< במדבר 6 >

וידבר יהוה אל משה לאמר 1
Yehova anawuza Mose kuti,
דבר אל בני ישראל ואמרת אלהם איש או אשה כי יפלא לנדר נדר נזיר--להזיר ליהוה 2
“Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Ngati mwamuna kapena mkazi afuna kuchita lonjezo lapadera, lonjezo lodzipatula yekha kwa Yehova ngati Mnaziri,
מיין ושכר יזיר חמץ יין וחמץ שכר לא ישתה וכל משרת ענבים לא ישתה וענבים לחים ויבשים לא יאכל 3
sayenera kumwa vinyo kapena zakumwa zosasa ndipo asamamwe chakumwa chilichonse cha mphesa. Asamamwe madzi a mphesa kapena kudya mphesa zaziwisi kapena zowuma.
כל ימי נזרו מכל אשר יעשה מגפן היין מחרצנים ועד זג--לא יאכל 4
Pa nthawi yonse imene ali Mnaziri, asamadye chilichonse chopangidwa kuchokera ku mphesa ngakhale mbewu zake kapena makungu ake.’
כל ימי נדר נזרו תער לא יעבר על ראשו עד מלאת הימם אשר יזיר ליהוה קדש יהיה--גדל פרע שער ראשו 5
“‘Pa nthawi yonse ya lonjezo lodzipatula yekhalo, asamete kumutu kwake ndi lumo. Akhale wopatulika mpaka nthawi yake yonse ya kudzipatula yekha kwa Yehova itatha. Alileke tsitsi la pamutu pake kuti likule.’
כל ימי הזירו ליהוה על נפש מת לא יבא 6
Pa nthawi yonse imene munthuyo wadzipatula yekha kwa Yehova asayandikire mtembo.
לאביו ולאמו לאחיו ולאחתו--לא יטמא להם במתם כי נזר אלהיו על ראשו 7
Ngakhale abambo ake kapena amayi ake kapena mchimwene wake kaya mchemwali wake atamwalira, asadzidetse pokhudza mitembo yawo chifukwa kulumbira kwake kwa kudzipatula yekha kwa Yehova kuli pamutu pake.
כל ימי נזרו קדש הוא ליהוה 8
Munthuyo ndi wopatulika masiku onse odzipereka kwake kwa Yehova.
וכי ימות מת עליו בפתע פתאם וטמא ראש נזרו--וגלח ראשו ביום טהרתו ביום השביעי יגלחנו 9
“Ngati munthu wina afa mwadzidzidzi pafupi naye ndi kudetsa tsitsi lake loperekedwalo, amete mutu wake pa tsiku lodziyeretsa, tsiku lachisanu ndi chiwiri.
וביום השמיני יבא שתי תרים או שני בני יונה אל הכהן--אל פתח אהל מועד 10
Tsono pa tsiku lachisanu ndi chitatu abweretse nkhunda ziwiri kapena mawunda awiri anjiwa kwa wansembe pa khomo lolowera ku tenti ya msonkhano.
ועשה הכהן אחד לחטאת ואחד לעלה וכפר עליו מאשר חטא על הנפש וקדש את ראשו ביום ההוא 11
Wansembe apereke imodzi kuti ikhale nsembe yauchimo ndi ina nsembe yopsereza yotetezera tchimo chifukwa anachimwa popezeka pafupi ndi mtembo. Ndipo tsiku lomwelo apatulenso tsitsi la pamutu pake.
והזיר ליהוה את ימי נזרו והביא כבש בן שנתו לאשם והימים הראשנים יפלו כי טמא נזרו 12
Adzipereke kwa Yehova pa nthawi yodzipatula ndipo abweretse nkhosa yayimuna ya chaka chimodzi ngati nsembe yopepesera. Masiku akale sawerengedwanso chifukwa anadzidetsa pa nthawi yodzipatulira kwake.
וזאת תורת הנזיר ביום מלאת ימי נזרו יביא אתו אל פתח אהל מועד 13
“Tsono ili ndi lamulo la Mnaziri pamene nthawi yodzipatula kwake yatha: Abwere naye pa khomo la tenti ya msonkhano.
והקריב את קרבנו ליהוה כבש בן שנתו תמים אחד לעלה וכבשה אחת בת שנתה תמימה לחטאת ואיל אחד תמים לשלמים 14
Pamenepo apereke chopereka chake kwa Yehova: Nkhosa yayimuna ya chaka chimodzi yopanda chilema kuti ikhale nsembe yopsereza, mwana wankhosa wamkazi mmodzi wopanda chilema kuti ikhale nsembe yauchimo, ndi nkhosa imodzi yayikulu yayimuna kuti ikhale nsembe yachiyanjano,
וסל מצות סלת חלת בלולת בשמן ורקיקי מצות משחים בשמן ומנחתם ונסכיהם 15
ndipo abwere pamodzi ndi nsembe yachakudya ndi nsembe yachakumwa ndi dengu la buledi wopanda yisiti, makeke opangidwa ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, ndi timitanda ta buledi topakidwa mafuta.
והקריב הכהן לפני יהוה ועשה את חטאתו ואת עלתו 16
“Wansembe apereke zimenezi pamaso pa Yehova ndi kuchita nsembe ya uchimo ndi nsembe yopsereza.
ואת האיל יעשה זבח שלמים ליהוה על סל המצות ועשה הכהן את מנחתו ואת נסכו 17
Apereke dengu la buledi wopanda yisiti ndiponso nsembe yachiyanjano kwa Yehova ya nkhosa yayimuna, pamodzi ndi chopereka cha chakudya ndi chopereka cha chakumwa.
וגלח הנזיר פתח אהל מועד--את ראש נזרו ולקח את שער ראש נזרו ונתן על האש אשר תחת זבח השלמים 18
“Mnaziriyo amete tsitsi limene analipereka lija pa khomo la tenti ya msonkhano. Atenge tsitsilo ndi kuliyika pa moto umene uli pansi pa nsembe yachiyanjano.
ולקח הכהן את הזרע בשלה מן האיל וחלת מצה אחת מן הסל ורקיק מצה אחד ונתן על כפי הנזיר אחר התגלחו את נזרו 19
“Mnaziriyo atatha kumeta tsitsi analiperekalo, wansembe ayike mʼmanja mwake mwendo wa mmwamba wankhosa yayimuna umene waphikidwa ndipo atengenso keke ndi kamtanda ka buledi, zonse zopanda yisiti zomwe zili mʼdengu lija.
והניף אותם הכהן תנופה לפני יהוה--קדש הוא לכהן על חזה התנופה ועל שוק התרומה ואחר ישתה הנזיר יין 20
Wansembe aziweyule pamaso pa Yehova ngati nsembe yoweyula. Zimenezi ndi zopatulika ndipo ndi za wansembe pamodzi ndi chidale chimene anachiweyula ndi ntchafu yomwe anayipereka ija. Zitatha izi, Mnaziri akhoza kumwa vinyo.
זאת תורת הנזיר אשר ידר קרבנו ליהוה על נזרו מלבד אשר תשיג ידו כפי נדרו אשר ידר--כן יעשה על תורת נזרו 21
“Ili ndi lamulo la Mnaziri yemwe walonjeza kudzipereka kwa Yehova podzipatula yekha kuphatikiza pa zomwe angathe kukwaniritsa. Ayenera kukwaniritsa lonjezo lomwe wachitalo potsata lamulo la Mnaziri.”
וידבר יהוה אל משה לאמר 22
Yehova anawuza Mose kuti,
דבר אל אהרן ואל בניו לאמר כה תברכו את בני ישראל אמור להם 23
“Uza Aaroni ndi ana ake aamuna kuti, ‘Umu ndi mmene muzidalitsira Aisraeli. Muzinena kuti,
יברכך יהוה וישמרך 24
“‘Yehova akudalitse ndi kukusunga;
יאר יהוה פניו אליך ויחנך 25
Yehova awalitse nkhope yake pa iwe, nakuchitira chisomo;
ישא יהוה פניו אליך וישם לך שלום 26
Yehova akweze nkhope yake pa iwe, nakupatse mtendere.’”
ושמו את שמי על בני ישראל ואני אברכם 27
Choncho akadzatchula dzina langa podalitsa Aisraeli, Ine ndidzawadalitsadi.

< במדבר 6 >