< הָרִאשׁוֹנָה לְיוֹחָנָן 4 >

אהובי אל תאמינו לכל רוח כי אם בחנו הרוחות אם מאלהים המה כי נביאי שקר רבים יצאו לעולם׃ 1
Anzanga okondedwa, musakhulupirire mzimu uliwonse, koma yesani mizimu ngati ikuchokera kwa Mulungu, chifukwa aneneri onama ambiri afalikira mʼdziko lapansi.
בזאת תכירו את רוח אלהים כל רוח המודה בישוע המשיח כי בא בבשר מאלהים הוא׃ 2
Mungathe kuzindikira Mzimu wa Mulungu motere: Mzimu uliwonse umene umavomereza kuti Yesu Khristu anabwera mʼthupi, ndi wochokera kwa Mulungu,
וכל רוח אשר איננו מודה בישוע האדון כי בא בבשר לא מאלהים הוא וזה הוא רוח צר המשיח אשר שמעתם עליו כי בוא יבא ועתה הנה הוא בעולם׃ 3
koma mzimu uliwonse umene suvomereza Yesu, siwochokera kwa Mulungu. Uwu ndi mzimu wa wokana Khristu umene munawumva kuti ukubwera ndipo ngakhale tsopano wabwera kale mʼdziko lapansi.
אתם הבנים הנכם מאלהים ונצחתם אתם כי אשר בכם גדול הוא מאשר בעולם׃ 4
Inu ana okondedwa, ndinu ochokera kwa Mulungu ndipo mwawagonjetsa aneneri onyengawa, chifukwa Iye amene ali mwa inu ndi wamkulu kuposa amene ali mʼdziko lapansi.
המה מן העולם על כן מהעולם ידברו והעולם ישמע אליהם׃ 5
Aneneri onyengawa ndi ochokera mʼdziko lapansi, nʼchifukwa chake amayankhula za dziko lapansi, ndipo dziko lapansi limawamvera.
ואנחנו מאלהים הננו היודע את האלהים ישמע אלינו ואשר איננו מאלהים לא ישמע אלינו בזאת נכיר את רוח האמת ואת רוח התועה׃ 6
Ife ndi ochokera kwa Mulungu, ndipo aliyense amene amadziwa Mulungu amamvera zimene timayankhula. Koma aliyense amene sachokera kwa Mulungu samvera zimene timayankhula. Mmenemu ndiye mmene timasiyanitsira pakati pa mzimu wachoonadi ndi Mzimu wachinyengo.
אהובי נאהב נא איש את רעהו כי האהבה מאלהים היא וכל אשר יאהב נולד מאלהים וידע את האלהים׃ 7
Anzanga okondedwa, tiyeni tikondane wina ndi mnzake, pakuti chikondi chimachokera kwa Mulungu. Aliyense amene ali ndi chikondi ndi mwana wa Mulungu ndipo amadziwa Mulungu.
ואשר איננו אהב לא ידע את האלהים כי האלהים הוא אהבה׃ 8
Aliyense amene alibe chikondi sadziwa Mulungu, chifukwa Mulungu ndiye chikondi.
בזאת נראתה אהבת האלהים לנו כי שלח האלהים את בנו את יחידו לעולם למען נחיה על ידו׃ 9
Mmene Mulungu anaonetsera chikondi chake pakati pathu ndi umu: Iye anatumiza Mwana wake mmodzi yekha ku dziko lapansi kuti mwa Iyeyo tikhale ndi moyo.
בזאת היא האהבה לא שאנחנו אהבנו את האלהים כי אם הוא אהב אותנו וישלח את בנו לכפרה על חטאתינו׃ 10
Chikondi ndi ichi: osati kuti ife ndife amene tinamukonda Mulungu, koma kuti Iyeyo ndiye amene anatikonda ndipo anatumiza Mwana wake kuti akhale nsembe yopepesera machimo athu.
אהובי אם ככה אהב אתנו האלהים גם אנחנו חיבים לאהבה איש את רעהו׃ 11
Anzanga okondedwa, popeza Mulungu anatikonda chotere, ifenso tiyenera kukondana wina ndi mnzake.
את האלהים לא ראה איש מעולם ואם נאהב איש את רעהו האלהים יעמד בקרבנו ואהבתו נשלמה בנו׃ 12
Palibe amene anaonapo Mulungu, koma tikakondana wina ndi mnzake, ndiye kuti Mulungu amakhala mwa ife ndipo chikondi chake chafika pachimake penipeni mwa ife.
בזאת נדע אשר בו נקום והוא בנו כי נתן לנו מרוחו׃ 13
Ife tikudziwa kuti timakhala mwa Iye ndipo Iyeyo amakhala mwa ife chifukwa anatipatsa Mzimu wake.
ואנחנו חזינו ונעידה כי האב שלח את הבן מושיע העולם׃ 14
Ndipo taona ndipo tikuchitira umboni, kuti Atate anatuma Mwana wake kuti akhale Mpulumutsi wa dziko lapansi.
כל המודה כי ישוע הוא בן האלהים האלהים שכן בו והוא באלהים׃ 15
Ngati aliyense avomereza kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu, Mulungu amakhala mwa iye ndipo iyeyo amakhala mwa Mulungu.
ואנחנו ידענו ונאמן באהבה אשר אלהים אהב אתנו האלהים הוא אהבה והעמד באהבה עמד באלהים והאלהים עמד בו׃ 16
Tikudziwa ndipo timadalira chikondi chimene Mulungu ali nacho pa ife. Mulungu ndiye chikondi. Aliyense amene amakhala moyo wachikondi, ali mwa Mulungu ndipo Mulungu amakhala mwa iye.
ובזאת נשלמה בנו האהבה בהיות לנו בטחון ביום הדין כי כמהו כן גם אנחנו בעולם הזה׃ 17
Chikondi chafika pachimake penipeni pakati pathu, kotero kuti pa tsiku lachiweruzo tidzakhala olimba mtima chifukwa mʼdziko lapansi moyo wathu uli ngati wa Khristu.
אין אימה באהבה כי אם האהבה השלמה תגרש את האימה כי באימה מעצבה ואשר באימה איננו שלם באהבה׃ 18
Mulibe mantha mʼchikondi. Koma chikondi ndi changwiro chimachotsa mantha, chifukwa mantha amabwera chifukwa choopa chilango. Munthu amene ali ndi mantha, chikondi chake sichangwiro.
אנחנו אהבים אתו כי הוא קדם לאהבה אתנו׃ 19
Ife timakonda Mulungu chifukwa ndiye anayamba kutikonda.
כי יאמר איש אהב אני את האלהים והוא שנא את אחיו כזב הוא כי אשר לא יאהב את אחיו אשר הוא ראה איככה יוכל לאהב את האלהים אשר איננו ראה אתו׃ 20
Ngati wina anena kuti, “Ine ndimakonda Mulungu,” koma namadana ndi mʼbale wake ndi wabodza ameneyo. Pakuti aliyense amene sakonda mʼbale wake, amene akumuona, sangathenso kukonda Mulungu amene sanamuone.
וזאת המצוה יש לנו מאתו כי האהב את האלהים יאהב גם את אחיו׃ 21
Ndipo Iye anatipatsa lamulo lakuti: Aliyense amene amakonda Mulungu ayenera kukondanso mʼbale wake.

< הָרִאשׁוֹנָה לְיוֹחָנָן 4 >