< 2-e Петра 2 >

1 Были и лжепророки в народе, как и у вас будут лжеучители, которые введут пагубные ереси и, отвергаясь искупившего их Господа, навлекут сами на себя скорую погибель.
Koma panalinso aneneri onama pakati pa Aisraeli, monga padzakhalanso aphunzitsi onyenga pakati panu. Iwo adzalowetsa mwamseri ziphunzitso zonama ndi zowononga, nadzakana Ambuye amene anawawombola, ndipo motero adzadziyitanira okha chiwonongeko mwadzidzidzi.
2 И многие последуют их разврату, и через них путь истины будет в поношении.
Ambiri adzatsata njira zawo zochititsa manyazi ndipo chifukwa cha iwowa, anthu adzanyoza njira ya choonadi.
3 И из любостяжания будут уловлять вас льстивыми словами; суд им давно готов, и погибель их не дремлет.
Pofuna kupeza chuma, aphunzitsiwa adzakudyerani chuma chanu pokuwuzani nkhani zopeka. Chiweruzo chawo chinakonzedwa kale, ndipo chikuwadikira.
4 Ибо, если Бог ангелов согрешивших не пощадил, но, связав узами адского мрака, предал блюсти на суд для наказания; (Tartaroō g5020)
Pakuti Mulungu sanalekerere angelo atachimwa paja, koma anawaponya mʼndende, nawayika mʼmaenje amdima, kuwasunga kuti adzaweruzidwe. (Tartaroō g5020)
5 и если не пощадил первого мира, но в восьми душах сохранил семейство Ноя, проповедника правды, когда навел потоп на мир нечестивых;
Iye sanalekerere dziko lapansi kalelo, koma anapulumutsa Nowa, mlaliki wa chilungamo, ndi anthu ena asanu ndi awiri atadzetsa chigumula pa dziko lapansi kwa anthu akhalidwe losapembedza Mulunguyo.
6 и если города Содомские и Гоморрские, осудив на истребление, превратил в пепел, показав пример будущим нечестивцам,
Mulungu anaweruza mizinda ya Sodomu ndi Gomora nayiwononga ndi moto, kuti ikhale chitsanzo cha zimene zidzachitikira anthu osapembedza Mulungu.
7 а праведного Лота, утомленного обращением между людьми неистово развратными, избавил
Koma Iye anapulumutsa Loti, munthu wolungama, amene ankavutika ndi khalidwe lonyansa la anthu oyipa.
8 ибо сей праведник, живя между ними, ежедневно мучился в праведной душе, видя и слыша дела беззаконные
(Pakuti munthu wolungamayo, pokhala pakati pawo tsiku ndi tsiku ankavutika mu mtima ndi makhalidwe awo oyipa amene ankawaona ndi kuwamva).
9 то, конечно, знает Господь, как избавлять благочестивых от искушения, а беззаконников соблюдать ко дню суда, для наказания,
Tsono mutha kuona kuti Ambuye amadziwa kuwapulumutsa kwake pa mayesero anthu opembedza. Amadziwanso kusunga osalungama kuti alangidwe mpaka tsiku la chiweruzo.
10 а наипаче тех, которые идут вслед скверных похотей плоти, презирают начальства, дерзки, своевольны и не страшатся злословить высших,
Makamaka amene amatsata zilakolako zonyansa zathupi nanyoza ulamuliro. Anthu amenewa ndi odzikuza, ndipo otsata chifuniro cha iwo eni, sasamala za munthu, saopa kuchitira chipongwe zolengedwa za mmwamba.
11 тогда как и Ангелы, превосходя их крепостью и силою, не произносят на них пред Господом укоризненного суда.
Komatu ngakhale angelo, amene ali akulu ndi amphamvu kuwaposa, sayankhula za chipongwe pobweretsa chiweruzo pa iwo kuchokera kwa Ambuye.
12 Они, как бессловесные животные, водимые природою, рожденные на уловление и истребление, злословя то, чего не понимают, в растлении своем истребятся.
Koma anthu awa amachita chipongwe zinthu zimene sakuzidziwa. Ali ngati zirombo zopanda nzeru. Zirombo zolengedwa kuti zigwidwe ndi kuwonongedwa, ndipo ngati zirombozo adzawonongedwa.
13 Они получат возмездие за беззаконие, ибо они полагают удовольствие во вседневной роскоши; срамники и осквернители, они наслаждаются обманами своими, пиршествуя с вами.
Iwo adzalangidwa chifukwa cha zoyipa zimene anachita. Koma chimene chimawakomera ndi kumangochita zokondweretsa thupi masanasana. Iwo ali ngati mawanga ndi zilema. Podya nanu pamodzi amakondwera kuchita za chinyengo.
14 Глаза у них исполнены любострастия и непрестанного греха; они прельщают неутвержденные души; сердце их приучено к любостяжанию: это сыны проклятия.
Ndi maso awo odzaza ndi chigololo, salekeza kuchimwa. Amanyengerera anthu osakhazikika. Iwo ndi akatswiri pa dyera ndi chuma, ndipo ndi ana otembereredwa!
15 Оставив прямой путь, они заблудились, идя по следам Валаама, сына Восорова, который возлюбил мзду неправедную,
Iwo anasiya njira yolungama ndipo anapatuka kutsata njira ya Baalamu mwana wa Beori, amene anakonda malipiro a chosalungama.
16 но был обличен в своем беззаконии: бессловесная ослица, проговорив человеческим голосом, остановила безумие пророка.
Koma anadzudzulidwa chifukwa cha kulakwa kwakeko. Bulu, nyama imene siyankhula, inayankhula ngati munthu kuletsa misala ya mneneriyo.
17 Это безводные источники, облака и мглы, гонимые бурею: им приготовлен мрак вечной тьмы. (questioned)
Anthu amenewa ali ngati akasupe wopanda madzi, ndiponso ngati nkhungu yowuluzidwa ndi mphepo yamkuntho. Mulungu wawasungira mdima wandiweyani.
18 Ибо, произнося надутое пустословие, они уловляют в плотские похоти и разврат тех, которые едва отстали от находящихся в заблуждении.
Pakuti anayankhula mawu opanda pake ndi onyada, ndipo ndi zilakolako zoyipa za thupi amanyenga anthu amene angopulumuka kumene pakati pa anzawo oyipa.
19 Обещают им свободу, будучи сами рабы тления; ибо, кто кем побежден, тот тому и раб.
Amawalonjeza ufulu, pomwe iwo eni ndi akapolo a zizolowezi zowononga. Pajatu munthu amakhala kapolo wa chilichonse chimene chikumulamulira.
20 Ибо если, избегнув скверн мира чрез познание Господа и Спасителя нашего Иисуса Христа, опять запутываются в них и побеждаются ими, то последнее бывает для таковых хуже первого.
Ngati anapulumuka ku zodetsa za dziko lapansi podziwa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu, pambuyo pake nagwidwanso ndi kugonjetsedwa ndi zomwezo, potsiriza adzakhala oyipa kuposa mmene analili poyamba.
21 Лучше бы им не познать пути правды, нежели, познав, возвратиться назад от преданной им святой заповеди.
Kukanakhala bwino akanapanda kudziwa njira ya chilungamo, koposa ndi kuyileka atadziwa lamulo loyera limene Mulungu anawapatsa.
22 Но с ними случается по верной пословице: пес возвращается на свою блевотину, и вымытая свинья идет валяться в грязи.
Kwa iwo miyambi iyi ndi yoona, “Galu wabwerera ku masanzi ake,” ndipo, “Nkhumba imene inasamba, yakunkhunizikanso mʼmatope.”

< 2-e Петра 2 >