< 예레미야 47 >

1 바로가 가사를 치기 전에 블레셋 사람에 대하여 선지자 예레미야에게 임한 여호와의 말씀이라
Uthenga umene Yehova anamupatsa mneneri Yeremiya wonena za Afilisti, Farao asanathire nkhondo Gaza ndi uwu:
2 여호와께서 이같이 말씀하시되 보라, 물이 북방에서 일어나 창일하는 시내를 이루어 그 땅과 그 중에 있는 모든 것과 그 성읍과 거기 거하는 자들을 엄몰시키리니 사람들이 부르짖으며 그 땅 모든 거민이 애곡할 것이라
Yehova akuti, “Taonani mmene madzi akubwerera kuchokera kumpoto; adzasanduka mtsinje wosefukira ndi a mkokomo. Adzasefukira mʼdziko monse ndi kumiza chilichonse mʼmenemo, mizinda ndi onse okhala mʼmenemo. Anthu adzafuwula; anthu onse okhala mʼdzikomo adzalira
3 힘센 것의 굽 치는 소리와 달리는 병거 바퀴의 울리는 소리에 아비의 손이 풀려서 그 자녀를 돌아보지 못하리니
akadzamva mgugu wa ngʼombe zazimuna zothamanga, phokoso la magaleta ake ndi kulira kwa mikombero yake. Makolo sadzatembenuka kuti athandize ana awo; manja awo adzangoti khoba.
4 이는 블레셋 사람을 진멸하시며 두로와 시돈에 남아 있는 바 도와줄 자를 다 끊어버리시는 날이 이름이라 여호와께서 갑돌섬에 남아 있는 블레셋 사람을 멸하시리라
Pakuti tsiku lafika lowononga Afilisti onse ndi kupha onse otsala, onse amene akanatha kuthandiza Turo ndi Sidoni. Yehova ali pafupi kuwononga Afilisti, otsala ochokera ku zilumba za ku Kafitori.
5 가사가 삭발되었고 아스글론과 그들에게 남아 있는 평지가 멸망되었나니 네가 네 몸 베기를 어느 때까지 하겠느냐?
Anthu a ku Gaza ameta mipala; anthu a ku Asikeloni akhala chete. Inu otsala a ku chigwa, mudzakhala mukudzichekacheka mpaka liti?
6 여호와의 칼이여, 네가 언제까지 쉬지 않겠느냐? 네 집에 들어가서 가만히 쉴지어다
“Mukulira kuti, ‘Aa, lupanga la Yehova, kodi udzapumula liti? Bwerera mʼmalo ako; ukhale momwemo ndipo ukhale chete.’
7 여호와께서 이를 명하셨은즉 어떻게 쉬겠느냐 아스글론과 해변을 치려 하여 그가 명정하셨느니라
Koma lupangalo lidzapumula bwanji pamene Yehova walilamulira kuti lithire nkhondo Asikeloni ndi anthu a mʼmbali mwa nyanja?”

< 예레미야 47 >