< Hebræos 2 >

1 Propterea abundantius oportet observare nos ea, quae audivimus ne forte pereffluamus.
Nʼchifukwa chake, ife tiyenera kusamalira kwambiri zimene tinamva, kuopa kuti pangʼono ndi pangʼono tingazitaye.
2 Si enim qui per Angelos dictus est sermo, factus est firmus, et omnis praevaricatio, et inobedientia accepit iustam mercedis retributionem:
Popeza uthenga umene unayankhulidwa kudzera mwa angelo unali okhazikika ndithu, choncho aliyense amene ananyozera ndi kusamvera analandira chilango choyenera.
3 quomodo nos effugiemus si tantam neglexerimus salutem? quae cum initium accepisset enarrari per Dominum ab eis, qui audierunt, in nos confirmata est,
Nanga ife tidzapulumuka bwanji tikapanda kusamala chipulumutso chachikulu chotere? Ambuye ndiye anayamba kuyankhula za chipulumutsochi, kenaka amenenso anamvawo anatitsimikizira.
4 contestante Deo signis et portentis, et variis virtutibus, et Spiritus sancti distributionibus secundum suam voluntatem.
Mulungu anachitiranso umboni pochita zizindikiro, zinthu zodabwitsa ndi zamphamvu zamitundumitundu ndi powapatsa mphatso za Mzimu Woyera monga mwachifuniro chake.
5 Non enim Angelis subiecit Deus orbem terrae futurum, de quo loquimur.
Mulungu sanapereke kwa angelo ulamuliro wa dziko limene likubwerali, limene ife tikulinena.
6 Testatus est autem in quodam loco quis, dicens: Quid est homo quod memor es eius, aut filius hominis quoniam visitas eum?
Koma palipo pena pamene wina anachitira umboni kuti, “Kodi munthu ndani kuti muzimukumbukira, kapena mwana wa munthu kuti muzimusamalira?
7 Minuisti eum paulominus ab Angelis: gloria et honore coronasti eum: et constituisti eum super opera manuum tuarum.
Munamuchepetsa pangʼono kusiyana ndi angelo; munamupatsa ulemerero ndi ulemu.
8 Omnia subiecisti sub pedibus eius: In eo enim quod omnia ei subiecit, nihil dimisit non subiectum ei. Nunc autem necdum videmus omnia subiecta ei.
Munamupatsa ulamuliro pa zinthu zonse.” Poyika zinthu zonse pansi pa ulamuliro wake, Mulungu sanasiye kanthu kamene sikali mu ulamuliro wake. Koma nthawi ino sitikuona zinthu pansi pa ulamuliro wake.
9 Eum autem, qui modico quam Angeli minoratus est, videmus Iesum propter passionem mortis, gloria et honore coronatum: ut gratia Dei, pro omnibus gustaret mortem.
Koma tikuona Yesu, amene kwa kanthawi kochepa anamuchepetsa pangʼono kwa angelo, koma tsopano wavala ulemerero ndi ulemu chifukwa anamva zowawa za imfa, kuti mwachisomo cha Mulungu, Iye afere anthu onse.
10 Decebat enim eum, propter quem omnia, et per quem omnia, qui multos filios in gloriam adduxerat, auctorem salutis eorum per passionem consummari.
Mulungu amene analenga zinthu zonse ndipo zinthu zonse zilipo chifukwa cha Iye ndi mwa Iye, anachiona choyenera kubweretsa ana ake ambiri mu ulemerero. Kunali koyenera kudzera mʼnjira ya zowawa, kumusandutsa Yesu mtsogoleri wangwiro, woyenera kubweretsa chipulumutso chawo.
11 Qui enim sanctificat, et qui sanctificantur, ex uno omnes. Propter quam causam non confunditur fratres eos vocare, dicens:
Popeza iye amene ayeretsa ndi oyeresedwa onse ndi abanja limodzi. Nʼchifukwa chake Yesu sachita manyazi kuwatcha iwo abale ake.
12 Nunciabo nomen tuum fratribus meis: in medio Ecclesiae laudabo te.
Iye akuti, “Ine ndidzawuza abale anga za dzina lanu. Ndidzakuyimbirani nyimbo zamatamando pamaso pa mpingo.”
13 Et iterum: Ego ero fidens in eum. Et iterum: Ecce ego, et pueri mei, quos dedit mihi Deus.
Ndiponso, “Ine ndidzakhulupirira Iyeyo.” Ndiponso Iye akuti, “Ine ndili pano pamodzi ndi ana amene Mulungu wandipatsa.”
14 Quia ergo pueri communicaverunt carni, et sanguini, et ipse similiter participavit eisdem: ut per mortem destrueret eum, qui habebat mortis imperium, id est, diabolum:
Tsono popeza kuti anawo ndi anthu, okhala ndi mnofu ndi magazi, Yesu nayenso anakhala munthu ngati iwowo kuti kudzera mu imfa yake awononge Satana amene ali ndi mphamvu yodzetsa imfa.
15 et liberaret eos, qui timore mortis per totam vitam obnoxii erant servituti.
Pakuti ndi njira yokhayi imene Iye angamasule amene pa moyo wawo wonse anali ngati akapolo chifukwa choopa imfa.
16 Nusquam enim Angelos apprehendit, sed semen Abrahae apprehendit.
Pakuti tikudziwanso kuti sathandiza angelo, koma zidzukulu za Abrahamu.
17 Unde debuit per omnia fratribus similari, ut misericors fieret, et fidelis pontifex ad Deum, et ut repropitiaret delicta populi.
Chifukwa cha zimenezi, Iye anayenera kukhala wofanana ndi abale ake pa zonse, kuti akhale mkulu wa ansembe wachifundo ndi wokhulupirika potumikira Mulungu, kuti potero achotse machimo a anthu.
18 In eo enim, in quo passus est ipse et tentatus, potens est et eis, qui tentantur, auxiliari.
Popeza Iye mwini anamva zowawa pamene anayesedwa, Iyeyo angathe kuthandiza amene akuyesedwanso.

< Hebræos 2 >