< ハガイ書 2 >

1 七月其月の二十一日ヱホバの言預言者ハガイによりて臨めり曰く
Pa tsiku la 21 la mwezi wachisanu ndi chiwiri, Yehova anayankhula kudzera mwa mneneri Hagai kuti:
2 シヤルテルの子ユダの方伯ゼルバベルとヨザダクの子祭司の長ヨシユアおよびその殘れる一切の民に告よ
“Yankhula kwa Zerubabeli mwana wa Sealatieli, bwanamkubwa wa Yuda, kwa Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndi kwa anthu onse otsala. Afunse kuti,
3 なんぢら遺れる者の中この殿の從前の榮光を見しものは誰ぞや 今これを如何に見るや かの殿にくらぶれば是は汝らの目に何もなきが如く見ゆるにあらずや
‘Kodi alipo amene watsala pakati panu amene anaona ulemerero wakale wa Nyumba iyi? Nanga tsopano ikuoneka motani kwa inu? Kodi sikuoneka ngati yopanda pake kwa inu?
4 ヱホバ曰たまふゼルバベルよ自ら強くせよ ヨザダクの子祭司の長ヨシユアよ自ら強くせよ ヱホバ言たまふ この地の民よ自らつよくしてはたらけ 我なんぢらとともに在り 萬軍のヱホバこれを言ふ
Iwe Zerubabeli, limba mtima tsopano,’ akutero Yehova. ‘Limba mtima, iwe Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe. Limbani mtima, anthu nonse a mʼdziko,’ akutero Yehova, ‘ndipo gwirani ntchito. Pakuti ine ndili nanu,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse.
5 汝らがエジプトよりいでし時わがなんぢらに約せし言およびわが靈なほなんぢらの中に留れり 懼るるなかれ
‘Izi ndi zimene ndinapangana nanu pamene munkatuluka ku Igupto. Ndipo Mzimu wanga uli pakati panu. Musachite mantha.’
6 萬軍のヱホバかくいひたまふ いま一度しばらくありてわれ天と地と海と陸とを震動はん
“Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Pakapita nthawi pangʼono ndidzagwedezanso thambo ndi dziko lapansi, nyanja ndi mtunda.
7 又われ萬國を震動はん また萬國の願ふところのもの來らん 又われ榮光をもてこの殿に充滿さん 萬軍のヱホバこれを言ふ
Ndidzagwedeza mitundu yonse ya anthu, ndipo chimene mitundu yonse ya anthu imachifuna chidzabwera, ndipo ndidzaza Nyumba ino ndi ulemerero,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse.
8 銀も我ものなり 金もわが物なりと萬軍のヱホバいひたまふ
‘Siliva yense ndi wanga, golide yense ndi wanganso,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse.
9 この殿の後の榮光は從前の榮光より大ならんと萬軍のヱホバいひたまふ この處においてわれ平康をあたへんと萬軍のヱホバいひたまふ
‘Ulemerero wa nyumba iyi udzaposa ulemerero wa nyumba yoyamba ija,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse. ‘Ndipo pamalo pano ndidzakhazikitsapo mtendere,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse.”
10 ダリヨスの二年九月二十四日ヱホバのことば預言者ハガイによりて臨めり曰く
Chaka chachiwiri cha Dariyo, pa tsiku la 24 la mwezi wachisanu ndi chinayi, Yehova anayankhula ndi mneneri Hagai kuti:
11 萬軍のヱホバかく曰たまふ 律法につきて祭司に問ふて曰ふべし
“Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Funsa ansembe za zimene lamulo likunena:
12 人衣の裾にて聖肉を携へたらんにその裾もしパン或は羮あるひは酒あるひは油あるひは他の食物に捫らばそれらは聖ものとなるや 祭司たち答へて曰けるはしからず
Ngati munthu wakulunga nyama yopatulika mu mkanjo wake, ndipo mkanjowo nʼkukhudza buledi kapena msuzi, kapena vinyo, mafuta kapena chakudya cha mtundu wina uliwonse, kodi zimenezo zimasanduka zopatulika?’” Ansembe anayankha kuti, “Ayi.”
13 ハガイまたいひけるは屍體に捫りて汚れしもの若これらの物にさはらば其ものはけがるべきや 祭司等こたへて曰けるは汚れん
Pamenepo Hagai anati, “Ngati munthu amene anayipitsidwa pokhudza mtembo akhudza chimodzi cha zinthu zimenezi, kodi chinthucho chimayipitsidwa?” Ansembe anayankha kuti, “Inde, chimayipitsidwa.”
14 ここに於てハガイ答へて曰けるはヱホバ曰たまふ 我前此民もかくの如くまた此國もかくの如し 又其手の一切のわざもかくのごとく彼等がその處に獻ぐるものもけがれたるものなり
Pamenepo Hagai anati, “‘Ndi mmene zilili ndi anthu awa ndi dziko ili pamaso panga,’ akutero Yehova. ‘Chilichonse amachita ndiponso chilichonse chimene amapereka nʼchodetsedwa.
15 また今われ汝らに乞 この日より以前すなはちヱホバの殿にて石の上に石の置れざりし時を憶念べし
“‘Tsopano muganizire zimenezi kuyambira lero mpaka mʼtsogolo. Ganizirani momwe zinthu zinalili asanayambe kumanga nyumba ya Yehova.
16 かの時には二十舛もあるべき麥束につきてわづかに十を得 また酒榨につきて五十桶汲んとせしにただ二十を得たるのみ
Pamene munthu ankayembekezera miyeso ya tirigu makumi awiri ankangopeza khumi yokha. Munthu akapita kuti akatunge miyeso makumi asanu ya vinyo mu mtsuko, ankangopeza miyeso makumi awiri yokha.
17 汝が手をもて爲せる一切の事に於てわれ不實穗と朽腐穗と雹を以てなんぢらを撃り されど汝ら我にかへらざりき ヱホバこれを言ふ
Ndinawononga ntchito yonse ya manja anu ndi chinsikwi, chiwawu ndi matalala, komabe inu simunatembenukire kwa Ine,’ akutero Yehova
18 なんぢらこの日より以前を憶念みよ 即ち九月二十四日よりヱホバの殿の基を置し日までをおもひ見よ
‘Kuyambira lero tsiku la 24 la mwezi wachisanu ndi chinayi mpaka mʼtsogolo, chonde ganizirani bwino tsiku limene munayika maziko a nyumba ya Yehova. Ganizirani bwino.
19 種子なほ倉にあるや 葡萄の樹 無花果の樹 石榴の樹 橄欖の樹もいまだ實を結ばざりき 此日よりのちわれ汝らを惠まん
Kodi mʼnkhokwe mwatsala mbewu? Mpaka lero, mpesa ndi mtengo wa mkuyu, makangadza ndi mtengo wa olivi sizinabereke zipatso. “‘Kuyambira lero mpaka mʼtsogolo ndidzakudalitsani.’”
20 此月の二十四日にヱホバのことば再びハガイに臨めり曰く
Yehova anayankhula ndi Hagai kachiwiri, pa tsiku la 24 la mwezi kuti:
21 ユダの方伯ゼルバベルに告よ われ天地を震動ん
“Uza Zerubabeli, bwanamkubwa wa Yuda, kuti ndidzagwedeza thambo ndi dziko lapansi.
22 列國の位を倒さん また異邦の諸國の權勢を滅さん 又車および之に駕る者を倒さん 馬および之に騎る者もおのおの其伴侶の劍によりてたふれん
Ndidzagwetsa mipando yaufumu ndi kuwononga mphamvu za maufumu achilendo. Ndidzagubuduza magaleta ndi okwerapo ake; akavalo ndi okwerapo ake adzagwa, aliyense adzaphedwa ndi lupanga la mʼbale wake.
23 萬軍のヱホバ曰たまはくシヤルテルの子わが僕ゼルバベルよヱホバいふその日に我なんぢを取りなんぢを印の如くにせん そはわれ汝をえらびたればなり 萬軍のヱホバこれを言ふ
“‘Tsiku limenelo,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse, ‘ndidzakutenga, iwe mtumiki wanga Zerubabeli mwana wa Sealatieli,’ akutero Yehova, ‘ndipo ndidzakusandutsa kukhala mphete yanga yolamulira, pakuti ndasankha iwe,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse.”

< ハガイ書 2 >