< 1-е Коринфянам 16 >

1 При сборе же для святых поступайте так, как я установил в церквах Галатийских.
Tsopano za zopereka zothandiza anthu a Ambuye a ku Yerusalemu. Muchite zomwe ndinawuza mipingo ya ku Galatiya kuti ichite.
2 В первый день недели каждый из вас пусть отлагает у себя и сберегает, сколько позволит ему состояние, чтобы не делать сборов, когда я приду.
Pa tsiku loyamba la sabata lililonse, aliyense wa inu azipatula ndalama molingana ndi zomwe wapezera. Asunge, kuti ndikabwera pasadzakhalenso msonkhamsonkha.
3 Когда же приду, то, которых вы изберете, тех отправлю с письмами для доставления вашего подаяния в Иерусалим.
Pamenepo, ndikadzafika, ndidzawapatsa makalata a umboni anthu amene mudzawasankhe ndi kuwatuma kuti akapereka mphatso zanu ku Yerusalemu.
4 А если прилично будет и мне отправиться, то они со мной пойдут.
Ngati kutaoneka kuti nʼkoyenera kuti ndipite nawo, adzapita nane limodzi.
5 Я приду к вам, когда пройду Македонию; ибо я иду через Македонию.
Ndidzafika kwanuko nditadutsa ku Makedoniya pakuti ndikuyembekezera kudzera ku Makedoniyako.
6 У вас же, может быть, поживу или и перезимую, чтобы вы меня проводили, куда пойду.
Mwina ndidzakhala nanu kanthawi kochepa kapenanso nyengo yonse yozizira, kuti mudzandithandize kupitiriza ulendo wanga kulikonse kumene ndingapite.
7 Ибо я не хочу видеться с вами теперь мимоходом, а надеюсь пробыть у вас несколько времени, если Господь позволит.
Sindikufuna kuti ndikuoneni tsopano mongodutsa chabe, koma ndikuyembekezera kudzakhala nanu kwa kanthawi, ngati Ambuye alola.
8 В Ефесе же я пробуду до Пятидесятницы,
Koma ndikhala ndili ku Efeso mpaka nthawi ya Pentekosite,
9 ибо для меня отверста великая и широкая дверь и противников много.
pakuti mwayi waukulu wapezeka woti nʼkugwira ntchito yaphindu, koma pali ambiri amene akutsutsana nane.
10 Если же придет к вам Тимофей, смотрите, чтобы он был у вас безопасен; ибо он делает дело Господне, как и я.
Ngati Timoteyo afike kwanuko, onetsetsani kuti pasakhale zina zomuchititsa mantha pamene ali pakati panu, pakuti iye akugwira ntchito ya Ambuye monga ine.
11 Посему никто не пренебрегай его, но проводите его с миром, чтобы он пришел ко мне, ибо я жду его с братиями.
Wina aliyense asamunyoze. Muthandizeni kupitiriza ulendo wake mwamtendere kubwereranso kuli ine. Ndikumuyembekeza pamodzi ndi abale ena.
12 А что до брата Аполлоса, я очень просил его, чтобы он с братиями пошел к вам; но он никак не хотел идти ныне, а придет, когда ему будет удобно.
Tsono kunena za mʼbale wathu, Apolo, ndinamuwumiriza kwambiri kuti abwere kwa inu abale, ndipo iye sanafune kupita tsopano. Koma akadzapeza mpata wabwino adzabwera.
13 Бодрствуйте, стойте в вере, будьте мужественны, тверды.
Khalani tcheru; khazikikani mʼchikhulupiriro chanu; limbani mtima; khalani amphamvu.
14 Все у вас да будет с любовью.
Chitani zonse mwachikondi.
15 Прошу вас, братия вы знаете семейство Стефаново, что оно есть начаток Ахаии и что они посвятили себя на служение святым,
Mukudziwa kuti a mʼbanja la Stefano ndiye anali oyamba kutembenuka mtima ku Akaya, ndipo akhala akudzipereka kutumikira oyera mtima. Choncho ndikukudandaulirani, inu abale,
16 будьте и вы почтительны к таковым и ко всякому содействующему и трудящемуся.
kuti muziwamvera anthu oterewa, ndiponso aliyense wogwira nawo ntchitoyi modzipereka.
17 Я рад прибытию Стефана, Фортуната и Ахаика: они восполнили для меня отсутствие ваше,
Ndikondwera kuti Stefano, Fortunato ndi Akayiko afika, chifukwa akhala akundithandiza pakuti inu simuli nane.
18 ибо они мой и ваш дух успокоили. Почитайте таковых.
Pakuti anatsitsimutsa mzimu wanga ndi wanu womwe. Anthu a mtundu oterewa ngofunika kuwalemekeza.
19 Приветствуют вас церкви Асийские; приветствуют вас усердно в Господе Акила и Прискилла с домашнею их церковью.
Mpingo wa mʼchigawo cha ku Asiya ukupereka moni. Akula ndi Prisila akuperekanso moni wachisangalalo, mwa Ambuye, ndiponso mpingo umene umakumana mʼnyumba mwawo ukupereka moni.
20 Приветствуют вас все братия. Приветствуйте друг друга святым целованием.
Abale onse kuno akupereka moni wawo. Patsanani moni wachikondi chenicheni.
21 Мое, Павлово, приветствие собственноручно.
Ineyo Paulo, ndikulemba ndi dzanja langa mawu awa akuti moni.
22 Кто не любит Господа Иисуса Христа, анафема, маран-афа.
Ngati wina sakonda Ambuye akhale wotembereredwa. Maranatha! (Ambuye athu bwerani)!
23 Благодать Господа нашего Иисуса Христа с вами,
Chisomo cha Ambuye Yesu chikhale ndi inu.
24 и любовь моя со всеми вами во Христе Иисусе. Аминь.
Chikondi changa chikhale ndi nonsenu mwa Khristu Yesu.

< 1-е Коринфянам 16 >