< エゼキエル書 34 >

1 ヱホバの言われに臨みて言ふ
Yehova anandiyankhula kuti:
2 人の子よ汝イスラエルの牧者の事を預言せよ預言して彼ら牧者に言ふべし主ヱホバかく言ふ己を牧ふところのイスラエルの牧者は禍なるかな牧者は群を牧ふべき者ならずや
“Iwe mwana wa munthu, yankhula mawu oyimba mlandu abusa a Israeli. Lengeza ndipo uwawuze kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti, ‘Tsoka kwa abusa a Israeli amene mumangodzisamala nokha! Kodi abusa sayenera kusamalira nkhosa?
3 汝らは脂を食ひ毛を纏ひ肥たる物を屠りその群をば牧はざるなり
Mumadya chambiko, mumadziveka zovala zaubweya, ndi kupha nyama zonenepa, koma simusamalira nkhosazo.
4 汝ら其弱き者を強くせずその病る者を醫さずその傷ける者を裹まず散されたる者をひきかへらず失たる者を尋ねず手荒に嚴刻く之を治む
Simunalimbitse nkhosa zofowoka, kapena kuchiritsa zodwala, kapena kumanga mabala a nkhosa zopweteka. Simunabweze zosochera kapena kufunafuna zotayika. Munaziweta mozunza ndi mwankhanza.
5 是は牧者なきに因て散り失せ野の諸の獸の餌となりて散失するなり
Kotero zinabalalika chifukwa zinalibe mʼbusa, ndipo pamene zinabalalika zinakhala chakudya cha zirombo zonse zakuthengo.
6 我羊は諸の山々に諸の高丘に迷ふ我羊全地の表に散りをれど之を索す者なく尋ぬる者なし
Nkhosa zanga zinayendayenda mʼmapiri onse ndi mʼzitunda zonse zazitali. Zinabalalika pa dziko lonse lapansi, ndipo palibe amene anazilondola kapena kuzifunafuna.
7 是故に牧者よ汝らヱホバの言を聽け
“‘Choncho Inu abusa, tamvani zimene Ine Yehova ndikukuwuzani.
8 主ヱホバ言たまふ我は活く我羊掠められわが羊野の諸の獸の餌となる又牧者あらず我牧者わが羊を尋ねず牧者己を牧ふてわが羊を牧はず
Pali Ine wamoyo, akutero Ambuye Wamphamvuzonse, ndithu, nkhosa zanga zinajiwa ndi zirombo zakuthengo, zinasanduka chakudya cha zirombo chifukwa panalibe abusa. Abusa anga sanafunefune nkhosa zanga. Iwo ankangosamala za iwo okha mʼmalo mosamala nkhosa zanga.
9 是故に牧者よ汝らヱホバの言を聞け
Chifukwa chake, inu abusa, tamvani zimene Ine Yehova ndikukuwuzani.
10 主ヱホバ斯言たまふ視よ我牧者等を罰し吾羊を彼らの手に討問め彼等をしてわが群を牧ふことを止しめて再び己を牧ふことなからしめ又わが羊をかれらの口より救とりてかれらの食とならざらしむべし
Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ine ndayipidwa nanu, inu abusa. Ndidzakulandani nkhosa zanga ndipo simudzazidyetsanso. Ndidzakuchotsani pa ntchito ya ubusa kuti musamangodzidyetsa nokha. Ndidzalanditsa nkhosa zanga kukamwa kwanu ndipo simudzazidyanso.
11 主ヱホバかく言たまふ我みづからわが群を索して之を守らん
“‘Tsono Ine Ambuye Yehova ndikuti, mwini wakene ndidzazifunafuna nkhosa zanga ndi kuzisamalira.
12 牧者がその散たる羊の中にある日にその群を守るごとく我わが群を守り之がその雲深き暗き日に散たる諸の處よりこれを救ひとるべし
Monga mʼbusa amanka nafunafuna nkhosa zake pamene zina zabalalikira kutali, moteronso Ine ndidzafunafuna nkhosa zanga. Ndidzazipulumutsa kuchoka kumalo onse kumene zinabalalikira pa nthawi yankhungu ndi mdima.
13 我かれらを諸の民の中より導き出し諸の國より集めてその國に携へいりイスラエルの山の上と谷の中および國の凡の住居處にて彼らを養はん
Ndidzazitulutsa pakati pa mitundu ya anthu ndi kuzisonkhanitsa kuchokera ku mayiko ena, ndipo ndidzazibwezera ku dziko lawo. Ndidzaziwetera ku mapiri a Israeli, mʼmbali mwa mitsinje ndi kumalo kumene kumakhala anthu.
14 善き牧場にて我かれらを牧はんその休息處はイスラエルの高山にあるべし彼處にて彼らは善き休息所に臥しイスラエルの山々の上にて肥たる牧場に草を食はん
Ndidzaziwetera kumalo a msipu wabwino. Mapiri okwera a Israeli adzakhala malo azidyetserako. Kumeneko zidzapumula ku abusa abwino a msipu ndipo zizidzadyadi msipu wonenepetsa pa mapiri a Israeli.
15 主ヱホバいひたまふ我みづから我群を牧ひ之を偃しむべし
Ine mwini wake ndidzaziweta nkhosa zanga ndi kuzilola kuti zipumule. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.
16 亡たる者は我これを尋ね逐はなたれたる者はこれを引返り傷けられたる者はこれを裹み病る者はこれを強くせん然ど肥たる者と強き者は我これを滅さん我公道をもて之を牧ふべし
Ndidzafunafuna zotayika ndi kubweza zosochera. Ndidzamanga mabala a zopweteka ndi kulimbikitsa zofowoka. Koma zonenepa ndi zamphamvu ndidzaziwononga. Ndidzaweta nkhosazo mwachilungamo.
17 主ヱホバかく言たまふ汝等わが群よ我羊と羊の間および牡羊と牡山羊の間の審判をなさん
“‘Kunena za inu, nkhosa zanga, Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndidzaweruza pakati pa nkhosa ndi nkhosa, pakati pa nkhosa zazimuna ndi mbuzi zazimuna.
18 汝等は善き牧場に草食ひ足をもてその殘れる草を蹈あらし又淸たる水を飮み足をもてその殘餘を濁す是汝等にとりて小き事ならんや
Kodi sikukukwanirani kudya msipu wabwino kuti muzichita kuponderezanso msipu umene simunadyewo? Kodi simukhutira ndi kumwa madzi abwino kuti muzinka mudetsanso madzi otsalawo ndi mapazi anu?
19 わが群汝等が足にて蹈あらしたる者を食ひ汝等が足にて濁したる者を飮べけんや
Kodi nkhosa zanga zidye zimene mwazipondaponda ndi kumwa madzi amene mwawadetsa ndi mapazi anu?
20 是をもて主ヱホバ斯かれらに言たまふ視よ我肥たる羊と痩たる羊の間を審判くべし
“‘Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Taonani, Ine mwini wake ndidzaweruza pakati pa nkhosa zonenepa ndi nkhosa zowonda.
21 汝等は脅と肩とをもて擠し角をもて弱き者を盡く衝て遂に之を外に逐散せり
Popeza zofowoka mumaziwomba ndi kuzikankhira kumbali, ndipo mumazigunda ndi nyanga zanu nʼkuzimwazira kutali,
22 是によりて我わが群を助けて再び掠められざらしめ又羊と羊の間をさばくべし
tsono Ine ndidzapulumutsa nkhosa zanga, ndipo sindidzalolanso kuti zijiwe. Ndidzaweruza pakati pa nkhosa ina ndi nkhosa inanso.
23 我かれらの上に一人の牧者をたてん其人かれらを牧ふべし是わが僕ダビデなり彼はかれらを牧ひ彼らの牧者となるべし
Ndidzaziyikira mʼbusa mmodzi, mtumiki wanga Davide. Iyeyo ndiye azidzazisamala. Adzakhala mʼbusa wawo.
24 我ヱホバかれらの神とならん吾僕ダビデかれらの中に君たるべし我ヱホバこれを言ふ
Ine Yehova ndidzakhala Mulungu wake ndipo mtumiki wanga Davide adzakhala mfumu pakati pa nkhosazo. Ine Yehova ndayankhula.
25 我かれらと平和の契約を結び國の中より惡き獸を滅し絕つべし彼らすなはち安かに野に住み森に眠らん
“‘Ndidzapangana nazo pangano la mtendere. Ndidzachotsa mʼdzikomo zirombo zolusa. Choncho nkhosa zanga zidzakhala mu mtendere mu chipululu ngakhalenso mʼthengo.
26 我彼らおよび吾山の周圍の處々に福祉を下し時に隨ひて雨を降しめん是すなはち福祉の雨なるべし
Ndidzakhazika anthu anga pafupi ndi phiri langa loyera ndipo ndidzawadalitsa. Ndidzawagwetsera mvula pa nthawi yake ndipo idzakhala mvula ya madalitso.
27 野の樹はその實を結び地はその產物を出さん彼等は安然にその國にあるべし我がかれらの軛を碎き彼らをその僕となせる人の手より救ひいだす時に彼等は我のヱホバなるを知べし
Mitengo ya mʼminda idzabereka zipatso zake, ndipo nthaka idzakhala ndi zokolola zake. Anthu adzakhala mwamtendere mʼdziko lawo. Iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pamene ndidzathyola magoli awo ndi kuwapulumutsa kuchoka mʼmanja mwa amene anawagwira ukapolo.
28 彼等は重ねて國々の民に掠めらるる事なく野の獸かれらを食ふことなかるべし彼等は安然に住はん彼等を懼れしむる者なかるべし
Anthu amitundu ina sadzawafunkhanso ndipo sadzadyedwa ndi zirombo zakuthengo. Adzakhala mwamtendere ndipo palibe amene adzawaopseze.
29 我かれらのために一の栽植處を起してその名を聞えしめん彼等は重ねて國の饑饉に滅ぶることなく再び外邦人の凌辱を蒙ることなかるべし
Ndidzawapatsa zokolola zochuluka motero kuti sadzavutikanso ndi njala. Anthu a mitundu ina sadzawanyozanso.
30 彼らはその神なる我ヱホバが己と共にあるを知り自己イスラエルの家はわが民なることを知るべし主ヱホバこれを言ふ
Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine Yehova Mulungu wawo ndili nawo pamodzi, ndipo kuti iwo, Aisraeli, ndi anthu anga. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.
31 汝等はわが羊わが牧場の群なり汝等は人なり我は汝らの神なりと主ヱホバ言たまふ
Inu ndinu nkhosa zanga, nkhosa zimene ndimazidyetsa. Ine ndine Mulungu wanu. Ndikutero Ine Ambuye Wamphamvuzonse.’”

< エゼキエル書 34 >