+ בראשית 1 >

בראשית ברא אלהים את השמים ואת הארץ 1
Pachiyambi Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.
והארץ היתה תהו ובהו וחשך על פני תהום ורוח אלהים מרחפת על פני המים 2
Dziko lapansi linali losakonzedwa ndi lopanda kanthu. Mdima wandiweyani unakuta nyanja ndipo Mzimu wa Mulungu unkayendayenda pamwamba pa madziwo.
ויאמר אלהים יהי אור ויהי אור 3
Pamenepo Mulungu anati, “Kuwale” ndipo kunawaladi.
וירא אלהים את האור כי טוב ויבדל אלהים בין האור ובין החשך 4
Mulungu anaona kuti kuwalako kunali bwino ndipo Iye analekanitsa kuwala ndi mdima.
ויקרא אלהים לאור יום ולחשך קרא לילה ויהי ערב ויהי בקר יום אחד 5
Mulungu anatcha kuwalako “usana” ndipo mdima anawutcha “usiku.” Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa pa tsiku loyamba.
ויאמר אלהים יהי רקיע בתוך המים ויהי מבדיל בין מים למים 6
Kenaka Mulungu anati, “Pakhale thambo pakati pa madzi kuti lilekanitse madzi a mʼmwamba ndi madzi a pansi.”
ויעש אלהים את הרקיע ויבדל בין המים אשר מתחת לרקיע ובין המים אשר מעל לרקיע ויהי כן 7
Ndipo Mulungu anapanga thambo nalekanitsa madzi amene anali pansi ndi pamwamba pa thambo lija, ndipo zinachitikadi.
ויקרא אלהים לרקיע שמים ויהי ערב ויהי בקר יום שני 8
Mulungu anatcha thambo lija “kumwamba.” Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa pa tsiku lachiwiri.
ויאמר אלהים יקוו המים מתחת השמים אל מקום אחד ותראה היבשה ויהי כן 9
Mulungu anati, “Madzi a pansi pa thambo asonkhane pa malo amodzi kuti mtunda uwoneke,” ndipo zinachitikadi.
ויקרא אלהים ליבשה ארץ ולמקוה המים קרא ימים וירא אלהים כי טוב 10
Mulungu anawutcha mtundawo “dziko,” madzi osonkhana pamodziwo anawatcha “nyanja.” Ndipo Mulungu anaona kuti zinali bwino.
ויאמר אלהים תדשא הארץ דשא עשב מזריע זרע עץ פרי עשה פרי למינו אשר זרעו בו על הארץ ויהי כן 11
Kenaka Mulungu anati, “Dziko libereke zomera zobala mbewu, mitengo yobala zipatso za mbewu, molingana ndi mitundu yake.” Ndipo zinachitikadi.
ותוצא הארץ דשא עשב מזריע זרע למינהו ועץ עשה פרי אשר זרעו בו למינהו וירא אלהים כי טוב 12
Dziko linabereka zomera zokhala ndi mbewu monga mwa mitundu yake ndi mitengo yokhala ndi zipatso za mbewu mʼkati mwake monga mwa mitundu yake. Ndipo Mulungu anaona kuti zinali bwino.
ויהי ערב ויהי בקר יום שלישי 13
Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa pa tsiku lachitatu.
ויאמר אלהים יהי מארת ברקיע השמים להבדיל בין היום ובין הלילה והיו לאתת ולמועדים ולימים ושנים 14
Mulungu anati, “Pakhale zowunikira kuthambo kuti zilekanitse usana ndi usiku. Ndipo zimenezi zikhale zizindikiro zoonetsa nyengo, masiku ndi zaka;
והיו למאורת ברקיע השמים להאיר על הארץ ויהי כן 15
zikhale kuthambo kuti ziwunikire pa dziko lapansi. Ndipo zinachitikadi.”
ויעש אלהים את שני המארת הגדלים את המאור הגדל לממשלת היום ואת המאור הקטן לממשלת הלילה ואת הכוכבים 16
Mulungu anapanga zowunikira zazikulu ziwiri; chachikulu chilamulire usana ndi chachingʼono chilamulire usiku. Iye anapanganso nyenyezi.
ויתן אתם אלהים ברקיע השמים להאיר על הארץ 17
Mulungu anaziyika mlengalenga kuti ziziwunikira pa dziko lapansi,
ולמשל ביום ובלילה ולהבדיל בין האור ובין החשך וירא אלהים כי טוב 18
kuti zilamulire usana ndi usiku, ndi kuti zilekanitse kuwala ndi mdima. Mulungu anaona kuti zinali bwino.
ויהי ערב ויהי בקר יום רביעי 19
Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa pa tsiku lachinayi.
ויאמר אלהים--ישרצו המים שרץ נפש חיה ועוף יעופף על הארץ על פני רקיע השמים 20
Mulungu anati, “Mʼmadzi mukhale zamoyo zochuluka ndipo mbalame ziwuluke mlengalenga pamwamba pa dziko lapansi.”
ויברא אלהים את התנינם הגדלים ואת כל נפש החיה הרמשת אשר שרצו המים למינהם ואת כל עוף כנף למינהו וירא אלהים כי טוב 21
Choncho Mulungu analenga zamoyo zikuluzikulu za mʼnyanja ndi chamoyo chamtundu uliwonse chokhala mʼmadzi ndi mbalame iliyonse ya mapiko monga mwa mtundu wake. Mulungu anaona kuti zinali bwino.
ויברך אתם אלהים לאמר פרו ורבו ומלאו את המים בימים והעוף ירב בארץ 22
Mulungu anazidalitsa nati, “Muswane, ndi kudzaza mʼmadzi a mʼnyanja, ndipo mbalame zichuluke pa dziko lapansi.”
ויהי ערב ויהי בקר יום חמישי 23
Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa pa tsiku lachisanu.
ויאמר אלהים תוצא הארץ נפש חיה למינה בהמה ורמש וחיתו ארץ למינה ויהי כן 24
Kenaka Mulungu anati, “Dziko lapansi litulutse zolengedwa zamoyo monga mwa mitundu yawo: ziweto, zolengedwa zokwawa ndi nyama zakuthengo, iliyonse monga mwa mtundu wake.” Ndipo zinaterodi.
ויעש אלהים את חית הארץ למינה ואת הבהמה למינה ואת כל רמש האדמה למינהו וירא אלהים כי טוב 25
Mulungu anapanga nyama zakuthengo monga mwa mitundu yawo, nyama zoweta monga mwa mitundu yawo ndi nyama zokwawa monga mwa mitundu yawo. Ndipo Mulungu anaona kuti zinali bwino.
ויאמר אלהים נעשה אדם בצלמנו כדמותנו וירדו בדגת הים ובעוף השמים ובבהמה ובכל הארץ ובכל הרמש הרמש על הארץ 26
Zitatha izi Mulungu anati, “Tipange munthu mʼchifanizo chathu, mofanana ndi ife kuti alamulire nsomba za mʼnyanja, mbalame zamlengalenga, nyama zonse zoweta ndi zonse zokwawa za pa dziko lapansi ndi zamoyo zonse zakutchire.”
ויברא אלהים את האדם בצלמו בצלם אלהים ברא אתו זכר ונקבה ברא אתם 27
Ndipo Mulungu analenga munthu mʼchifanizo chake. Anawalengadi mʼchifanizo cha Mulungu; analenga iwo, mwamuna ndi mkazi.
ויברך אתם אלהים ויאמר להם אלהים פרו ורבו ומלאו את הארץ וכבשה ורדו בדגת הים ובעוף השמים ובכל חיה הרמשת על הארץ 28
Mulungu anawadalitsa nati kwa iwo, “Muberekane, muchulukane, mudzaze dziko lapansi ndipo muligonjetse. Mulamulire nsomba zamʼnyanja, mbalame zamlengalenga ndi cholengedwa chamoyo chilichonse chimene chimayenda mokwawa pa dziko lapansi.”
ויאמר אלהים הנה נתתי לכם את כל עשב זרע זרע אשר על פני כל הארץ ואת כל העץ אשר בו פרי עץ זרע זרע לכם יהיה לאכלה 29
Kenaka Mulungu anati, “Ine ndakupatsani chomera chilichonse cha pa dziko lapansi chimene chili ndi mbewu komanso mtengo uliwonse wobala zipatso zokhala ndi mbewu mʼkati mwake kuti zikhale chakudya chanu.
ולכל חית הארץ ולכל עוף השמים ולכל רומש על הארץ אשר בו נפש חיה את כל ירק עשב לאכלה ויהי כן 30
Ndaperekanso msipu kwa nyama zonse za pa dziko lapansi ndi kwa mbalame zamlengalenga ndi kwa cholengedwa chamoyo chilichonse chimene chimakwawa, chilichonse chimene chili ndi moyo.” Ndipo zinachitikadi.
וירא אלהים את כל אשר עשה והנה טוב מאד ויהי ערב ויהי בקר יום הששי 31
Mulungu anaona zonse zimene anazilenga kuti zinali zabwino kwambiri. Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa, tsiku lachisanu ndi chimodzi.

+ בראשית 1 >