< 1-я Паралипоменон 11 >

1 И собрались все Израильтяне к Давиду в Хеврон и сказали: вот, мы кость твоя и плоть твоя;
Aisraeli onse anasonkhana pamaso pa Davide ku Hebroni ndipo anati, “Ife ndife abale anu.
2 и вчера, и третьего дня, когда еще Саул был царем, ты выводил и вводил Израиля, и Господь Бог твой сказал тебе: “ты будешь пасти народ Мой, Израиля, и ты будешь вождем народа Моего Израиля”.
Kale lija, ngakhale pamene Sauli anali mfumu, inu ndinu amene munkatsogolera Aisraeli pa nkhondo zawo. Ndipo Yehova Mulungu wanu anakuwuzani kuti, ‘Iwe udzaweta anthu anga Aisraeli, ndipo udzakhala mfumu yawo.’”
3 И пришли все старейшины Израилевы к царю в Хеврон, и заключил с ними Давид завет в Хевроне пред лицем Господним; и они помазали Давида в царя над Израилем, по слову Господню, чрез Самуила.
Akuluakulu onse a Israeli atafika kwa Mfumu Davide ku Hebroni, iye anachita nawo pangano pamaso pa Yehova, ndipo anamudzoza Davide kukhala mfumu ya Israeli, monga momwe Yehova analonjezera kudzera mwa Samueli.
4 И пошел Давид и весь Израиль к Иерусалиму, то есть к Иевусу. А там были Иевусеи, жители той земли.
Davide ndi Aisraeli onse anapita ku Yerusalemu (ku Yebusi). Ayebusi amene ankakhala kumeneko
5 И сказали жители Иевуса Давиду: не войдешь сюда. Но Давид взял крепость Сион; это город Давидов.
anamuwuza Davide kuti, “Simulowa muno.” Komabe Davide analanda linga la Ziyoni, limene ndi mzinda wa Davide.
6 И сказал Давид: кто прежде всех поразит Иевусеев, тот будет главою и военачальником. И взошел прежде всех Иоав, сын Саруи, и сделался главою.
Davide anali atanena kuti “Aliyense amene adzatsogolere kukathira nkhondo Ayebusi adzakhala mkulu wa asilikali.” Yowabu mwana wa Zeruya ndiye anayamba kupita, motero anakhala mkulu wa asilikali.
7 Давид жил в той крепости, потому и называли ее городом Давидовым.
Tsono Davide anakhazikika mu lingamo, ndipo mzindawu anawutcha Mzinda wa Davide.
8 И он обстроил город кругом, начиная от Милло, всю окружность, а Иоав возобновил остальные части города.
Iye anamanga malo onse ozungulira, kuyambira ku matsitso ozungulira khoma. Ndipo Yowabu anakonzanso mbali ina ya mzindawu.
9 И преуспевал Давид, и возвышался более и более, и Господь Саваоф был с ним.
Ndipo mphamvu za Davide zinkakulirakulira chifukwa anali ndi Yehova Wamphamvuzonse.
10 Вот главные из сильных у Давида, которые крепко подвизались с ним в царстве его, вместе со всем Израилем, чтобы воцарить его, по слову Господню, над Израилем,
Awa ndiye anali atsogoleri amphamvu a Davide. Iwo pamodzi ndi Aisraeli onse, anathandiza kulimbikitsa ufumu wake kuti ukwanire madera onse, monga momwe Yehova analonjezera.
11 и вот число храбрых, которые были у Давида: Иесваал, сын Ахамани, главный из тридцати. Он поднял копье свое на триста человек и поразил их в один раз.
Nawa mayina a ankhondo amphamvu a Davide: Yasobeamu Mhakimoni anali mkulu wa atsogoleri. Iye anapha ndi mkondo ankhondo 300 nthawi imodzi.
12 По нем Елеазар, сын Додо Ахохиянина, из трех храбрых:
Wotsatana naye anali Eliezara mwana wa Dodo Mwahohi, mmodzi mwa ankhondo atatu amphamvu.
13 он был с Давидом в Фасдамиме, куда Филистимляне собрались на войну. Там часть поля была засеяна ячменем, и народ побежал от Филистимлян;
Iye anali ndi Davide ku Pasi-Damimu pamene Afilisti anasonkhana kudzachita nkhondo. Ankhondo anathawa Afilistiwo pamalo pamene panali munda wodzaza ndi barele.
14 но они стали среди поля, сберегли его и поразили Филистимлян. И даровал Господь спасение великое!
Koma awiriwo anayima pakati pa mundawo. Iwo anawuteteza, nakantha Afilistiwo ndipo Yehova anawapambanitsa koposa.
15 Трое сих главных из тридцати вождей взошли на скалу к Давиду, в пещеру Одоллам, когда стан Филистимлян был расположен в долине Рефаимов.
Atatu mwa atsogoleri makumi atatu aja anabwera kwa Davide ku thanthwe ku phanga la Adulamu pamene gulu la Afilisti linali litamanga misasa mʼchigwa cha Refaimu.
16 Давид тогда был в укрепленном месте, а охранное войско Филистимлян было тогда в Вифлееме.
Nthawi imeneyo Davide anali mu linga, ndipo boma la Afilisti linali ku Betelehemu.
17 И сильно захотелось пить Давиду, и он сказал: кто напоит меня водою из колодезя Вифлеемского, что у ворот?
Davide analakalaka madzi ndipo anati, “Haa, pakanapezeka munthu wokanditungira madzi a mʼchitsime chomwe chili pafupi ndi chipata cha ku Betelehemu!”
18 Тогда эти трое пробились сквозь стан Филистимский и почерпнули воды из колодезя Вифлеемского, что у ворот, и взяли, и принесли Давиду. Но Давид не захотел пить ее и вылил ее во славу Господа,
Choncho anthu atatuwa anadutsa mizere ya Afilisti, natunga madzi amene anali mʼchitsime chomwe chinali pafupi ndi chipata cha ku Betelehemu nabwera nawo kwa Davide. Koma iye anakana kumwa. Mʼmalo mwake anathira pansi pamaso pa Yehova.
19 и сказал: сохрани меня Господь, чтоб я сделал это! Стану ли я пить кровь мужей сих, полагавших души свои! Ибо с опасностью собственной жизни они принесли воду. И не захотел пить ее. Вот что сделали трое этих храбрых.
Iye anati, “Inu Mulungu, musalole kuti ine ndichite chinthu ichi! Kodi ndimwe magazi a anthu amene anayika miyoyo yawo pachiswe?” Chifukwa iwo anayika miyoyo yawo pachiswe kuti abweretse madziwo, Davide sanamwe. Zimenezi ndi zimene anachita anthu amphamvu atatuwo.
20 И Авесса, брат Иоава, был главным из трех: он убил копьем своим триста человек, и был в славе у тех троих.
Abisai mʼbale wa Yowabu ndiye anali mtsogoleri wa anthu atatuwa. Iye anapha ndi mkondo ankhondo 300. Choncho iyeyo anali wotchuka pakati pa anthu atatu aja.
21 Из трех он был знатнейшим и был начальником; но с теми тремя не равнялся.
Iye analandira ulemu woposa atatuwo. Kotero anakhala mtsogoleri wawo ngakhale kuti iyeyo sanali mʼgulu la anthu atatu aja.
22 Ванея, сын Иодая, мужа храброго, великий по делам, из Кавцеила: он поразил двух сыновей Ариила Моавитского; он же сошел и убил льва во рву, в снежное время;
Benaya mwana wa Yehoyada wa ku Kabizeeli anali munthu wolimba mtima amene anachita zinthu zamphamvu. Iye anakantha ankhondo awiri otchuka a ku Mowabu. Tsiku lina kukuzizira kwambiri, iye analowa mʼdzenje ndi kuphamo mkango.
23 он же убил Египтянина, человека ростом в пять локтей: в руке Египтянина было копье, как навой у ткачей, а он подошел к нему с палкою и, вырвав копье из руки Египтянина, убил его его же копьем:
Ndipo iye anakanthanso Mwigupto amene anali wotalika mamita awiri ndi theka. Ngakhale kuti Mwiguptoyo anali ndi mkondo wofanana ndi ndodo yowombera nsalu mʼdzanja mwake, Benaya anapita kukamenyana naye ali ndi chibonga chokha mʼmanja. Iye analanda mkondo mʼdzanja la Mwiguptoyo ndi kumupha ndi mkondo wake womwe.
24 вот что сделал Ванея, сын Иодая. И он был в славе у тех троих храбрых;
Izi ndi zamphamvu zimene Benaya mwana wa Yehoyada anachita. Iyeyo analinso wotchuka ngati anthu atatu amphamvu aja.
25 он был знатнее тридцати, но с тремя не равнялся, и Давид поставил его ближайшим исполнителем своих приказаний.
Iye ankalemekezedwa kuposa wina aliyense mwa anthu makumi atatu, koma sanali mʼgulu la anthu atatu aja. Ndipo Davide anamuyika kukhala woyangʼanira asilikali omuteteza.
26 А главные из воинов: Асаил, брат Иоава; Елханан, сын Додо, из Вифлеема;
Ankhondo amphamvuwa anali: Asaheli mʼbale wa Yowabu, Elihanani mwana wa Dodo wa ku Betelehemu,
27 Шамма Гародитянин; Херец Пелонитянин;
Samoti Mharori, Helezi Mpeloni.
28 Ира, сын Икеша, Фекоитянин; Евиезер Анафофянин;
Ira mwana wa Ikesi wa ku Tekowa, Abiezeri wa ku Anatoti,
29 Сивхай Хушатянин; Илай Ахохиянин;
Sibekai Mhusati, Ilai Mwahohi,
30 Магарай Нетофафянин; Хелед, сын Вааны, Нетофафянин;
Maharai Mnetofa, Heledi mwana wa Baana Mnetofa,
31 Иттай, сын Рибая, из Гивы Вениаминовой; Ванея Пирафонянин;
Itai mwana wa Ribai wa ku Gibeya ku Benjamini, Benaya Mpiratoni,
32 Хурай из Нагале-Гааша; Авиел из Аравы;
Hurai wa ku zigwa za Gaasi, Abieli Mwaribati,
33 Азмавеф Бахарумиянин; Елияхба Шаалбонянин.
Azimaveti Mbaharumi, Eliyahiba Msaaliboni,
34 Сыновья Гашема Гизонитянина: Ионафан, сын Шаге, Гараритянин;
ana a Hasemu Mgizoni, Yonatani mwana wa Sage Mharari,
35 Ахиам, сын Сахара, Гараритянин; Елифал, сын Уры;
Ahiamu mwana wa Sakari Mharari, Elifali mwana wa Uri,
36 Хефер из Махеры; Ахиа Пелонитянин;
Heferi Mmekerati, Ahiya Mpeloni,
37 Хецрой Кармилитянин; Наарай, сын Езбая;
Heziro wa ku Karimeli Naara mwana wa Ezibai,
38 Иоиль, брат Нафана; Мивхар, сын Гагрия;
Yoweli mʼbale wa Natani, Mibihari mwana wa Hagiri,
39 Целек Аммонитянин; Нахарай Берофянин, оруженосец Иоава, сына Саруи;
Zeleki Mwamoni, Naharai wa ku Beeroti, mnyamata wonyamula zida za Yowabu mwana wa Zeruya.
40 Ира Ифриянин; Гареб Ифриянин;
Ira Mwitiri, Garebu Mwitiri,
41 Урия Хеттеянин; Завад, сын Ахлая;
Uriya Mhiti, Zabadi mwana wa Ahilai,
42 Адина, сын Шизы, Рувимлянин, Глава Рувимлян, и у него было тридцать;
Adina mwana wa Siza Mrubeni, amene anali mtsogoleri wa Arubeni ndi anthu makumi atatu pamodzi naye,
43 Ханан, сын Маахи; Иосафат Мифниянин;
Hanani mwana wa Maaka, Yehosafati Mmitini,
44 Уззия Аштерофянин; Шама и Иеиел, сыновья Хофама Ароерянина;
Uziya Mwasiterati, Sama ndi Yeiyeli ana a Hotamu Mwaroeri,
45 Иедиаел, сын Шимрия, и Иоха, брат его, Фициянин;
Yediaeli mwana wa Simiri, ndi Yoha Mtizi mʼbale wake,
46 Елиел из Махавима, и Иеривай и Иошавия, сыновья Елнаама, и Ифма Моавитянин;
Elieli Mhavati, Yeribai ndi Yosaviya ana a Elinaamu, Itima Mmowabu,
47 Елиел, Овед и Иасиел из Мецоваи.
Elieli, Obedi ndi Yaasieli Mmeobai.

< 1-я Паралипоменон 11 >