< ירמיה 48 >

למואב כה אמר יהוה צבאות אלהי ישראל הוי אל נבו כי שדדה הבישה נלכדה קריתים הבישה המשגב וחתה 1
Ponena za Mowabu: Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, “Tsoka kwa mzinda wa Nebo, chifukwa wawonongedwa. Mzinda wa Kiriyataimu wachititsidwa manyazi ndipo wagonjetsedwa; linga lichititsidwa manyazi ndipo lagumulidwa.
אין עוד תהלת מואב--בחשבון חשבו עליה רעה לכו ונכריתנה מגוי גם מדמן תדמי אחריך תלך חרב 2
Palibenso amene akutamanda Mowabu; ku Hesiboni anthu anamupanganira zoyipa: ‘Bwerani, tiyeni timuwonongeretu kuti asakhalenso mtundu wa anthu.’ Inunso anthu a ku Madimena, adzakukhalitsani chete; ankhondo adzakupirikitsani.
קול צעקה מחרונים--שד ושבר גדול 3
Tamvani mfuwu wa anthu a ku Horonaimu. Iwo akulira kuti, ‘Kusakazika ndi kuwonongeka kwakukulu.’
נשברה מואב השמיעו זעקה צעוריה (צעיריה) 4
Mowabu wawonongeka; ana ake angʼonoangʼono akulira kwambiri.
כי מעלה הלחות (הלחית) בבכי יעלה בכי כי במורד חורנים צרי צעקת שבר שמעו 5
Anthu akukwera chikweza cha ku Luhiti, akulira kwambiri pamene akupita. Kulira chifukwa cha chiwonongeko kukumveka pa njira yotsikira ku Horonaimu.
נסו מלטו נפשכם ותהיינה כערוער במדבר 6
Thawani! Dzipulumutseni; khalani ngati mbidzi ya mʼchipululu.
כי יען בטחך במעשיך ובאוצרותיך גם את תלכדי ויצא כמיש (כמוש) בגולה כהניו ושריו יחד (יחדו) 7
Popeza inu munkadalira ntchito zanu ndi chuma chanu, nanunso mudzatengedwa ukapolo, ndipo Kemosi adzapita ku ukapolo, pamodzi ndi ansembe ake ndi akuluakulu ake.
ויבא שדד אל כל עיר ועיר לא תמלט ואבד העמק ונשמד המישר--אשר אמר יהוה 8
Wowononga adzabwera ndi kusakaza mzinda uliwonse, ndipo palibe mzinda umene udzapulumuke. Chigwa chidzasanduka bwinja ndipo malo athyathyathya a pamwamba pa phiri adzawonongedwa monga Yehova wayankhulira.
תנו ציץ למואב כי נצא תצא ועריה לשמה תהיינה מאין יושב בהן 9
Mtsineni khutu Mowabu chifukwa adzasakazika; mizinda yake idzasanduka mabwinja, wopanda munthu wokhalamo.
ארור עשה מלאכת יהוה--רמיה וארור מנע חרבו מדם 10
“Wotembereredwa munthu amene amagwira ntchito ya Yehova monyinyirika! Wotembereredwa munthu amene amaletsa lupanga lake kupha anthu!
שאנן מואב מנעוריו ושקט הוא אל שמריו ולא הורק מכלי אל כלי ובגולה לא הלך על כן עמד טעמו בו וריחו לא נמר 11
“Mowabu wakhala pa mtendere kuyambira ubwana wake, ngati vinyo wokhazikika pa masese ake, osapungulidwa kuchoka mu mtsuko wina kuthira mu mtsuko wina; iye sanatengedwepo ukapolo. Nʼchifukwa chake kukoma kwake nʼkomwe kuja ndipo fungo lake silinasinthe.
לכן הנה ימים באים נאם יהוה ושלחתי לו צעים וצעהו וכליו יריקו ונבליהם ינפצו 12
Nʼchifukwa chake masiku akubwera,” akutero Yehova, “pamene ndidzatuma anthu amene amakhuthula vinyo mʼmitsuko ndipo adzamukhutula; adzakhuthula vinyo yense mitsuko yake pambuyo pake nʼkuphwanya mitsukoyo.
ובש מואב מכמוש כאשר בשו בית ישראל מבית אל מבטחם 13
Pamenepo Mowabu adzachita manyazi ndi Kemosi, monga momwe Aisraeli anachitira manyazi ndi Beteli amene ankamukhutulira.
איך תאמרו גבורים אנחנו ואנשי חיל למלחמה 14
“Kodi munganene bwanji kuti, ‘Ife ndife asilikali. Ife ndife ngwazi, anthu amphamvu pa nkhondo?’
שדד מואב ועריה עלה ומבחר בחוריו ירדו לטבח נאם המלך--יהוה צבאות שמו 15
Owononga Mowabu ndi mizinda yake abwera ndipo ankhondo adzalowa mʼmidzi yake; anyamata ake okongola apita kukaphedwa,” ikutero Mfumu, imene dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.
קרוב איד מואב לבוא ורעתו מהרה מאד 16
Kugwa kwa Mowabu kuli pafupi; masautso ake akubwera posachedwa.
נדו לו כל סביביו וכל ידעי שמו אמרו איכה נשבר מטה עז--מקל תפארה 17
Mulireni kwambiri, inu nonse amene mwamuzungulira, inu nonse amene mumadziwa za kutchuka kwake; nenani kuti, “Taonani momwe yathyokera ndodo yamphamvu yaufumu ija, taonani momwe ndodo yaulemu yathyokera!”
רדי מכבוד ישבי (ושבי) בצמא ישבת בת דיבון כי שדד מואב עלה בך שחת מבצריך 18
“Tsikani pa ulemerero wanu ndipo khalani pansi powuma, inu anthu okhala ku Diboni, pakuti wowononga Mowabu wabwera kudzamenyana nanu, wasakaza mizinda yanu yotetezedwa.
אל דרך עמדי וצפי יושבת ערוער שאלי נס ונמלטה אמרי מה נהיתה 19
Inu amene mumakhala ku Aroeri, imani mʼmbali mwa msewu ndi kumaonerera. Funsani mwamuna amene akuthawa ndiponso mkazi amene wapulumuka, afunseni kuti, ‘Kodi chachitika nʼchiyani?’”
הביש מואב כי חתה הילילי (הילילו) וזעקי (וזעקו) הגידו בארנון כי שדד מואב 20
Iwo adzayankha kuti, “Mowabu wachititsidwa manyazi, pakuti wasakazika. Lirani mwachisoni ndipo fuwulani! Lengezani ku mtsinje wa Arinoni kuti Mowabu wawonongedwa.
ומשפט בא אל ארץ המישר--אל חלון ואל יהצה ועל מופעת (מיפעת) 21
Chiweruzo chabwera ku mizinda ya ku mapiri, ndiyo Holoni, Yaza, Mefaati,
ועל דיבון ועל נבו ועל בית דבלתים 22
Diboni, Nebo, Beti-Dibilataimu,
ועל קריתים ועל בית גמול ועל בית מעון 23
Kiriyataimu, Beti-Gamuli, Beti-Meoni,
ועל קריות ועל בצרה ועל כל ערי ארץ מואב--הרחקות והקרבות 24
Keriyoti ndi Bozira ndi mizinda yonse ya Mowabu, yakutali ndi yapafupi yomwe.
נגדעה קרן מואב וזרעו נשברה--נאם יהוה 25
Mphamvu za Mowabu zawonongeka; mkono wake wathyoka,” akutero Yehova.
השכירהו כי על יהוה הגדיל וספק מואב בקיאו והיה לשחק גם הוא 26
“Muledzeretseni Mowabu, chifukwa anadzikuza powukira Yehova. Mulekeni Mowabu avivinizike mʼmasanzi ake; mulekeni akhale chinthu chomachiseka.
ואם לוא השחק היה לך ישראל אם בגנבים נמצאה (נמצא) כי מדי דבריך בו תתנודד 27
Kodi suja Israeli anali kwa iwe ngati chinthu chomachiseka? Kodi Israeli anapezeka pakati pa akuba kuti nthawi zonse poyankhula za iye, iwe uzimupukusira mutu momunyoza?
עזבו ערים ושכנו בסלע ישבי מואב והיו כיונה תקנן בעברי פי פחת 28
Inu amene mumakhala ku Mowabu, siyani mizinda yanu ndi kukakhala pakati pa matanthwe. Khalani ngati nkhunda imene imamanga chisa chake pa khomo la phanga.
שמענו גאון מואב גאה מאד גבהו וגאונו וגאותו ורם לבו 29
“Tamva za kunyada kwa Mowabu, kunyada kwake nʼkwakukulu. Ndi wodzitama, wonyada ndi wodzitukumula. Ali ndi mtima wodzikweza.
אני ידעתי נאם יהוה עברתו ולא כן בדיו לא כן עשו 30
Ine ndikuzidziwa ntchito zake, akutero Yehova. Ntchitozo ndi nʼzosapindulitsa kanthu.
על כן על מואב איליל ולמואב כלה אזעק אל אנשי קיר חרש יהגה 31
Nʼchifukwa chake ndidzamulira Mowabu, ine ndikulira chifukwa cha anthu onse a ku Mowabu, ndikubuwula chifukwa cha anthu a ku Kiri Heresi.
מבכי יעזר אבכה לך הגפן שבמה נטישתיך עברו ים עד ים יעזר נגעו--על קיצך ועל בצירך שדד נפל 32
Ndikukhetsa misozi chifukwa cha inu, kupambana momwe ndinalirira Yazeri. Inu anthu a ku Sibina muli ngati mipesa imene nthambi zake zatambalala mpaka ku Nyanja; zafika mpaka ku nyanja ya Yazeri. Wowononga wasakaza zipatso zake zachilimwe ndi mpesa.
ונאספה שמחה וגיל מכרמל ומארץ מואב ויין מיקבים השבתי--לא ידרך הידד הידד לא הידד 33
Chimwemwe ndi chisangalalo zatha ku minda ya zipatso ya ku Mowabu. Ndaletsa kuchucha kwa vinyo mopsinyira mphesa; palibe amene akufuwula mokondwa akamapsinya mphesa. Ngakhale kufuwula kulipo, koma sikufuwula kwa chimwemwe.
מזעקת חשבון עד אלעלה עד יהץ נתנו קולם--מצער עד חרנים עגלת שלשיה כי גם מי נמרים למשמות יהיו 34
“A ku Hesiboni ndi Eleali akulira ndipo mfuwu wawo ukumveka mpaka ku Yahazi, kuchokera ku Zowari mpaka ku Horonaimu ndi ku Egilati Selisiya. Ngakhale madzi a ku Nimurimu aphwa.
והשבתי למואב נאם יהוה מעלה במה ומקטיר לאלהיו 35
Ndidzawaletsa anthu a ku Mowabu kupereka nsembe mʼmalo awo opembedzera ndi kufukiza lubani kwa milungu yawo,” akutero Yehova.
על כן לבי למואב כחללים יהמה ולבי אל אנשי קיר חרש כחלילים יהמה על כן יתרת עשה אבדו 36
“Nʼchifukwa chake mtima wanga ukulirira Mowabu ngati chitoliro. Mtima wanga ukulirira anthu a ku Kiri Heresi ngati chitoliro chifukwa chuma chimene anachipata chatha.
כי כל ראש קרחה וכל זקן גרעה על כל ידים גדדת ועל מתנים שק 37
Aliyense wameta mutu wake ndi ndevu zake; manja a munthu aliyense ndi ochekacheka, ndipo munthu aliyense wavala chiguduli mʼchiwuno mwake.
על כל גגות מואב וברחבתיה כלה מספד כי שברתי את מואב ככלי אין חפץ בו--נאם יהוה 38
Pa madenga onse a ku Mowabu ndiponso mʼmisewu yake anthu akungolira, pakuti ndaphwanya Mowabu ngati mtsuko wopanda ntchito,” akutero Yehova.
איך חתה הילילו איך הפנה ערף מואב בוש והיה מואב לשחק ולמחתה לכל סביביו 39
“Taonani mmene waphwanyikira! Tamvani momwe akulirira! Taonani momwe Mowabu wachititsidwira manyazi. Mowabu wasanduka chinthu chonyozeka, chinthu chochititsa mantha kwa onse amene amuzungulira.”
כי כה אמר יהוה הנה כנשר ידאה ופרש כנפיו אל מואב 40
Yehova akuti, “Mtundu wina udzachita kuwuluka nʼkugwera pa Mowabu ngati chiwombankhanga chimene chatambalitsa mapiko ake.
נלכדה הקריות והמצדות נתפשה והיה לב גבורי מואב ביום ההוא כלב אשה מצרה 41
Mizinda idzagwidwa ndipo malinga adzalandidwa. Pa tsiku limenelo mitima ya ankhondo a ku Mowabu idzakhala ngati mtima wa mayi pa nthawi yake yochira.
ונשמד מואב מעם כי על יהוה הגדיל 42
Mowabu sudzakhala mtundu wa anthu chifukwa unadzikuza powukira Yehova.
פחד ופחת ופח--עליך יושב מואב נאם יהוה 43
Zoopsa, dzenje ndi msampha zikudikira inu anthu a ku Mowabu,” akutero Yehova.
הניס (הנס) מפני הפחד יפל אל הפחת והעלה מן הפחת ילכד בפח כי אביא אליה אל מואב שנת פקדתם נאם יהוה 44
“Aliyense wothawa zoopsa adzagwera mʼdzenje, aliyense wotuluka mʼdzenje adzakodwa mu msampha. Ndigwetsa zimenezi pa Mowabu pa nthawi ya chilango chake,” akutero Yehova.
בצל חשבון עמדו מכח נסים כי אש יצא מחשבון ולהבה מבין סיחון ותאכל פאת מואב וקדקד בני שאון 45
“Anthu othawa nkhondo ayima pa mthunzi wa Hesiboni chifukwa chotopa. Koma moto wayaka kuchokera ku Hesiboni, malawi a moto abuka kuchokera ku nyumba ya mfumu Sihoni. Motowo ukuwononga mapiri a ku Mowabu, dziko la anthu onyada.
אוי לך מואב אבד עם כמוש כי לקחו בניך בשבי ובנתיך בשביה 46
Tsoka kwa iwe Mowabu! Anthu opembedza Kemosi awonongeka. Ana ako aamuna ndi aakazi atengedwa ukapolo.
ושבתי שבות מואב באחרית הימים נאם יהוה עד הנה משפט מואב 47
“Komabe masiku akutsogolo ndidzabwezeranso Mowabu chuma chake,” akutero Yehova. Chiweruzo cha Mowabu chathera pamenepa.

< ירמיה 48 >