< 歴代誌Ⅱ 33 >

1 マナセは十二歳で王となり、五十五年の間エルサレムで世を治めた。
Manase anali wa zaka khumi ndi ziwiri pamene anakhala mfumu, ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka 55.
2 彼は主がイスラエルの人々の前から追い払われた国々の民の憎むべき行いに見ならって、主の目の前に悪を行った。
Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova, potsatira machitidwe a mitundu imene Yehova anayithamangitsa pamaso pa Aisraeli.
3 すなわち、その父ヒゼキヤがこわした高き所を再び築き、またもろもろのバアルのために祭壇を設け、アシラ像を造り、天の万象を拝んで、これに仕え、
Iyeyo anamanganso malo opembedzerapo mafano amene Hezekiya abambo ake anawaphwasula; anamanganso maguwa ansembe a Baala ndi kupanga mafano a Asera. Iye amagwadira zolengedwa zonse zamlengalenga ndi kumazipembedza.
4 また主が「わが名は永遠にエルサレムにある」と言われた主の宮のうちに数個の祭壇を築き、
Manase anamanga maguwa mʼNyumba ya Yehova, mʼmene Yehova ananena kuti, “Ine ndidzakhala mu Yerusalemu mpaka muyaya.”
5 主の宮の二つの庭に天の万象のために祭壇を築いた。
Mʼmabwalo onse awiri a Nyumba ya Yehova anamangamo maguwa ansembe a zolengedwa zonse zamlengalenga.
6 彼はまたベンヒンノムの谷でその子供を火に焼いて供え物とし、占いをし、魔法をつかい、まじないを行い、口寄せと、占い師を任用するなど、主の前に多くの悪を行って、その怒りをひき起した。
Iye ankakapereka ana ake aamuna ngati nsembe yopsereza ku chigwa cha Hinomu, ankachita zamatsenga, kuwombeza ndi ufiti, ankakafunsira kwa woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa. Iye anachita zoyipa zambiri pamaso pa Yehova, kumukwiyitsa Iyeyo.
7 彼はまた刻んだ偶像を造って神の宮に安置した。神はこの宮についてダビデとその子ソロモンに言われたことがある、「わたしはこの宮と、わたしがイスラエルのすべての部族のうちから選んだエルサレムとに、わたしの名を永遠に置く。
Manase anatenga fano losema limene anapanga ndi kuliyika mʼNyumba ya Mulungu, zimene Mulungu ananena kwa Davide ndi kwa mwana wake Solomoni kuti, “Mʼnyumba ya Mulungu muno, mu Yerusalemu muno, malo amene ndawasankha pakati pa mafuko onse a Israeli, ndidzakhalamo mpaka muyaya.
8 彼らがもし、わたしがすべて命じた事、すなわち、モーセが伝えたすべての律法と定めとおきてとを慎んで行うならば、わたしがあなたがたの先祖のために定めた地から、重ねてイスラエルの足を移すことをしない」と。
Ine sindidzachotsanso phazi la Aisraeli kuchoka mʼdziko limene ndawapatsa makolo ako, ngatitu iwowa adzasamalira kuchita chilichonse chimene ndinawalamulira za malamulo onse, malangizo ndi miyambo imene inapatsidwa kudzera mwa Mose.”
9 マナセはこのようにユダとエルサレムの住民を迷わせ、主がイスラエルの人々の前に滅ぼされた国々の民にもまさって悪を行わせた。
Koma Manase anasocheretsa anthu a ku Yuda ndi Yerusalemu, kotero anachita zoyipa zambiri kupambana mitundu imene Yehova anayiwononga pamaso pa Aisraeli.
10 主はマナセおよびその民に告げられたが、彼らは心に留めなかった。
Yehova anayankhula kwa Manase ndi anthu ake, koma iwo sanasamaleko.
11 それゆえ、主はアッスリヤの王の軍勢の諸将をこれに攻めこさせられたので、彼らはマナセをかぎで捕え、青銅のかせにつないで、バビロンに引いて行った。
Kotero Yehova anawatumizira atsogoleri a ankhondo a ku Asiriya amene anagwira Manase ukapolo, anayika ngowe mʼmphuno mwake, namumanga ndi zingwe zamkuwa ndi kupita naye ku Babuloni.
12 彼は悩みにあうに及んで、その神、主に願い求め、その先祖の神の前に大いに身を低くして、
Ali pa mavuto akewo anafunafuna kuti Yehova Mulungu wake amukomere mtima ndipo anadzichepetsa kwakukulu pamaso pa Mulungu wa makolo ake.
13 神に祈ったので、神はその祈を受けいれ、その願いを聞き、彼をエルサレムに連れ帰って、再び国に臨ませられた。これによってマナセは主こそ、まことに神にいますことを知った。
Ndipo atapemphera, Yehova anakhudzidwa ndi kupempha kwakeko ndipo anamvera madandawulo ake. Kotero anamubweretsanso ku Yerusalemu ndi ku ufumu wake. Ndipo Manase anadziwa kuti Yehova ndi Mulungu.
14 この後、彼はダビデの町の外の石がきをギホンの西の方の谷のうちに築き、魚の門の入口にまで及ぼし、またオペルに石がきをめぐらして、非常に高くこれを築き上げ、ユダのすべての堅固な町に軍長を置き、
Zitapita izi iye anamanga khoma la kunja kwa Mzinda wa Davide kumadzulo kwa kasupe wa Gihoni ku chigwa mpaka polowera ku Chipata cha Nsomba kuzungulira phiri la Ofeli. Iyeyo anakweza kwambiri khomalo. Anayikanso atsogoleri a nkhondo ku mizinda yonse yotetezedwa ya Yuda.
15 また主の宮から、異邦の神々および偶像を取り除き、主の宮の山とエルサレムに自分で築いたすべての祭壇を取り除いて、町の外に投げ捨て、
Iye anachotsa milungu yonse yachilendo ndi fano mʼNyumba ya Yehova komanso maguwa ansembe onse amene anamanga pa phiri la Nyumba ya Mulungu ndi mu Yerusalemu, nazitayira kunja kwa mzinda.
16 主の祭壇を築き直して、酬恩祭および感謝の犠牲を、その上にささげ、ユダに命じてイスラエルの神、主に仕えさせた。
Kenaka anabwezeretsa guwa lansembe la Yehova ndi kupereka zopereka zachiyanjano ndiponso zopereka zamatamando ndipo anawuza Yuda kuti atumikire Yehova Mulungu wa Israeli.
17 しかし民は、なお高き所で犠牲をささげた。ただしその神、主にのみささげた。
Komabe anthu anapitiriza kupereka nsembe ku malo achipembedzo, koma kwa Yehova, Mulungu wawo yekha.
18 マナセのそのほかの行為、その神にささげた祈、およびイスラエルの神、主の名をもって彼に告げた先見者たちの言葉は、イスラエルの列王の記録のうちにしるされている。
Zina ndi zina zokhudza ulamuliro wa Manase, kuphatikiza mapemphero ake kwa Mulungu wake ndi mawu amene alosi anayankhula kwa iye mʼdzina la Yehova Mulungu wa Israeli, zalembedwa mʼmabuku a mafumu a Israeli.
19 またその祈と、祈の聞かれた事、そのもろもろの罪と、とが、その身を低くする前に高き所を築いて、アシラ像および刻んだ像を立てた場所などは、先見者の記録のうちにしるされている。
Pemphero lake ndi momwe Mulungu anakhudzidwira ndi kupempha kwakeko, pamodzinso ndi machimo ake onse ndi kusakhulupirika kwake, ndiponso malo onse amene anamanga, malo azipembedzo ndi mafano a Asera ndi mafano asanadzichepetse, zonse zalembedwa mʼmbiri ya alosi.
20 マナセはその先祖たちと共に眠ったので、その家に葬られた。その子アモンが彼に代って王となった。
Manase anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda mʼnyumba yake yaufumu. Ndipo Amoni mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
21 アモンは王となった時二十二歳で、二年の間エルサレムで世を治めた。
Amoni anali wa zaka 22 pamene anakhala mfumu ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka ziwiri.
22 彼はその父マナセのしたように主の前に悪を行った。すなわちアモンはその父マナセが造ったもろもろの刻んだ像に犠牲をささげて、これに仕え、
Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova, monga anachitira Manase abambo ake. Amoni analambira ndi kupereka nsembe kwa mafano onse amene anapanga Manase.
23 その父マナセが身を低くしたように主の前に身を低くしなかった。かえってこのアモンは、いよいよそのとがを増した。
Koma kusiyana ndi abambo ake Manase, iye sanadzichepetse pamaso pa Yehova. Amoni anawonjeza kulakwa kwake.
24 その家来たちは党を結んで彼にそむき、彼をその家で殺した。
Akuluakulu a Amoni anamuchita chiwembu ndipo anamupha mʼnyumba yake yaufumu.
25 しかし国の民は、党を結んでアモン王にそむいた者どもをことごとく撃ち殺した。そして国の民はその子ヨシヤを王となして、そのあとを継がせた。
Koma anthu a mʼdzikomo anapha onse amene anakonzera chiwembu mfumu Amoni, ndipo anayika mwana wake Yosiya kukhala mfumu mʼmalo mwake.

< 歴代誌Ⅱ 33 >