< Actuum Apostolorum 26 >

1 Agrippa vero ad Paulum ait: Permittitur tibi loqui pro temetipso. Tunc Paulus extenta manu coepit rationem reddere.
Ndipo Agripa anawuza Paulo kuti, “Takulola kuti unene mawu ako.” Paulo anatambasula dzanja lake nayamba kudziteteza kuti,
2 De omnibus, quibus accusor a Iudaeis, rex Agrippa, aestimo me beatum apud te, cum sim defensurus me hodie,
“Mfumu Agripa ine ndikudziyesa wa mwayi kuyima pamaso panu lero lino ndi kudziteteza, kutsutsa zonse zimene Ayuda andinenera,
3 maxime te sciente omnia, et quae apud Iudaeos sunt consuetudines, et quaestiones: propter quod obsecro patienter me audias.
ndipo makamaka chifukwa inu mukudziwa bwino miyambo yonse ya Chiyuda ndiponso zonse zimene amatsutsana. Nʼchifukwa chake ndikukupemphani kuti mundimvetsere moleza mtima.
4 Et quidem vitam meam a iuventute, quae ab initio fuit in gente mea in Ierosolymis, noverunt omnes Iudaei:
“Ayuda onse akudziwa za moyo wanga mmene ndakhalira kuyambira ndili mwana, kuchokera pachiyambi cha moyo wanga mʼdziko lathu ndiponso mu Yerusalemu.
5 praescientes me ab initio (si velint testimonium perhibere) quoniam secundum certissimam sectam nostrae religionis vixi Pharisaeus.
Iwo akundidziwa kuyambira kalekale ndipo angathe kuchitira umboni kuti ndakhala ndili Mfarisi moyo wanga wonse, mmodzi wa gulu limene limasamala chipembedzo chathu koposa.
6 Et nunc in spe, quae ad patres nostros repromissionis facta est a Deo, sto iudicio subiectus:
Ndipo tsopano ndikuyimbidwa mlandu lero chifukwa cha chiyembekezo changa pa zimene Mulungu analonjeza makolo athu.
7 in quam duodecim tribus nostrae nocte ac die deservientes, sperant devenire. De qua spe accusor a Iudaeis, rex.
Ili ndi lonjezo limene mafuko athu khumi ndi awiri akuyembekezera kuti likwaniritsidwe pamene akupembedza Mulungu molimbika usana ndi usiku. Wolemekezeka Mfumu, nʼchifukwa cha chiyembekezo chimenechi Ayuda kuti akundiyimba mlandu.
8 Quid incredibile iudicatur apud vos, si Deus mortuos suscitat?
Nʼchifukwa chiyani ena a inu mukuganiza kuti nʼkosatheka kuti Mulungu aukitse akufa?
9 Et ego quidem existimaveram, me adversus nomen Iesu Nazareni debere multa contraria agere.
“Inenso ndimaganiza kuti ndimayenera kuchita zinthu zambiri pofuna kuthana ndi dzina la Yesu wa ku Nazareti.
10 quod et feci Ierosolymis, et multos sanctorum ego in carceribus inclusi, a principibus sacerdotum potestate accepta: et cum occiderentur, detuli sententiam.
Ndipo izi ndi zimene ndinazichita ku Yerusalemu. Ndi ulamuliro wa akulu a ansembe, ine ndinayika mʼndende oyera mtima ambiri, ndipo pamene amaphedwa, ine ndimavomereza.
11 Et per omnes synagogas frequenter puniens eos, compellebam blasphemare: et amplius insaniens in eos, persequebar usque in exteras civitates.
Nthawi zambiri ndinkapita mʼsunagoge iliyonse kuti alangidwe, ndipo ndinayesera kuwakakamiza kuti achitire chipongwe Mulungu. Mu mkwiyo wangawo, ndimapita ngakhale ku mizinda yachilendo kuti ndikawazunze.
12 In quibus dum irem Damascum cum potestate, et permissu principum sacerdotum,
“Pa ulendo wina wotere, ndikupita ku Damasiko ndi mphamvu ndi ulamuliro ochokera kwa akulu a ansembe,
13 die media in via, vidi, rex, de caelo supra splendorem solis circumfulsisse me lumen, et eos, qui mecum simul erant.
Wolemekezeka Mfumu, nthawi ya masana pamene ndimayenda pa msewu, ndinaona kuwala kuchokera kumwamba koposa kuwala kwa dzuwa kutandizungulira ine pamodzi ndi anzangawo.
14 Omnesque nos cum decidissemus in terram, audivi vocem loquentem mihi Hebraica lingua: Saule, Saule, quid me persequeris? durum est tibi contra stimulum calcitrare.
Tonse tinagwa pansi ndipo ndinamva mawu mʼChihebri akuti, ‘Saulo, Saulo chifukwa chiyani ukundizunza Ine? Nʼkovuta kulimbikira mtunda wopanda madzi.’”
15 Ego autem dixi: Quis es Domine? Dominus autem dixit: Ego sum Iesus, quem tu persequeris.
Ndipo ine ndinafunsa kuti, “Ndinu ndani Ambuye?” Ambuye anayankha kuti, “Ndine Yesu, amene iwe ukumuzunza.
16 Sed exurge, et sta super pedes tuos: ad hoc enim apparui tibi, ut constituam te ministrum, et testem eorum, quae vidisti, et eorum, quibus apparebo tibi,
Tsopano dzuka ndipo imirira. Ine ndaonekera kwa iwe kuti ndikusankhe kuti ukhale mtumiki ndiponso mboni ya zimene waziona za Ine ndiponso zimene ndidzakuonetsa.
17 eripiens te de populis, et gentibus, in quas nunc ego mitto te,
Ine ndidzakulanditsa mʼmanja mwa anthu a mtundu wako ndiponso mwa anthu a mitundu ina. Ine ndikukutuma kwa iwo,
18 aperire oculos eorum, ut convertantur a tenebris ad lucem, et de potestate satanae ad Deum, ut accipiant remissionem peccatorum, et sortem inter sanctos per fidem, quae est in me.
kuti ukatsekule maso awo kuti atembenuke mtima kuchoka ku mdima ndi kulowa mʼkuwala, kuchoka ku mphamvu za Satana ndi kupita kwa Mulungu, kuti alandire chikhululukiro cha machimo awo ndi kukhala mʼgulu la amene akuyeretsedwa chifukwa chokhulupirira Ine.
19 Unde rex Agrippa, non fui incredulus caelesti visioni:
“Nʼchifukwa chake Mfumu Agripa, sindinakane kumvera masomphenya wochokera kumwamba.
20 sed his, qui sunt Damasci primum, et Ierosolymis, et in omnem regionem Iudaeae, et Gentibus annunciabam, ut poenitentiam agerent, et converterentur ad Deum, digna poenitentiae opera facientes.
Kuyambira kwa anthu a ku Damasiko, a ku Yerusalemu, a ku Yudeya konse ndi kwa anthu a mitundu inanso, ndinalalikira kuti akuyenera kulapa ndi kutembenukira kwa Mulungu ndikuti aonetse kulapa kwawo mwa ntchito zawo.
21 Hac ex causa me Iudaei, cum essem in templo, comprehensum tentabant interficere.
Ichi nʼchifukwa chake Ayuda anandigwira mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu nafuna kundipha.
22 Auxilio autem adiutus Dei usque in hodiernum diem sto, testificans minori, atque maiori, nihil extra dicens quam ea, quae Prophetae locuti sunt futura esse, et Moyses,
Koma Mulungu wakhala akundithandiza mpaka lero lino. Ine ndayima pano kuti ndichitire umboni kwa anthu onse otchuka ndi anthu wamba. Ine sindikunena zina zowonjezera koma zimene Aneneri ndi Mose ananena kuti zidzachitika.
23 si passibilis Christus, si primus ex resurrectione mortuorum, lumen annunciaturus est populo, et Gentibus.
Iwo ananena kuti Khristu adzamva zowawa ndipo popeza Iye adzakhala woyamba kuuka kwa akufa, adzalalikira za kuwunika kwa anthu a mtundu wake ndiponso kwa anthu a mitundu ina.”
24 Haec loquente eo, et rationem reddente, Festus magna voce dixit: Insanis Paule: multae te litterae ad insaniam convertunt.
Paulo akudziteteza, Festo anakweza mawu nati, “Wazungulira mutu Paulo! Kuphunzira kwako kwakuchititsa misala.”
25 Et Paulus: Non insanio (inquit) optime Feste, sed veritatis, et sobrietatis verba loquor.
Paulo anayankha nati, “Wolemekezeka Festo, sindine wozungulira mutu. Zimene ndikunena ndi zoona ndiponso za nzeru.
26 Scit enim de his rex, ad quem et constanter loquor: latere enim eum nihil horum arbitror. Neque enim in angulo quidquam horum gestum est.
Mfumu ikuzidziwa bwino zinthu izi, ndipo ndikuyankhula momasuka kwa iyo. Ine ndikukhulupirira kuti palibe kanthu nʼkamodzi komwe kamene sukukadziwa, chifukwa izi sizinachike mseri.
27 Credis rex Agrippa prophetis? Scio quia credis.
Mfumu Agripa, kodi mumakhulupirira mawu a aneneri? Ine ndikudziwa kuti mumakhulupirira.”
28 Agrippa autem ad Paulum: In modico suades me Christianum fieri.
Kenaka Agripa anati kwa Paulo, “Kodi ukuganiza kuti mʼkanthawi kochepa kotere ungandikope kuti ndikhale Mkhristu?”
29 Et Paulus: Opto apud Deum, et in modico, et in magno, non tantum te, sed etiam omnes, qui audiunt, hodie fieri tales, qualis et ego sum, exceptis vinculis his.
Paulo anayankha kuti, “Ngakhale kanthawi kochepa kapena nthawi yayitali, ine ndikupempha kwa Mulungu kuti osati inu nokha koma aliyense amene akundimva lero lino akhale monga ine, kupatulapo maunyolo okhawa.”
30 Et exurrexit rex, et praeses, et Bernice, et qui assidebant eis.
Mfumu inayimirira pamodzi ndi bwanamkubwa ndi Bernisi ndiponso anthu onse amene anakhala nawo pamodzi.
31 Et cum secessissent, loquebantur ad invicem, dicentes: Quia nihil morte, aut vinculis dignum quid fecit homo iste.
Inatuluka mʼchipindamo, ndipo pamene imayankhula inati, “Munthu uyu sanachite kanthu koyenera kuphedwa kapena kumangidwa.”
32 Agrippa autem Festo dixit: Dimitti poterat homo hic, si non appellasset Caesarem.
Agripa anati kwa Festo, “Munthu uyu akanamasulidwa akanakhala kuti sanapemphe zokaonekera kwa Kaisara.”

< Actuum Apostolorum 26 >