< תהילים 105 >

הודו ליהוה קראו בשמו הודיעו בעמים עלילותיו 1
Yamikani Yehova, itanani dzina lake; lalikirani pakati pa anthu a mitundu ina zimene Iye wachita.
שירו-לו זמרו-לו שיחו בכל-נפלאותיו 2
Imbirani Iye, imbani matamando kwa Iyeyo; fotokozani za machitidwe ake onse odabwitsa.
התהללו בשם קדשו ישמח לב מבקשי יהוה 3
Munyadire dzina lake loyera; mitima ya iwo amene amafunafuna Yehova ikondwere.
דרשו יהוה ועזו בקשו פניו תמיד 4
Dalirani Yehova ndi mphamvu zake; funafunani nkhope yake nthawi yonse.
זכרו--נפלאותיו אשר-עשה מפתיו ומשפטי-פיו 5
Kumbukirani zodabwitsa zimene Iye anazichita, zozizwitsa zake ndi maweruzo amene anapereka,
זרע אברהם עבדו בני יעקב בחיריו 6
inu zidzukulu za Abrahamu mtumiki wake, inu ana a Yakobo, osankhika ake.
הוא יהוה אלהינו בכל-הארץ משפטיו 7
Iye ndiye Yehova Mulungu wathu; maweruzo ake ali pa dziko lonse lapansi.
זכר לעולם בריתו דבר צוה לאלף דור 8
Iyeyo amakumbukira pangano lake kwamuyaya, mawu amene analamula kwa mibado yonse,
אשר כרת את-אברהם ושבועתו לישחק 9
pangano limene Iye anapanga ndi Abrahamu, lumbiro limene analumbira kwa Isake.
ויעמידה ליעקב לחק לישראל ברית עולם 10
Iye analitsimikiza kwa Yakobo monga zophunzitsa, kwa Israeli monga pangano lamuyaya:
לאמר--לך אתן את-ארץ-כנען חבל נחלתכם 11
“Ndidzapereka kwa iwe dziko la Kanaani ngati gawo la cholowa chako.”
בהיותם מתי מספר כמעט וגרים בה 12
Pamene iwo anali ngati anthu ochepa mʼchiwerengero, ochepa ndithu, ndiponso alendo mʼdzikolo,
ויתהלכו מגוי אל-גוי מממלכה אל-עם אחר 13
ankayendayenda kuchoka ku mtundu wina wa anthu ndi kupita ku mtundu wina, kuchoka mu ufumu wina kupita ku wina.
לא-הניח אדם לעשקם ויוכח עליהם מלכים 14
Iye sanalole wina aliyense kuwapondereza; anadzudzula mafumu chifukwa cha iwo:
אל-תגעו במשיחי ולנביאי אל-תרעו 15
“Musakhudze odzozedwa anga; musachitire choyipa aneneri anga.”
ויקרא רעב על-הארץ כל-מטה-לחם שבר 16
Iye anabweretsa njala pa dziko ndipo anawononga chakudya chonse;
שלח לפניהם איש לעבד נמכר יוסף 17
Iyeyo anatumiza munthu patsogolo pawo, Yosefe anagulitsidwa ngati kapolo.
ענו בכבל רגליו (רגלו) ברזל באה נפשו 18
Iwo anavulaza mapazi ake ndi matangadza, khosi lake analiyika mʼzitsulo,
עד-עת בא-דברו-- אמרת יהוה צרפתהו 19
mpaka zimene Iye ananeneratu zitakwaniritsidwa, mpaka mawu a Yehova ataonetsa kuti Iye ananena zoona.
שלח מלך ויתירהו משל עמים ויפתחהו 20
Mfumu inatuma munthu kukamumasula, wolamulira wa mitundu ya anthu anamasula iyeyo.
שמו אדון לביתו ומשל בכל-קנינו 21
Anamuyika kukhala wolamulira nyumba yake, wolamulira zonse zimene iye anali nazo,
לאסר שריו בנפשו וזקניו יחכם 22
kulangiza ana a mfumu monga ankafunira ndi kuphunzitsa nzeru akuluakulu.
ויבא ישראל מצרים ויעקב גר בארץ-חם 23
Tsono Israeli analowa mu Igupto; Yakobo anakhala monga mlendo mʼdziko la Hamu.
ויפר את-עמו מאד ויעצמהו מצריו 24
Yehova anachulukitsa anthu ake; ndipo anachititsa kuti akhale ochuluka kwambiri kuposa adani awo;
הפך לבם לשנא עמו להתנכל בעבדיו 25
amene mitima yawo anayitembenuza kuti idane ndi anthu ake, kukonzera chiwembu atumiki ake.
שלח משה עבדו אהרן אשר בחר-בו 26
Yehova anatuma Mose mtumiki wake, ndi Aaroni amene Iye anamusankha.
שמו-בם דברי אתותיו ומפתים בארץ חם 27
Iwo anachita zizindikiro zozizwitsa pakati pawo, zodabwitsa zake mʼdziko la Hamu.
שלח חשך ויחשך ולא-מרו את-דבריו (דברו) 28
Yehova anatumiza mdima nasandutsa dziko kuti likhale la mdima. Koma anthuwo anakaniratu mawu a Yehova.
הפך את-מימיהם לדם וימת את-דגתם 29
Yehova anasandutsa madzi awo kukhala magazi, kuchititsa kuti nsomba zawo zife.
שרץ ארצם צפרדעים בחדרי מלכיהם 30
Dziko lawo linadzaza ndi achule amene analowa mʼzipinda zogona za olamulira awo.
אמר ויבא ערב כנים בכל-גבולם 31
Iye anayankhula, ndipo kunabwera ntchentche zochuluka ndi nsabwe mʼdziko lawo lonse.
נתן גשמיהם ברד אש להבות בארצם 32
Iyeyo anatembenuza mvula yawo kukhala matalala, ndi zingʼaningʼani mʼdziko lawo lonse;
ויך גפנם ותאנתם וישבר עץ גבולם 33
Anagwetsa mitengo yawo ya mpesa ndi mitengo yawo ya mkuyu, nawononganso mitengo ina ya mʼdziko lawolo.
אמר ויבא ארבה וילק ואין מספר 34
Iye anayankhula, ndipo dzombe linabwera, ziwala zosawerengeka;
ויאכל כל-עשב בארצם ויאכל פרי אדמתם 35
zinadya chilichonse chobiriwira cha mʼdziko lawo, zinadya zonse zotuluka mʼnthaka yawo.
ויך כל-בכור בארצם ראשית לכל-אונם 36
Kenaka anakantha ana onse oyamba kubadwa a mʼdziko lawo, zipatso zoyamba za umunthu wawo wonse.
ויוציאם בכסף וזהב ואין בשבטיו כושל 37
Yehova anatulutsa Israeli, atatenga siliva ndi golide wambiri, ndipo pakati pa mafuko awo palibe mmodzi amene anafowoka.
שמח מצרים בצאתם כי-נפל פחדם עליהם 38
Dziko la Igupto linakondwa pamene iwo anachoka, pakuti kuopsa kwa Israeli kunawagwera iwo.
פרש ענן למסך ואש להאיר לילה 39
Iye anatambasula mitambo ngati chofunda chawo, ndi moto owawunikira usiku.
שאל ויבא שלו ולחם שמים ישביעם 40
Iwo anapempha, ndipo Iye anawabweretsera zinziri ndipo anawakhutitsa ndi chakudya chochokera kumwamba.
פתח צור ויזובו מים הלכו בציות נהר 41
Iye anatsekula thanthwe, ndipo madzi anatuluka; ngati mtsinje anayenda mʼchipululu.
כי-זכר את-דבר קדשו את-אברהם עבדו 42
Pakuti anakumbukira lonjezo lake loyera limene linaperekedwa kwa Abrahamu mtumiki wake.
ויוצא עמו בששון ברנה את-בחיריו 43
Iye anatulutsa anthu ake akukondwera, osankhika ake akufuwula mwachimwemwe;
ויתן להם ארצות גוים ועמל לאמים יירשו 44
Iye anawapatsa mayiko a anthu a mitundu ina ndipo anakhala olowamʼmalo a zimene ena anazivutikira,
בעבור ישמרו חקיו-- ותורתיו ינצרו הללו-יה 45
kuti iwo asunge malangizo ake ndi kutsatira malamulo ake. Tamandani Yehova.

< תהילים 105 >