна - в кровь, прежде нежели наступит день Господень, великий и славный.
Dzuwa lidzadetsedwa ndipo mwezi udzaoneka ngati magazi lisanafike tsiku lalikulu ndi laulemerero la Ambuye.
21 И будет: всякий, кто призовет имя Господне, спасется.
Ndipo aliyense amene adzayitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka.’
22 Мужи Израильские! выслушайте слова сии: Иисуса Назорея, Мужа, засвидетельствованного вам от Бога силами, и чудесами, и знамениями, которые Бог сотворил через Него среди вас, как и сами знаете,
“Inu Aisraeli mverani mawu awa; Yesu wa ku Nazareti anali munthu amene anaperekedwa kwa inu ndi Mulungu. Ndipo Mulungu anakutsimikizirani zimenezi ndi zamphamvu, zodabwitsa ndi zizindikiro zimene anachita mwa Iye pakati panu, monga inu mukudziwa.
23 Сего, по определенному совету и предведению Божию преданного, вы взяли и, пригвоздив руками беззаконных, убили;
Yesu ameneyu anaperekedwa kwa inu mwa kufuna ndi kudziwiratu kwa Mulungu; ndipo inu mothandizidwa ndi anthu oyipa, munamupha Iye pomupachika pa mtanda.
24 но Бог воскресил Его, расторгнув узы смерти, потому что ей невозможно было удержать Его.
Koma Mulungu anamuukitsa kwa akufa, kumumasula Iye ku zowawa za imfa, chifukwa kunali kosatheka kuti agwiridwe ndi imfa.
25 Ибо Давид говорит о Нем: видел я пред собою Господа всегда, ибо Он одесную меня, дабы я не поколебался.
Pakuti Davide ananena za Iye kuti, “‘Ndinaona Ambuye pamaso panga nthawi zonse. Chifukwa Iye ali kudzanja langa lamanja, Ine sindidzagwedezeka.
26 Оттого возрадовалось сердце мое и возвеселился язык мой; даже и плоть моя упокоится в уповании,
Chifukwa chake mtima wanga ndi wokondwa ndipo lilime langa likukondwera; thupi langanso lidzakhala ndi chiyembekezo.
27 ибо Ты не оставишь души моей в аде и не дашь святому Твоему увидеть тления. (Hadēs g86)
Chifukwa simudzasiya moyo wanga kumalo a anthu akufa, ku manda, kapena kulekerera Woyerayo kuti awole. (Hadēs g86)
28 Ты дал мне познать путь жизни, Ты исполнишь меня радостью пред лицом Твоим.
Inu munandidziwitsa ine njira zamoyo; Inu mudzandidzaza ndi chimwemwe pamaso panu.’
29 Мужи братия! да будет позволено с дерзновением сказать вам о праотце Давиде, что он и умер, и погребен, и гроб его у нас до сего дня.
“Abale, ine ndikuwuzani motsimikiza kuti kholo lathu Davide anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda, ndipo manda ake alipo lero lino.
30 Будучи же пророком и зная, что Бог с клятвою обещал ему от плода чресл его воздвигнуть Христа во плоти и посадить на престоле его,
Koma iye anali mneneri ndipo anadziwa kuti Mulungu analonjeza ndi lumbiro kuti adzayika mmodzi wa zidzukulu zake pa mpando waufumu.
31 Он прежде сказал о воскресении Христа, что не оставлена душа Его в аде и плоть Его не видела тления. (Hadēs g86)
Davide ataoneratu zimene zinali mʼtsogolo anayankhula za kuuka kwa Khristu, kuti Iye sanasiyidwe mʼmanda, ndipo thupi lake silinawole. (Hadēs g86)
32 Сего Иисуса Бог воскресил, чему все мы свидетели.
Mulungu wamuukitsa Yesu ameneyu, ndipo ife ndife mboni za zimenezi.
33 Итак Он, быв вознесен десницею Божиею и приняв от Отца обетование Святаго Духа, излил то, что вы ныне видите и слышите.
Khristu anakwezedwa kukhala kudzanja lamanja la Mulungu, nalandira Mzimu Woyera amene Atate anamulonjeza, ndipo watipatsa ife zimene mukuona ndi kumvazi.
34 Ибо Давид не восшел на небеса; но сам говорит: сказал Господь Господу моему: сиди одесную Меня,
Pakuti si Davide anakwera kumwamba koma iye akuti, “‘Ambuye anawuza Ambuye anga kuti: Khala kudzanja langa lamanja
35 доколе положу врагов Твоих в подножие ног Твоих.
mpaka nditasandutsa adani ako kukhala chopondapo mapazi ako.’
36 Итак твердо знай, весь дом Израилев, что Бог соделал Господом и Христом Сего Иисуса, Которого вы распяли.
“Nʼchifukwa chake, Aisraeli onse adziwe ndithu kuti, Yesu amene inu munamupachika, Mulungu wamuyika kukhala Ambuye ndiponso Mpulumutsi.”
37 Услышав это, они умилились сердцем и сказали Петру и прочим Апостолам: что нам делать, мужи братия?
Anthu atamva zimenezi, anatsutsika kwambiri mu mtima ndipo anati kwa Petro ndi atumwi enawo, “Abale, kodi ife tichite chiyani?”
38 Петр же сказал им: покайтесь, и да крестится каждый из вас во имя Иисуса Христа для прощения грехов; и получите дар Святаго Духа.
Petro anawayankha kuti, “Lapani ndipo mubatizidwe aliyense wa inu, mʼdzina la Yesu Khristu kuti machimo anu akhululukidwe. Ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera.
39 Ибо вам принадлежит обетование, и детям вашим, и всем дальним, кого ни призовет Господь Бог наш.
Pakuti lonjezoli ndi lanu ndi ana anu ndiponso la onse amene ali kutali, ndi iwo onse amene Ambuye Mulungu wathu adzawayitane.”
40 И другими многими словами он свидетельствовал и увещевал, говоря: спасайтесь от рода сего развращенного.
Petro anawachenjeza ndi mawu ena ambiri, ndipo anawadandaulira iwo kuti, “Mudzipulumutse ku mʼbado owonongeka uno.”
41 Итак охотно принявшие слово его крестились, и присоединилось в тот день душ около трех тысяч.
Iwo amene anawulandira uthenga wake anabatizidwa ndipo tsiku lomwelo miyoyo pafupifupi 3,000 inawonjezedwa ku gulu lawo.
42 И они постоянно пребывали в учении Апостолов, в общении и преломлении хлеба и в молитвах.
Iwo ankasonkhana pamodzi kuphunzitsidwa ndi atumwi, pachiyanjano, pachakudya ndi popemphera.
43 Был же страх на всякой душе; и много чудес и знамений совершилось через Апостолов в Иерусалиме.
Aliyense ankachita mantha chifukwa cha zodabwitsa ndi zizindikiro zambiri zimene atumwi ankachita.
44 Все же верующие были вместе и имели все общее.
Okhulupirira onse anali pamodzi ndipo aliyense ankapereka zinthu zake kuti zikhale za onse.
45 И продавали имения и всякую собственность, и разделяли всем, смотря по нужде каждого.
Ankagulitsa minda yawo ndi katundu wawo, ndi kugawira kwa aliyense molingana ndi zosowa zake.
46 И каждый день единодушно пребывали в храме и, преломляя по домам хлеб, принимали пищу в веселии и простоте сердца,
Tsiku ndi tsiku ankasonkhana pamodzi pa bwalo la pa Nyumba ya Mulungu. Ankadya pamodzi mʼnyumba zawo mwasangala ndi mtima woona.
47 хваля Бога и находясь в любви у всего народа. Господь же ежедневно прилагал спасаемых к Церкви.
Ankayamika Mulungu ndipo anthu onse ankawakomera mtima. Ndipo tsiku ndi tsiku Ambuye ankawonjezera ena pa chiwerengero cha olandira chipulumutso.

< Деяния 2 >