< תהילים 132 >

שיר המעלות זכור-יהוה לדוד-- את כל-ענותו 1
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Inu Yehova, kumbukirani Davide ndi mavuto onse anapirira.
אשר נשבע ליהוה נדר לאביר יעקב 2
Iye analumbira kwa Yehova ndi kulonjeza kwa Wamphamvu wa Yakobo kuti,
אם-אבא באהל ביתי אם-אעלה על-ערש יצועי 3
“Sindidzalowa mʼnyumba mwanga kapena kugona pa bedi langa:
אם אתן שנת לעיני לעפעפי תנומה 4
sindidzalola kuti maso anga agone, kapena zikope zanga ziwodzere,
עד-אמצא מקום ליהוה משכנות לאביר יעקב 5
mpaka nditamupezera malo Yehova, malo okhala a Wamphamvu wa Yakobo.”
הנה-שמענוה באפרתה מצאנוה בשדי-יער 6
Zoonadi, tinamva za Bokosi la Chipangano ku Efurata, tinalipeza mʼminda ya ku Yaara:
נבואה למשכנותיו נשתחוה להדם רגליו 7
“Tiyeni tipite ku malo ake okhalamo; tiyeni tikamulambire pa mapazi ake.
קומה יהוה למנוחתך אתה וארון עזך 8
‘Dzukani Yehova, ndipo bwerani ku malo anu opumulira, Inuyo ndi Bokosi la Chipangano limene limafanizira mphamvu zanu.
כהניך ילבשו-צדק וחסידיך ירננו 9
Ansembe anu avekedwe chilungamo; anthu anu oyera mtima ayimbe nyimbo mwachimwemwe.’”
בעבור דוד עבדך-- אל-תשב פני משיחך 10
Chifukwa cha Davide mtumiki wanu, musakane wodzozedwa wanu.
נשבע-יהוה לדוד אמת-- לא-ישוב ממנה מפרי בטנך-- אשית לכסא-לך 11
Yehova analumbira kwa Davide, lumbiro lotsimikizika kuti Iye sadzasintha: “Mmodzi wa ana ako ndidzamuyika pa mpando waufumu;
אם-ישמרו בניך בריתי-- ועדתי זו אלמדם גם-בניהם עדי-עד-- ישבו לכסא-לך 12
ngati ana ako azisunga pangano langa ndi malamulo amene ndiwaphunzitsa, pamenepo ana awo adzakhala pa mpando wako waufumu kwamuyaya ndi muyaya.”
כי-בחר יהוה בציון אוה למושב לו 13
Pakuti Yehova wasankha Ziyoni, Iye wakhumba kuti akhale malo ake okhalamo:
זאת-מנוחתי עדי-עד פה-אשב כי אותיה 14
“Awa ndi malo anga opumapo ku nthawi za nthawi; ndidzakhala pano pa mpando waufumu, pakuti ndakhumba zimenezi.
צידה ברך אברך אביוניה אשביע לחם 15
Ndidzadalitsa mzindawu ndi zinthu zambiri; anthu ake osauka ndidzawakhutitsa ndi chakudya.
וכהניה אלביש ישע וחסידיה רנן ירננו 16
Ndidzaveka ansembe ake chipulumutso, ndipo anthu ake oyera mtima adzayimba nthawi zonse nyimbo zachimwemwe.
שם אצמיח קרן לדוד ערכתי נר למשיחי 17
“Pano ndidzachulukitsa mphamvu za Davide ndi kuyikapo nyale ya wodzozedwa wanga.
אויביו אלביש בשת ועליו יציץ נזרו 18
Ndidzaveka adani ake manyazi, koma chipewa chaufumu pamutu pake chidzakhala chowala.”

< תהילים 132 >