< איוב 31 >

ברית כרתי לעיני ומה אתבונן על-בתולה 1
“Ndinachita pangano ndi maso anga kuti sindidzapenya namwali momusirira.
ומה חלק אלוה ממעל ונחלת שדי ממרמים 2
Kodi Mulungu kumwambako wandisungira zotani? Kodi cholowa changa chochokera kwa Wamphamvuzonse kumwambako nʼchotani?
הלא-איד לעול ונכר לפעלי און 3
Kodi si chiwonongeko kwa anthu oyipa, tsoka kwa iwo amene amachita zolakwa?
הלא-הוא יראה דרכי וכל-צעדי יספור 4
Kodi Mulungu saona zochita zanga, ndi kudziwa mayendedwe anga?
אם-הלכתי עם-שוא ותחש על-מרמה רגלי 5
“Ngati ndachita zinthu mwachiphamaso, kapena kufulumira kukachita zachinyengo,
ישקלני במאזני-צדק וידע אלוה תמתי 6
Mulungu andiyeze ndi muyeso wake wolungama ndipo Iye adzadziwa kuti ine ndine wosalakwa,
אם תטה אשרי מני הדרך ואחר עיני הלך לבי ובכפי דבק מאום 7
ngati mayendedwe anga asempha njira, ngati mtima wanga wakhumbira zimene maso anga aona, kapena ngati ndachita choyipa chilichonse.
אזרעה ואחר יאכל וצאצאי ישרשו 8
Pamenepo ena adye zimene ndinadzala, ndipo zomera zanga zizulidwe.
אם-נפתה לבי על-אשה ועל-פתח רעי ארבתי 9
“Ngati mtima wanga unakopekapo ndi mkazi, ndipo ngati ndinalakalaka mkazi wa mnansi wanga,
תטחן לאחר אשתי ועליה יכרעון אחרין 10
pamenepo mkazi wanga aphikire mwamuna wina chakudya, ndipo amuna ena azigona naye.
כי-הוא (היא) זמה והיא (והוא) עון פלילים 11
Pakuti zimenezo zikanakhala zochititsa manyazi, tchimo loyenera kulangidwa nalo.
כי אש היא עד-אבדון תאכל ובכל-תבואתי תשרש 12
Ndi moto umene umayaka mpaka chiwonongeko; ukanapsereza zokolola zanga.
אם-אמאס--משפט עבדי ואמתי ברבם עמדי 13
“Ngati ndinkapondereza mlandu wa akapolo anga aamuna kapena aakazi, pamene ankabwera kwa ine ndi milandu yawo,
ומה אעשה כי-יקום אל וכי-יפקד מה אשיבנו 14
ndidzatani pamene Mulungu adzanditsutsa? Nanga ndidzayankha chiyani akadzandifunsa?
הלא-בבטן עשני עשהו ויכננו ברחם אחד 15
Kodi amene anapanga ine mʼmimba mwa amayi anga si yemwe anapanganso iwo? Kodi si mmodzi yemweyo amene anatipanga tonsefe mʼmimba mwa amayi athu?
אם-אמנע מחפץ דלים ועיני אלמנה אכלה 16
“Ngati ndinawamana aumphawi zinthu zimene ankazikhumba, kapena kuwagwiritsa fuwa lamoto akazi amasiye amene amafuna thandizo kwa ine,
ואכל פתי לבדי ולא-אכל יתום ממנה 17
ngati chakudya changa ndinadya ndekha, wosagawirako mwana wamasiye,
כי מנעורי גדלני כאב ומבטן אמי אנחנה 18
chonsechotu kuyambira unyamata wanga ndinamulera monga abambo ake, ndipo moyo wanga wonse ndakhala ndikusamalira akazi amasiye,
אם-אראה אובד מבלי לבוש ואין כסות לאביון 19
ngati ndinaona wina aliyense akuzunzika ndi usiwa, kapena munthu wosauka alibe chofunda,
אם-לא ברכוני חלצו ומגז כבשי יתחמם 20
ndipo ngati iyeyo sananditamandepo chifukwa chomufunditsa ndi nsalu ya ubweya wankhosa,
אם-הניפותי על-יתום ידי כי-אראה בשער עזרתי 21
ngati ndinaopsezapo mwana wamasiye, poganiza kuti ndinali ndi mphamvu mʼbwalo la milandu,
כתפי משכמה תפול ואזרעי מקנה תשבר 22
pamenepo phewa langa lipokonyeke, mkono wanga ukonyoke polumikizira pake.
כי פחד אלי איד אל ומשאתו לא אוכל 23
Popeza ine ndinaopa kwambiri chiwonongeko chochokera kwa Mulungu, ndinachitanso mantha ndi ulemerero wake, sindikanatha kuchita zinthu zimenezi.
אם-שמתי זהב כסלי ולכתם אמרתי מבטחי 24
“Ngati ndinayika mtima wanga pa chuma kapena kunena kwa golide wabwino kwambiri kuti, ‘Iwe ndiye chitetezo changa,’
אם-אשמח כי-רב חילי וכי-כביר מצאה ידי 25
ngati ndinakondwera chifukwa choti chuma changa chinali chambiri, zinthu zimene manja anga anazipeza,
אם-אראה אור כי יהל וירח יקר הלך 26
ngati pamene ndinaona dzuwa likuwala, kapena mwezi ukuyenda mwa ulemerero wake,
ויפת בסתר לבי ותשק ידי לפי 27
ndipo kuti mtima wanga unakopeka nazo nʼkuyika dzanja langa pakamwa mozilemekeza,
גם-הוא עון פלילי כי-כחשתי לאל ממעל 28
pamenepo zimenezinso zikanakhala machimo oti ndilangidwe nawo, chifukwa ndikanakhala wosakhulupirika kwa Mulungu wakumwamba.
אם-אשמח בפיד משנאי והתעררתי כי-מצאו רע 29
“Ngati ndinasangalala ndi kuwonongeka kwa mdani wanga, kapena kusekera mavuto pamene mavuto anamugwera,
ולא-נתתי לחטא חכי-- לשאל באלה נפשו 30
ine sindinachimwe ndi pakamwa panga potulutsa matemberero a mdani wanga kuti awonongeke,
אם-לא אמרו מתי אהלי מי-יתן מבשרו לא נשבע 31
ngati anthu amene ndimakhala nawo mʼnyumba mwanga sananenepo kuti, ‘Kodi ndani amene sakhuta ndi chakudya cha Yobu?’
בחוץ לא-ילין גר דלתי לארח אפתח 32
Komatu mlendo sindinamusiye pa msewu usiku wonse, pakuti khomo langa linali lotsekuka nthawi zonse kwa alendo,
אם-כסיתי כאדם פשעי-- לטמון בחבי עוני 33
ngati ndinabisa tchimo langa monga amachitira anthu ena, kubisa kulakwa mu mtima mwanga
כי אערוץ המון רבה-- ובוז-משפחות יחתני ואדם לא-אצא פתח 34
chifukwa choopa gulu la anthu, ndi kuchita mantha ndi mnyozo wa mafuko kotero ndinakhala chete ndipo sindinatuluke panja.
מי יתן-לי שמע לי-- הן-תוי שדי יענני וספר כתב איש ריבי 35
“Aa, pakanakhala wina wondimva! Tsopano ndikutsiriza mawu anga odzitetezera. Wamphamvuzonse andiyankhe; mdani wanga achite kulemba pa kalata mawu ake ondineneza.
אם-לא על-שכמי אשאנו אענדנו עטרות לי 36
Ndithu ine ndikanakoleka kalatayo pa phewa langa, ndikanayivala kumutu ngati chipewa chaufumu.
מספר צעדי אגידנו כמו-נגיד אקרבנו 37
Ndikanamufotokozera zonse zimene ndinachita; ndikanafika pamaso pake ngati kalonga.
אם-עלי אדמתי תזעק ויחד תלמיה יבכיון 38
“Ngati minda yanga ikulira monditsutsa ine ndipo malo ake onse osalimidwa anyowa ndi misozi,
אם-כחה אכלתי בלי-כסף ונפש בעליה הפחתי 39
ngati ndinadya za mʼminda mwake osapereka ndalama kapena kukhumudwitsa anthu olima mʼmindamo,
תחת חטה יצא חוח--ותחת-שערה באשה תמו דברי איוב 40
pamenepo mʼmindamo mumere namsongole mʼmalo mwa tirigu ndi udzu mʼmalo mwa barele.” Mawu a Yobu athera pano.

< איוב 31 >