< 2-е Фессалоникийцам 3 >

1 Итак молитесь за нас, братия, чтобы слово Господне распространялось и прославлялось, как и у вас,
Potsiriza, abale, mutipempherere kuti uthenga wa Ambuye ufalikire msanga ndi kulemekezedwa monga momwe munachitira inu.
2 и чтобы нам избавиться от беспорядочных и лукавых людей, ибо не во всех вера.
Ndipo pempherani kuti tilanditsidwe mʼmanja mwa anthu ovuta ndi oyipa, pakuti si onse amene ali nacho chikhulupiriro.
3 Но верен Господь, Который утвердит вас и сохранит от лукавого.
Koma Ambuye ndi wokhulupirika, ndipo adzakulimbikitsani ndi kukutetezani kwa woyipayo.
4 Мы уверены о вас в Господе, что вы исполняете и будете исполнять то, что мы вам повелеваем.
Tili ndi chikhulupiriro mwa Ambuye kuti mukuchita zonse ndipo mudzapitirira kuchita zimene tinakulamulirani.
5 Господь же да управит сердца ваши в любовь Божию и в терпение Христово.
Ambuye atsogolere mitima yanu kuti mudziwe chikondi cha Mulungu ndiponso kupirira kumene Khristu amapereka.
6 Завещаваем же вам, братия, именем Господа нашего Иисуса Христа, удаляться от всякого брата, поступающего бесчинно, а не по преданию, которое приняли от нас,
Abale, tikukulamulani mʼdzina la Ambuye Yesu Khristu, kuti mupewe mʼbale aliyense amene ndi waulesi ndi wachisokonezo, wosafuna kutsata zimene tinakuphunzitsani.
7 ибо вы сами знаете, как должны вы подражать нам; ибо мы не бесчинствовали у вас,
Pakuti inu mukudziwa zimene muyenera kuchita pofuna kutitsatira. Ife sitinali alesi pamene tinali nanu
8 ни у кого не ели хлеба даром, но занимались трудом и работою ночь и день, чтобы не обременить кого из вас,
ndipo sitinadye chakudya cha aliyense osalipira. Komatu tinkagwira ntchito mwamphamvu usiku ndi usana kuti tisakhale cholemetsa kwa aliyense.
9 не потому, чтобы мы не имели власти, но чтобы себя самих дать вам в образец для подражания нам.
Sitinachite zimenezi chifukwa choti tinalibe mphamvu zolamula kuti mutithandize koma kuti tikhale chitsanzo choti mutsatire.
10 Ибо когда мы были у вас, то завещевали вам сие: если кто не хочет трудиться, тот и не ешь.
Pakuti ngakhale pamene tinali nanu, tinakupatsani lamulo lakuti, “Munthu wosafuna kugwira ntchito, asadye.”
11 Но слышим, что некоторые у вас поступают бесчинно, ничего не делают, а суетятся.
Ife tikumva kuti pakati panu pali ena amene ndi alesi. Iwo safuna kugwira ntchito, koma amangolowerera pa za eni.
12 Таковых увещеваем и убеждаем Господом нашим Иисусом Христом, чтобы они, работая в безмолвии, ели свой хлеб.
Mʼdzina la Ambuye Yesu Khristu, tikuwalamula ndi kuwakakamiza kuti azigwira ntchito mwabata ndi kumadya chakudya chodzigwirira ntchito okha.
13 Вы же, братия, не унывайте, делая добро.
Koma inu abale, musatope nʼkuchita zabwino.
14 Если же кто не послушает слова нашего в сем послании, того имейте на замечании и не сообщайтесь с ним, чтобы устыдить его.
Ngati wina aliyense akana kumvera malangizo athu a mʼkalatayi, mumuonetsetse ameneyo ndipo musayanjane naye kuti achite manyazi.
15 Но не считайте его за врага, а вразумляйте, как брата.
Komatu musamutenge kukhala mdani, koma muchenjezeni ngati mʼbale.
16 Сам же Господь мира да даст вам мир всегда во всем. Господь со всеми вами!
Tsopano Ambuye mwini mtendere akupatseni mtendere nthawi zonse mwa njira iliyonse. Ambuye akhale ndi inu nonse.
17 Приветствие моею рукою, Павловою, что служит знаком во всяком послании; пишу я так:
Ine Paulo, ndikulemba malonje awa ndi dzanja langa, chimene ndi chizindikiro chodziwika mʼmakalata anga onse. Umo ndi mmene ndimalembera.
18 благодать Господа нашего Иисуса Христа со всеми вами. Аминь.
Chisomo cha Ambuye athu Yesu Khristu chikhale ndi inu nonse.

< 2-е Фессалоникийцам 3 >