< イザヤ書 9 >

1 今くるしみを受れども後には闇なかるべし 昔しはゼブルンの地ナフタリの地をあなどられしめ給ひしかど 後には海にそひたる地ヨルダンの外の地 ことくに人のガリラヤに榮をうけしめ給へり
Anthu amene anali ndi nkhawa, sadzakhalanso otaya mtima. Masiku amakedzana Mulungu ananyozetsa dziko la Zebuloni ndi dziko la Nafutali, koma kutsogolo kuno dera lonse la Galileya, limene lili dziko la anthu a mitundu ina, kuyambira ku nyanja yayikulu, mʼmbali mwa Yorodani, adzalisandutsa laulemu.
2 幽暗をあゆめる民は大なる光をみ 死蔭の地にすめる者のうへに光てらせり
Anthu oyenda mu mdima awona kuwala kwakukulu; kwa iwo okhala mʼdziko la mdima wandiweyani kuwunika kwawafikira.
3 なんぢ民をましその歡喜を大にしたまひければ かれらは收穫時によろこぶがごとく掠物をわかつときに樂むがごとく汝の前によろこべり
Inu mwauchulukitsa mtundu wanu ndipo mwawonjezera chimwemwe chawo. Iwo akukondwa pamaso panu, ngati mmene anthu amakondwera nthawi yokolola, ngatinso mmene anthu amakondwera pamene akugawana zolanda ku nkhondo.
4 そは汝かれらがおへる軛とその肩の笞と虐ぐるものの杖とを折り これを折りてミデアンの日のごとくなし給ひたればなり
Monga munachitira pogonjetsa Amidiyani, inu mwathyola goli limene limawalemera, ndodo zimene amamenyera mapewa awo, ndiponso mikwapulo ya anthu owazunza.
5 すべて亂れたたかふ兵士のよろひと血にまみれたる衣とはみな火のもえくさとなりて焚るべし
Nsapato iliyonse ya munthu wankhondo, ndiponso chovala chilichonse chodonthekera magazi zidzatenthedwa pa moto ngati nkhuni.
6 ひとりの嬰兒われらのために生れたり 我儕はひとりの子をあたへられたり 政事はその肩にあり その名は奇妙また議士 また大能の神とこしへのちち 平和の君ととなへられん
Chifukwa mwana watibadwira, mwana wamwamuna wapatsidwa kwa ife, ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake. Ndipo adzamutcha dzina lake lakuti Phungu Wodabwitsa, Mulungu Wamphamvu, Atate Amuyaya, ndi Mfumu ya Mtendere.
7 その政事と平和とはましくははりて窮りなし 且ダビデの位にすわりてその國ををさめ今よりのちとこしへに公平と正義とをもてこれを立これを保ちたまはん 萬軍のヱホバの熱心これを成たまふべし
Ulamuliro ndi mtendere wake zidzakhala zopanda malire. Iye adzalamulira ufumu wake ali pa mpando waufumu wa Davide, ndipo adzawukhazikitsa ndi kuwuchirikiza mwa chiweruzo cholungama ndi pochita zachilungamo kuyambira nthawi imeneyo mpaka muyaya. Ndi mtima wake wonse, Yehova Wamphamvuzonse watsimikiza kuchita zimenezi.
8 主一言をヤコブにおくり之をイスラエルの上にのぞませ給へり
Ambuye atumiza mawu otsutsa Yakobo; ndipo mawuwo agwera pa Israeli.
9 すべてのこの民エフライムとサマリヤに居るものとは知ならん かれらは高ぶり誇る心をもていふ
Anthu onse okhala mu Efereimu ndi okhala mu Samariya, adzadziwa zimenezi. Iwo amayankhula modzikuza kuti,
10 瓦くづるるともわれら斫石をもて建 くはの木きらるるともわれら香柏をもて之にかへんと
“Ngakhale njerwa zagumuka, koma ife tidzamanga ndi miyala yosema. Mitanda ya mkuyu yagwetsedwa, koma ife tidzayika mitanda ya mkungudza mʼmalo mwake.”
11 この故にヱホバ、レヂンの敵をあげもちゐてイスラエルを攻しめ その仇をたけび勇しめたまはん
Koma Yehova wadzutsa adani kuti alimbane nawo ndipo wawafulumiza adani awo kuti amenyane nawo.
12 前にアラム人あり後にペシリテ人あり 口をはりてイスラエルを呑んとす 然はあれどヱホバの怒やまずして尚その手をのばしたまふ
Asiriya ochokera kummawa ndi Afilisti ochokera kumadzulo ndipo ayasama pakamwa kuti adye a Israeli. Komabe, mkwiyo wake sunawachokere, mkono wake uli chitambasulire.
13 然どこの民はおのれをうつものに歸らず萬軍のヱホバを求めず
Koma anthu sanabwerere kwa amene anawakantha uja, ngakhale kufunafuna Yehova Wamphamvuzonse.
14 斯るゆゑにヱホバ一日のうちに首と尾と椶櫚のえだと葦とをイスラエルより斷切たまはん
Choncho Yehova adzadula mutu wa Israeli pamodzi ndi mchira womwe, nthambi ya kanjedza ndi bango lomwe tsiku limodzi;
15 その首とは老たるもの尊きもの その尾とは謊言をのぶる預言者をいふなり
mutuwo ndiye akuluakulu ndi olemekezeka, mchira ndiye aneneri ophunzitsa zabodza.
16 この民をみちびく者はこれを迷はせその引導をうくる者はほろぶるなり
Amene amatsogolera anthuwa ndiwo amawasocheretsa, ndipo otsogoleredwa amatayika.
17 このゆゑに主はその少壯者をよろこびたまはず その孤兒と寡婦とを憐みたまはざるべし 是その民はことごとく邪まなり惡をおこなふ者なり おのおのの口は愚かなる言をかたればなり 然はあれどヱホバの怒やまずして尚その手をのばしたまふ
Nʼchifukwa chake Ambuye adzakondwera nawo achinyamata, ngakhale kuwachitira chifundo ana amasiye ndi akazi amasiye, pakuti aliyense ndi wosapembedza Mulungu ndiponso ndi wochimwa ndipo aliyense amayankhula zopusa. Komabe, mkwiyo wake sunawachokere, mkono wake uli chitambasulire.
18 惡は火のごとくもえ棘と荊とを食つくし茂りあふ林をやくべければみな煙となりむらがりて上騰らん
Ndithu kuyipa kwa anthuwo kumayaka ngati moto; moto wake umanyeketsa mkandankhuku ndi minga, umayatsa nkhalango yowirira, ndipo utsi wake umachita kuti toloo ngati mtambo.
19 萬軍のヱホバの怒によりて地はくろく燒 その民は火のもえくさとなり人々たがひに相憐むことなし
Dziko lidzatenthedwa ndi ukali wa Yehova Wamphamvuzonse, dziko lidzatenthedwa ndipo anthu adzakhala ngati nkhuni zosonkhera moto; palibe munthu amene adzachitire chifundo mʼbale wake.
20 人みぎに攫めどもなほ饑 ひだりに食へども尚あかず おのおのその腕の肉をくらふべし
Kudzanja lamanja adzapeza chakudya nʼkudya, koma adzakhalabe ndi njala; kudzanja lamanzere adzapeza chakudya nʼkudya, koma sadzakhuta. Aliyense azidzadya ana ake omwe.
21 マナセはエフライムを エフライムはマナセをくらひ 又かれら相合てユダを攻めん 然はあれどヱホバの怒やまずして尚その手をのばしたまふ
Manase adzadya Efereimu ndipo Efereimu adzadya Manase; onsewa pamodzi adzadya Yuda. Komabe pa zonsezi, mkwiyo wake sunawachokere, mkono wake uli chitambasulire.

< イザヤ書 9 >