< サムエル記Ⅰ 2 >

1 ハンナは祈って言った、「わたしの心は主によって喜び、わたしの力は主によって強められた、わたしの口は敵をあざ笑う、あなたの救によってわたしは楽しむからである。
Ndipo Hana anapemphera nati, “Moyo wanga ukukondwera mwa Yehova; Ndiyenda mwa tukumutukumu chifukwa cha Yehova. Pakamwa panga pakula ndi kuseka adani anga mowanyogodola. Ndikukondwa chifukwa mwandipulumutsa.
2 主のように聖なるものはない、あなたのほかには、だれもない、われわれの神のような岩はない。
“Palibe wina woyera ngati Yehova, palibe wina koma inu nokha, palibe thanthwe lofanana ndi Mulungu wathu.
3 あなたがたは重ねて高慢に語ってはならない、たかぶりの言葉を口にすることをやめよ。主はすべてを知る神であって、もろもろのおこないは主によって量られる。
“Musandiyankhulenso modzitama, pakamwa panu pasatuluke zonyada, pakuti Yehova ndi Mulungu wanzeru, ndipo ndiye amene amayesa ntchito za anthu onse.
4 勇士の弓は折れ、弱き者は力を帯びる。
“Mauta a anthu ankhondo athyoka koma anthu ofowoka avala dzilimbe.
5 飽き足りた者は食のために雇われ、飢えたものは、もはや飢えることがない。うまずめは七人の子を産み、多くの子をもつ女は孤独となる。
Amene kale anali okhuta tsopano akukagula chakudya, koma iwo amene anali ndi njala sakumvanso njala. Amene anali wosabereka, wabereka ana aamuna asanu ndi awiri, koma iye wobereka ana ambiri watsala yekha.
6 主は殺し、また生かし、陰府にくだし、また上げられる。 (Sheol h7585)
“Yehova amabweretsa imfa ndipo amaperekanso moyo, amatsitsira ku manda ndipo amawatulutsakonso. (Sheol h7585)
7 主は貧しくし、また富ませ、低くし、また高くされる。
Yehova amasaukitsa ndipo amalemeretsa, amatsitsa ndipo amakweza.
8 貧しい者を、ちりのなかから立ちあがらせ、乏しい者を、あくたのなかから引き上げて、王侯と共にすわらせ、栄誉の位を継がせられる。地の柱は主のものであって、その柱の上に、世界をすえられたからである。
Iye amakweza osauka kuwachotsa pa fumbi, ndipo amachotsa anthu osowa pa dzala. Iye amawakhazika pamodzi ndi ana a mafumu, amawapatsa mpando waulemu. “Pakuti nsanamira za dziko lapansi ndi za Yehova, anakhazika dziko lapansi pa nsanamirazo.
9 主はその聖徒たちの足を守られる、しかし悪いものどもは暗黒のうちに滅びる。人は力をもって勝つことができないからである。
Iye adzateteza moyo wa anthu okhulupirika koma anthu oyipa adzawonongedwa mu mdima. “Pakuti munthu sapambana ndi mphamvu zake.
10 主と争うものは粉々に砕かれるであろう、主は彼らにむかって天から雷をとどろかし、地のはてまでもさばき、王に力を与え、油そそがれた者の力を強くされるであろう」。
Yehova adzaphwanya omutsutsa. Adzawaopsa ndi bingu kuchokera kumwamba; Yehova adzaweruza mathero a dziko lapansi. “Koma adzapereka mphamvu kwa mfumu yake, adzakuza mphamvu za odzozedwa wake.”
11 エルカナはラマにある家に帰ったが、幼な子は祭司エリの前にいて主に仕えた。
Tsono Elikana anapita ku mudzi kwawo ku Rama, koma mnyamatayo amatumikira Yehova pansi pa ulamuliro wa wansembe Eli.
12 さて、エリの子らは、よこしまな人々で、主を恐れなかった。
Ana a Eli anali ana achabechabe pakuti samasamala za Yehova.
13 民のささげ物についての祭司のならわしはこうである。人が犠牲をささげる時、その肉を煮る間に、祭司のしもべは、みつまたの肉刺しを手に持ってきて、
Ndipo chizolowezi cha ansembe pakati pa anthu chinali motere kuti pamene munthu aliyense ankapereka nsembe ndipo nyama ija ikuwira pa moto, mtumiki wa wansembe ankabwera ndi chifoloko cha mano atatu mʼdzanja lake.
14 それをかま、またはなべ、またはおおがま、または鉢に突きいれ、肉刺しの引き上げるものは祭司がみな自分のものとした。彼らはシロで、そこに来るすべてのイスラエルの人に、このようにした。
Iye ankachipisa mu mʼphikamo, ndipo wansembeyo amatenga chilichonse chimene folokoyo yabaya. Umu ndi mmene ansembewo amachitira ndi Aisraeli onse amene amabwera ku Silo.
15 人々が脂肪を焼く前にもまた、祭司のしもべがきて、犠牲をささげる人に言うのであった、「祭司のために焼く肉を与えよ。祭司はあなたから煮た肉を受けない。生の肉がよい」。
Ndipo ngakhale mafuta asanatenthedwe, mtumiki wansembe amabwera ndi kunena kwa munthu amene akupereka nsembeyo kuti, “Ndipatse nyama kuti ndiwotche, pakuti Yehova salandira nyama yophika koma yayiwisi.”
16 その人が、「まず脂肪を焼かせましょう。その後ほしいだけ取ってください」と言うと、しもべは、「いや、今もらいたい。くれないなら、わたしは力づくで、それを取ろう」と言う。
Ngati munthuyo anena kuti, “Apseretu mafuta poyamba, ndipo kenaka mutenge mmene mufunira,” mtumikiyo amayankha kuti, “Ayi ndipatse tsopano lino. Ngati sutero, ine nditenga molanda.”
17 このように、その若者たちの罪は、主の前に非常に大きかった。この人々が主の供え物を軽んじたからである。
Tchimo la ana a Eli linali lalikulu kwambiri pamaso pa Yehova pakuti iwo amanyoza nsembe za Yehova.
18 サムエルはまだ幼く、身に亜麻布のエポデを着けて、主の前に仕えていた。
Koma Samueli amatumikira pamaso pa Yehova atavala efodi ya nsalu yofewa yosalala.
19 母は彼のために小さい上着を作り、年ごとに、夫と共にその年の犠牲をささげるために上る時、それを持ってきた。
Chaka chilichonse amayi ake ankamusokera kamkanjo ndi kukamupatsa akamapita ndi mwamuna wake kukapereka nsembe za pa chaka.
20 エリはいつもエルカナとその妻を祝福して言った、「この女が主にささげた者のかわりに、主がこの女によってあなたに子を与えられるように」。そして彼らはその家に帰るのを常とした。
Tsono Eli amadalitsa Elikana ndi mkazi wake ndi mawu akuti “Yehova akupatseni ana mwa mkazi uyu kulowa mʼmalo mwa amene anapempha ndi kumupereka kwa Yehova.”
21 こうして主がハンナを顧みられたので、ハンナはみごもって、三人の男の子とふたりの女の子を産んだ。わらべサムエルは主の前で育った。
Ndipo Yehova anamukomera mtima Hana. Anakhala ndi pathupi ndi kubereka ana aamuna atatu ndi ana aakazi awiri. Ndipo Samueli ankakula pamaso pa Yehova.
22 エリはひじょうに年をとった。そしてその子らがイスラエルの人々にしたいろいろのことを聞き、また会見の幕屋の入口で勤めていた女たちと寝たことを聞いて、
Tsono Eli anakalamba kwambiri. Iye ankamva zonse zimene ana ake aamuna ankachitira Aisraeli onse, ndiponso kuti ankagona ndi akazi pa chipata cha tenti ya msonkhano.
23 彼らに言った、「なにゆえ、そのようなことをするのか。わたしはこのすべての民から、あなたがたの悪いおこないのことを聞く。
Choncho anawafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukuchita zinthu zotere? Ine ndikumva kuchokera kwa anthu onse za zoyipa zanuzo.
24 わが子らよ、それはいけない。わたしの聞く、主の民の言いふらしている風説は良くない。
Ayi, ana anga si mbiri yabwino imene ndikumva anthu a Mulungu akufalitsa.
25 もし人が人に対して罪を犯すならば、神が仲裁されるであろう。しかし人が主に対して罪を犯すならば、だれが、そのとりなしをすることができようか」。しかし彼らは父の言うことに耳を傾けようともしなかった。主が彼らを殺そうとされたからである。
Ngati munthu alakwira munthu mnzake, mwina Mulungu adzamupepesera, koma ngati munthu achimwira Yehova adzamupepesera ndani?” Koma ana ake sanamvere kudzudzula kwa abambo awo, pakuti chinali cholinga cha Yehova kuti awaphe.
26 わらべサムエルは育っていき、主にも、人々にも、ますます愛せられた。
Ndipo mnyamata Samueli anapitirira kukula mu msinkhu, ndipo ankapeza kuyanja pamaso pa Yehova ndi anthu.
27 このとき、ひとりの神の人が、エリのもとにきて言った、「主はかく仰せられる、『あなたの先祖の家がエジプトでパロの家の奴隷であったとき、わたしはその先祖の家に自らを現した。
Tsiku lina munthu wa Mulungu anabwera kwa Eli ndipo anamuwuza kuti, “Yehova akuti, ‘Kodi Ine sindinadziwulule ndekha kwa banja la kholo lako pamene iwo anali akapolo a Farao ku Igupto?
28 そしてイスラエルのすべての部族のうちからそれを選び出して、わたしの祭司とし、わたしの祭壇に上って、香をたかせ、わたしの前でエポデを着けさせ、また、イスラエルの人々の火祭をことごとくあなたの先祖の家に与えた。
Ndipo ndinamusankha pakati pa mafuko a Israeli kuti akhale wansembe wanga ndi kuti azipita pa guwa langa la nsembe, kufukiza Lubani ndi kuvala efodi pamaso panga. Ndinapatsa banja la abambo ako gawo la nsembe zonse zopsereza zimene Aisraeli amapereka.
29 それにどうしてあなたがたは、わたしが命じた犠牲と供え物をむさぼりの目をもって見るのか。またなにゆえ、わたしよりも自分の子らを尊び、わたしの民イスラエルのささげるもろもろの供え物の、最も良き部分をもって自分を肥やすのか』。
Nʼchifukwa chiyani ukunyoza nsembe ndi zopereka zanga zimene ndinalamula? Nʼchifukwa chiyani ukupereka ulemu kwa ana ako kuposa Ine podzinenepetsa nokha ndi zopereka zabwino kwambiri za nsembe zimene Aisraeli amapereka?’”
30 それゆえイスラエルの神、主は仰せられる、『わたしはかつて、「あなたの家とあなたの父の家とは、永久にわたしの前に歩むであろう」と言った』。しかし今、主は仰せられる、『決してそうはしない。わたしを尊ぶ者を、わたしは尊び、わたしを卑しめる者は、軽んぜられるであろう。
“Paja Ine Yehova Mulungu wa Israeli ‘Ndinalonjeza kuti anthu a pa banja lako ndi a pa banja la abambo ako azidzanditumikira nthawi zonse.’ Koma tsopano ndikuti, ‘Zonsezi zithe!’ Tsopano anthu amene amandilemekeza Inenso ndidzawalemekeza koma iwo amene amandinyoza Ine ndidzawanyoza.
31 見よ、日が来るであろう。その日、わたしはあなたの力と、あなたの父の家の力を断ち、あなたの家に年老いた者をなくするであろう。
Nthawi ikubwera imene ndidzachotsa anyamata ako ndi anyamata a pa banja la abambo ako, kotero kuti sipadzakhala munthu wokalamba pa banja lako.
32 そのとき、あなたは災のうちにあって、イスラエルに与えられるもろもろの繁栄を、ねたみ見るであろう。あなたの家には永久に年老いた者がいなくなるであろう。
Pa mavuto ako udzayangʼana ndi maso ansanje zabwino zimene ndidzachitira Aisraeli ena. Mʼbanja lako simudzapezeka munthu wokalamba.
33 しかしあなたの一族のひとりを、わたしの祭壇から断たないであろう。彼は残されてその目を泣きはらし、心を痛めるであろう。またあなたの家に生れ出るものは、みなつるぎに死ぬであろう。
Komabe pa banja lako mmodzi yekha ndidzamuleka wosamuchotsa kuti azidzanditumikira. Iyeyu azidzakuliritsa ndi kukumvetsa chisoni. Koma ena onse pa banja lako adzafa akanali aangʼono.”
34 あなたのふたりの子ホフニとピネハスの身に起ることが、あなたのためにそのしるしとなるであろう。すなわちそのふたりは共に同じ日に死ぬであろう。
“‘Ndipo chimene chidzachitike kwa ana ako awiriwa, Hofini ndi Finehasi, chidzakhala chizindikiro kwa iwe. Onse awiri adzafa pa tsiku limodzi.
35 わたしは自分のために、ひとりの忠実な祭司を起す。その人はわたしの心と思いとに従って行うであろう。わたしはその家を確立しよう。その人はわたしが油そそいだ者の前につねに歩むであろう。
Pambuyo pake ndidzasankha wansembe wokhulupirika, amene adzachita zimene zili mu mtima ndi mʼmaganizo mwanga. Ndidzakhazikitsa banja lako kolimba ndipo adzatumikira pamaso pa wodzozedwa wanga nthawi zonse.
36 そしてあなたの家で生き残っている人々はみなきて、彼に一枚の銀と一個のパンを請い求め、「どうぞ、わたしを祭司の職の一つに任じ、一口のパンでも食べることができるようにしてください」と言うであろう』」。
Ndipo aliyense wotsala wa banja lako adzabwera ndi kugwada pamaso pake kupempha ndalama kapena chakudya.’ Adzati, ‘Chonde ndiloleni kuti ndizithandizako pa ntchito iliyonse ya unsembe kuti ndipeze chakudya.’”

< サムエル記Ⅰ 2 >