< תהילים 90 >

תפלה למשה איש-האלהים אדני--מעון אתה היית לנו בדר ודר 1
Pemphero la Mose munthu wa Mulungu. Ambuye, mwakhala muli malo athu okhalamo pa mibado yonse.
בטרם הרים ילדו-- ותחולל ארץ ותבל ומעולם עד-עולם אתה אל 2
Mapiri asanabadwe, musanalenge nʼkomwe dziko lapansi ndi dziko lonse, kuyambira muyaya mpaka muyaya Inu ndinu Mulungu.
תשב אנוש עד-דכא ותאמר שובו בני-אדם 3
Inu mumabwezera anthu ku fumbi, mumati, “Bwerera ku fumbi iwe mwana wa munthu.”
כי אלף שנים בעיניך-- כיום אתמול כי יעבר ואשמורה בלילה 4
Pakuti zaka 1,000 pamaso panu zili ngati tsiku limene lapita kapena ngati kamphindi ka usiku.
זרמתם שנה יהיו בבקר כחציר יחלף 5
Inu mumasesa anthu mʼtulo ta imfa, iwo ali ngati udzu watsopano wa mmawa,
בבקר יציץ וחלף לערב ימולל ויבש 6
ngakhale kuti mmawa umaphuka watsopano, pofika madzulo wauma ndi kufota.
כי-כלינו באפך ובחמתך נבהלנו 7
Ife tathedwa ndi mkwiyo wanu; ndipo taopsezedwa ndi kuyipidwa kwanu.
שת (שתה) עונתינו לנגדך עלמנו למאור פניך 8
Mwayika mphulupulu zathu pamaso panu, machimo athu obisika poonekera pamaso panu.
כי כל-ימינו פנו בעברתך כלינו שנינו כמו-הגה 9
Masiku athu onse amatha ali pansi pa ukali wanu; timatsiriza zaka zathu ndi kubuwula.
ימי-שנותינו בהם שבעים שנה ואם בגבורת שמונים שנה-- ורהבם עמל ואון כי-גז חיש ונעפה 10
Kuchuluka kwa masiku athu ndi 70, kapena 80 ngati tili ndi mphamvu; komabe zaka zonsezi ndi za mavuto ndi nkhawa, zimatha mofulumira ndipo ife timawulukira kutali.
מי-יודע עז אפך וכיראתך עברתך 11
Kodi ndani amadziwa mphamvu ya mkwiyo wanu? Pakuti ukali wanu ndi waukulu ngati ulemu umene uyenera Inu.
למנות ימינו כן הודע ונבא לבב חכמה 12
Tiphunzitseni kuwerenga masiku athu molondola, kuti tikhale ndi mtima wanzeru.
שובה יהוה עד-מתי והנחם על-עבדיך 13
Lezani mtima Inu Yehova! Kodi mudzatikwiyira mpaka liti? Achitireni chifundo atumiki anu.
שבענו בבקר חסדך ונרננה ונשמחה בכל-ימינו 14
Mutikhutitse mmawa ndi chikondi chanu chosatha, kuti tiyimbe ndi chimwemwe ndi kukhala okondwa masiku athu onse.
שמחנו כימות עניתנו שנות ראינו רעה 15
Tisangalatseni masiku ambiri monga masiku amene mwatisautsa, kwa zaka zambiri monga momwe tinaonera mavuto.
יראה אל-עבדיך פעלך והדרך על-בניהם 16
Ntchito zanu zionetsedwe kwa atumiki anu, kukongola kwanu kwa ana awo.
ויהי נעם אדני אלהינו-- עלינו ומעשה ידינו כוננה עלינו ומעשה ידינו כוננהו 17
Kukoma mtima kwa Ambuye Mulungu wathu kukhale pa ife; tikhazikitsireni ntchito ya manja athu; inde, khazikitsani ntchito ya manja athu.

< תהילים 90 >