< Деяния 18 >

1 После сего Павел, оставив Афины, пришел в Коринф;
Zitatha izi, Paulo anachoka ku Atene ndipo anapita ku Korinto.
2 и, найдя некоторого Иудея, именем Акилу, родом Понтянина, недавно пришедшего из Италии, и Прискиллу, жену его, - потому что Клавдий повелел всем Иудеям удалиться из Рима, - пришел к ним;
Kumeneko anakumana ndi Myuda wina dzina lake Akula, nzika ya ku Ponto amene anali atangofika kumene kuchokera ku Italiya pamodzi ndi mkazi wake Prisila, chifukwa Klaudiyo analamula Ayuda onse kuti achoke ku Roma. Paulo anapita kukawaona.
3 и, по одинаковости ремесла, остался у них и работал; ибо ремеслом их было делание палаток.
Popeza Paulo anali mʼmisiri wosoka matenti monga iwo, iye anakhala nawo namagwirira ntchito pamodzi.
4 Во всякую же субботу он говорил в синагоге и убеждал Иудеев и Еллинов.
Tsiku la Sabata lililonse Paulo amakambirana ndi anthu mʼsunagoge, kufuna kukopa Ayuda ndi Agriki.
5 А когда пришли из Македонии Сила и Тимофей, то Павел понуждаем был духом свидетельствовать Иудеям, что Иисус есть Христос.
Sila ndi Timoteyo atafika kuchokera ku Makedoniya, Paulo ankangogwira ntchito yolalikira yokha basi, kuchitira umboni Ayuda kuti Yesu ndiye Khristu.
6 Но как они противились и злословили, то он, отрясши одежды свои, сказал к ним: кровь ваша на главах ваших; я чист; отныне иду к язычникам.
Koma pamene Ayuda anatsutsana naye ndi kumuchita chipongwe, iye anakutumula zovala zake nati, “Magazi anu akhale pamitu yanu! Ine ndilibe mlandu. Kuyambira tsopano ndipita kwa anthu a mitundu ina.”
7 И пошел оттуда, и пришел к некоторому чтущему Бога, именем Иусту, которого дом был подле синагоги.
Ndipo Paulo anatuluka mʼsunagoge napita ku nyumba yoyandikana ndi sunagoge ya Tito Yusto, munthu wopembedza Mulungu.
8 Крисп же, начальник синагоги, уверовал в Господа со всем домом своим, и многие из Коринфян, слушая, уверовали и крестились.
Krispo, mkulu wa sunagoge, pamodzi ndi a pa banja lake lonse anakhulupirira Ambuye; ndiponso Akorinto ambiri amene anamva Paulo akulalikira anakhulupiriranso nabatizidwa.
9 Господь же в видении ночью сказал Павлу: не бойся, но говори и не умолкай,
Usiku wina Ambuye anaonekera kwa Paulo mʼmasomphenya namuwuza kuti, “Usaope, pitiriza kuyankhula, usakhale chete.
10 ибо Я с тобою, и никто не сделает тебе зла, потому что у Меня много людей в этом городе.
Pakuti Ine ndili nawe, palibe aliyense amene adzakukhudza ndi kukuchitira choyipa, chifukwa mu mzinda muno ndili ndi anthu ambiri.”
11 И он оставался там год и шесть месяцев, поучая их слову Божию.
Choncho Paulo anakhala kumeneko chaka ndi miyezi isanu ndi umodzi akuphunzitsa Mawu a Mulungu.
12 Между тем, во время проконсульства Галлиона в Ахаии, напали Иудеи единодушно на Павла и привели его пред судилище,
Galiyo ali mkulu wa boma wa ku Akaya, Ayuda mogwirizana anamugwira Paulo napita naye ku bwalo la milandu.
13 говоря, что он учит людей чтить Бога не по закону.
Iwo anati, “Munthu uyu akukopa anthu kuti azipembedza Mulungu mwanjira zotsutsana ndi malamulo athu.”
14 Когда же Павел хотел открыть уста, Галлион сказал Иудеям: Иудеи! если бы какая-нибудь была обида или злой умысел, то я имел бы причину выслушать вас,
Pamene Paulo ankati ayankhule, Galiyo anati kwa Ayuda, “Ukanakhala mlandu wochita choyipa kapena wolakwira mnzake, bwenzi nditakumverani bwinobwino.
15 но когда идет спор об учении, и об именах, и о законе вашем, то разбирайте сами; я не хочу быть судьею в этом.
Koma popeza ndi nkhani yokhudza mawu, mayina ndi malamulo anu, kambiranani nokhanokha. Ine sindidzaweruza zinthu zimenezi.”
16 И прогнал их от судилища.
Kotero iye anawapirikitsa mʼbwalo la milandu.
17 А все Еллины, схватив Сосфена, начальника синагоги, били его перед судилищем; и Галлион нимало не беспокоился о том.
Kenaka iwo anagwira Sositene, mkulu wa sunagoge, ndipo anamumenya mʼbwalo la milandu momwemo. Koma Galiyo sanasamale zimenezi.
18 Павел, пробыв еще довольно дней, простился с братиями и отплыл в Сирию, - и с ним Акила и Прискилла, - остригши голову в Кенхреях, по обету.
Paulo anakhalabe ku Korinto masiku ambiri. Kenaka anawasiya abale nakwera sitima ya pamadzi kupita ku Siriya, pamodzi ndi Prisila ndi Akula. Asanakakwere sitima ya pamadzi, anameta tsitsi lake ku Kenkreya chifukwa anali atalumbira.
19 Достигнув Ефеса, оставил их там, а сам вошел в синагогу и рассуждал с Иудеями.
Iwo anafika ku Efeso, kumene Paulo anasiyako Prisila ndi Akula. Iye yekha analowa mʼsunagoge nakambirana ndi Ayuda.
20 Когда же они просили его побыть у них долее, он не согласился,
Iwo atapempha kuti akakhale nawo nthawi yayitali, iye anakana.
21 а простился с ними, сказав: мне нужно непременно провести приближающийся праздник в Иерусалиме; к вам же возвращусь опять, если будет угодно Богу. И отправился из Ефеса. Акила же и Прискилла остались в Ефесе.
Koma pamene amachoka anawalonjeza kuti, “Ndidzabweranso Mulungu akalola.” Ndipo anakwera sitima ya pamadzi kuchoka ku Efeso.
22 Побывав в Кесарии, он приходил в Иерусалим, приветствовал церковь и отошел в Антиохию.
Pamene Paulo anafika ku Kaisareya, anakwera kukapereka moni ku mpingo kenaka anatsikira ku Antiokeya.
23 И, проведя там несколько времени, вышел, и проходил по порядку страну Галатийскую и Фригию, утверждая всех учеников.
Atakhala kwa kanthawi ku Antiokeya, Paulo anachokako nayendera madera onse a ku Galatiya ndi ku Frugiya kulimbikitsa ophunzira onse.
24 Некто Иудей, именем Аполлос, родом из Александрии, муж красноречивый и сведущий в Писаниях, пришел в Ефес.
Pa nthawi yomweyi Myuda wina dzina lake Apolo, mbadwa ya ku Alekisandriya anafika ku Efeso. Anali munthu wophunzira ndi wodziwa bwino Malemba.
25 Он был наставлен в начатках пути Господня и, горя духом, говорил и учил о Господе правильно, зная только крещение Иоанново.
Apoloyu anaphunzitsidwa njira ya Ambuye, ndipo anayankhula ndi changu chachikulu naphunzitsa za Yesu molondola, ngakhale amadziwa ubatizo wa Yohane wokha.
26 Он начал смело говорить в синагоге. Услышав его, Акила и Прискилла приняли его и точнее объяснили ему путь Господень.
Iye anayamba kuyankhula mʼsunagoge molimba mtima. Pamene Prisila ndi Akula anamva, iwo anamuyitanira ku nyumba yawo ndipo anamufotokozera njira ya Mulungu molongosoka bwino.
27 А когда он вознамерился идти в Ахаию, то братия послали к тамошним ученикам, располагая их принять его; и он, прибыв туда, много содействовал уверовавшим благодатью,
Pamene Apolo anafuna kupita ku Akaya, abale anamulimbikitsa, nalemba kalata kwa ophunzira a kumeneko kuti amulandire. Atafika kumeneko, anathandiza kwambiri amene anakhulupirira mwachisomo.
28 ибо он сильно опровергал Иудеев всенародно, доказывая Писаниями, что Иисус есть Христос.
Pakuti iye anatsutsa Ayuda mwamphamvu pamaso pa anthu, natsimikiza kuchokera mʼMalemba kuti Yesu ndiye Khristu.

< Деяния 18 >