< 1-я Царств 24 >

1 Когда Саул возвратился от Филистимлян, его известили, говоря: вот, Давид в пустыне Ен-Гадди.
Sauli atabwera kuchokera kumene amathamangitsa Afilisti anamva kuti, “Davide ali mʼchipululu cha Eni Gedi.”
2 И взял Саул три тысячи отборных мужей из всего Израиля и пошел искать Давида и людей его по горам, где живут серны.
Tsono Sauli anatenga asilikali 3,000 odziwa kumenya bwino nkhondo kuchokera pakati pa Aisraeli onse ndipo anapita kukafunafuna Davide ndi anthu ake ku Matanthwe a Mbalale.
3 И пришел к загону овечьему, при дороге; там была пещера, и зашел туда Саул для нужды; Давид же и люди его сидели в глубине пещеры.
Iye anafika ku makola a nkhosa amene anali mʼmbali mwa njira. Kumeneko kunali phanga, ndipo Sauli analowa mʼphangamo kuti akadzithandize. Davide ndi anthu ake ankabisala mʼkati mwenimweni mwa phangalo.
4 И говорили Давиду люди его: вот день, о котором говорил тебе Господь: “вот, Я предам врага твоего в руки твои, и сделаешь с ним, что тебе угодно”. Давид встал и тихонько отрезал край от верхней одежды Саула.
Tsono anthu a Davide anamuwuza kuti, “Tsiku lija lafika limene Yehova anakuwuzani kuti, ‘Ndidzapereka mdani wanu mʼmanja mwanu, ndi kumuchita chimene chidzakukomereni.’” Koma Davide anapita mwakachetechete ndi kukadula msonga ya mkanjo wa Sauli.
5 Но после сего больно стало сердцу Давида, что он отрезал край от одежды Саула.
Atachita izi, Davide anatsutsika mu mtima chifukwa anadula msonga ya mkanjo wa Sauli.
6 И сказал он людям своим: да не попустит мне Господь сделать это господину моему, помазаннику Господню, чтобы наложить руку мою на него, ибо он помазанник Господень.
Tsono anawuza anthu ake kuti, “Yehova asalole kuti ndimuchite choyipa mbuye wanga, wodzozedwa wa Yehova. Ndisamupweteke pakuti ndi wodzozedwa wa Yehova.”
7 И удержал Давид людей своих сими словами и не дал им восстать на Саула. А Саул встал и вышел из пещеры на дорогу.
Choncho Davide anabweza mitima ya anthu ake ndi mawu amenewa, ndipo sanawalole kuti aphe Sauli. Pambuyo pake Sauli anatuluka mʼphangamo ndipo anachoka.
8 Потом встал и Давид, и вышел из пещеры, и закричал вслед Саула, говоря: господин мой, царь! Саул оглянулся назад, и Давид пал лицем на землю и поклонился ему.
Kenaka Davide anatuluka mʼphanga muja ndipo anayitana Sauli, “Mbuye wanga!” Sauli atayangʼana mʼmbuyo, Davide anawerama ndi kugunditsa nkhope yake pansi.
9 И сказал Давид Саулу: зачем ты слушаешь речи людей, которые говорят: “вот, Давид умышляет зло на тебя”?
Anafunsa Sauli kuti, “Nʼchifukwa chiyani mumamvera mawu a anthu kuti, ‘Davide wakukonzerani chiwembu?’
10 Вот, сегодня видят глаза твои, что Господь предавал тебя ныне в руки мои в пещере; и мне говорили, чтоб убить тебя; но я пощадил тебя и сказал: “не подниму руки моей на господина моего, ибо он помазанник Господа”.
Lero lino inu mwadzionera nokha kuti Yehova anakuperekani mʼmanja mwanga mʼphanga muja. Ena anandiwuza kuti ndikupheni, koma ndakusiyani. Ndinati, ‘Sindidzapha mbuye wanga pakuti ndiye wodzozedwa wa Yehova.’
11 Отец мой! посмотри на край одежды твоей в руке моей; я отрезал край одежды твоей, а тебя не убил: узнай и убедись, что нет в руке моей зла, ни коварства, и я не согрешил против тебя; а ты ищешь души моей, чтоб отнять ее.
Tsono abambo anga, onanitu kansalu ka mkanjo wanu kali mʼdzanja langali! Popeza kuti ndinatha kudula msonga ya mkanjo wanu koma osakuphani, pamenepo mudziwe kuti ine ndilibe maganizo woti ndikuchiteni choyipa kapena kukuwukirani. Sindinakulakwireni ngakhale kuti inu mukufuna moyo wanga kuti mundiphe.
12 Да рассудит Господь между мною и тобою, и да отмстит тебе Господь за меня; но рука моя не будет на тебе,
Yehova aweruze pakati pa inu ndi ine, akulangeni chifukwa cha zoyipa zimene mukundichitazi, koma dzanja langa silidzakukhudzani.
13 как говорит древняя притча: “от беззаконных исходит беззаконие”. А рука моя не будет на тебе.
Paja anthu akale anati, ‘Munthu woyipa, ntchito zakenso ndi zoyipa.’ Kotero dzanja langa silidzakukhudzani.
14 Против кого вышел царь Израильский? За кем ты гоняешься? За мертвым псом, за одною блохою.
“Kodi mfumu ya Israeli yadzalondola yani. Inu mukuthamangitsa yani? Galu wakufa kodi? Nsabwe kodi?
15 Господь да будет судьею и рассудит между мною и тобою. Он рассмотрит, разберет дело мое, и спасет меня от руки твоей.
Nʼchifukwa chake Yehova agamule, inde aweruze pakati pa inu ndi ine ndi kupeza wolakwa. Yehova anditeteze ndi kundipulumutsa mʼdzanja lanu.”
16 Когда кончил Давид говорить слова сии к Саулу, Саул сказал: твой ли это голос, сын мой Давид? И возвысил Саул голос свой, и плакал,
Davide atatsiriza kuyankhula mawu awa, Sauli anafunsa kuti, “Kodi mawu amenewa ndi akodi mwana wanga Davide?” Sauli anayamba kulira mokweza.
17 и сказал Давиду: ты правее меня, ибо ты воздал мне добром, а я воздавал тебе злом;
Anawuza Davide kuti, “Ndiwe wolungama kuposa ine. Iwe wandikomera mtima pamene ine ndakuchitira zoyipa.
18 ты показал это сегодня, поступив со мною милостиво, когда Господь предавал меня в руки твои, ты не убил меня.
Iweyo lero lino wandifotokozera zabwino zimene wandichitira. Yehova anandipereka mʼdzanja lako koma iwe sunandiphe.
19 Кто, найдя врага своего, отпустил бы его в добрый путь? Господь воздаст тебе добром за то, что сделал ты мне сегодня.
Kodi munthu atapeza mdani wake angamulole kuti apite wosamuvulaza? Motero Yehova akuchitire iwe zabwino chifukwa cha zimene wandichitira lerozi.
20 И теперь я знаю, что ты непременно будешь царствовать, и царство Израилево будет твердо в руке твоей.
Ona tsono, Ine ndikudziwa kuti udzakhala mfumu ndithu ndipo ufumu wa Israeli udzakhazikika mʼmanja mwako.
21 Итак поклянись мне Господом, что ты не искоренишь потомства моего после меня и не уничтожишь имени моего в доме отца моего.
Tsopano undilonjeze molumbira lero mʼdzina la Yehova kuti sudzapha zidzukulu zanga ine nditamwalira kapena kufuta dzina langa pa banja la makolo anga.”
22 И поклялся Давид Саулу. И пошел Саул в дом свой, Давид же и люди его взошли в место укрепленное.
Choncho Davide analumbira pamaso pa Sauli. Pambuyo pake Sauli anabwerera kwawo, koma Davide ndi anthu ake anapitanso ku phanga kuja.

< 1-я Царств 24 >