< חבקוק 3 >

תפלה לחבקוק הנביא--על שגינות 1
Pemphero la mneneri Habakuku potsata mayimbidwe a Sigionoti.
יהוה שמעתי שמעך יראתי--יהוה פעלך בקרב שנים חייהו בקרב שנים תודיע ברגז רחם תזכור 2
Inu Yehova, ndamva za kutchuka kwanu; Inu Yehova, ntchito zanu zandiopsa. Muzichitenso masiku athu ano, masiku athu ano zidziwike; mu ukali wanu mukumbukire kuchita chifundo.
אלוה מתימן יבוא וקדוש מהר פארן סלה כסה שמים הודו ותהלתו מלאה הארץ 3
Mulungu anabwera kuchokera ku Temani, Woyerayo kuchokera ku Phiri la Parani. (Sela) Ulemerero wake unaphimba mlengalenga ndipo dziko lapansi linadzaza ndi matamando ake.
ונגה כאור תהיה קרנים מידו לו ושם חביון עזה 4
Kuwala kwa ulemerero wake kunali ngati kutuluka kwa dzuwa; kunyezimira kunkatuluka mʼdzanja lake, mʼmene anabisamo mphamvu zake.
לפניו ילך דבר ויצא רשף לרגליו 5
Patsogolo pake pankagwa mliri; nthenda yoopsa inkagwa kumbuyo kwake.
עמד וימדד ארץ ראה ויתר גוים ויתפצצו הררי עד שחו גבעות עולם הליכות עולם לו 6
Iye anayimirira ndi kugwedeza dziko lapansi; anayangʼana ndipo mitundu ya anthu inanjenjemera. Mapiri okhazikika anagumuka ndipo zitunda zakalekale zinatitimira. Njira zake ndi zachikhalire.
תחת און ראיתי אהלי כושן ירגזון יריעות ארץ מדין 7
Ndinaona matenti a ku Kusani ali pa mavuto, mokhala a ku Midiyani muli ululu waukulu.
הבנהרים חרה יהוה--אם בנהרים אפך אם בים עברתך כי תרכב על סוסיך מרכבתיך ישועה 8
Inu Yehova, kodi munakwiyira mitsinje? Kodi munakalipira timitsinje? Kodi munapsera mtima nyanja pamene munakwera pa akavalo anu ndiponso magaleta anu achipulumutso?
עריה תעור קשתך שבעות מטות אמר סלה נהרות תבקע ארץ 9
Munasolola uta wanu mʼchimake, munayitanitsa mivi yambiri. (Sela) Munagawa dziko lapansi ndi mitsinje;
ראוך יחילו הרים זרם מים עבר נתן תהום קולו רום ידיהו נשא 10
mapiri anakuonani ndipo anagwedezeka. Madzi amphamvu anasefukira; nyanja yozama inakokoma ndipo mafunde ake anakwera kwambiri.
שמש ירח עמד זבלה לאור חציך יהלכו לנגה ברק חניתך 11
Dzuwa ndi mwezi zinayima chilili mlengalenga, pa kungʼanima kwa mivi yanu yowulukayo, pa kunyezimira kwa mkondo wanu.
בזעם תצעד ארץ באף תדוש גוים 12
Munayendayenda mʼdziko lapansi muli ndi ukali, ndipo munapondereza mitundu ya anthu muli ndi mkwiyo.
יצאת לישע עמך לישע את משיחך מחצת ראש מבית רשע ערות יסוד עד צואר סלה 13
Munapita kukalanditsa anthu anu, kukapulumutsa wodzozedwa wanu. Munakantha mtsogoleri wa dziko la anthu oyipa, munawononga anthu ake onse. (Sela)
נקבת במטיו ראש פרזו יסערו להפיצני עליצתם כמו לאכל עני במסתר 14
Ndi mkondo wake womwe munalasa mtsogoleri wake pamene ankhondo ake anabwera mwamphamvu kudzatibalalitsa, ankasangalala ngati kuti akudzawononga osauka amene akubisala.
דרכת בים סוסיך חמר מים רבים 15
Munapondaponda pa nyanja ndi akavalo anu, kuvundula madzi amphamvu.
שמעתי ותרגז בטני לקול צללו שפתי--יבוא רקב בעצמי ותחתי ארגז אשר אנוח ליום צרה לעלות לעם יגודנו 16
Ndinamva ndipo mtima wanga unagunda kwambiri, milomo yanga inanjenjemera pakumva phokosolo; mafupa anga anaguluka, ndipo mawondo anga anawombana. Komabe ndikuyembekezera mofatsa, tsiku la masautso limene lidzafike pa mtundu wa anthu umene ukutithira nkhondo.
כי תאנה לא תפרח ואין יבול בגפנים--כחש מעשה זית ושדמות לא עשה אכל גזר ממכלה צאן ואין בקר ברפתים 17
Ngakhale mtengo wa mkuyu usachite maluwa, ndipo mipesa ikhale yopanda mphesa. Ngakhale mitengo ya olivi isabereke zipatso, ndipo mʼminda musatuluke kanthu. Ngakhale nkhosa ndi ngʼombe zithe mʼkhola,
ואני ביהוה אעלוזה אגילה באלהי ישעי 18
komabe ine ndidzakondwera mwa Yehova, ndidzasangalala mwa Mulungu Mpulumutsi wanga.
יהוה אדני חילי וישם רגלי כאילות ועל במותי ידרכני למנצח בנגינותי 19
Ambuye Yehova ndiye mphamvu yanga; amalimbitsa miyendo yanga ngati ya mbawala yayikazi, amandithandiza kukafika pamwamba pa phiri. Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za nsambo.

< חבקוק 3 >